Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova

Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova

 Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova

YOSIYA mwana wazaka zisanu wa mfumu ya Yuda ayenera kuti wachita mantha. A Yedida omwe ali amayi ake akulira. Akulira chifukwa agogo ake aamuna, Mfumu Manase, amwalira.​—2 Mafumu 21:18.

Abambo a Yosiya, a Amoni, adzakhala mfumu ya Yuda tsopano. (2 Mbiri 33:20) Patapita zaka ziŵiri (659 B.C.E.), Amoni akuphedwa ndi anyamata ake. Anthu akupha achiwembuwo ndipo akulonga Yosiya mnyamatayo kukhala mfumu. (2 Mafumu 21:24; 2 Mbiri 33:25) Panthaŵi imene Amoni amalamulira, Yosiya anali atazoloŵera fungo la zofukiza limene linali guu m’Yerusalemu chifukwa cha maguwa a nsembe okhala pamadenga amene anthu amagwadirako milungu yonama. Ansembe achikunja anali kuoneka akuyendayenda, ndipo olambira​—ngakhale ena amene anali kudzinenera kuti akulambira Yehova​—anali kulumbira mwa mulungu wotchedwa Malikamu.​—Zefaniya 1:1, 5, NW.

Yosiya akudziŵa kuti Amoni anachita zoipa polambira milungu yonama. Mfumu ya Yuda yachinyamatayi ikumvetsetsanso zolengeza za Zefaniya mneneri wa Mulungu. Pamene Yosiya ali ndi zaka 15 (652B.C.E.), akulamulira chaka cha chisanu ndi zitatu ndipo watsimikiza kulabadira mawu a Zefaniya. Adakali mnyamatabe, Yosiya akuyamba kufunafuna Yehova.​—2 Mbiri 33:21, 22; 34:3.

Yosiya Aiyamba Ntchito!

Papita zaka zinayi tsopano ndipo Yosiya wayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu kuchotsa chipembedzo chonyenga (648 B.C.E.). Akuwononga mafano, milongoti yopatulika, ndi maguwa a nsembe zofukiza ogwiritsidwa ntchito ndi olambira Baala. Mafano a milungu yonama akuwapera kukhala aufaufa umenenso akuumwaza pa manda a anthu amene anali kupereka nsembe kwa milunguyo. Maguwa a nsembe amene anali kugwiritsidwa ntchito pa kulambira kodetsedwa akuwaipitsa kenako akuwawonongeratu.​—2 Mafumu 23: 8-14.

Ntchito yoyeretsa ya Yosiya ili pachimake pamene Yeremiya, mwana wa wansembe wa Alevi, akufika ku Yerusalemu (647 B.C.E.). Yehova Mulungu wamuika mnyamatayo Yeremiya kukhala mneneri wake. Ndipotu akulengeza mwamphamvu uthenga wa Yehova kutsutsa chipembedzo chonyenga! Zaka za Yosiya, mfumu yachinyamatayo, sizinali zosiyana kwenikweni ndi za Yeremiya. Komabe, ngakhale kuti Yosiya walimba mtima pochita ntchito yake yoyeretsa ndiponso Yeremiya walengeza zinthu mopanda mantha, anthu mofulumira ayambiranso kulambira konyenga.​—Yeremiya 1:1-10.

Apeza Chinthu Chamtengo Wapatali!

Papita zaka zisanu tsopano. Yosiya wazaka 25 wakhala akulamulira kwa zaka pafupifupi 18. Akuitana Safani, mlembi; Maseya, kazembe wa mudzi; ndi Yoha wolemba mbiri. Mfumu ikulamula Safani kuti: ‘Uza Hilikiya, mkulu wa ansembe, atenge ndalama zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu azipereke kwa ogwira ntchito kuti akonze nyumba ya Yehova.’​—2 Mafumu 22: 3-6; 2 Mbiri 34:8.

Kuchokera m’mamaŵa, okonza kachisi ameneŵa akugwira ntchito mwakhama. Ndithudi Yosiya akuthokoza Yehova kuti ogwira ntchito akukonza mbali  za nyumba ya Mulungu zimene makolo ake ena oipa anawononga. Ntchito ili m’kati, Safani akubwera kudzamuuza zina zake. Nanga chimene wanyamulacho n’chiyani? Wanyamula mpukutu! Akufotokoza kuti Hilikiya Mkulu wa Ansembe wapeza “buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.” (2 Mbiri 34:12-18) Limene anapezalo mosakayikira linali buku lenileni la Chilamulo!

Yosiya akufunitsitsa kumva mawu onse a bukulo. Pamene Safani akuŵerenga, mfumuyo ikuyesetsa kuona mmene lamulo lililonse likugwirira ntchito kwa iye ndi kwa anthu ake. Makamaka akukondwera ndi mmene bukulo likufotokozera kwambiri za kulambira koona ndi kuneneratu za miliri ndi kuchotsedwa m’dziko zimene zingadze ngati anthu adziloŵetsa m’chipembedzo chonyenga. Podziŵa tsopano kuti malamulo ena a Mulungu sanatsatiridwe, Yosiya akung’amba chovala chake nalamula Hilikiya, Safani, ndi ena kuti: ‘Funsirani kwa Yehova za mawu a buku ili; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvera mawu a buku ili.’​—2 Mafumu 22:11-13; 2 Mbiri 34:19-21.

Auzidwa Mawu a Yehova

Amithenga a Yosiya apita kwa Hulida mneneri wamkazi ku Yerusalemu ndipo abwerako ndi mawu. Hulida wawauza mawu a Yehova, kunena kuti masoka amene analembedwa m’buku limene langopezedwa kumenelo adzagweradi mtundu wopandukawo. Komabe, chifukwa cha kudzichepetsa kwake pamaso pa Yehova Mulungu, Yosiya sadzaona masokawo. Adzam’sonkhanitsa kukhala ndi makolo ake ndipo adzatengedwa aloŵe m’manda mwake mwamtendere.​—2 Mafumu 22:14-20; 2 Mbiri 34:22-28.

Popeza kuti Yosiya anamwalira kunkhondo, kodi ulosi wa Hulida unali wolondola? (2 Mafumu 23:28-30) Inde, popeza kuti “mtendere” umene anatengedwa nawo kuloŵa m’manda ndi wosiyana ndi “choipa” chimene chidzafikira Yuda. (2 Mafumu 22:20; 2 Mbiri 34:28) Yosiya anamwalira tsoka la mu 609-607 B.C.E. lisanachitike pamene Ababulo anazinga ndi kuwononga Yerusalemu. Ndipo ‘kusonkhanitsidwa kukhala ndi makolo’ kwenikweni sikulepheretsa wina kufa imfa yachiwawa. Mawu onga ameneŵa amagwiritsidwa ntchito ponena zonse ziŵiri imfa yachiwawa kapena yosakhala yachiwawa.​—Deuteronomo 31:16; 1 Mafumu 2:10; 22:34, 40.

Kulambira Koona Kupita Patsogolo

Yosiya akusonkhanitsa anthu a Yerusalemu kukachisi ndipo akuwaŵerengera “mawu onse a m’buku la chipangano” limene analipeza m’nyumba ya Yehova. Kenako akuchita pangano “kutsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mawu a chipangano cholembedwa m’buku ili.” Anthu onse aimira panganoli.​—2 Mafumu 23:1-3.

Mfumu Yosiya ikuchita ndawala inanso imene mwachionekere n’njaikulu kwambiri yothetsa kupembedza mafano. Ansembe a milungu yachilendo a Yuda akuchotsedwa. Alevi ansembe ochita nawo kulambira kodetsedwa akuwalanda udindo wawo wotumikira kuguwa la nsembe la Yehova, ndipo misanje imene inamangidwa nthaŵi ya ulamuliro wa Mfumu Solomo akuiipitsa kukhala yosayenera kulambirira. Kuyeretsako kukuphatikizapo madera a ufumu wakale wa mafuko khumi a Israyeli, umene unawonongedwa kalelo ndi Asuri (740 B.C.E.).

Pokwaniritsa mawu amene ananenedwa zaka 300 pasadakhale ndi “munthu wa Mulungu woona” amene sanatchulidwe dzina lake, Yosiya akutentha mafupa a ansembe a Baala paguwa la nsembe limene Mfumu Yerobiamu 1 anamanga ku Beteli. Misanje ikuchotsedwa kumeneko ndi ku mizinda ina. Ndiponso ansembe opembedza mafano akuphedwera pamaguwa a nsembe omwewo amene ankatumikirako.​—1 Mafumu 13:1-4; 2 Mafumu 23:4-20.

Phwando Lalikulu la Paskha Lichitika

Mulungu akuchirikiza ntchito ya Yosiya yolimbikitsa kulambira koyera. Pamoyo wake wonse, mfumuyo idzathokoza Mulungu kuti anthu “sanapambuka kusam’tsata Yehova Mulungu wa makolo awo.” (2 Mbiri 34:33) Ndipo kodi Yosiya angaiŵale bwanji zodabwitsa zimene zinachitika pamene anali kulamulira chaka chake cha 18?

Mfumu ikulamulira anthu ake kuti: “M’chitireni Yehova Mulungu wanu Paskha, monga mulembedwa m’buku ili [limene lapezedwa kumeneli] la chipangano.” (2 Mafumu 23:21) Yosiya akukondwera kuona anthu akulabadira. Ndipo paphwando limeneli, akupereka zoweta za Paskha 30,000 ndi ng’ombe 3,000. Analitu Paskha wadzaoneni! Pazopereka zakezo, makonzedwe olinganizidwa bwino komanso  chiŵerengero cha olambira, Paskhayo anaposa Paskha wina aliyense amene anachitika kuyambira masiku a mneneri Samueli.​—2 Mafumu 23:22, 23; 2 Mbiri 35:1-19.

Am’lira Kwambiri Atamwalira

Kwa zaka zonse 31 za kulamulira kwake (659-629 B.C.E.), Yosiya walamulira monga mfumu yabwino. Chakumapeto kwa ulamuliro wake, wamva kuti Farao Neko wakonza zodutsa m’Yuda kupita kukalimbana ndi magulu a nkhondo a Babulo pofuna kuthandiza mfumu ya Asuri pa Karikemisi ku mtsinje wa Firate. Pachifukwa chosadziŵika, Yosiya akupita kukamenyana ndi Mwaiguptoyo. Neko akutumiza amithenga kwa iye, kunena kuti: “Lekani kuvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuwonongeni.” Koma Yosiya akudzizimbaitsa ndipo akuyesa kuwabweza Aigupto ku Megido.​—2 Mbiri 35:20-22.

Zachisonitu kwa mfumu ya Yuda! Adani oponya mivi am’lasa. Ndipo iye akuuza anyamata ake kuti: “Ndichotseni ndalasidwa ndithu.” Akum’chotsa Yosiya m’galeta lake, kumuika m’galeta linanso ndi kubwerera naye ku Yerusalemu. Kumeneko kapena panjira yopita ku mzindawo, Yosiya akutsirizika, “nafa iye naikidwa m’manda a makolo ake,” ikutero nkhani youziridwayo. “Ayuda onse ndi Yerusalemu nalira Yosiya.” Yeremiya anamuimbira nyimbo yom’lira, ndipo pambuyo pake mfumuyo inali kutchulidwa m’nyimbo zamaliro zoimbidwa pa zochitika zapadera.​—2 Mbiri 35:23-25.

Inde, Mfumu Yosiya inachita cholakwa chodandaulitsa pamene inakachita nkhondo ndi Aigupto. (Salmo 130:3) Komabe, kudzichepetsa kwake ndi kulimbikira kulambira koyera kunachititsa kuti ayanjidwe ndi Mulungu. Moyo wa Yosiya ukusonyezeratu bwino kuti Yehova amayanja atumiki ake odzipereka komanso amtima wodzichepetsa!​—Miyambo 3:34; Yakobo 4:6.

[Chithunzi patsamba 29]

Mfumu Yosiya yachinyamata inafunafuna Yehova mwakhama

[Chithunzi patsamba 31]

Yosiya anawononga misanje nachirikiza kulambira koona