Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Nthaŵi Yake Siinafike”

“Nthaŵi Yake Siinafike”

 “Nthaŵi Yake Siinafike”

“Palibe wina anam’gwira kumanja, chifukwa nthaŵi yake siinafike.”​—YOHANE 7:30.

1. Kodi zochita za Yesu zinali kutsogoleredwa ndi zinthu ziŵiri ziti?

“MWANA wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri,” Yesu Kristu anawauza motero atumwi ake. (Mateyu 20:28) Poyankhula ndi kazembe wa Roma Pontiyo Pilato, Yesu anati: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Yesu anali kudziŵa bwino lomwe chifukwa chimene adzafera ndiponso ntchito imene ayenera kugwira asanafe. Anali kudziŵanso nthaŵi imene anali nayo kuti agwire ntchito yakeyo. Utumiki wake padziko lapansi monga Mesiya unali kudzakhala wa zaka zitatu ndi theka basi. Unayambika ndi ubatizo wake wa m’madzi mu mtsinje wa Yordano (mu 29 C.E.) kuchiyambi cha sabata la 70 lophiphiritsa loloseredwalo ndipo unathera pa imfa yake ya pamtengo wozunzirapo chapakati pa sabata limenelo (mu 33 C.E.). (Danieli 9:24-27; Mateyu 3:16, 17; 20:17-19) Chotero, zochita zonse za Yesu padziko lapansi zinali kutsogoleredwa ndi zinthu ziŵiri kwenikweni: cholinga cha kubwera kwake ndiponso kutsatira nthaŵi mosamalitsa.

2. Kodi Mauthenga Abwino amasonyeza Yesu Kristu kukhala munthu wotani, ndipo anasonyeza motani kuti akudziŵa bwino zimene anabwerera?

2 Nkhani za Mauthenga Abwino zimasonyeza Yesu Kristu kukhala munthu wachangu amene anayendayenda m’dziko lonse la Palestina, kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kuchita zozizwitsa zambiri zamphamvu. Ponena za chigawo choyambirira cha ntchito yake yamphamvu, timaŵerenga kuti: “Nthaŵi yake siinafike.” Yesu iyemwini anati: “Nthaŵi yanga siinakwanire.” Pamene utumiki  wake unali pafupi kutha, anagwiritsa ntchito mawu akuti “yafika nthaŵi.” (Yohane 7:8, 30; 12:23) Zonena ndi zochita za Yesu ziyenera kuti zinakhudzidwa ndi kudziŵa kwake bwino nthaŵi yoti achite ntchito yake yomwe anapatsidwa, kuphatikizapo imfa yake ya nsembe. Kumvetsa zimenezi kungatisonyeze zinthu zina ponena za umunthu wake ndi malingaliro ake, zomwe zidzatithandiza ‘kulondola mapazi ake’ mosamalitsa kwambiri.​—1 Petro 2:21.

Kwake Kunali Kuchita Chifuniro cha Mulungu

3, 4 (a) N’chiyani chimene chikuchitika pa phwando la ukwati ku Kana? (b) N’chifukwa chiyani Mwana wa Mulungu akukana pempho la Mariya lakuti athandize pamene vinyo wapereŵera, ndipo tikuphunzira chiyani pamenepa?

3 Chaka chake ndi cha 29 C.E. Pangopita masiku angapo kuchokera pamene Yesu anadzisankhira ophunzira ake oyamba. Onse tsopano afika pamudzi wa Kana m’dera la Galileya kuphwando laukwati. Mariya, amayi wa Yesu, alinso pomwepo. Vinyo watha. Pofuna kumuuza kuti athandizepo, Mariya akuuza mwana wake wamwamunayo kuti: “Alibe vinyo.” Koma Yesu akuyankha kuti: “Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu? Nthaŵi yanga siinafike.”​—Yohane 1:35-51; 2:1-4.

4 Yankho la Yesu lakuti, “Mkazi, ndili ndi chiyani ndi inu?” ndi kafunsidwe kakale kosonyeza kuti munthuyo sakufuna kuchita zimene akupemphedwa. N’chifukwa chiyani Yesu sakufuna kutsatira mawu a Mariya? Iye tsopano ali ndi zaka 30 zakubadwa. Pangopita milungu yochepa kuchokera pamene anabatizidwa, kudzozedwa ndi mzimu woyera, pamenenso Yohane Mbatizi anamutcha kuti “Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi.” (Yohane 1:29-34; Luka 3:21-23) Iye tsopano ayenera kutsogoleredwa ndi Wolamulira Wamkulu Koposa amene anam’tuma. (1 Akorinto 11:3) Palibe aliyense, ngakhale mbale wake weniweni, akanaloledwa kusokoneza ntchito imene Yesu anabwera kudzachita padziko lapansi. Yankho la Yesu kwa Mariya likusonyezadi kuti mtima wake unali pa kuchita chifuniro cha Atate wake! Ifenso tikhale ndi mtima womwewo pofuna kukwaniritsa “choyenera” chathu kwa Mulungu.​—Mlaliki 12:13.

5. Kodi ndi chozizwitsa chotani chimene Yesu Kristu akuchita ku Kana, ndipo anthu ena chikuwakhudza motani?

5 Atazindikira mfundo ya mawu a mwana wake, nthaŵi yomweyo Mariya akulabadira ndipo akulangiza otumikira kuti: “Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani.” Ndipo Yesu akuthetsa vuto la vinyolo. Akuuza otumikira kuti adzaze mitsuko ndi madzi, ndipo madziwo akuwasandutsa vinyo wokoma kwambiri. Zimenezi zikuchitika monga chiyambi cha mphamvu yochita zozizwitsa ya Yesu, kupereka chizindikiro chakuti mzimu wa Mulungu uli pa iye. Pamene ophunzira atsopano aona chozizwitsachi, chikhulupiriro chawo chikulimbitsidwa.​—Yohane 2:5-11.

Wachangu pa Nyumba ya Yehova

6. N’chifukwa chiyani Yesu akunyansidwa ndi zimene akuona pakachisi m’Yerusalemu, ndipo akuchitapo chiyani?

6 Posapita nthaŵi ndi m’ngululu ya 30 C.E., ndipo Yesu ndi anzakewo ali paulendo wa ku Yerusalemu kukachita Paskha. Ali kumeneko, ophunzira ake akuona Mtsogoleri wawo akuchita zinthu m’njira imene mwina sanamuonepo akuchita. Amalonda achiyuda adyera akugulitsa ziŵeto ndi mbalame za nsembe m’kati mwenimweni mwa kachisi. Ndipo akuzigulitsa pamtengo wokwera kwambiri kwa olambira achiyuda okhulupirika. Atanyansidwa kwakukulu, Yesu akuchitapo kanthu. Akutenga zingwe ndi kupanga mkwapulo ndipo akutulutsira amalondawo panja. Kenako akukhuthula ndalama za osintha ndalama, kugubuduza matebulo awo. “Chotsani izi muno,” akulamula ogulitsa nkhunda. Ophunzira a Yesu atamuona akuchita zinthu motengeka maganizo chotero, akukumbukira ulosi wonena za Mwana wa Mulungu wakuti: “Changu cha pa nyumba yanu chandidya ine.” (Yohane 2:13-17; Salmo 69:9) Ifenso tiyenera kupeŵa malingaliro a dziko mwachangu kuti asaipitse kulambira kwathu.

7. (a) N’chiyani chikupangitsa Nikodemo kuchezera Mesiya? (b) Kodi umboni umene Yesu anachitira kwa mkazi wachisamariya umatiphunzitsa chiyani?

7 Ku Yerusalemu komweko, Yesu akuchita zizindikiro zodabwitsa, ndipo anthu ambiri akum’khulupirira. Ngakhale Nikodemo, woweruza m’Sanihedirini, kapena kuti bwalo lamilandu lalikulu lachiyuda, akukopeka ndi Yesu ndipo akudza  kwa iye usiku kuti aphunzire zowonjezeka. Kenako, Yesu ndi ophunzira ake akukhala mu “dziko la Yudeya” pafupifupi miyezi isanu ndi itatu, kulalikira ndi kupanga ophunzira. Koma Yohane Mbatizi atamangidwa, iwo akutulukamo m’Yudeya kupita ku Galileya. Pamene akudutsa m’chigawo cha Samariya, Yesu akugwiritsa ntchito mpata wina kuchitira umboni wabwino kwa mkazi wachisamariya. Zimenezi zikupangitsa kuti Asamariya ambiri akhale okhulupirira. Ifenso tiyeni tizikhala okonzeka kuyankhula za Ufumu pamipata yabwino.​—Yohane 2:23; 3:1-22; 4:1-42; Marko 1:14.

Ntchito Yaikulu Yophunzitsa M’Galileya

8. Kodi Yesu akuyamba ntchito yotani m’Galileya?

8 “Nthaŵi” ya imfa ya Yesu isanakwane, iye adakali ndi ntchito yaikulu yoti achite mu utumiki wa Atate wake wakumwamba. Ku Galileya, Yesu akuyamba utumiki waukulu kusiyananso ndi umene anachita ku Yudeya ndi ku Yerusalemu. Iye akuyendayenda ‘m’Galileya monse, kuphunzitsa m’masunagoge mwawo, kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, kuchiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu.’ (Mateyu 4:23) Mawu ake odzutsa chidwi akuti: “Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira,” akumveka m’dera lonselo. (Mateyu 4:17) Patapita miyezi ingapo, pamene ophunzira aŵiri a Yohane Mbatizi afika kwa iye kudzadzimvera okha za Yesu, iye akuwauza kuti: “Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwawo, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphaŵi ulalikidwa Uthenga Wabwino. Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”​—Luka 7:22, 23.

9. N’chifukwa chiyani makamu akukhamukira kwa Kristu Yesu, ndipo tingatengepo phunziro lotani pamenepa?

9 ‘Mbiri yonena za Yesu ikubuka kudziko lonse loyandikira,’ ndipo makamu akukhamukira kwa iye​—kuchokera m’Galileya, ku Dekapoli, Yerusalemu, Yudeya, ndi kutsidya lina la Mtsinje wa Yordano. (Luka 4:14, 15; Mateyu 4:24, 25) Akudza kwa iye osati chabe chifukwa cha machiritso ake ozizwitsa komanso chifukwa cha kuphunzitsa kwake  kodabwitsa. Uthenga wake ndi wosangalatsa ndiponso wolimbikitsa. (Mateyu 5:1–7:27) Mawu a Yesu ndi achisomo ndiponso okondweretsa. (Luka 4:22) Makamuwo ‘akuzizwa ndi chiphunzitso chake’ chifukwa chakuti akuyankhula za m’Malemba monga mwinimphamvu. (Mateyu 7:28, 29; Luka 4:32) Ndani sangakopeke ndi munthu wotereyu? Ifenso tiyeni tikulitse luso la kuphunzitsa kotero kuti anthu oona mtima akopeke ndi choonadi.

10. N’chifukwa chiyani anthu a m’Nazarete akufuna kupha Yesu, nanga akulephereranji?

10 Komabe, si omvetsera onse a Yesu amene akusangalala. Ngakhale atangoyamba kumene utumiki, pamene akuphunzitsa m’mudzi wakwawo wa Nazarete, anthu akufuna kumupha. Ngakhale kuti anthu a m’mudzimo akudabwa ndi “mawu [ake] a chisomo,” iwo akufuna kuona zozizwitsa. Koma m’malo mochita zozizwitsa zamphamvu zambiri kumeneko, Yesu akuvumbula dyera lawo ndi kupanda kwawo chikhulupiriro. Atakwiya, awo amene ali m’sunagoge akuimirira, kum’gwira Yesu, ndi kupita naye kunja kuphiri kuti am’ponye kuphedi chozondoka. Koma akuwapulumuka m’manja ndi kuthaŵa. “Nthaŵi” ya imfa yake siinafikebe.​—Luka 4:16-30.

11. (a) Kodi atsogoleri ena achipembedzo akubwera kudzamvetsera Yesu pachifukwa chiti? (b) N’chifukwa chiyani Yesu akuimbidwa mlandu wa kuswa Sabata?

11 Atsogoleri achipembedzo​—alembi, Afarisi, Asaduki ndi ena​—kaŵirikaŵiri akumapezeka pamene Yesu akulalikira. Ambiri a iwo akupezekapo, osati kuti amvetsere ndi kuphunzira, koma kuti am’tole chifukwa ndi kumuyesa. (Mateyu 12:38; 16:1; Luka 5:17; 6:1, 2) Mwachitsanzo, pomwe ali ku Yerusalemu kudzachita Paskha wa mu 31 C.E., Yesu akuchiritsa mwamuna wina yemwe wakhala akudwala kwa zaka 38. Atsogoleri achipembedzo achiyuda akuimba mlandu Yesu wa kuswa Sabata. Akuwayankha kuti: “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, Inenso ndigwira ntchito.” Ayuda tsopano akumuimba mlandu wochitira mwano Mulungu ati chifukwa wanena kuti ndi Mwana wa Mulungu pomutcha kuti Atate. Akufuna kupha Yesu, koma iyeyo ndi ophunzira ake akutulukamo m’Yerusalemu kupita ku Galileya. Ifenso ndi bwino kupeŵa mikangano yosafunikira ndi anthu otsutsa pamene tikuthera nyonga yathu pa ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira.​—Yohane 5:1-18; 6:1.

12. Kodi Yesu akufola motani gawo lonse m’Galileya?

12 M’chaka chotsatira, mwinanso ndi theka kapena kuposapo, Yesu akuchitira utumiki wake wochulukira m’Galileya, kupita ku Yerusalemu kokha pokachita madyerero atatu apachaka a Ayuda. Onse pamodzi, wapanga maulendo atatu olalikira m’Galileya: ulendo woyamba ali ndi ophunzira anayi atsopano, wachiŵiri ndi atumwi 12, ndipo waukulu pamene akutumizanso atumwi ake ophunzitsidwawo. Ndi umboni waukulutu zedi wa choonadi womwe waperekedwa m’Galileya!​—Mateyu 4:18-25; Luka 8:1-3; 9:1-6.

Kuchitira Umboni Molimba Mtima M’Yudeya ndi M’Pereya

13, 14. (a) Kodi ndi pachochitika chotani pamene Ayuda akuyesa kugwira Yesu? (b) N’chifukwa chiyani anyamata akulephera kumanga Yesu?

13 Ndi m’dzinja la mu 32 C.E., ndipo “nthaŵi” ya Yesu idakali kutsogolo. Phwando la Misasa lili pafupi. Tsopano abale a Yesu om’peza akum’limbikitsa kuti: “Chokani pano, mumuke ku Yudeya.” Iwo akufuna kuti Yesu akasonyeze mphamvu zake zochita zozizwitsa kwa onse amene asonkhanira phwandolo ku Yerusalemu. Koma Yesu akudziŵa ngozi imene ilipo. Chotero akuuza abale akewo kuti: “Sindikwera Ine ku phwando ili tsopano apa; pakuti nthaŵi yanga siinakwanire.”​—Yohane 7:1-8.

14 Atakhala pang’ono m’Galileya, Yesu akupita ku Yerusalemu “si poonekera, koma monga mobisalika.” Ayuda akum’funafunadi paphwandopo, ndipo akuti: “Ali kuti uja?” Phwandolo lili pakati, Yesu akuloŵa m’kachisi ndi kuyamba kuphunzitsa molimba mtima. Akuyesa kum’gwira, mwina kuti am’ponye m’ndende kapena kumupha. Komabe, iwo akulephera chifukwa chakuti “nthaŵi yake siinafike.” Ambiri tsopano akukhulupirira Yesu. Ngakhale anyamata amene Afarisi anatuma kuti akam’gwire akubwerako chimanjamanja, nati: “Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.”​—Yohane 7:9-14, 30-46.

15. N’chifukwa chiyani Ayuda akutola miyala kuti am’ponye Yesu, ndipo ndi ntchito yotani yolalikira imene iye akuiyambitsa tsopano?

15 Kuwombana kwa Yesu ndi Ayuda om’tsutsa kukupitirira pamene iye akuphunzitsabe za Atate wake m’kachisi pamasiku a phwandolo. Tsiku lomaliza la phwandolo, atakwiya ndi mawu a Yesu  onena kuti analipo kale asanakhale munthu, Ayuda akutola miyala kuti am’ponye. Koma iye akubisala ndi kuthaŵa osavulazidwa. (Yohane 8:12-59) Atakakhala kunja kwa Yerusalemu, Yesu akuyamba ntchito yaikulu yolalikira m’Yudeya. Akusankha ophunzira 70 ndipo, atawalangiza, akuwatumiza aŵiriaŵiri kuti akafole gawo. Iwo akutsogola kufika kumalo ndi mudzi uliwonse umene Yesu, pamodzi ndi atumwi ake, akufuna kukafika.​—Luka 10:1-24.

16. Kodi Yesu akuthaŵa ngozi yotani pa Phwando la Kukonzetsanso, ndipo akutanganidwanso ndi ntchito yotani?

16 M’nyengo ya chisanu ya mu 32 C.E., “nthaŵi” ya Yesu ikuyandikira. Akufika ku Yerusalemu kudzachita Phwando la Kukonzetsanso. Ayuda akufunabe kumupha. Pamene Yesu akuyenda m’khumbi la kachisi, iwo akum’zinga. Pomuimbanso mlandu wochitira mwano Mulungu, iwo akutola miyala kuti amuphe. Koma monga momwe anachitira poyamba paja, Yesu akuthaŵa. Posapita nthaŵi iye ali mumsewu kuphunzitsa, panopo akuphunzitsa mumzinda ndi mzinda ndiponso mudzi ndi mudzi m’chigawo cha Pereya, kudutsa Yordano kuchokera ku Yudeya. Ndipo ambiri akum’khulupirira. Koma uthenga wonena za bwenzi lake Lazaro ukum’bweza ku Yudeya.​—Luka 13:33; Yohane 10:20-42.

17. (a) Ndi uthenga wofulumira wotani umene Yesu akuulandira pamene akulalikira ku Pereya? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu akudziŵa chifuno cha chinthu chimene akufuna kuchita ndi nthaŵi yabwino ya zochita zake?

17 Uthenga wofulumirawo wachokera kwa Marita ndi Mariya, alongo a Lazaro, amene amakhala ku Betaniya wa ku Yudeya. “Ambuye, onani, amene mum’konda adwala,” akulongosola motero mthenga. “Kudwala kumene sikuli kwa imfa,” akuyankha motero Yesu, “koma chifukwa cha ulemerero wa Mulungu, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe nako.” Kuti akwaniritse chifuno chimenechi, Yesu akuchedwera dala kumene ali kwa masiku aŵiri. Ndiyeno akuti kwa ophunzira ake: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” Posafuna kupita, iwo akuti: “Ambuye, Ayuda analikufuna kukuponyani miyala tsopano apa; ndipo mumkanso komweko kodi?” Koma Yesu akudziŵa kuti ‘maola a usana’ otsalirawo, kapena kuti nthaŵi imene Mulungu wam’patsa kuti achite utumiki wake padziko lapansi, ndi ochepa. Iye akudziŵa mwatsatanetsatane zimene ayenera kuchita komanso chifukwa chimene ayenera kuzichitira.​—Yohane 11:1-10.

Chozizwitsa Chosanyalanyazika ndi Munthu Aliyense

18. Pamene Yesu akufika ku Betaniya, kodi zinthu zili motani kumeneko, ndipo n’chiyani chikuchitika atafika?

18 Ku Betaniya, Marita ndiye woyamba kulonjera Yesu, ndipo akuti: “Ambuye, mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.” Mariya ndi awo amene anali atabwera kunyumba kwawo akutsatira m’mbuyo. Onse akulira. “Mwamuika iye kuti?” Yesu akufunsa motero. Iwo akuyankha kuti: “Ambuye, tiyeni, mukaone.” Atafika kumanda​—phanga lokhala ndi mwala wotsekera pakhomo pake​—Yesu akuti: “Chotsani mwala.” Posamvetsa zimene Yesu akufuna kuchita, Marita akudandaula kuti: “Ambuye, adayamba kununkha; pakuti wagona masiku anayi.” Koma Yesu akum’funsa kuti: “Kodi sindinati kwa iwe, kuti, ngati ukhulupira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”​—Yohane 11:17-40.

19. N’chifukwa chiyani Yesu akupemphera poyera asanaukitse Lazaro?

19 Pamene mwala wotseka pakhomo la manda a Lazaro uchotsedwa, Yesu akupemphera mokweza kuti anthu adziŵe kuti zimene adzachita zidzatheka mwa mphamvu ya Mulungu. Kenako akufuula ndi mawu aakulu kuti: “Lazaro, tuluka.” Lazaro akutuluka miyendo yake ndi manja ake zili zomangidwabe ndi nsalu zakumanda ndipo nkhope  yake ili yokutidwa ndi nsalu. Yesu akuti: “M’masuleni iye, ndipo m’lekeni amuke.”​—Yohane 11:41-44.

20. Kodi amene akuona Yesu akuukitsa Lazaro akutani?

20 Ataona chozizwitsa chimenechi, Ayuda ambiri amene anadza kudzatonthoza Marita ndi Mariya akhulupirira Yesu. Ena akupita kukauza Afarisi zimene zachitika. Kodi Afarisiwo akutani? Nthaŵi yomweyo mwadzidzidzi, iwo ndi ansembe aakulu akuitanitsa msonkhano wa Sanihedirini. Mothedwa nzeru, akudandaula kuti: “Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri. Ngati tim’leka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.” Koma Mkulu wa Ansembe Kayafa akuwauza kuti: “Simuganiza kuti n’kokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usawonongeke.” Chotero, kuyambira tsikuli apangana kuti aphe Yesu.​—Yohane 11:45-53.

21. Kodi chozizwitsa choukitsa Lazaro n’chiyambi cha chiyani?

21 Chotero ndi mmene zikuchitikira kuti posafika msanga m’Betaniya, Yesu watha kuchita chozizwitsa chosatheka kunyalanyazidwa ndi munthu. Ndi mphamvu yopatsidwa ndi Mulungu, Yesu akuukitsa munthu amene wakhala wakufa kwa masiku anayi. Ngakhale Sanihedirini yolemekezedwayo ikukakamizika kuzindikira zimene zachitika ndi kugamula kuti Wochita Zozizwitsayo aphedwe! Choncho chozizwitsacho chikukhala chiyambi cha kusintha kwakukulu kwa utumiki wa Yesu​—kuchoka kunthaŵi imene ‘nthaŵi yake inali isanafike’ kufika kunthaŵi yonena kuti “yafika nthaŵi.”

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali kudziŵa ntchito imene anapatsidwa ndi Mulungu?

• Kodi Yesu akukaniranji kuchita zimene amayi wake akum’pempha pankhani yokhudza vinyo?

• Tingaphunzirenji panjira imene Yesu kaŵirikaŵiri ankachitira ndi om’tsutsa?

• N’chifukwa chiyani Yesu akuzengereza kuchitapo kanthu pamatenda a Lazaro?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 12]

Yesu anathera nyonga yake pantchito imene Mulungu anam’patsa