Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Sunga Malangizo Anga, Nukhale ndi Moyo”

“Sunga Malangizo Anga, Nukhale ndi Moyo”

 “Sunga Malangizo Anga, Nukhale ndi Moyo”

ANALI mnyamata, wanzeru, “wokoma thupi ndi wokongola.” Mkazi wa bwana wake anali kufunitsitsa kukwaniritsa chilakolako chake champhamvu ndipo anali wolimba mtima. Atakopeka mosapeŵeka ndi mnyamata ameneyu, tsiku lililonse anayesa kum’nyengerera. “Ndipo panali, nthaŵi yomweyo, iye analoŵa m’nyumba kuti agwire ntchito yake; ndipo munalibe amuna a m’nyumba m’katimo. Ndipo mkazi anagwira iye chofunda chake, nati, Gona ndi ine.” Koma Yosefe, mwana wa kholo lakale Yakobo, anasiya chofunda chakecho nathaŵa mkazi wa Potifara.​—Genesis 39:1-12.

Komatu si aliyense amene amathaŵa chiyeso ngati chimenechi. Mwachitsanzo, talingalirani za mnyamata yemwe Mfumu Solomo ya Israyeli wakale inamuona akuyenda m’msewu usiku. Mkazi wadama atam’nyengerera, “mnyamatayo am’tsata posachedwa, monga ng’ombe ipita kukaphedwa.”​—Miyambo 7:21, 22.

Akristu akuchenjezedwa ‘kuthaŵa dama.’ (1 Akorinto 6:18) Mtumwi Paulo analembera Timoteo, wophunzira wachikristu wachinyamata kuti: “Thaŵa zilakolako za unyamata.” (2 Timoteo 2:22) Tikaona kuti tili m’mikhalidwe yomwe ingatiumirize kuchita dama, chigololo, kapena makhalidwe ena osayenera, nafenso tiyenera kuthaŵa mosazengereza monga momwe Yosefe anathaŵira mkazi wa Potifara. Kodi chingatithandize kulimba mtima kuti tichitedi zimenezo n’chiyani? M’chaputala 7 cha buku la m’Baibulo la Miyambo, Solomo akutipatsa malangizo amtengo wapatali. Iye akunena ziphunzitso zomwe zingatiteteze ku misampha ya anthu akhalidwe loipa. Koma si zokhazo, chifukwa akuvumbulanso njira zimene anthu akhalidwe loipaŵa amagwiritsa ntchito mwa kufotokoza momveka bwino zomwe zinachitikira mnyamata wina amene mkazi wachiwerewere anam’kopa ndi mawu onyengerera.

‘Manga Malangizo Anga ku Zala Zako’

Mfumu ikuyamba ndi malangizo onga a tate kuti: “Mwananga, sunga mawu anga, ukundike malangizo anga; sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo; ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.”​Miyambo 7:1, 2.

Makolo, makamaka atate, ali ndi udindo wopatsidwa ndi Mulungu wophunzitsa ana awo miyezo ya Mulungu ya chabwino ndi choipa. Mose analimbikitsa atate kuti: “Mawu aŵa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula aŵa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deuteronomo 6:6, 7) Ndipo mtumwi Paulo analemba kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Choncho malangizo akholo ofunika kuwasunga, kapena kuwaona monga amtengo wapatali, mwachionekere akuphatikizapo zikumbutso, malangizo ndi malamulo opezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo.

Ziphunzitso za makolo zingaphatikizepo malangizo ena​—malamulo am’banja. Ameneŵa n’ngopindulitsa kwa anthu am’banjamo. Inde, malinga ndi zosoŵa za m’banjamo, mabanja angathe kukhala ndi malamulo osiyanasiyana. Komabe, makolo ali ndi ntchito yosankha abwino omwe angathandize m’banja lawolo. Ndipo malamulo omwe amapangawo nthaŵi zambiri amasonyeza chikondi chawo chenicheni ndi kudera nkhaŵa moona mtima. Uphungu kwa achinyamata n’ngwakuti atsatire malamulo ameneŵa limodzi ndi ziphunzitso za m’Malemba zomwe makolo awo akuwapatsa. Inde, m’pofunika kuteteza malangizo oterowo “ngati mwana wa diso  lako”​—kuwasunga mosamala kwambiri. Imeneyo ndi njira yopeŵera zotsatira zosakaza za kunyalanyaza miyezo ya Yehova kotero kuti ‘tikhalebe ndi moyo.’

Solomo akupitiriza kuti: “Uwamange [malangizo anga] pa zala zako, uwalembe pamtima pako.” (Miyambo 7:3) Monga zala zomwe timaziona mosavuta ndikuti zimatithandiza pochita zomwe tikufuna, momwemonso zimene timaphunzira m’malangizo a m’Malemba kapena popeza chidziŵitso cha m’Baibulo ziyenera kumatikumbutsa nthaŵi zonse ndi kutitsogolera pa chilichonse chomwe timachita. Tilembe malangizoŵa pamtima pathu, kuwapanga kukhala chotisonkhezera.

Pokumbukira kufunika kwa nzeru ndi luntha, mfumu ikulimbikitsa kuti: “Nena kwa nzeru, ndiwe mlongo wanga; nutchule luntha mbale wako.” (Miyambo 7:4) Nzeru ndizo kukhoza kugwiritsa ntchito bwino chidziŵitso chopatsidwa ndi Mulungu. Nzeru tiyenera kuzikonda monga momwe tingakondere mchemwali wathu wokondedwa. Kodi luntha n’chiyani? Ndilo kudya mutu pankhani inayake ndi kumvetsa mfundo yake mwa kuzindikira mmene zigawo za nkhaniyo zikugwirizanira ndi nkhani yonse. Luntha tiyenera kumamatirana nalo nthaŵi zonse monga bwenzi la ponda apa m’pondepo.

N’chifukwa chiyani tiyenera kumamatira ku zomwe tikuphunzira kuchokera m’Malemba ndikuti tikulitse unansi wathu ndi nzeru ndi luntha? Cholinga n’chakuti “zi[ti]chinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mawu ake.” (Miyambo 7:5) Inde, kuchita zimenezo kudzatiteteza ku njira zokopa mwachinyengo za mlendo​—munthu wakhalidwe loipa. *

Mnyamata Akumana ndi ‘Mkazi Wochenjera’

Kenako mfumu ya Israyeli ikufotokoza chochitika chomwe yachiona ndi maso ake kuti: “Pa zenera la nyumba yanga ndinapenyera pa made ake; ndinaona pakati pa achibwana, ndinazindikira pakati pa ang’ono mnyamata wopanda nzeru, alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo, ndi kuyenda panjira ya ku nyumba yake; pa madzulo kuli sisiro, pakati pa usiku pali mdima.”​Miyambo 7:4-9.

Zenera lomwe Solomo ankasuzumira linali ndi made​—mwachionekere made ameneŵa anali amatabwa ndipo mwinamwake ozokotedwa mwaukatswiri. Pamene cheza cha dzuŵa lamadzulo chikuchepa, mdima wausiku ukugwa m’msewumo. Ndiyeno akuona mnyamata yemwe akuonekeratu kuti ali pangozi. Mopanda luntha, kapena kuti mosalingalira bwino, akuchita mopanda nzeru. N’zodziŵikiratu kuti akudziŵa bwino zochitika za m’dera lomwe wapitalo ndi zomwe zingam’chitikire kumeneko. Mnyamatayu akuyandikira “mphambano ya pa mkaziyo,” yomwe ili m’njira yopita kunyumba ya mkaziyo. Kodi mkaziyu ndani? Nanga akuchita chiyani?

 Mfumu yomwe inali kungoonerera ikupitiriza kuti: “Ndipo taona, mkaziyo anam’chingamira, atavala zadama wochenjera mtima, ali wolongolola ndi wosaweruzika, mapazi ake samakhala m’nyumba mwake. Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo, nabisalira pa mphambano zonse.”​Miyambo 7:10-12.

Momwe mkaziyu wavalira zangosonyezeratu cholinga chake. (Genesis 38:14, 15) Wavala mosadzilemekeza, monga mkazi wachigololo. Komanso, n’ngwochenjera mtima​—maganizo ake ndi “onyenga” zolinga zake “n’zaukathyali.” (An American Translation; New International Version) N’ngwolongolola ndi wosaweruzika, wamkamwa ndi wosaugwira mtima, wopokosera ndi wofuna zake zokha, wouma mtima ndi wamakani. M’malo mongokhala kunyumba, amakonda kukhala m’malo omwe anthu amangoti piringupiringu, kuima m’mphambano za m’misewu kuti akole yemwe wam’funa. Amadikira wina wake ngati mnyamata uja.

‘Mawu Ambiri Onyengerera’

Chotero mnyamata akukumana ndi mkazi wachiwerewere wamalingaliro ofuna kunyengerera mochenjera. Solomo ayeneratu kuti anachita chidwi zedi poona zimenezi! Iye akusimba kuti: “Anagwira mnyamatayo, nam’mpsompsona; nati kwa iye ndi nkhope yachipongwe, Nsembe za mtendere [zoyamika] zili nane; lero ndachita zoŵinda zanga. Chifukwa chake ndatuluka kudzakuchingamira, kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza.”​Miyambo 7:13-15.

Mkazi ameneyu ali m’pakamwa pochenjeretsa. Kankhope kali gwaa! Alankhula mawu akewo molimba mtima. Chilichonse chimene akunena, akuchinena mochenjera kwambiri kuti akope mnyamatayo. Mwa kunena kuti wapereka nsembe yoyamika tsiku lomwelo, ndi kuchita choŵinda chake, akufuna kudzionetsa ngati ndi wachilungamo, kutsimikizira kuti mkhalidwe wake wauzimu ndi wabwino. Nsembe zoyamika ku kachisi wa ku Yerusalemu zinkaphatikizapo nyama, ufa, mafuta, ndi vinyo. (Levitiko 19:5, 6; 22:21; Numeri 15:8-10) Popeza kuti wopereka nsembe amatha kutenga chigawo china cha nsembe yoyamika ndi kukadya limodzi ndi banja lake, choncho mkaziyu akufotokoza kuti kunyumba kwake kuli zakudya ndi zakumwa zochuluka. Mfundo yake n’njodziŵikiratu, iye akutanthauza kuti: Mnyamatayo akasangalala kwambiri kumeneko. Wachoka kunyumba kwakeko kwenikweni kudzafunafuna iyeyu basi. Komatu munthu atati akhulupirire nkhani imeneyo ingam’gwire mtima kwabasi koma angalembe m’madzi. Katswiri wina wodziŵa za Baibulo anati: “N’zoona kuti anatuluka kukafunafuna winawake, koma kodi anatuluka kukafuna mnyamata wake ameneyu yekha basi? Wopanda nzeru​—mwinamwake mnyamata ameneyu​—ndi amene angam’khulupirire mkaziyu.”

Atadzikometsera ndi zovala zake, ndi mngoli wa timawu take tosyasyalika, ndi mmene anam’kumbatirira mnyamatayu, komanso mmene anam’mpsompsonera, mkazi wonyengerera ameneyu akufuna am’kope pogwiritsa ntchito zonunkhira. Akuti: “Ndayala zopfunda pakama panga, nsalu zamaŵangamaŵanga za thonje la ku Aigupto, ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira a mvunja ndi chisiyo ndi mtanthanyerere.” (Miyambo 7:16, 17) Wayala kama wake mwaukatswiri ndi nsalu zokongola za ku Aigupto ndi kuthirapo mafuta onunkhira apamtima pake a mvunja, chisiyo, ndi mtanthanyerere.

“Tiye tikondwere ndi chikondano mpaka mamaŵa,” iye akupitiriza motero, “tidzisangalatse ndi chiyanjano,” [“tisangalatsane ndi chikondi,” NW]. Akumuitanira zinazake osati chakudya chokoma chokha cha anthu aŵiri. Akum’lonjeza kukasangalala mwa kugonana. Kwa mnyamatayu, pempholitu n’lochititsa chidwi ndi losangalatsa! Popitiriza kum’nyengerera, akunena kuti: “Pakuti mwamuna kulibe kwathu, wapita ulendo wa kutali; watenga thumba la ndalama m’dzanja lake, tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.” (Miyambo 7:18-20) Akum’tsimikizira kuti palibe aliyense adzawapezerera, chifukwa chakuti mwamuna wake wachoka wapita kukachita bizinesi ndipo akakhala kumeneko kwakanthaŵi ndithu asanabwerere kunyumba. N’katswiridi pokopa mnyamata ndi mawu onyengerera! “Am’kakamiza ndi kukoka kwa mawu ake, am’patutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake.” (Miyambo 7:21) Munthu wanzeru ndi wakhalidwe labwino ngati Yosefe, ndi yekhayo angathe kupeŵa mawu onyengerera ngati  ameneŵa. (Genesis 39:9, 12) Kodi mnyamata uyu angathe kupeŵa mkhalidwewu?

‘Ngati Ng’ombe Yopita Kukaphedwa’

“Mnyamatayo am’tsata posachedwa, monga ng’ombe ipita kukaphedwa; ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru; mpaka muvi ukapyoza mphafa yake [“chiŵindi chake,” NW]; am’tsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziŵa kuti adzawononga moyo wake.”​Miyambo 7:22, 23.

Pempholi linali losapeŵeka kwa mnyamata ameneyu. Mopanda nzeru, akutsatira mkaziyu ‘monga ng’ombe yopita kukaphedwa’. Monga momwe mwamuna womangidwa unyolo m’miyendo sangathe kuthaŵa chilango, momwemonso mnyamatayo akukokedwera m’tchimo. Sakuona kuopsa kwake kufikira pamene ‘muvi upyoza chiŵindi chake,’ kapena kuti mpaka pamene walandira chilonda chomwe chingathe kumupha. Angafedi chifukwa chakuti angatenge matenda akupha opatsirana mwa kugonana. * Chilondacho chingamuphenso mwauzimu; ‘angawononge moyo wake.’ Umunthu wake wonse ndi moyo wake womwe zili pangozi yaikulu, ndipo wachimwira kwambiri Mulungu. Chotero athamangira m’msampha wa imfa monga mbalame yothamangira m’msampha!

“Usasochere M’mayendedwe Ake”

Kutengera phunziro pa zomwe waona, mfumu yanzeruyo ikuchenjeza kuti: “Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, labadirani mawu a m’kamwa mwanga. Mtima wako usapatukire ku njira ya mkaziyo, usasochere m’mayendedwe ake. Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa; ndipo ophedwa ndi iye achulukadi. Nyumba yake ndiyo njira ya kumanda, yotsikira ku zipinda za imfa.”​Miyambo 7:24-27.

Mwachionekere, malangizo a Solomoŵa n’ngakuti tipatuke m’njira zakupha za munthu wamakhalidwe oipa ‘nitikhale ndi moyo.’ (Miyambo 7:2) Malangizo ameneŵatu afika m’nthaŵi yake m’masiku athu ano! Ndithudi m’pofunika kupeŵa kupita m’malo omwe nthaŵi zonse m’makhala anthu adama akudikirira woti akachite naye chiwerewere. N’kupitiranji m’malo oterowo kukadzipereka ku njira zawo zokopa zachinyengozo? Indedi, mukhaliranji “wopanda nzeru” ndi kusochera potsata njira za “mlendo”?

“Mkazi wachiwerewere” yemwe mfumu inamuona anakopa mnyamata mochenjera mwa kumuitana kuti “asangalatsane ndi chikondi.” Kodi achinyamata ambiri​—makamaka atsikana​—sakukakamizidwa kuchita zosayenera m’njira ngati imeneyi? Koma taganizani: Pamene winawake ayesa kukukopani kuti mugone naye, kodi chimakhaladi chikondi chenicheni kapena amangofuna kukhutiritsa chilakolako chake chadyeracho? Kodi mwamuna yemwe amakondadi mkazi angam’kakamizirenji kuchita zosemphana ndi miyezo yachikristu ndi chikumbumtima chake? “Mtima wako usapatukire ku njira” zimenezo, akuchenjeza motero Solomo.

Mawu a munthu wonyengerera nthaŵi zambiri amakhala osalala ndi okopa mochenjera. Kukhala wanzeru ndi waluntha nthaŵi zonse kudzatithandiza kudziŵa cholinga chenicheni chamawuwo. Kukumbukira malangizo a Yehova nthaŵi zonse kudzatitchinjiriza. Chotero, tiyesetsetu nthaŵi zonse ‘kusunga malangizo a Mulungu, nitikhale ndi moyo’ kunthaŵi zonse.​—1 Yohane 2:17.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Mawu akuti “mlendo” ankagwiritsidwa ntchito potchula anthu amene anadzipanga okha kukhala adani a Yehova mwa kuchita zinthu zosemphana ndi Chilamulo. Chotero, mkazi wachiwerewere, monga hule, akutchedwanso “mlendo wamkazi.”

^ ndime 24 Matenda ena opatsirana mwa kugonana amawononga chiŵindi. Mwachitsanzo, chindoko chikafika poipa, tizilombo toyambitsa matendawo timawononga chiŵindi. Ndipo tizilombo tomwe timayambitsa matenda a chinzonono tingatupitse chiŵindi.

[Zithunzi patsamba 29]

Kodi malamulo a makolo m’mawaona motani?

[Chithunzi patsamba 31]

Kusunga malangizo a Mulungu kumateteza moyo