Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Makhalidwe Abwino Akumka Nachepa

Makhalidwe Abwino Akumka Nachepa

Makhalidwe Abwino Akumka Nachepa

“KALE zinthu zoterezi sizinkachitika,” anatero Helmut Schmidt, nduna yaikulu yakale ya dziko la Germany. Iyeyu anali kudandaula chifukwa cha nkhani za kusaona mtima kosaneneka kochitidwa ndi akuluakulu aboma, zomwe panthaŵiyo zinali zitalembedwa patsamba loyamba m’manyuzipepala. Iye anati: “Makhalidwe abwino atayika chifukwa cha dyera.”

Ambiri angavomerezane naye. Makhalidwe abwino ozikika m’Mawu a Mulungu, Baibulo, amenenso kuyambira kalekale avomerezedwa ndi anthu ambirimbiri kukhala osonyeza chomwe chili chabwino ndi choipa, akuonedwa ngati osafunika. Ndi mmene zilili ngakhale m’mayiko odziŵika monga achikristu.

Kodi Makhalidwe a M’Baibulo N’ngothandiza?

Makhalidwe ozikidwa m’ziphunzitso za m’Baibulo amaphatikizapo kuona mtima ndi kukhulupirika. Komabe, ukathyali, ziphuphu ndi katangale zili ponseponse. Nyuzipepala ya The Times ya ku London inati anthu ena apolisi “akuwaganizira kuti ankachita katangale n’kumapeza ndalama pafupifupi mapaundi 100,000 aliyense panthaŵi imodzi pozembetsa mankhwala osokoneza bongo omwe apolisi anzawo anali atalanda ndi kuwagulitsanso kapena potaya maumboni a milandu ya zigaŵenga zotchuka za m’magulu akuluakulu aupandu.” Chinyengo cha ma inshuwalansi akuti n’chofala zedi ku Austria. Ndipo ku Germany a zasayansi anazizwa pamene ofufuza posachedwapa anatulukira “umodzi wa milandu yochititsa manyazi kwambiri ya chinyengo mu sayansi ya ku German.” Pulofesa wina, amene ali “katswiri wotchuka koposa wa sayansi yokhudza chibadwa ku Germany,” anali kuimbidwa mlandu wonama kapena wopeka nkhani zambiri zachinyengo.

Makhalidwe ozikidwa m’Baibulo amaphatikizanso kukhulupirika m’banja, lomwe cholinga chake ndicho kupanga ubwenzi wosatha. Koma okwatirana ochuluka akuthetsa mabanja awo m’mabwalo amilandu. Nyuzipepala ya Katolika yotchedwa Christ in der Gegenwart (Mkristu Wamakono) inati “ngakhale ku Switzerland kumene anthu ‘amasunga mwambo,’ mabanja owonjezereka akutha.” Ku Netherlands, maukwati 33 pa maukwati 100 alionse amasudzulana. Mkazi wina amene anaona kusintha kwa makhalidwe a anthu ku Germany m’zaka zingapo zapitazo anadandaula mwa kulemba kuti: “Masiku ano anthu akuona ukwati ngati chinthu chachikale ndiponso wosuluka. Anthu sakukwatirana kuti adzakhalire limodzi moyo wawo wonse.”

Komabe, anthu mamiliyoni ochuluka amaona kuti miyezo ya makhalidwe abwino yomwe Baibulo limaphunzitsa n’njodalirika ndiponso yothandiza m’moyo m’dziko lathu lamakonoli. Banja lina lomwe likukhala m’malire a dziko la Switzerland ndi la Germany linazindikira kuti kuphunzira kukhala mogwirizana ndi makhalidwe a m’Baibulo kunaŵapatsa chimwemwe chochuluka. Kwa iwowo, “pali chinthu chimodzi chokha chotsogolera munthu m’moyo. Chinthu chimenecho ndicho Baibulo.”

Nanga inuyo mukulingalira bwanji? Kodi Baibulo lingathedi kutsogolera munthu modalirika? Kodi makhalidwe ophunziridwa m’Baibulo n’ngothandiza lerolino?