Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

 Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwasangalala kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, yesani kuyankha mafunso otsatiraŵa:

Kodi chofunika kwambiri ndi chiyani pothetsa kusamvana ndi munthu wina?

Choyamba tiyenera kuzindikira kuti tonse timakhala ndi maganizo olakwika. Ndiyeno tiyenera kulingalira kwambiri ngati ndife amene tayambitsa vutolo m’malo moganiza kuti ndi munthu winayo.​—8/15, tsamba 23.

Kodi “nthaŵi za kukonzanso zinthu zonse,” zotchulidwa pa Machitidwe 3:21 zidzachitika liti?

Kukonzanso kudzachitika kaŵiri. Koyamba, pali kukonzanso kwa paradaiso wauzimu kumene kwakhala kukuchitika kuyambira 1919. Kukonzanso kowonjezereka kudzachitika pamene dziko lathuli lidzabwezeretsedwa kukhala paradaiso weniweni.​—9/1, masamba 17, 18.

Monga mmene Miyambo 6:6-8 imanenera, kodi nyerere zilibe mfumu motani, ndipo zimatipatsa chitsanzo chabwino chotani?

Pokhala nyerere, pamakhala manthu, koma ntchito yake n’njoikira mazira basi ndi kukhala mayi wa nyerere zonsezo. Nyerere zimagwira ntchito mosatopa, nafenso tiyenera kutero, kuyesetsa kuti tichite bwino pantchito yathu, ngakhale ngati palibe wotiyang’anira.​—9/15, tsamba 26.

Popeza kuti Yosiya anamwalira pambuyo povulazidwa zedi kunkhondo, kodi ulosi wa Hulida wopezeka pa 2 Mafumu 22:20 wonena kuti Yosiya adzafa mu “mtendere” unali woona?

Inde, anafa mu mtendere m’lingaliro lakuti anamwalira tsoka la mu 609-607B.C.E. lisanachitike, pamene Ababulo anazinga ndi kuwononga Yerusalemu.​—9/15, tsamba 30.

N’chifukwa chiyani tinganene kuti Solomo anali kuyamikira mkazi ponena kuti ali “ngati mbaŵala yokonda ndi chinkhoma chachisomo [“mbuzi ya kumapiri yosiririka,” NW]”? (Miyambo 5:18, 19)

Mbuzi ya kumapiri yaikazi ndi yofatsa mwachibadwa komanso yokongola m’mapangidwe a thupi lake. Ngakhale zili choncho, imapirira ndipo imakaberekera m’malo a miyala ikuluikulu m’mapiri, malo osafikika kumene chakudya chili chosoŵa.​—10/1, masamba 30, 31.

Kodi Henry Grew ndi George Storrs anali ndani?

Amuna aŵiri ameneŵa anakhala ndi moyo m’zaka za m’ma 1800 ndipo anali ophunzira Baibulo akhama kwambiri. Grew anaphunzira kuti chiphunzitso cha Utatu si cha m’malemba, mofanana ndi kusafa kwa mzimu ndi moto wa helo. Storrs anazindikira kuti ena adzakhala ndi moyo kwamuyaya padziko lapansi. Anthu ameneŵa ndiwo anali akalambula bwalo a Charles Taze Russell, yemwe anayamba kusindikiza magazini ino mu 1879.​—10/15, masamba 26-30.

Kodi Mboni za Yehova zimaona motani njira zachipatala zogwiritsa ntchito magazi ako omwe pokupatsa chithandizo?

Mogwirizana ndi zikhulupiriro zawo za m’Baibulo, sasunga magazi awo omwe kuti kenako adzawaikenso m’thupi mwawo. Mkristu aliyense ayenera kudzisankhira yekha njira imene magazi ake adzasamalidwira pa opaleshoni, popimidwa, kapena pamene akulandira chithandizo cha mankhwala cha mtundu uliwonse. Ayenera kulingalira zimene Baibulo limanena ponena za magazi ndipo ayenera kukumbukira kuti anadzipereka kwathunthu kwa Mulungu.​—10/15, masamba 30, 31.

Kufufuza kumene kunachitika kumayambiriro a chaka chino kwasonyeza kuti Mboni za Yehova padziko lonse lapansi zikufunika chiyani kwenikweni?

Pakufunika Nyumba za Ufumu zoposa 11,000 m’mayiko omwe akutukuka kumene, momwe kupeza chuma kuli kovuta. Zopereka za Akristu a m’mayiko ambiri zikusonkhanitsidwa kuti zithandize m’kumanga Nyumba zosonkhaniramo zokwanira.​—11/1, masamba 30.

Kodi ndi mawu ena ati m’chilankhulo choyambirira amene agwiritsidwa ntchito m’Baibulo okhudzana ndi kulambira?

Limodzi ndi lei·tour·giʹa, lomwe latembenuzidwa kuti “utumiki wothandiza anthu.” Lina ndi la·treiʹa, lomwe latembenuzidwa kuti “utumiki wopatulika.” (Ahebri 10:11, NW; Luka 2:36, 37, NW)​—11/15, masamba 11-12.

Kodi ndi phunziro lofunika kwambiri liti limene tingaphunzire pankhani ya m’Baibulo ya Adamu ndi Hava?

Kuyesa mwanjira iliyonse kupeza ufulu wathuwathu wosadalira Yehova Mulungu ndi kupusa kwenikweni.​—11/15, masamba 24-7.

Kodi pali umboni wa m’Malemba wotani wosonyeza kuti Mulungu amapatsa mphamvu atumiki ake?

Davide, Habakuku, ndi mtumwi Paulo onseŵa anapereka umboni wakuti Yehova Mulungu anawapatsa mphamvu, kapena nyonga. (Salmo 60:12; Habakuku 3:19; Afilipi 4:13) Choncho, tingakhale otsimikiza kuti Mulungu ndi wofunitsitsa ndiponso wokhoza kutilimbikitsa.​—12/1, masamba 10, 11.