Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tingaphunzire ku Banja Loyamba la Anthu

Tingaphunzire ku Banja Loyamba la Anthu

 Tingaphunzire ku Banja Loyamba la Anthu

MULUNGU analiyang’ana Dziko Lapansi. Anali kulikonza kuti anthu akhalemo. Iye anaona kuti chilichonse chimene anali kupanga chinali chabwino. Inde, pamene ntchito imeneyi inatha, iye ananena kuti inali ‘yabwino ndithu.’ (Genesis 1:12, 18, 21, 25, 31) Komabe, asanamalize kwenikweni, Mulungu ananena za chinthu chinachake chimene sichinali ‘bwino.’ Inde, Mulungu sanapange chinachake chosakhala bwino. Kungoti chabe anali asanamalize kulenga. “Si kwabwino kuti munthu akhale yekha,” anatero Yehova. “Ndidzam’pangira wom’thangatira iye.”​—Genesis 2:18.

Chinali cholinga cha Yehova kuti banja la anthu likhale ndi moyo wosatha wathanzi, wachimwemwe, komanso ndi zinthu zambiri m’paradaiso padziko lapansi. Adamu anali tate wa anthu onse. Mkazi wake, Hava, anakhala  “amake wa amoyo onse.” (Genesis 3:20) Ngakhale kuti tsopano dziko lapansi likudzaza ndi mabiliyoni a mbadwa zawo, anthu si angwiro n’komwe.

Nkhani ya Adamu ndi Hava ndi yodziŵika bwino. Koma kodi ili ndi phindu lanji kwa ife? Kodi tingaphunzirenji pa zimene zinachitikira banja loyamba limeneli la anthu?

“Adalenga Iwo Mwamuna ndi Mkazi”

Pamene Adamu anali kutchula nyama mayina, anaona kuti nyamazo zinali ndi zinzake ndipo iye analibe. Choncho pamene iye anaona cholengedwa chokongola chimene Yehova anapanga ndi nthiti yake, anakondwera. Poona kuti mkazi yekhayo ndiye anali mbali ya thupi lake, Adamu analengeza kuti: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga, ndi mnofu wa mnofu wanga; ndipo adzatchedwa Mkazi, chifukwa anam’tenga mwa mwamuna.”​—Genesis 2:18-23.

Mwamuna anafunika “wom’thangatira.” Anali naye tsopano amene anali woyenereradi. Hava anali woyenera bwino ndithu kukhala wom’kwaniritsa Adamu​—posamalira munda wa mudzi wawo ndi nyama, pobala ana, ndiponso monga bwenzi lenileni lom’thandiza kuganiza mwanzeru ndi kum’chirikiza.​—Genesis 1:26-30.

Yehova anapereka chilichonse chabwino chimene banjali linafuna. Popititsa Hava kwa mwamuna wake ndipo mwa kuwalola kuti akhalire limodzi, Mulungu anakhazikitsa mwambo wa ukwati ndi banja umene anthu anali kudzatsatira. Nkhani ya pa Genesis imati: “Mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” Ndipo pamene Yehova anadalitsa banja loyamba ndi kuwauza kuti abalane, n’zachionekere kuti iye anafuna kuti mwana aliyense abadwe m’banja losamalira, lokhala ndi abambo ndi amayi kuti aliyang’anire.​—Genesis 1:28; 2:24.

“M’chifanizo cha Mulungu”

Adamu anali mwana wangwiro wa Mulungu, wopangidwa ‘m’chifanizo ndi m’chikhalidwe’ Chake. Koma popeza kuti “Mulungu ndiye mzimu,” kufanana kwake sikungakhale kwakuthupi. (Genesis 1:26; Yohane 4:24) Kufanana kwake ndi kwa mikhalidwe imene inapangitsa munthu kukhala wapamwamba kuposa nyama. Inde, kuyambira pachiyambi munthu anaikidwa mikhalidwe ya chikondi, nzeru, mphamvu, ndi chilungamo. Anapatsidwa ufulu wodzisankhira komanso mphamvu yokonda zauzimu. Nzeru yobadwa nayo yozindikira khalidwe labwino, kapena kuti chikumbumtima, inam’thandiza kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Munthu anali ndi nzeru zom’thandiza kusinkhasinkha chifukwa chimene anthu anakhalirako, kudziŵa zambiri ponena za Mlengi wake, ndi kufika podziŵana Naye. Choncho pokhala ndi zonsezo, Adamu anali ndi zonse zofunika kuti akwaniritse udindo wake woyang’anira ntchito ya manja a Mulungu ya padziko lapansi.

Hava Achimwa

Mosakayikira, Adamu sanachedwe kuuza Hava chinthu chimodzi chimene Yehova analetsa: Akanatha kudya zipatso za mitengo yonse m’mundamo kupatula umodzi​—mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa. Sanayenere kudya zipatso za mtengo umenewo. Ngati akanadya, anayenera kufa tsiku lomwelo.​—Genesis 2:16, 17.

Posakhalitsa, panabuka nkhani yokhudza chipatso choletsedwa. Hava inam’peza njoka, imene mzimu wosaoneka unagwiritsa ntchito kulankhulira. Kukhala ngati yosadziŵa kanthu, njokayo inafunsa kuti: “Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Hava anayankha kuti kunali kololedwa kudya chipatso cha mtengo uliwonse kupatula umodzi. Koma kenaka njokayo inatsutsa Mulungu, ikumauza mkaziyo kuti: “Kufa simudzafai; chifukwa adziŵa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.” Mkaziyo anayamba kuona mtengo woletsedwawo mwanjira ina. “Mtengo unali wabwino kudya, ndi . . . wokoma m’maso.” Atanyengedwa ndithu, Hava anaswa lamulo la Mulungu.​—Genesis 3:1-6; 1 Timoteo 2:14.

Kodi tchimo la Hava silikanapeŵeka? Ayi ndithu! Dziyerekezeni inuyo kukhala Hava. Mawu a njoka anapotozeratu zimene Mulungu ndi Adamu anali atanena. Mukanamva bwanji ngati  mlendo atsutsa winawake amene mumakonda ndi kum’khulupirira kukhala wabodza? Hava akanatha kutsutsa, kusonyeza kuipidwa ndi ukali, ngakhale kukana kumvetsera. Ndipo kodi njokayo ndi ndaninso yoti n’kukayikira chilungamo cha mawu a Mulungu ndi mawu a mwamuna wake? Polemekeza lamulo la umutu, Hava akanayamba wafunsira uphungu kaye asanachite chilichonse. N’zimene tiyenera kuchita ngati mwina tauzidwa zinthu zosiyana ndi malangizo ochokera kwa Mulungu. Koma pofuna kuti azidzisankhira yekha chabwino ndi choipa, Hava anakhulupirira mawu a Woyesayo. Poganizabe za mfundoyo, inam’kopa kwambiri. Iye analakwa kwabasi popitiriza kulakalaka zosayenera, m’malo moiŵala malingaliro amenewo kapena kukambirana nkhaniyo ndi mutu wa banja lake!​—1 Akorinto 11:3; Yakobo 1:14, 15.

Adamu Amvera Mawu a Mkazi Wake

Posakhalitsa, Hava ananyengerera Adamu kuti nayenso achimwe. Kodi tingakufotokoze bwanji kugonja kwake kosayesa kulimbako n’pang’ono pomwe? (Genesis 3:6, 17) Adamu anagwira njakata pankhani ya kukhulupirika. Kodi anayenera kumvera Mlengi wake, amene anam’patsa zinthu zonse, kuphatikizapo mkazi wake wokondedwa, Hava? Kodi Adamu adzafuna thandizo la Mulungu kuti adziŵe kuti atani tsopano? Kapena kodi adzagwirizana ndi mkazi wake? Adamu anadziŵa bwino lomwe kuti zimene Hava anayembekeza kupeza podya chipatso choletsedwa zinali zabodza. Mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analoŵa m’kulakwa.” (1 Timoteo 2:14) Choncho Adamu anachita kufuna kuti asamvere Yehova. Mantha ake akuti adzasiyana ndi mkazi wake mwachionekere anakula kuposa chikhulupiriro chake chakuti Mulungu anali ndi mphamvu yokonza zinthu.

Mmene Adamu anachitira kunali kudzipha yekha. Kunalinso kupha ana ake onse amene Yehova mwachifundo analola kuti abereke, popeza kuti onse anabadwa ochimwa oweruzidwa kufa.  (Aroma 5:12) Kuŵaŵa kwaketu kwa kusamvera ndi dyera lakelo!

Zotsatira za Uchimo

Zotsatira zake atangochimwa anali manyazi. M’malo mochita kuthamangira kukalankhula ndi Yehova mwaufulu, aŵiriwo anabisala. (Genesis 3:8) Ubwenzi wawo ndi Mulungu unatha. Atafunsidwa zimene anachita, iwo sanasonyeze chisoni, ngakhale kuti onse anadziŵa kuti anali ataswa lamulo la Mulungu. Podya chipatso choletsedwa chimenecho, iwo anakana ubwino wa Mulungu.

Pachifukwa chimenecho, Mulungu ananena kuti padzakhala ululu waukulu pobereka. Hava adzakhumba mwamuna wake, ndipo mwamunayo adzam’lamulira. Choncho poyesa kupeza ufulu anapeza zosiyaniratu ndi zimenezo. Adamu tsopano adzadya zochokera m’nthaka m’kusauka. M’malo moti adzikhuta mosavutikira mu Edene, iye adzazunzika kuti apeze zofunika m’moyo mpaka atabwerera kufumbi limene anapangidwira.​—Genesis 3:16-19.

Pomaliza, Adamu ndi Hava anathamangitsidwa m’munda wa Edene. Yehova anati: “Taonani, munthuyo akhala ngati mmodzi wa ife, wakudziŵa zabwino ndi zoipa: ndipo tsopano kuti asatambasule dzanja lake ndi kutenga za mtengo wa moyo, ndi kudya, ndi kukhala ndi moyo nthaŵi zonse. . . ” “Mawuŵa anathera m’malere,” anatero katswiri wamaphunziro Gordon Wenham, ndipo tiyenera kuganiza tokha mbali yotsalayo ya maganizo a Mulungu​—mwinamwake kuti, “koma ndim’thamangitse m’mundamu.” Nthaŵi zambiri, wolemba Baibulo amalemba maganizo onse a Mulungu. Koma panopa, Wenham akutero, “kusiyidwa kwa mawu omalizawo kumasonyeza changu chimene Mulungu anachita. Iye anali asanamalize n’komwe kulankhula pamene anawathamangitsa m’mundamo.” (Genesis 3:22, 23) Zitatero, zikuoneka kuti Yehova ndi anthu aŵiri oyambawo analekeratu kulankhulana.

Adamu ndi Hava sanafe mwakuthupi maola 24 a tsiku limenelo. Komabe, anafa m’lingaliro lauzimu. Potalikirana ndi Gwero la moyo kosadzabwereranso, iwo anayamba kufooka mpaka imfa. Taganizani kupweteka kwake ataona koyamba mmene imfa imakhalira pamene mwana wawo wamwamuna wachiŵiri, Abele, anaphedwa ndi Kaini, mwana wawo woyamba!​—Genesis 4:1-16

Zitachitika zimenezo, tikupeza kuti n’zochepa chabe zimene zimadziŵika ponena za banja loyamba limenelo la anthu. Mwana wawo wamwamuna wachitatu, Seti, anabadwa Adamu ali ndi zaka 130. Adamu anamwalira zaka 800 pambuyo pake, ali ndi zaka 930, atabereka “ana aamuna ndi aakazi.”​—Genesis 4:25; 5:3-5.

Phunziro kwa Ife

Kupatula kuvumbula chifukwa chake masiku ano anthu ali mu mkhalidwe woipa, nkhani ya banja loyambalo imatiphunzitsa phunziro lofunika kwambiri. Kuyesa mwanjira iliyonse kupeza ufulu wathuwathu wosadalira Yehova Mulungu ndi kupusa kwenikweni. Anthu amene ali anzerudi amakhulupirira Yehova ndi Mawu ake, osati chidziŵitso chawo chimene aganiza kuti ali nacho chokwanira. Yehova ndiye amatchula chimene chili chabwino ndi choipa, ndipo kuchita chabwino ndiko kum’mvera iye. Kulakwa ndiko kuswa malamulo ake ndi kunyalanyaza mfundo zake.

Mulungu anapereka ndipo akuperekabe zinthu zonse zimene anthu onse angafune​—moyo wosatha, ufulu, kukhutira, chimwemwe, thanzi labwino, mtendere, kutukuka, ndiponso kutulukira zinthu zatsopano. Komabe, kuti tipeze zonsezi, tiyenera kudziŵa kuti tifunika kudalira Atate wathu wakumwamba, Yehova kotheratu.​—Mlaliki 3:10-13; Yesaya 55:6-13.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]

Nkhani ya Adamu ndi Hava​—Kodi Ndi Nthano Chabe?

Kale Ababulo, Asuri, Aigupto, ndi ena ambiri ankakhulupirira kuti pachiyambi kunali paradaiso amene anatayika chifukwa cha uchimo. Nkhani zambiri zimanena za mtengo wa moyo​—chipatso chimene chikanapereka moyo wosatha kwa amene akanachidya. Choncho anthu amakumbukira kuti m’Edene munachitika chinachake chokhumudwitsa.

Masiku ano, anthu ambiri amakana nkhani ya m’Baibulo imeneyi ya Adamu ndi Hava akumati ndi nthano chabe. Komabe, asayansi ambiri amavomereza kuti mitundu ya anthu ndi banja limodzi lochokera ku gwero limodzi. Akatswiri ambiri azaumulungu zimawavuta kukana kuti zotsatira za tchimo loyambirira limene kholo lathu linachita zinayambukira anthu onse. Chikhulupiriro chakuti anthu anachokera ku magwero osiyanasiyana chingawakakamize kunena kuti tchimo loyambirira linachitidwa ndi makolo ambirimbiri. Kenaka, zimenezi zingawakakamize kukana kuti Kristu, “Adamu wotsirizayo,” anawombola anthu onse. Koma Yesu ndi ophunzira ake sanakumane ndi vuto ngati limenelo. Iwo anadziŵa kuti nkhani ya m’Genesis ndi yoona.​—1 Akorinto 15:22, 45; Genesis 1:27; 2:24; Mateyu 19:4, 5; Aroma 5:12-19.