Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Miyambo ya Khirisimasi—Kodi Ndi Yachikristu?

Miyambo ya Khirisimasi—Kodi Ndi Yachikristu?

 Miyambo ya Khirisimasi​—Kodi Ndi Yachikristu?

NYENGO ya Khirisimasi yafika. Kodi zimenezo zimatanthauza chiyani kwa inu, banja lanu, ndiponso mabwenzi anu? Kodi ndi mwambo wauzimu, kapena kodi ndi nthaŵi yachikondwerero? Kodi ndi nthaŵi yokumbukira za kubadwa kwa Yesu Kristu kapena nthaŵi yokhala womasuka ku makhalidwe achikristu?

Pamene mukulingalira za mafunso amenewo, kumbukirani kuti miyambo ya Khirisimasi ingathe kusiyana malinga ndi komwe mukukhala. Mwachitsanzo, ku Mexico ndi ku mayiko ena a ku Latin America, ngakhale dzina la Khirisimasi ndi linanso. Buku lina lamaumboni limanena kuti dzina lachingelezi lakuti Khirisimasi “lachokera ku Chingelezi chakale chakuti Christes Masse, Misa ya Kristu.” Komabe, La Navidad, kapena kuti Kubadwa kwa Yesu, malinga ndi mmene mwambowu umatchulidwira m’madera ameneŵa a ku Latin America, umatanthauza kubadwa, kwa Kristu. Talingalirani za miyambo ina ya ku Mexico. Zimenezi zingakuthandizeni kukhala ndi malingaliro anuanu okhudza nyengo ya tchuthi imeneyi.

Miyambo ya Posadas, “Anzeru Atatu a Kum’maŵa,” ndi Nacimiento

Mapwando amayambika pa December 16 ndi mwambo wotchedwa posadas. Buku lakuti Mexico’s Feasts of Life limafotokoza kuti: “Ndi panyengo ya posadas, nyengo ya masiku asanu ndi anayi achikoka kwambiri kukafika m’kati mwa usiku wotsatizana ndi tsiku la Khirisimasi, pamene anthu amakumbukira za kuyendayenda kwa Yosefe ndi Mariya mu mzinda wa Betelehemu popanda wowaperekeza mpaka pamene wina anawakomera mtima n’kuwapatsa nyumba. Mabanja ndi mabwenzi awo amasonkhana pamodzi usiku uliwonse kuti achite zinthu zomwe zinachitika m’kati mwa masiku apafupi ndi kubadwa kwa Kristu.”

Malinga ndi mwambo, gulu la anthu limanyamula zithunzi za Mariya ndi Yosefe kupita nazo panyumba ina yake, likuimba nyimbo yopemphera malo ogona, kapena posada. Anthu omwe ali m’nyumbamo amaimba moyankha nyimboyo kufikira alendowo ataloledwa kuloŵa m’nyumbamo pomalizira pake. Ndiyeno pamayambika phwando, pamene ena​— omangidwa kumaso atanyamula ndodo​—amasinthanasinthana pamene akuyesayesa kuswa piñata, mtsuko waukulu wadothi ndi wokongoletsedwa umene amaulendeweretsa pachingwe. Akauswa, anthu opezekapowo amasonkhanitsa zinthu zomwe zinali m’kati mwake (masiwiti, zipatso, ndi zina zotero). Kenako pamakhala zakudya, zakumwa, ndi kuvina. Mapwando asanu ndi atatu a posadas amachitika kuyambira pa December 16 mpaka kukafika pa December 23. Pa 24, pamakhala phwando la Nochebuena (usiku wotsatizana ndi tsiku la Khirisimasi), ndipo mabanja amayesetsa kuti adyere pamodzi chakudya chamadzulo chapadera.

Posakhalitsa pamafika Tsiku la Chaka Chatsopano, lomwe limakhala ndi mapwando aphokoso kwambiri. Madzulo a January 5, Tres Reyes Magos (“anzeru atatu a kum’maŵa”) amayembekezeredwa kupatsa ana zidole. Chimake cha zimenezi chimakhala phwando la pa January 6, pamene anthu amadya rosca de Reyes (keke yozungulira yabowo pakati ngati mphete yakumanja). Pamene anthu akudya makeke ameneŵa, wina mu keke yake amapezamo kachidole kakang’ono kamene kamaimira khandalo, Yesu. Munthu yemwe wakapezayo ndiye amakonza ndi kuchititsa phwando lomaliza pa February 2. (M’madera ena pamakhala tizidole titatu, tomwe timaimira “anzeru atatu a kum’maŵa.”) Monga momwe mukuoneramu, kusangalala mogwirizana ndi Khirisimasi kumapitirirabe.

M’kati mwa nthaŵi imeneyi, nacimiento (chithunzi cha Kubadwa kwa Yesu) chimakhala chofala kwambiri. Kodi chimachitika n’chiyani? M’malo amene kumapezeka anthu ambiri chimodzimodzinso m’matchalitchi ndi m’nyumba, mumaimikidwa zidole zoumba kapena zosema (zikuluzikulu kapena  zing’onozing’ono). Zidolezo zimasonyeza Yosefe ndi Mariya atagwada moyang’ana chodyera cha ng’ombe mmene muli khanda. Kaŵirikaŵiri pamakhala abusa ndiponso Los Reyes Magos (“anzeru a kum’maŵa”). Zidolezo zimasonyeza zimenezi kukhala zikuchitikira m’khola, ndipo nthaŵi zina zinyama zingasonyezedwenso pamenepo. Komabe, chidole chofunika kwambiri chimakhala cha khanda longobadwa kumene, lomwe m’Chisipanya limatchedwa kuti el Niño Dios (Mulungu Mwana). Chidole cha khanda chimenechi chingakhale chitaimikidwa pamenepo usiku wotsatizana ndi tsiku la Khirisimasi.

Kupenda Bwinobwino Miyambo ya Kubadwa kwa Yesu

Ponena za phwando la Khirisimasi malinga ndi momwe anthu ambiri amalidziŵira padziko lapansi pano, buku lotchedwa The Encyclopedia Americana limati: “Miyambo yochuluka imene tsopano ndi ya Khirisimasi poyambirira sinali miyambo ya Khirisimasi koma inali miyambo yomwe inkachitika Chikristu chisanakhale ndi ina yosakhala yachikristu imene tchalitchi chachikristu chinayamba kuitsatira. Saturnalia, phwando lachiroma lomwe linkachitika m’katikati mwa December, ndilo maziko a miyambo yambiri ya kusangalala kochitika pa Khirisimasi. Mwachitsanzo, kuchita madyerero monkitsa, kupereka mphatso, ndi kuyatsa makandulo, zinatengedwa kuphwando limeneli.”

Ku Latin America, miyambo ya Kubadwa kwa Yesu imeneyo ingathe kuchitidwa pamodzi ndi miyambo ina. Mungathe kudabwa kuti, ‘Ndi yochokera kuti?’ Kunena mosapita m’mbali, anthu ambiri amene amafuna kutsatira Baibulo mosamalitsa kwambiri, amazindikira kuti miyambo ina ndi yochokera ku ziphunzitso za a Aztec. Nyuzipepala yotchedwa El Universal, ya mu mzinda wa Mexico City, inathirira ndemanga kuti: “Agulupa ochokera m’magulu osiyanasiyana anapezerapo mwayi pa mfundo yakuti masiku a mapwando a miyambo ya Amwenye ankafanana ndi masiku a mapemphero a Akatolika, choncho anagwiritsa ntchito zimenezi pofuna kuchirikiza ntchito yawo yolalikira ndi yaumishonale. Iwo analoŵetsa mapwando a milungu yachikristu m’malo mwa miyambo yokumbukira milungu ya mafuko a anthu omwe analiko Asipanya asanadze, anayambitsa mapwando ndiponso zochitachita zachizungu, komanso anaphatikizamo mapwando achimwenye, zimene zinayambitsa kuphatikizika kwa zikhulupiriro ndiponso miyambo. Pamenepa ndi pomwe kwenikweni panayambira mayina achimekisiko.”

 The Encyclopedia Americana imafotokoza kuti: “N’kale kwambiri pamene maseŵero a Kubadwa kwa Yesu anakhala mbali ya mapwando a Khirisimasi . . . Anthu amanena kuti Francis Woyera ndiye anayambitsa kuika crèche [zithunzi za modyera ziŵeto] m’tchalitchi.” Maseŵero ameneŵa osonyeza kubadwa kwa Kristu ankachitikira m’matchalitchi chakumayambiriro kwa ulamuliro wautsamunda m’dziko la Mexico. Maseŵeroŵa omwe cholinga chake chinali kuphunzitsa Amwenye za Kubadwa kwa Yesu, anali kukonzedwa ndi amonke a gulu lomwe linayambitsidwa ndi Francis Woyera. Pambuyo pake, mwambo wa posadas unakhala wotchuka kwambiri. Kaya panali cholinga chotani poyambirirapo, koma mmene miyambo ya posadas imachitidwira lerolino zimavumbula cholinga chake chenicheni. Ngati panyengo imeneyi mungakhale kuti muli ku Mexico, mungathe kuona kapena kuzindikira kanthu kenakake kamene wolemba nyuzipepala yotchedwa El Universal anatsindika kwambiri m’ndemanga yake, kuti: “Miyambo ya posadas, yomwe inkachitika n’cholinga chofuna kutikumbutsa za ulendo wa makolo a Yesu wofunafuna nyumba yomwe Mulungu Mwanayo akanabadwiramo, lerolino ndi masiku oledzera, kuchita zinthu mopitirira muyeso, kudya mopambanitsa, makhalidwe achabechabe, ndi masiku a ziwawa zosaneneka.”

Mwambo wa nacimiento unaonekera m’nthaŵi za ulamuliro wa Atsamunda mu Mexico kuchokera pa maseŵero oyambirira amene ankachitikira m’matchalitchi. Ngakhale kuti ena amaona mwambowu kukhala wochititsa chidwi, kodi umasonyeza molongosoka zimene Baibulo limanena? Limenelo ndi funso lofunika kwambiri. Pamene amuna omwe anthu amawatcha kuti anzeru atatu a kum’maŵa​—omwe kwenikweni anali openda nyenyezi​—anafika, Yesu limodzi ndi banja lake sanalinso kukhala m’khola. Panali patapita nthaŵi yaitali, ndipo banjali n’kuti likukhala m’nyumba. Mudzasangalala kudziŵa nkhani imeneyi kuchokera m’nkhani youziridwa yopezeka pa Mateyu 2:1, 11. Mungathenso kuona kuti Baibulo silinena kuti ndi openda nyenyezi angati amene analipo. *

Ku Latin America, anzeru atatu a kum’maŵa amaloŵa m’malo mwa Father Christmas. Komabe, monga momwe zimachitikiranso m’mayiko ena, makolo ambiri amabisa zidole m’nyumba mwawo. Ndiyeno m’maŵa wa January 6, ana amafufuza zidolezo, ndiye ngati kuti anzeru atatu a kum’maŵa ndiwo abweretsa. Kwa anthu ogulitsa zidole, imeneyi ndiyo nthaŵi yopanga ndalama, ndipo anthu ena apeza ndalama zochuluka kwambiri kuchokera pa zinthu zomwe anthu ambiri oona mtima amazidziŵa kuti ndi zinthu zongoyerekezera. Anthu ochuluka ndithu ngakhalenso ana ang’onoang’ono sakukhulupiriranso nthano yonena za anzeru atatu akum’maŵa. Ngakhale kuti anthu ena akukhumudwa chifukwa chakuti ena sakukhulupiriranso nthano imeneyi, kodi munthu wina aliyense angayembekezere chiyani ponena za chinthu chongoyerekezera chomwe chikuchirikizidwa kokha chifukwa cha mwambo ndiponso chifukwa cha malonda?

Khirisimasi, kapena mwambo wa Kubadwa kwa Yesu, siinkachitidwa ndi Akristu oyambirira. Ponena za nkhani imeneyi, buku lina lamaumboni limati: “Phwando limeneli silinkachitidwa m’zaka mazana oyambirira za tchalitchi chachikristu, chifukwa chakuti chizoloŵezi cha Akristu chinali chokumbukira za imfa za anthu odziŵika bwino m’malo mwa kukumbukira kubadwa kwa anthuwo.” Baibulo limagwirizanitsa kukondwerera masiku a kubadwa ndi zochita za anthu achikunja, osati ndi olambira oona a Mulungu.​—Mateyu 14:6-10.

Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti kuphunzira ndi kukumbukira zinthu zomwe zinachitika pa kubadwa kwa Mwana wa Mulungu n’kosapindulitsa.  Nkhani yoona ya m’Baibulo imapereka chidziŵitso ndiponso maphunziro, zomwe ndi zofunika kwa anthu onse amene akufuna kuchita chifuniro cha Mulungu.

Kubadwa kwa Yesu Malinga ndi Kafotokozedwe ka Baibulo

Mudzapeza chidziŵitso chodalirika chonena za kubadwa kwa Yesu m’Mauthenga Abwino a Mateyu ndi Luka. Amasonyeza kuti mngelo Gabrieli anafika kwa msungwana wosakwatiwa wotchedwa Mariya m’tauni ya ku Galileya yotchedwa Nazarete. Kodi anafikitsa uthenga wotani? “Taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzam’patsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo Iye adzachita ufumu pa banja la Yakobo ku nthaŵi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.”​—Luka 1:31-33.

Mariya anadabwa kwambiri ndi uthenga umenewu. Pokhala wosakwatiwa, iye anati: “Ichi chidzachitika bwanji, popeza ine sindidziŵa mwamuna?” Mngeloyo anayankha kuti: “Mzimu Woyera adzafika pa iŵe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iŵe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.” Mariya atazindikira kuti ichi chinali chifuniro cha Mulungu, ananena kuti: “Onani, mdzakazi wa Ambuye; kukhale kwa ine monga mwa mawu anu.”​—Luka 1:34-38.

Mngelo anauza Yosefe za kubadwa kodabwitsa kumeneku kotero kuti asasudzule Mariya, zinthu zimene ankaganiza kuti achite atamva kuti Mariya ali ndi pakati. Ndiyeno kenako, Yosefe anali wofunitsitsa kulandira udindo wosamalira Mwana wa Mulungu.​—Mateyu 1:18-25.

Ndiyeno lamulo la Kaisara Augusto linachititsa kuti Yosefe ndi Mariya achoke mu mzinda wa Nazarete, m’chigawo cha Galileya n’kupita ku Betelehemu, m’chigawo cha Yudeya, mzinda wa makolo awo, kuti akalembetse m’kaundula. “Ndipo panali pokhala iwo komweko, masiku ake a kubala anakwanira. Ndipo iye anabala mwana wake wamwamuna woyamba; nam’kulunga Iye m’nsalu, nam’goneka modyera ng’ombe, chifukwa kuti anasoŵa malo m’nyumba ya alendo.”​—Luka 2:1-7.

Luka 2:8-14 amafotokoza zomwe zinachitika pambuyo pake kuti: “Ndipo panali abusa m’dziko lomwelo, okhala kubusa ndi kuyang’anira zoŵeta zawo usiku. Ndipo mngelo wa Ambuye anaimirira pa awo, ndi kuŵala kwa Ambuye kunawaunikira kozungulira: ndipo anawopa ndi mantha aakulu. Ndipo mngelo anati kwa iwo, musawope; pakuti onani, ndikuuzani inu uthenga wabwino wachikondwerero chachikulu, chimene chidzakhala kwa anthu onse; pakuti wakubadwirani inu lero, m’mudzi wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye. Ndipo ichi ndi chizindikiro kwa inu: mudzapeza mwana wakhanda wokuta ndi nsalu atagona modyera. Ndipo dzidzidzi panali pamodzi ndi mngeloyo ambirimbiri a gulu la Kumwamba, natamanda Mulungu, nanena, Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.”

Openda Nyenyezi

Nkhani ya Mateyu imafotokoza kuti openda nyenyezi ochokera Kum’maŵa anabwera ku Yerusalemu kudzafunafuna kumene Mfumu ya Ayuda yabadwira. Mfumu Herode anasangalala kwambiri ndi zimenezi​—koma kusangalalako kunali kwachiphamaso. ‘Powatumiza ku Betelehemu, iye anati, Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzam’peza, mundibwezere mawu, kuti inenso ndidzadze kudzam’lambira iye.’ Openda nyenyeziwo anapeza mwanayo, “namasula chuma chawo, nam’patsa iye mitulo, ndiyo golidi ndi libano ndi mure.” Koma sanabwererenso kwa Herode. ‘Anachenjezedwa [ndi Mulungu, NW] m’kulota kuti asabwerere kwa Herode.’ Mulungu anagwiritsa ntchito mngelo kuti achenjeze Yosefe za malingaliro a Herode. Ndiyeno Yosefe ndi Mariya limodzi ndi mwana wawo anathaŵira ku Igupto. Kenako, poyesayesa kufuna kupha Mfumu yatsopanoyo, Mfumu yankhanzayo Herode, inalamulira anyamata kupha ana aamuna a m’dera la Betelehemu. Kodi ana ake anali ati? Ana a zaka ziŵiri zakubadwa ndi kucheperapo.​—Mateyu 2:1-16.

Kodi Tingaphunzirenji pa Nkhani Imeneyi?

Openda nyenyezi amene anadzacheza​—kaya anali angati​—sankalambira Mulungu woona. Baibulo lotchedwa La Nueva Biblia Latinoamérica (la mu 1989) limanena izi m’mawu a m’munsi, kuti: “Amagiwo sanali mafumu, koma alauli ndi ansembe a chipembedzo chinachake chachikunja.” Iwo anabwera mwa chidziŵitso chawo pa za nyenyezi zomwe ankazikhulupirira kwambiri. Kukanakhala kuti Mulungu anafuna kuwatsogolera kwa khandalo, iwo akanatsogoleredwa mwachindunji kumalo oyenerera osafunikiranso  kudzera ku Yerusalemu choyamba ndi kupita ku nyumba yachifumu ya Herode. Pambuyo pake, Mulungu analoŵererapo kuti asokoneze zochita zawo n’cholinga chofuna kuteteza mwanayo.

Kaŵirikaŵiri, panyengo ya Khirisimasi nkhani imeneyi imaphatikizidwa ndi zochitachita za m’nthano ndiponso zinthu zongolingalira chabe zomwe zimabisa mfundo yofunika kwambiri iyi: yakuti mwana ameneyu anabadwa kuti adzakhale Mfumu yaulemerero kwambiri, monga momwe zinafotokozedwera kwa Mariya ndiponso kwa abusa a ziŵeto aja. Yesu Kristu panopo salinso khanda, kapena mwana, ayi. Iye ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, umene posachedwapa udzafafaniza maulamuliro onse amene amatsutsana ndi chifuno cha Mulungu, ndipo iye adzathetsa mavuto onse a anthu. Ndiwo Ufumu womwe timapempha mu Pemphero la Ambuye.​—Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.

Mwa zimene angelo anauza abusa a ziŵeto aja, timaphunzira kuti onse amene akufunitsitsa kumva uthenga wabwino ali ndi mwayi wa kupulumuka. Awo amene ayanjidwa ndi Mulungu amakhala “anthu amene akondwera nawo.” Pali ziyembekezo zabwino kwambiri za mtendere padziko lonse mu Ufumu wa Yesu Kristu, koma anthu ayenera kukhala ofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu. Kodi nyengo ya Khirisimasi imalimbikitsa zimenezi, ndipo kodi nyengoyo imagwirizana ndi chifuno chimenecho? Anthu ambiri omwe ndi oona mtima amene akufuna kutsatira Baibulo akudziŵa kuti imeneyi si nkhani yochita kufunsa.​—Luka 2:10, 11, 14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Nkhani inanso siyenera kunyalanyazidwa: Pa mwambo wa nacimiento ku Mexico, mwanayo amatchulidwa kuti “Mulungu Mwana” chifukwa cha malingaliro akuti anali Mulungu mwiniyo yemwe anabwera padziko lapansi monga khanda. Koma Baibulo limalongosola Yesu kukhala Mwana wa Mulungu yemwe anadzabadwa padziko lapansi; sanali Mulungu mwiniyo kapena wolingana ndi Yehova, Mulungu wamphamvuyonse. Talingalirani za zoona zake za nkhani imeneyi, zomwe zafotokozedwa pa Luka 1:35; Yohane 3:16; 5:37; 14:1, 6, 9, 28; 17:1, 3; 20:17.

[Bokosi patsamba 4]

ENA ANGADABWE

M’buku lake lakuti The Trouble With Christmas, (Vuto la Khirisimasi) mkonzi Tom Flynn anafotokoza zomwe anapeza pambuyo pa kafukufuku wa zaka zingapo wokhudzana ndi Khirisimasi:

“Miyambo yambiri yomwe tsopano timaigwirizanitsa ndi Khirisimasi inayambira ku miyambo ya chipembedzo chachikunja chomwe chinkachitika Chikristu chisanayambe. Ina mwa miyambo imeneyi imakhudza zachikhalidwe, zachiwerewere, kapena za sayansi yachilengedwe zomwe zingachititse anthu ophunzira, amasiku ano odziŵa bwino zachikhalidwe kusiya miyamboyi ngati atamvetsetsa magwero ake.”​—Tsamba 19.

Atafotokoza mfundo zambirimbiri zochirikiza zonena zake, Flynn anafotokozanso mfundo yaikulu yakuti: “Chimodzi mwa zinthu zodabwitsa kwambiri ponena za Khirisimasi ndiko kuchepa kwake kwa zinthu zomwe zimachitika zomwe zilidi zachikristu. Titapatula miyambo yomwe inkachitika Chikristu chisanayambe, yambiri mwa imene ingatsaleyo si yachikristu chenicheni choyambiriracho.”​—Tsamba 155.

[Chithunzi patsamba 7]

Chilengezo cha kubadwa kwa Yesu chinayala maziko a ntchito yake ya m’tsogolo monga Mfumu yosankhidwa ya Mulungu