Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’kukhaliranji Wodzimana?

N’kukhaliranji Wodzimana?

 N’kukhaliranji Wodzimana?

Bill, mwamuna wa zaka za m’ma 50, ali ndi banja ndipo ndi mphunzitsi wa zomangamanga. Kwa chaka chonse, pogwiritsa ntchito ndalama zake, amathera milungu yambiri kuthandiza kulemba mapulani ndi kumanga Nyumba za Ufumu za mipingo ya Mboni za Yehova. Emma ali ndi zaka 22 zakubadwa, ndi wosakwatiwa, koma n’ngwophunzira kwambiri. M’malo mochita zolinga zake zaumwini ndi zom’sangalatsa, amathera maola oposa 70 mwezi uliwonse monga mtumiki, kuthandiza anthu kulimvetsa bwino Baibulo. Maurice ndi Betty anapuma pantchito. M’malo mochepetsa zochita tsopano, iwo asamukira kudziko lina kukathandiza anthu kumeneko kuphunzira za chifuno cha Mulungu cha dziko lapansi.

ANTHU ameneŵa samadziona ngati apadera kapena osiyana ndi ena. Nawonso ndi anthu monga wina aliyense ndipo akuchita chomwe akulingalira kuti ndicho choyenera kuchichita. N’chifukwa chiyani akugwiritsa ntchito nthaŵi yawo, mphamvu, maluso, ndi chuma chawo kusamalira zosoŵa za ena? Chomwe chikuwasonkhezera ndicho chikondi chakuya cha pa Mulungu ndi cha pa mnansi wawo. Chikondi chimenechi chabutsa mwa aliyense wa iwo mzimu weniweni wa kudzimana.

Kodi tikati mzimu wa kudzimana tikutanthauzanji? Kudzimana sikufuna kukhala m’moyo wodzizunza, iyayi. Sikufuna kudzikana konyanyira komwe kungachotse chimwemwe chathu kapena chikhutiro. Monga momwe dikishonale yotchedwa The Shorter Oxford English Dictionary imanenera, kudzimana kumangotanthauza “kunyalanyaza zokonda zako, zosangalatsa zako, ndi zofuna zako n’cholinga chotumikira kapena kusamalira zosoŵa za ena.”

Yesu Kristu​—Chitsanzo Chabwino

Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, Yesu Kristu, n’chitsanzo chabwino cha munthu wa mzimu wodzimana. Asanadzakhale munthu padziko lapansi, moyo wake uyenera kuti unali wosonkhezera ndi wokhutiritsa kwambiri. Ankayanjana nthaŵi zonse mwachikondi ndi Atate ake limodzi ndi zolengedwa zauzimu. Komanso, Mwana wa Mulungu anali kugwiritsa ntchito maluso ake pa zinthu zovuta ndi zokondweretsa monga “mmisiri.” (Miyambo 8:30, 31) Mwachionekere iye anakhala m’mikhalidwe yapamwamba kwambiri pa chilichonse mwakuti ngakhale munthu wolemera kwambiri padziko lapansi sangafikepo. Monga wachiŵiri kwa Yehova Mulungu, anali ndi malo okwezeka kwambiri ndi aulemu kumwamba.

 Komabe, Mwana wa Mulungu “anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu.” (Afilipi 2:7) Iye mofunitsitsa anasiya ulemerero wake wonse mwa kukhala munthu ndi kupereka moyo wake monga dipo kuti athetse kuipa kochitidwa ndi Satana kumeneku. (Genesis 3:1-7; Marko 10:45) Zimenezo zinatanthauza kudzakhalira limodzi ndi mtundu wa anthu ochimwa m’dziko logona m’mphamvu za Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Zinatanthauzanso kupirira mavuto ndi zopinga zomwe anakumana nazo. Komabe, kaya zimenezo zinam’sautsa motani, Yesu Kristu anatsimikiza mtima kuchita chifuno cha Atate wake. (Mateyu 26:39; Yohane 5:30; 6:38) Zimenezi zinayesa chikondi ndi kukhulupirika kwa Yesu moyenera. Kodi iye anali wofunitsitsa kudzipereka mpaka pati? “Anadzichepetsa yekha,” anatero mtumwi Paulo, “nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.”​—Afilipi 2:8.

‘Mukhale Nawo Mtima Umenewu M’kati Mwanu’

Tikulimbikitsidwa kutsanzira chitsanzo cha Yesu. “Mukhale nawo mtima m’kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,” analimbikitsa motero Paulo. (Afilipi 2:5) Tingachite motani zimenezi? Njira imodzi ndiyo mwa ‘kusapenyerera zathu za ife zokha, koma yense kupenyereranso za mnzake.’ (Afilipi 2:4) Chikondi chenicheni “sichitsata za mwini yekha.”​—1 Akorinto 13:5.

Anthu olingalira za ena nthaŵi zonse asonyeza kudzipereka mosadzikonda potumikira ena. Koma lerolino, anthu ambiri amangofuna zowakomera. M’dzikoli ali ndi mzimu wongofuna kuti iwo azikhala oyamba. Tifunikira kupeŵa mzimu wadziko chifukwa chakuti ngati udzaumba malingaliro ndi mtima wathu, mosakayika tidzapanga zofuna zathu kukhala zofunika koposa. Kotero kuti chilichonse chimene tidzapanga​—mmene timagwiritsira ntchito nthaŵi yathu, mphamvu zathu, chuma chathu​—zidzalamulidwa ndi mzimu wodzikonda. Chotero ife tifunikira kumenya nkhondo zolimba yolimbana ndi zisonkhezero zimenezi.

Malangizo operekedwa ndi zolinga zabwino nawonso nthaŵi zina angathe kuipitsa mzimu wathu wodzipereka. Pozindikira komwe kudzipereka kwa Yesu kunali kum’tsogolera, mtumwi Petro anati: “Dzichitireni chifundo, Ambuye.” (Mateyu 16:22) Mwachionekere zinam’vuta kuvomereza kufunitsitsa kwa Yesu kufera zifuno za ulamuliro wa Atate wake ndi chipulumutso cha mtundu wa anthu. Choncho anayesa kunyengerera Yesu kuti asachite zimenezo.

‘Dzikanizeni Nokha’

Kodi Yesu anachitanji? Nkhaniyo imati: “Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, nam’dzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga, Satana iwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.” Ndiyeno Yesu anadziitanira khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake, nati kwa iwo: “Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake [“mtengo wake wozunzirapo,” NW], nanditsate Ine.”​—Marko 8:33, 34.

Zaka 30 zitatha kuchokera pamene anapereka malangizo ameneŵa kwa Yesu, Petro anasonyeza kuti nthaŵiyo anali atamvetsa tanthauzo la kudzimana. Sanalimbikitse okhulupirira anzake kufooka pa zochita zawo ndi kudzimvera okha chifundo. M’malo mwake, Petro anawalimbikitsa kukhala ndi mtima wokonzekera ntchito ndi kuleka kutsata zomwe ankalakalaka kale pamene anali mbali ya dziko. Ngakhale adzakumane ndi mayesero, anafunikira kuika patsogolo kuchita chifuno cha Mulungu m’miyoyo yawo.​—1 Petro 1:6, 13, 14; 4:1, 2.

Njira yopindulitsa kwambiri imene aliyense wa ife angalondole ndiyo kudzipereka kwa Yehova, kutsatira Yesu Kristu mokhulupirika ndi kulola Mulungu atsogolere zochita zathu. Pankhani imeneyi, Paulo anapereka chitsanzo chabwino. Changu chake ndi kukondwera kwake  mwa Yehova zinam’sonkhezera kusiya zinthu zokopa zakudziko kapena ziyembekezo zomwe zikanatha kum’lepheretsa kuchita chifuno cha Mulungu. Iye anati: ‘Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse mokondweratu’ chifukwa cha ena. (2 Akorinto 12:15) Paulo anagwiritsa ntchito maluso ake popititsa patsogolo zifuno zaumulungu, osati zake.​—Machitidwe 20:24; Afilipi 3:8.

Kodi tingadzipende motani kuti tione ngati tili ndi malingaliro angati a mtumwi Paulo? Tingadzifunse mafunso ngati aŵa: Kodi nthaŵi yanga, mphamvu zanga, maluso anga, ndi chuma changa ndikuzigwiritsa ntchito motani? Kodi mphatso zimenezi ndi zinanso zamtengo wapatali ndikuzigwiritsa ntchito pongofuna kupititsa patsogolo zofuna zanga, kapena kodi ndikuzigwiritsa ntchito pothandiza ena? Kodi ndalingalira zotenga nawo mbali mokwanira m’ntchito yopulumutsa moyo yolengeza uthenga wabwino, mwinamwake monga wolengeza Ufumu wanthaŵi zonse? Kodi ndingadzipereke kotheratu m’ntchito monga zomanga kapena kukonza Nyumba za Ufumu? Kodi ndikugwiritsa ntchito mwayi wothandiza osoŵa? Kodi ndikum’patsa Yehova zanga zabwino koposa?​—Miyambo 3:9.

“Kupatsa Kutidalitsa”

Komabe, kodi n’chanzeru kudzimana? Ndithudi n’chanzeru! Chifukwa chakuti zinam’chitikirapo, Paulo anadziŵa kuti mzimu wotero umadzetsa mphoto zochuluka. Zinam’dzetsera chimwemwe chochuluka ndipo anakhutira kwambiri. Iye anafotokozera zimenezi amuna achikulire ochokera ku Efeso pamene anakumana nawo ku Mileto. Paulo anati: “M’zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito [modzimana], kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mawu a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mamiliyoni a anthu aona kuti kusonyeza mzimu woterewu kumadzetsa chimwemwe chochuluka tsopano lino. Kudzadzetsanso chimwemwe m’tsogolo pamene Yehova adzafupa awo amene amaika zifuno zake ndi za anthu ena patsogolo.​—1 Timoteo 4:8-10.

Atam’funsa chifukwa chomwe anadziperekera kotheratu pothandiza ena kumanga Nyumba za Ufumu, Bill anati: “Kuthandiza yomwe nthaŵi zambiri imakhala mipingo ing’onoing’ono m’njira imeneyi kumandikhutiritsa kwambiri. Ndimasangalala kwambiri kugwiritsa ntchito maluso alionse ndi chidziŵitso chonse chimene ndili nacho kupindulitsa ena.” N’chifukwa chiyani Emma wasankha kuthera mphamvu zake ndi maluso ake pothandiza ena kuphunzira  choonadi cha Malemba? “Sinditha kuyerekeza kuti ndikugwira ntchito ina yosiyana. Ndikufuna kuti ndidakali wachinyamata komanso wokhoza kuchita ntchitoyi, ndichite zonse zomwe ndingathe kuti ndikondweretse Yehova ndi kuthandiza ena. Kudzimana chuma chomwe ndikanatha kukhala nacho ndi nkhani yaing’ono kwa ine.”

Maurice ndi Betty sakudandaula chifukwa chakuti sanapume m’moyo mwawo, pambuyo pogwira ntchito yolemetsa kwa zaka zingapo kuti athe kusamalira ndi kupeza zosoŵa za banja lawo. Popeza kuti anapuma ntchito tsopano, asankha kupitirizabe kuchita chinachake chofunika ndi chatanthauzo m’moyo mwawo. “Sitikufuna kuti tizingokhala osachita chilichonse panopa,” iwo akutero. “Kuthandiza ena kuphunzira za Yehova m’dziko lina kwatipatsa mwayi wopitirizabe kuchita chinachake chatanthauzo.”

Kodi mwatsimikiza mtima kukhala wodzimana? Kuchita zimenezi sikudzakhala kophweka. Nthaŵi zonse pali kulimbana pakati pa zikhumbo zathu za umunthu wopanda ungwirowu ndi kufunitsitsa kwathu moona mtima kukondweretsa Mulungu. (Aroma 7:21-23) Komatu tingapambane pankhondo imeneyi ngati tingalole Yehova kutsogolera miyoyo yathu. (Agalatiya 5:16, 17) Ndithudi iye adzakumbukira kumutumikira kwathu modzimana ndipo adzatidalitsa zedi. Inde, Yehova Mulungu ‘adzatsegula mazenera a kumwamba, ndi kutitsanulira mdalitso wakuti adzasoŵeka malo akuulandira.’​—Malaki 3:10; Ahebri 6:10.

[Chithunzi patsamba 23]

Yesu anali ndi mzimu wodzimana. Kodi inu mulinawo?

[Zithunzi patsamba 24]

Paulo anagwira ntchito yolalikira Ufumu ndi mphamvu zake zonse