Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amapereka Mphamvu kwa Wotopa

Yehova Amapereka Mphamvu kwa Wotopa

 Yehova Amapereka Mphamvu kwa Wotopa

“[Yehova] alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.”​—YESAYA 40:29.

1. Perekani chitsanzo cha mphamvu zopezeka m’zinthu zolengedwa ndi Mulungu.

YEHOVA n’ngwamphamvu zopanda malire. Ndipotu zinthu zomwe analenga n’zamphamvu zochuluka kwabasi! Timaatomu tating’ono kwambiri​—tomwe timapanga thunthu la chinthu chilichonse​—n’tating’ono kwabasi mwakuti dontho limodzi lokha la madzi n’lopangidwa ndi maatomu 100 biliyoni biliyoni. * Chamoyo chilichonse m’pulaneti lathu lino chimadalira mphamvu zomwe maatomu a padzuŵa amatulutsa. Koma kodi pamafunika mphamvu ya dzuŵa yochuluka chotani kuti zinthu zikhale ndi moyo padziko lapansi? Dziko lapansi limangolandira tizigawo toŵerengeka chabe mwa mphamvu zonse zomwe dzuŵa limatulutsa. Ngakhale kuti zili choncho, kachigawo kochepa kameneko ka mphamvu ya dzuŵa komwe kamafika padziko lapansi n’kochuluka kwambiri kuposa mphamvu zonse zomwe zimagwiritsidwa ntchito m’mafakitale a padziko lonse.

2. Kwenikweni, kodi Yesaya 40:26 amanenanji zokhudza mphamvu za Yehova?

2 Kaya tikulingalira za maatomu kapena tatembenukira ku chilengedwe chonse, chomwe chikutichititsa chidwi ndicho mphamvu zozizwitsa za Yehova. N’zosadabwitsa kuti iye anati: “Kwezani maso  anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.” (Yesaya 40:26) Inde, Yehova ali “wolimba mphamvu,” ndipo ndiye Gwero la “mphamvu zazikulu” zomwe anazigwiritsa ntchito pokhazikitsa chilengedwe chonse.

Pakufunika Mphamvu Zoposa Zachibadwa

3, 4. (a) Kodi zina mwa zinthu zomwe zingatitopetse n’ziti? (b) Ndi funso liti lofunika kulilingalira?

3 Ngakhale kuti Mulungu mphamvu zake n’zopanda malire, anthu amatopa. Kulikonse komwe tingapite, timaonako anthu otopa. Amadzuka ali otopa, kupita kuntchito kapena kusukulu ali otopa, kubwerera kunyumba ali otopa, ndi kupita kukagona osati ali ongotopa chabe komanso ali olefuka. Ena amangofuna atapita kwinakwake n’kukapuma pang’ono. Monga atumiki a Yehova, nafenso timatopa, chifukwa chakuti moyo wathu wodzipereka mwaumulungu umafuna kuyesetsa mwamphamvu. (Marko 6:30, 31; Luka 13:24; 1 Timoteo 4:8) Ndipotu pali zinthu zinanso zambiri zimene zimatifoola nkhongono.

4 Ngakhale kuti ndife Akristu, mavuto omwe anthu onse amakumana nawo samatiphonya. (Yobu 14:1) Matenda, umphaŵi wazachuma, kapena mavuto enanso ofala m’moyo angatifoole, ndi mphamvu zake zolefulazo. Kuwonjezera pa mavuto ameneŵa kulinso mayesero ogwera okhawo omwe amazunzidwa chifukwa cha chilungamo. (2 Timoteo 3:12; 1 Petro 3:14) Chifukwa cha zisonkhezero zakudziko zatsiku ndi tsiku ndi kutsutsidwa kwa ntchito yathu yolalikira Ufumu, ena a ife tingalefuke kwabasi mwakuti tingaganize zochepetsa kaye changu chathu potumikira Yehova. Komanso, poyesetsa kuswa kukhulupirika kwathu kwa Mulungu, Satana Mdyerekezi akugwiritsa ntchito njira ina iliyonse yomwe angafune. Nanga tsono mphamvu zauzimu zomwe zingatithandize kuti tisaleme ndi kuleka tingazipeze motani?

5. N’chifukwa chiyani pakufunika mphamvu zoposa zaumunthu kuti tichite utumiki wachikristu?

5 Kuti tipeze nyonga zauzimu, tiyenera kudalira Yehova, Mlengi wamphamvuyonse. Mtumwi Paulo ananena kuti utumiki wachikristu udzafuna mphamvu zochuluka kuposa zachibadwa za anthu opanda ungwiro. Iye analemba kuti: “Tili ndi chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti mphamvu yoposa yachibadwa ikhale ya Mulungu ndipo osati yochokera mwa ife eni.” (2 Akorinto 4:7, NW) Akristu odzozedwa akuchita “utumiki wa chiyanjanitso” mothandizidwa ndi anzawo omwe ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi. (2 Akorinto 5:18; Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9) Popeza kuti anthu opanda ungwirofe tikugwira ntchito ya Mulungu m’kati mwa chizunzo, sitingathe kuigwira m’mphamvu zathu zokha. Yehova amatithandiza ndi mzimu wake woyera, ndipo pachifukwa chimenecho kufooka kwathu kumakweza mphamvu zake. Ndipotu tikutonthozedwa ndi chitsimikizo chakuti “Yehova achirikiza olungama”!​—Salmo 37:17.

‘Yehova Ndiye Mphamvu Yathu’

6. Kodi Malemba amatitsimikizira motani kuti Yehova ndiye Gwero la mphamvu zathu?

6 Atate wathu wakumwamba ndi “wolimba mphamvu” ndipo angathe kutilimbitsa mosavuta. Kwenikweni, akutiuza kuti: “[Yehova] alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu. Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu: koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziwombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.” (Yesaya 40:29-31) Chifukwa cha kuwonjezereka kwa zopsinja, nthaŵi zina tingadzimve ngati wothamanga wolema yemwe miyendo yake ikuoneka kuti yalefukiratu kwakuti sangathenso kupitiriza kuthamangako. Komatu tayandikira pothera kuthamanga liŵiro la kumoyo, ndipo sitiyenera kulekera panjira. (2 Mbiri 29:11) Mdani wathu, Mdyerekezi, akuyendayenda “monga mkango wobuma,” ndipo akufuna kutiletsa. (1 Petro 5:8) Tikumbukiretu kuti ‘Yehova ndiye mphamvu yathu, ndi chikopa chathu,’ ndipo wapereka zinthu zochuluka zothandiza ‘kulimbitsa olefuka.’​—Salmo 28:7.

7, 8. Kodi pali umboni wotani wakuti Yehova analimbitsa Davide, Habakuku, ndi Paulo?

7 Yehova anam’patsa Davide mphamvu yofunikayo kuti apitirizebe m’nthaŵi ya masautso aakulu. Ndiyeno, ndi chikhulupiriro chonse ndi chidaliro, Davide analemba kuti: “Mwa Mulungu tidzachita molimbika mtima, ndipo Iye adzapondereza otisautsa.”  (Salmo 60:12) Yehova analimbitsanso Habakuku kuti athe kumaliza ntchito yomwe anam’patsa monga mneneri. Habakuku 3:19 amati: “Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga, asanduliza mapazi anga ngati mbaŵala, nadzandipondetsa pa misanje yanga.” Chitsanzo china chodziŵikanso bwino n’cha Paulo, yemwe analemba kuti: “Ndikhoza zonse mwa [Mulungu] wondipatsa mphamvuyo.”​—Afilipi 4:13.

8 Mofanana ndi Davide, Habakuku, ndi Paulo, tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu akhoza kutilimbitsa ndikuti angathe kutipulumutsa ndi mphamvu zake. Popeza kuti tadziŵa kuti Ambuye Mfumu Yehova ndiye Gwero la “mphamvu” zathu, tsopano tiyeni tione zina mwa njira zomwe tingapezere nyonga zauzimu kuchokera m’zinthu zomwe Mulungu akugaŵira moŵirikiza.

Zogaŵira Zauzimu Zotipatsa Mphamvu

9. Kodi zofalitsa zachikristu zimachita mbali yofunika yotani potilimbitsa?

9 Kuphunzira Malemba mwakhama ndi thandizo la zofalitsa zachikristu kungatilimbitse ndi kutichirikiza. Wamasalmo anaimba kuti: “Wodala munthuyo . . . [yemwe] m’chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m’chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku. Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” (Salmo 1:1-3) Monga momwe timafunira kudya kuti thupi lathu likhalebe lamphamvu, n’kofunikanso kuti tizidya chakudya chauzimu choperekedwa ndi Mulungu kudzera m’Mawu ake ndi zofalitsa zachikristu kuti tikhalebe amphamvu mwauzimu. Choncho, phunziro latanthauzo ndi kusinkhasinkha n’zofunika kwabasi.

10. Kodi ndi liti pamene tingathe kupeza nthaŵi yophunzira ndi kusinkhasinkha?

10 Kusinkhasinkha m’zinthu “zakuya za Mulungu” n’kopindulitsadi. (1 Akorinto 2:10) Koma kodi ndi liti pamene tingapeze nthaŵi yosinkhasinkha? Isake, mwana wa Abrahamu “anatuluka kulingalira [“kuti akasinkhesinkhe,” NW] m’munda madzulo.” (Genesis 24:63-67) Wamasalmo Davide ‘anasinkhasinkha za Mulungu m’maulonda a usiku.’ (Salmo 63:6) Tingaphunzire Mawu a Mulungu ndi kuwasinkhasinkha m’maŵa, madzulo, usiku​—inde, panthaŵi ina iliyonse. Kuphunzira ndi kusinkhasinkha kotereku kumatsogolera ku chogaŵira chinanso cha Yehova cholimbitsa mwauzimu​—pemphero.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kupemphera nthaŵi zonse kukhala kofunika kwambiri?

11 Kupemphera kwa Mulungu nthaŵi zonse kumatithandiza kuti tikhale olimba. Chotero ‘tilimbiketu chilimbikire m’kupemphera.’ (Aroma 12:12) Nthaŵi zina, tingafunikire kupempha nzeru ndi mphamvu mwapadera kuti zitithandize kupirira chiyeso. (Yakobo 1:5-8) Tiyeninso tizithokoza ndi kutamanda Mulungu tikaona kukwaniritsidwa kwa zifuno zake kapena tikaona kuti watilimbitsa kuti tipitirizebe muutumiki wake. (Afilipi 4:6, 7) Tikamayandikira kwa Yehova nthaŵi zonse m’pemphero, sadzatinyalanyaza. “Taonani,” anaimba motero Davide, “Mulungu ndiye mthandizi wanga.”​—Salmo 54:4.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake woyera?

12 Atate wathu wakumwamba amatipatsa nyonga ndi kutilimbitsa mwa mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito. Paulo analemba kuti: “Ndipinda maondo anga kwa Atate . . . kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa mzimu wake, m’kati mwanu.” (Aefeso 3:14-16) Tingapempherere mzimu woyera, ndi chidaliro chakuti Yehova adzatidalitsa nawo. Yesu anafunsa kuti: Ngati mwana wapempha nsomba, kodi atate wake wachikondi angam’patse njoka? Ndithudi ayi. Choncho, anatsiriza ndi mawu akuti: “Ngati inu, okhala [ochimwa, ndikuti chifukwa cha kuchimwaku osasiyana kwenikweni ndi] oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye!” (Luka 11:9-13) Tiyeneratu kupemphera ndi chidaliro chonse ndikuti nthaŵi zonse tikumbukire kuti Mulungu ‘angalimbitse’ atumiki ake okhulupirika ndi mphamvu mwa mzimu wake.

 Mpingo Umatonthoza Mtima

13. Kodi misonkhano yachikristu tiyenera kuiona motani?

13 Yehova amatilimbitsa kupyolera m’misonkhano ya mpingo wachikristu. Yesu anati: “Kumene kuli aŵiri kapena atatu asonkhanira m’dzina langa, ndili komweko pakati pawo.” (Mateyu 18:20) Pamene Yesu amapereka lonjezo limeneli, ankafotokoza zinthu zofunika kwambiri zoti omwe akutsogolera m’mpingo azisamalire. (Mateyu 18:15-19) Ngakhale kuti ndi choncho, mawu akewo amagwiranso ntchito kwabasi pamisonkhano yathu yonse ya kumpingo, misonkhano yapadera, ndi misonkhano yachigawo, yomwe imayamba ndi pemphero ndi kutsiriza ndi pemphero lothera m’dzina lake. (Yohane 14:14) Choncho kukapezeka pa misonkhano yachikristu yoteroyo ndi mwayi waukulu zedi, mosasamala kanthu kuti osonkhana akhale ochepa kapena masauzande. Choterotu tisonyeze kuyamikira mapulogalamu ameneŵa omwe cholinga chake n’kuti atilimbikitse mwauzimu ndi kutisonkhezera ku chikondano ndi ntchito zabwino.​—Ahebri 10:24, 25.

14. Kodi khama la akulu achikristu timapindula nalo motani?

14 Akulu achikristu amapereka thandizo ndi chilimbikitso chauzimu. (1 Petro 5:2, 3) Paulo anathandiza ndi kulimbikitsa mipingo yomwe amaitumikira, monga momwe oyang’anira oyendayenda amachitira lerolino. Kwenikweni, iye analakalaka atakhalira limodzi ndi okhulupirira anzake kotero kuti athe kulimbikitsana nawo. (Machitidwe 14:19-22; Aroma 1:11, 12) Nthaŵi zonse tisonyezetu kuyamikira akulu akwathu ndi oyang’anira ena achikristu, omwe amachita mbali yaikulu kuti atilimbitse mwauzimu.

15. Kodi okhulupirira anzathu mu mpingo wathu ‘angatitonthoze mtima’ motani?

15 Okhulupirira anzathu a m’mpingo wathu angathenso ‘kutitonthoza mtima.’ (Akolose 4:10, 11) Monga ‘mabwenzi enieni’ angatithandize m’nthaŵi za mavuto. (Miyambo 17:17) Mwachitsanzo, atumiki a Mulungu okwana 220 atatulutsidwa m’ndende yachibalo ya Sachsenhausen yoyang’aniridwa ndi asilikali a Nazi m’chaka cha 1945, anali ndi mtunda wautali wa makilomita 200 wakuti ayende. Anayendera limodzi monga gulu, ndipo omwe anali ndi mphamvu ankakoka ngolo zochepa atakwezamo anzawo omwe anali atalefuka. N’zotsatira zotani? Paulendo wokaphedwa womwe unapululutsa miyoyo ya akaidi anzawo am’ndende yachibalo oposa 10,000, panalibe ndi mmodzi yemwe wa Mboni za Yehova amene anaphedwa. Nkhani ngati zimenezi zomwe zalembedwa m’zofalitsa za Watch Tower, kuphatikizapo mu Yearbook of Jehovah’s Witnesses ndi m’buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom, zikusonyeza kuti Mulungu amalimbitsa anthu ake, n’cholinga chakuti asabwerere m’mbuyo.​—Agalatiya 6:9. *

Kulimbitsidwa ndi Utumiki Wathu Wakumunda

16. Kodi kutenga nawo mbali nthaŵi zonse muutumiki kumatilimbitsa motani mwauzimu?

16 Kutenga nawo mbali m’ntchito yolalikira Ufumu nthaŵi zonse kumatilimbitsa mwauzimu. Ntchito imeneyi imatithandiza kuika malingaliro  athu onse pa Ufumu wa Mulungu ndi kuyembekezera umuyaya ndi madalitso ake. (Yuda 20, 21) Malonjezo a m’Malemba omwe timauza ena muutumiki wathu amatipatsa chiyembekezo ndipo amatitsimikizitsa mtima monga mneneri Mika, yemwe anati: “Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.”​—Mika 4:5.

17. Ndi malingaliro otani omwe aperekedwa okhudza phunziro la Baibulo lapanyumba?

17 Ubwenzi wathu ndi Yehova umalimba pamene tigwiritsa ntchito kwambiri Malemba pophunzitsa ena. Mwachitsanzo, pochititsa phunziro la Baibulo lapanyumba ndi buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, n’chinthu chanzeru kuŵerenga ndi kukambirana malemba angapo osonyezedwawo. Zimenezi zimathandiza wophunzirayo komanso zimakulitsa kuzindikira kwathu kwauzimu. Ngati wophunzira sakumvetsa mfundo inayake ya m’Baibulo kapena fanizo, mungathe kumaphunzira ndime zochepa nthaŵi zonse m’mutu umodzimodziwo wa m’buku la Chidziŵitso kufikira mutu umenewo mutaumaliza. Ndifetu okondwa kwabasi kuti timakonzekera bwino ndi kuchita khama moŵirikiza kuti tithandize ena kuyandikira kwa Mulungu!

18. Fotokozani chitsanzo chosonyeza momwe buku la Chidziŵitso likugwiritsidwira ntchito mopambana.

18 Chaka chilichonse, buku la Chidziŵitso likugwiritsidwa ntchito bwino zedi pothandiza anthu masauzande ambiri kuti akhale atumiki a Yehova odzipatulira, ndipotu ochuluka mwa ameneŵa n’ngoti Baibulo samalidziŵa n’komwe. Mwachitsanzo, mwamuna wina wachihindu wa ku Sri Lanka, ali mwana, anangomva Mboni ina ikufotokozera winawake za Paradaiso. Zaka zingapo zitadutsa mnyamatayu anafikira mlongoyo, ndipo posakhalitsa mwamuna wake anayamba kuphunzira naye Baibulo. Kwenikweni, mnyamatayu amapita tsiku ndi tsiku kukaphunzira, ndipo anamaliza kuphunzira buku la Chidziŵitso m’nthaŵi yochepa zedi. Anayamba kufika pa misonkhano yonse, analekeratu kupita ku chipembedzo chake chakale, ndipo anakhala wofalitsa Ufumu. Pamene amabatizidwa, anali atayamba kale kuphunzitsa Baibulo mwamuna wina yemwe amadziŵana naye.

19. Pamene tikufunafuna Ufumu choyamba, kodi tingakhale otsimikizira za chiyani?

19 Kufunafuna Ufumu choyamba kumatipatsa chimwemwe cholimbitsa. (Mateyu 6:33) Ngakhale kuti tikukumana ndi ziyeso zosiyanasiyana, tikupitirizabe kulengeza uthenga wabwino mokondwa komanso mwachangu. (Tito 2:14) Ambiri a ife tikukwaniritsa ziyeneretso zofunika kwa ofuna kuchita utumiki wa upainiya wanthaŵi zonse, ndipo ena akutumikira kumene alaliki a uthenga wabwino akufunika kwambiri. Kaya tikuchirikiza zinthu za Ufumu mwachimwemwe m’njira zimenezi kapena m’njira zina, tili ndi chidaliro chonse kuti Yehova sadzaiŵala ntchito zathu ndi chikondi zomwe tinazionetsera ku dzina lake.​—Ahebri 6:10-12.

Pitirizanibe mu Mphamvu ya Yehova

20. Kodi tingasonyeze motani kuti timayembekezera Yehova kutipatsa mphamvu?

20 Tiyeneratu kusonyeza, mulimonse mmene tingathere, kuti tili n’chiyembekezo mwa Yehova ndikuti tikudalira iye kutipatsa mphamvu. Tingachite zimenezo mwa kudzipindulitsa mokwanira ndi zogaŵira zauzimu zomwe watipatsa kudzera mwa ‘kapolo wokhulupirika.’ (Mateyu 24:45) Kuphunzira Mawu a Mulungu patokha kapena limodzi ndi mpingo mwa kugwiritsa ntchito zofalitsa zachikristu, kupemphera kuchokera mu mtima, thandizo lauzimu la akulu, zitsanzo zabwino za okhulupirira anzathu okhulupirika, ndiponso kutenga nawo mbali nthaŵi zonse muutumiki zili zina mwa zogaŵira zomwe zimalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova ndi kutipatsa mphamvu kuti tipitirizebe muutumiki wake wopatulika.

21. Kodi mtumwi Petro ndi mtumwi Paulo anasonyeza motani kufunika kwa mphamvu zopatsidwa ndi Mulungu?

 21 Ngakhale kuti ndife anthu ofooka, Yehova adzatilimbitsa kuti tichite chifuno chake ngati tim’dalira iye kaamba ka thandizo. Pozindikira kufunika kwa thandizo loterolo, mtumwi Petro analemba kuti: “Wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu am’patsa.” (1 Petro 4:11) Ndipo Paulo anasonyeza kuti amadaliradi mphamvu zopatsidwa ndi Mulungu pamene anati: “Ndisangalala m’maufoko, m’ziŵaŵa, m’zikakamizo, m’mazunzo, m’zipsinjiko, chifukwa cha Kristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akorinto 12:10) Tisonyezetu chidaliro chofananacho ndi kudzetsa ulemerero kwa Ambuye Mfumu Yehova wopereka mphamvu kwa otopa.​—Yesaya 12:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 1 Chiŵerengero chimenechi, kuti tichilembe m’manambala tingalembe 1 ndi maziro 20.

^ ndime 15 Ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani anthu a Yehova amafunikira mphamvu zoposa zachibadwa?

• Ndi umboni uti wa m’Malemba wosonyeza kuti Mulungu amalimbitsa atumiki ake?

• Kodi zina mwa zogaŵira zauzimu zomwe Yehova wapereka kuti atilimbitse n’zotani?

• Kodi tingasonyeze motani kuti timadalira Mulungu kuti ndiye adzatilimbitsa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 12]

Ubwenzi wathu ndi Yehova umalimbitsidwa pamene tigwiritsa ntchito Baibulo pophunzitsa ena