Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tumikirani Mulungu ndi Mzimu Wofunitsitsa

Tumikirani Mulungu ndi Mzimu Wofunitsitsa

 Tumikirani Mulungu ndi Mzimu Wofunitsitsa

“NDIDZAPEREKA ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu,” analemba choncho mtumwi Paulo. (2 Akorinto 12:15) Kodi mawu ameneŵa amakuuzani chiyani ponena za maganizo amene atumiki a Yehova ayenera kuyesetsa kukhala nawo? Malinga ndi mmene katswiri wina wamaphunziro a Baibulo ananenera, pamene Paulo analembera mawu amenewo Akristu a ku Korinto, ankanena kuti: “Ndikufunitsitsa kupereka mphamvu zanga, ndi nthaŵi yanga, komanso moyo wanga, ndi zonse zimene ndili nazo chifukwa cha moyo wanu, monga mmene tate amachitira ana ake mwachimwemwe.” Paulo anali wokonzeka “kuperekedwa konse” kapena “kutopa ndi kufookeratu,” ngati kuteroko kukanakhala kofunika kuti akwaniritse utumiki wake wachikristu.

Komatu, Paulo anachita zonsezo “mokondweratu.” Iye anali “wofunitsitsadi” kutero, limatero Baibulo la The Jerusalem Bible. Bwanji nanga inuyo? Kodi mukufunitsitsa kupereka nthaŵi yanu, mphamvu zanu, luso lanu, ndi chuma chanu kutumikira Yehova Mulungu ndi zofuna za ena, ngakhale kuteroko kungakuchititseni “kutopa ndi kufookeratu” nthaŵi zina? Ndipo kodi mungachite zimenezi “mokondweratu”?

Amakaniratu Kutumikira

Anthu ambiri samangokayika kutumikira Mulungu koma amakaniratu kutero. Ali ndi mzimu wosayamika, wodzigangira, ngakhale wopanduka. Satana ananyengerera Adamu ndi Hava kuti aganize mwanjira imeneyo. Iye anawanamiza kuti ‘adzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa’​—okhoza kudzisankhira okha chabwino ndi choipa. (Genesis 3:1-5) Amene ali ndi mzimu ngati umenewo masiku ano amaganiza kuti iwo ayenera kukhala ndi ufulu wonse wochita chilichonse chimene akufuna popanda kuyankha mlandu kwa Mulungu kapena popanda iye kuloŵererapo. (Salmo 81:11, 12) Iwo amafuna kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene ali nazo pa zofuna za iwo okha.​—Miyambo 18:1.

N’kutheka kuti maganizo anu sali ngati maganizo oipa ameneŵa. Mwina mumayamikiradi mphatso ya moyo umene muli nawo pakali pano ndiponso, ngakhale chiyembekezo chabwino kwambiri chokhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Salmo 37:10, 11; Chivumbulutso 21:1-4) Mungakhale mukum’yamikira kwambiri Yehova chifukwa cha ubwino wake kwa inu. Koma tonsefe tifunika kusamala ndi ngozi imene ilipo yakuti Satana angapotoze maganizo athu moti utumiki wathu n’kukhala wosavomerezedwa ndi Mulungu. (2 Akorinto 11:3) Kodi zimenezi zingachitike bwanji?

Kukhala Wofunitsitsa pa Utumiki N’kofunika

Yehova amafuna kuti tichite utumiki mofunitsitsa komanso ndi mtima wonse. Satikakamiza kuchita chifuniro chake. Satana ndiye amene amachita zonse zotheka kupanikiza anthu kapena kuwanyengerera kuti achite chifuniro chake. Ponena za kutumikira Mulungu, Baibulo limanena za udindo, malamulo, zofunika, ndi zina zotero. (Mlaliki 12:13; Luka 1:6) Komabe, cholinga chathu chachikulu potumikira Mulungu n’chakuti timam’konda.​—Eksodo 35:21; Deuteronomo 11:1.

 Ngakhale kuti Paulo anadzipereka kwambiri potumikira Mulungu, anadziŵa kuti kuteroko kukanakhala kopanda pake ngati ‘analibe chikondi.’ (1 Akorinto 13:1-3) Pamene olemba Baibulo amatcha Akristu akapolo a Mulungu, sanena za ukapolo weniweni wochita kum’panikiza munthu. (Aroma 12:11; Akolose 3:24) Zimene akutanthauza n’kugonjera Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu mofunitsitsa chifukwa chowakonda kwambiri kuchokera pansi pa mtima.​—Mateyu 22:37; 2 Akorinto 5:14; 1 Yohane 4:10, 11.

Utumiki wathu kwa Mulungu uyeneranso kusonyeza chikondi chakuya pokonda anthu. “Tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha,” analemba choncho Paulo kulembera mpingo wa ku Tesalonika. (1 Atesalonika 2:7) M’mayiko ambiri masiku ano, amayi ali ndi udindo walamulo wosamalira ana awo. Koma kunena zoona amayi ambiri satero chifukwa chongofuna kugonjera lamulo, amatero ngati? Ayi. Iwo amatero chifukwa chakuti amakonda kwambiri ana awo. Zoonadi, mayi wolera ana amakondwera kudzimana zinthu zambiri chifukwa cha ana ake! Chifukwa chakuti Paulo ‘anawakondanso koposa’ (NW) anthu amene anawatumikira, iye ‘anakondwera’ (‘anafunitsitsa,’ King James Version; ‘anakondwera kwambiri’ New International Version) kugwiritsa ntchito moyo wake weniweniwo powathandiza. (1 Atesalonika 2:8) Chikondi chimatisonkhezera kuti titsanzire chitsanzo cha Paulo.​—Mateyu 22:39.

Bwanji za Kukhala Wamphwayi pa Utumiki?

Inde, sitiyenera kulola kudzikonda kwathu kupose kukonda Mulungu ndi anthu. Chifukwatu, pangakhale ngozi yakuti tingatumikire ndi mitima iŵiri kapenanso mwamphwayi. Tingayambe ngakhale kuipidwa, inde kukwiya kuti sitikukhala mmene timafunira kukhalira m’moyo wathu. Zimenezi zinachitikira Aisrayeli ena amene anasiya kum’konda Mulungu koma n’kumam’tumikirako chabe chifukwa chakuti linali lamulo. N’chiyani chinatsatira? Kutumikira Mulungu kunakhala ‘cholemetsa’ kwa iwo.​—Malaki 1:13.

Nsembe iliyonse imene anapereka kwa Mulungu inayenera kukhala “yopanda chilema,” “yabwino koposa” imene anali nayo. (Levitiko 22:17-20; Eksodo 23:19, NW) Komabe, m’malo mopatsa Yehova nyama zawo zabwino koposa, anthu m’masiku a Malaki anayamba kupereka nyama zimene iwo sanazifune n’komwe. Kodi Yehova anachitanji? Iye anauza ansembe kuti: “Pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzam’komera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? . . . Ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira ku dzanja lanu?”​—Malaki 1:8, 13.

Kodi zimenezi zingachitike bwanji kwa wina aliyense wa ife? Nsembe zathu zingakhale ‘chotilemetsa’ ngati titasoŵa mtima ndi mzimu wofunitsitsadi. (Eksodo 35:5, 21, 22; Levitiko 1:3; Salmo 54:6; Ahebri 13:15, 16) Mwachitsanzo, kodi timapatsa Yehova “makombo” a nthaŵi yathu, titero kunena kwake?

Kodi alipo wina aliyense amene mofatsa angaganize kuti Mulungu akanalola ngati, pofuna kuthandiza, wina m’banja kapena Mlevi wachangu mwanjira ina yake akanaumiriza Mwisrayeli wosafunayo kuti asankhe nyama yake yabwino koposa yoti apereke nsembe pamene iye sanafune n’komwe kuti aipereke? (Yesaya 29:13; Mateyu 15:7, 8) Yehova anakana nsembe zoterozo ndipo pomaliza pake anakana anthu amene anapereka nsembezo.​—Hoseya 4:6; Mateyu 21:43.

Kukondwera Kuchita Chifuniro cha Mulungu

Kuti tichite utumiki umene Mulungu angalandire, tiyenera kutsanzira chitsanzo cha Yesu Kristu. “Sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma Ine.” (Yohane 5:30) Yesu anapeza chimwemwe chochuluka potumikira Mulungu mofunitsitsa. Yesu anakwaniritsa mawu olosera a Davide akuti: “Kuchita chikondwero [“chifuniro,” NW] chanu kundikonda, Mulungu wanga.”​—Salmo 40:8.

Ngakhale kuti Yesu anakondwera kuchita chifuniro cha Yehova, sikuti nthaŵi zonse kunali kwapafupi. Taganizani zimene zinachitika atangotsala pang’ono kuti agwidwe, kuzengedwa mlandu, ndipo kuphedwa. Pamene anali m’munda wa Getsemane, Yesu ‘anazingidwa ndi chisoni’ ndipo ‘anakhala Iye m’chipsinjo mtima.’ Anavutika kwambiri maganizo moti, pamene anali kupemphera,  “thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.”​—Mateyu 26:38; Luka 22:44.

N’chifukwa chiyani Yesu anapsinjika mtima choncho? Ndithudi sichinali chifukwa chodzikonda kapena kuti sanafune kuchita chifuniro cha Mulungu. Iye anali wokonzeka kufa, mpaka kukaniratu mawu a Petro akuti: “Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa Inu ayi.” (Mateyu 16:21-23) Yesu anali kuganiza mmene imfa yake yochititsa manyazi monga mpandu ikakhudzira Yehova ndi dzina Lake loyera. Yesu anali kudziŵa kuti Atate wake akamva ululu kwambiri kuona Mwana wawo wokondedwa akuphedwa mwanjira yankhanza ngati imeneyo.

Yesu anadziŵanso kuti iye anali kuyandikira nthaŵi yofunika kwambiri pa kukwaniritsidwa kwa cholinga cha Yehova. Mosakayika, kumvera mokhulupirika malamulo a Mulungu kukanasonyeza kuti Adamu akanatha kuchita chimodzimodzi. Kukhulupirika kwa Yesu kukanasonyeza poyera kuti zonena za Satana kuti anthu akamayesedwa sangatumikire Mulungu mofunitsitsa komanso mokhulupirika ndi bodza lamkunkhuniza. Pogwiritsa ntchito Yesu, Yehova pomaliza pake adzawononga Satana ndi kuchotsa zotsatira za chipanduko chake.​—Genesis 3: 15.

Ati ntchito kukula imene Yesu anali nayo! Dzina la Atate wake, mtendere wa chilengedwe chonse, ndi chipulumutso cha anthu zonsezo zinadalira kukhulupirika kwa Yesu. Podziŵa zimenezo, anapemphera kuti: “Atate, ngati n’kutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.” (Mateyu 26:39) Ngakhale pamene anali wopsinjika kwambiri, Yesu sanalephere pakufunitsitsa kwake kugonjera chifuniro cha Atate wake.

‘Mzimu Uli Wakufuna, Koma Thupi Lili Lolefuka’

Monga momwedi Yesu anapsinjikira maganizo kwambiri potumikira Yehova, tingayembekeze kuti Satana adzativutitsa ife monga atumiki a Mulungu. (Yohane 15:20; 1 Petro 5:8) Ndiponsotu, ndife opanda ungwiro. Ndiye ngakhale tikufunitsitsa kutumikira Mulungu, sizingakhale zapafupi kwa ife kutero. Yesu anaona mmene atumwi ake anavutikira kuti achite zonse zimene anawauza kuti achite. Ndiye chifukwa chake iye anati: “Mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.” (Mateyu 26:41) Iye analibe kufooka kulikonse kwachibadwa m’thupi lake langwiro laumunthu. Komabe, ankaganiza za kufooka kwa thupi la ophunzira ake, kupanda ungwiro kumene iwo analandira kwa Adamu wopanda ungwiro. Yesu anadziŵa kuti chifukwa cha kupanda ungwiro kobadwa nako kumene kumachititsa anthu kukhala ndi polekezera, iwo adzavutika pochita zonse zimene amafuna kuchita potumikira Yehova.

Choncho, tingamve ngati mmene mtumwi Paulo anamvera, amene anavutika kwambiri maganizo pamene kupanda ungwiro kunam’lepheretsa kutumikira Mulungu mokwanira. “Kufuna ndili nako,” analemba choncho Paulo, “koma kuchita chabwino sindikupeza.” (Aroma 7:18) Ifenso timaona kuti sitingathe kuchita bwinobwino zinthu zonse zabwino zimene timafuna kuchita. (Aroma 7:19) Sikuti zimakhala choncho chifukwa chakuti tili ndi mphwayi. Koma ndi chifukwa chakuti kufooka kwa thupi kumalepheretsa ngakhale kuyesetsa kwathu konse.

Tiyeni tisataye mtima. Ngati tikufunitsitsa ndi mtima wonse kuchita zonse zimene tingathe, ndithudi Mulungu adzalandira utumiki wathu. (2 Akorinto 8:12) Tiyeni ‘tichite changu’ kutsanzira mzimu wa Kristu wogonjera chifuniro cha Mulungu kotheratu. (2 Timoteo 2:15; Afilipi 2:5-7; 1 Petro 4:1, 2) Yehova adzafupa ndi kuthandiza mzimu wofunitsitsa wotero. Iye adzatipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa” kukwaniritsa zofooka zathu. (2 Akorinto 4:7-10, NW) Ndi thandizo la Yehova, ife mofanana ndi Paulo, ‘tidzapereka ndi kuperekedwa konse mokondweratu’ mu utumiki Wake wamtengo wapatali.

[Chithunzi patsamba 21]

Paulo anatumikira Mulungu mofunitsitsa mmene anathera

[Chithunzi patsamba 23]

Ngakhale pamene anapsinjika maganizo kwambiri, Yesu anachitabe chifuniro cha Atate wake