Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo wa ku Zilumba za M’nyanja ya Pacific Kuntchito!

Ulendo wa ku Zilumba za M’nyanja ya Pacific Kuntchito!

 Ulendo wa ku Zilumba za M’nyanja ya Pacific Kuntchito!

M’ZIPINDA zodikiriramo ndege pamabwalo aakulu a ndege m’mizinda ya Brisbane ndi Sydney, ku Australia, munali anthu ansangala kusiyana ndi mmene zimakhalira nthaŵi zonse. Gulu la anthu 46 anali kudikira ndege yopita ku chilumba cha dzuŵa lotentha cha Samoa kukakumana ndi enanso 39 ochokera ku New Zealand, Hawaii, ndi United States. Katundu wawo anali wachilendo zedi​—zinali zida zokhazokha, monga mahamala, masowo, ndi makina oboolera zinthu​—wosiyana ndi katundu amene munthu wopita ku chilumba chokongola cha m’Pacific amanyamula nthaŵi zambiri. Komatu ulendo wawo unalinso wapadera.

Podzilipirira ulendo wawo, anali okonzeka kuthera milungu iŵiri monga antchito odzifunira okha ndiponso osalipidwa pantchito yomanga nyumba. Ntchitoyo ndi yoyang’aniridwa ndi Ofesi ya Chigawo Yoyang’anira Ntchito Zomanga m’chigawo chimenecho cha dziko lapansi yomwe ili pa ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ya ku Australia. Ntchito imeneyo, yochirikizidwa ndi zopereka zaufulu, ndi yokhudza kumanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Misonkhano, nyumba za amishonale, ndi maofesi anthambi kapena a otembenuza zofalitsa kaamba ka mipingo ya Mboni za Yehova imene ikuwonjezeka kwambiri m’zilumba za m’nyanja ya Pacific. Tiyeni ticheze ndi ena mwa antchito ameneŵa, amene anali m’magulu omanga Nyumba za Ufumu kumayiko akwawo.

Max, wantchito yokhoma malata padenga, kwawo ndi ku Cowra m’chigawo cha New South Wales, Australia. Iye ali pabanja ndipo ali ndi ana asanu. Arnold kwawo ndi ku Hawaii. Iyeyo ndi mkazi wake ali ndi ana aamuna aŵiri, komanso ndi mpainiya, kapena kuti mtumiki wanthaŵi zonse. Mofanana ndi Max, Arnold amatumikiranso monga mkulu mumpingo wakwawo. N’zoonekeratu kuti amunaŵa ndiponso ena ochuluka ogwira ntchito yomangayi sanadzipereke kukagwira ntchitoyo chifukwa chakuti ali ndi nthaŵi yoiwononga. M’malo mwake, iwo ndi mabanja awo akuona kuti penapake pakufunikira thandizo, ndipo akufuna kuyesetsa kupereka thandizolo.

Antchito Ochokera M’mayiko Osiyanasiyana Apereka Thandizo Lofunika

Malo amodzi kumene kunafunikira maluso awo ndi ntchito yawo ndi ku Tuvalu, dziko la m’Pacific la anthu ngati 10,500 lopangidwa ndi kagulu ka tizilumba tisanu ndi tinayi tamapiri pafupi ndi equator ndiponso kum’poto koma chakumadzulo kwa chilumba cha Samoa. Tizilumba timeneto, kalikonse n’kokwanira avareji ya makilomita aŵiri ndi theka ukulu wake. Podzafika 1994, Mboni 61 za kumeneko zinafunikira Nyumba ya Ufumu yatsopano mwamsanga ndi maofesi enanso a otembenuza zofalitsa.

M’chigawo cha dzuŵa lotentha chimenechi cha m’Pacific, nyumba ziyenera kulinganizidwa ndi kumangidwa  m’njira yoti zizilimba pokanthidwa ndi mphepo zamphamvu zamkuntho zobwera kaŵirikaŵiri. Komano pazilumbapo palibe zomangira zambiri zabwino. Ndiyeno anatani? Zomangira zonse, kuyambira malata ndi zitsulo zopangira denga kudzanso mipando, matebulo, ndi makatani, za m’zimbudzi ndi mipope ya m’bafa, ngakhalenso misomali, zinatumizidwa m’mabokosi akuluakulu kuchokera ku Australia.

Zomangirazo zisanadze, gulu lina laling’ono loyambirira linayeretsa malowo ndi kumanga maziko. Kenako antchito ochokera kumayiko ena anabwera kudzamanga nyumbazo, kuzipaka penti, ndi kuika zonse zam’kati.

Zinangochitika kuti zochitika zonsezi m’Tuvalu zinapsetsa mtima m’tsogoleri wina wachipembedzo komweko amene analengeza pawailesi kuti Mboni zikumanga “Nsanja ya Babele”! Komano kodi zenizeni zake zinali zotani? “Omanga Nsanja ya Babele ataona kuti asiya kumvana chifukwa chakuti Mulungu anasokoneza chiyankhulo chawo, analeka ntchito yawoyo ndipo nsanja yawoyo sanaimalize,” anatero wantchito wodzifunira wotchedwa Graeme. (Genesis 11:1-9) “Koma pogwirira ntchito Yehova Mulungu sizitero. Ngakhale kuti omangawo sayankhula chiyankhulo chofanana ndiponso chikhalidwe chawo n’chosiyana, ntchito zawo zimamalizidwabe.” Ndipo imeneyi inamalizidwadi m’milungu iŵiri yokha. Eetu, anthu 163, kuphatikizapo mkazi wa nduna yaikulu ya dzikolo, anafika pamwambo wopatulira nyumbazi.

Doug, woyang’anira ntchitoyo, pokumbukira zochitika, akuti: “Zinali zosangalatsa kugwira ntchito pamodzi ndi anthu odzipereka okha ochokera kumayiko ena. Timachita zinthu m’njira zosiyanasiyana, tili ndi mayina osiyana a zinthu, ngakhalenso njira zosiyana zopimira zinthu, koma zonsezi sizinapereke vuto lililonse.” Popeza wachita ntchito imeneyi m’madera angapo tsopano, akuwonjezera kuti: “Zimenezi zimandipatsa chitsimikiziro mumtima mwanga chakuti ndi chichirikizo cha Yehova anthu ake angamange nyumba kwina kulikonse m’dziko lapansili, kaya malowo akhale akutali chotani kapena akhale ovuta chotani. N’zoona kuti tili ndi akatswiri ambiri, koma ndi mzimu wa Yehova umene umatheketsa zonse.”

Mzimu wa Mulungu umapangitsanso mabanja a Mboni m’zilumbazo kupereka chakudya ndi malo ogona, zimene ena amayenera kudzimana kaye kuti achite zimenezo. Ndipo awo amene amasamalidwa chotero amayamikira kwambiri. Ken, amene kwawo ndi ku Melbourne, Australia, anagwirapo ntchito yofananayo ku chilumba cha French Polynesia. Iye akuti: “Tinabwera monga akapolo, koma anatisamalira monga mafumu.” Nthaŵi zinanso, Mboni zakomweko zimathandiza nawo ntchito yomangayo. Ku Solomon Islands, akazi anali kupanga konkire, komatu ndi manja. Amuna ndi akazi zana limodzi anali kukwera m’mapiri nthaŵi yamvula ndipo anatsika ndi mitengo ya matabwa yokwanira matani oposa 40. Achinyamatanso anathandiza nawo. Wantchito wina wochokera ku New Zealand akusimba kuti: “Ndikukumbukira mbale wina wachinyamata wapachilumbapo amene ankanyamula matumba aŵiri kapena atatu a simenti nthaŵi imodzi. Ndipo anali kufoshola miyala tsiku lonse dzuŵa lili phwe ndi pa mvula.”

 Kulola Mboni zakomweko kugwira nawo ntchitoyo kumadzetsa phindu linanso. Ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku Samoa ikusimba kuti: “Abale apachilumba pano aphunzira luso la ntchito zamanja limene angagwiritse ntchito pomanga Nyumba za Ufumu ndi pokonza ndi kumanganso nyumba zowonongedwa ndi mphepo ya mkuntho. Lusoli lingawathandizenso kulembedwa ntchito yowathandiza kupeza zofunika m’moyo m’dera limene ambiri amavutika kutero.”

Ntchito Yomanga Ipereka Umboni Wabwino

Colin anali ku Honiara ndipo anaona Nyumba ya Misonkhano ya ku Solomon Islands ikumangidwa. Pochita chidwi, analembera ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ya komweko uthenga uwu m’Chingelezi chosakanikirana ndi chiyankhulo chakwawoko, nati: “Onse ndi ogwirizana ndipo palibe wokwiya, alinso banja limodzi.” Mwamsanga pambuyo pake, atabwerera kumudzi kwawo ku Aruligo, mtunda wa makilomita 40, iyeyo ndi banja lake anamanga Nyumba ya Ufumu yawoyawo. Ndiyeno anatumiza uthenga winanso ku ofesiyo kuti: “Nyumba yathu ya Ufumu, ndi thebulonso lokambirapo nkhani, tamaliza, chotero kodi tingamasonkhaniremo?” Nthaŵi yomweyo zinalinganizidwa, ndipo anthu oposa 60 amasonkhanira pamenepo mokhazikika.

Mlangizi wa bungwe la European Union anaona ntchito ya ku Tuvalu ili m’kati. “Ndikhulupirira kuti aliyense amakuuzani zomwezi,” iye anatero kwa wantchito wina, “komanso kwa ine chimenechi n’chozizwitsa chenicheni!” Mkazi wogwira ntchito pamalo pofikira matelefoni onse anafunsa wantchito wodzifunira wochokera kwina kuti: “M’matha bwanji nonsenu kukhala achimwemwe chonchi m’dziko lotentha ngati lino?” Anali asanaonepo Chikristu chili pantchito m’njira yeniyeni ndi yodzipereka ngati imeneyo.

Kudzipereka Mosamva Chisoni Pambuyo Pake

“Iye wakufesa mowolowa manja, mowolowa manjanso adzatuta,” limatero Baibulo pa 2 Akorinto 9:6. Antchitowo, mabanja awo, ndi mipingo yawo akupitirizabe kufesa mowolowa manja pothandiza Mboni zinzawo m’nyanja ya Pacific. “Mpingo wanga unapereka chigawo chachikulu cha ndalama zanga zokwerera ndege,” akutero Ross, mkulu wochokera ku Kincumber, pafupi ndi mzinda wa Sydney, “ndipo mulamu wanga wamwamuna, yemwenso ndinayenda naye ulendowo, anawonjezera ndalama zokwana madola 500.” Wantchito winanso anapeza ndalama zoyendera ulendo wake mwa kugulitsa galimoto lake. Winanso anagulitsa munda wake. Kevin anafunikira madola 900 owonjezera, chotero anaganiza zogulitsa nkhunda zake 16 za zaka ziŵiri zakubadwa. Kudzera mwa mnzake wina, anapeza munthu yemwe anati angam’patse madola 900 pogula nkhundazo, ndendende ndi ndalama zomwe ankazifuna!

“Kodi zinali zoti n’kuwonongerapodi madola 6,000 okwerera ndege pamodzi ndi ndalama zimene mukanalandira pogwira ntchito yamalipiro?” Danny ndi Cheryl anafunsidwa motero. “Inde! Ngakhalenso kuŵirikiza kaŵiri ndalama zimenezo, zikanakhaladi zoyenerera kuzigwiritsa ntchito moteromo,” anayankha motero. Alan, wochokera ku Nelson, New Zealand, anawonjezera kuti: “Ndi ndalama zimene ndinagwiritsa ntchito popita ku Tuvalu, ndikanapita ku Ulaya ndi kutsalanso ndi zina. Koma kodi ndinakalandira madalitso, kapena kupanga mabwenzi ambiri chotero okhala ndi ziyambi zosiyanasiyana, kapena kodi ndikanatha kuthandiza ena m’malo modzipindulitsa ndekha? Ayinso! Ngakhale ndi tero, zonse zimene ndinapatsa abale athu a pachilumbachi, anandibwezera zochuluka kuposanso zimenezo.”

Chinsinsi chinanso cha chipambano cha ntchito imeneyi ndicho chichirikizo cha mabanja. Pamene kuli kwakuti akazi ena amatha kutsagana ndi amuna awo ngakhalenso kugwira nawo ntchitoyo, ena ali ndi ana opita ku sukulu ofunika kuwasamalira kapenanso zochita zina za banja zoti azisamalire. “Kuvomereza kwa mkazi wanga kuti asamalire ana athu ndi nyumba ineyo n’tachoka,” anatero Clay, “kunali kudzipereka kwakukulu kuposanso kudzipereka kwanga.” Zoonadi, amuna onse amene sanathe kupita ndi akazi awo angayankhe mawu amenewo ndi mtima wonse kuti “Amen!”

Kuchokera pamene ntchito yomanga nyumbazo inamalizidwa ku Tuvalu, antchito odzifunira amanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Misonkhano, nyumba za amishonale, ndi maofesi a otembenuza zofalitsa pa zilumba za Fiji, Tonga, Papua New Guinea, New Caledonia, ndi m’malo ena. Ntchito zomanga zambiri, kuphatikizapo za ku Southeast Asia, zikulinganizidwabe. Kodi padzakhala antchito okwanira?

Zikuoneka kuti limenelo silidzakhala vuto. “Aliyense kunoko amene anamanga nawo nyumba kumayiko ena amapempha kuti adzakumbukiridwe pakadzakhalanso ntchito ina,” inalemba motero ofesi yanthambi ya ku Hawaii. “Akangobwerako, amayambiranso kusungiratu ndalama zodzapitira kuntchito inanso.” Kodi ntchito ngati imeneyo singakhale yopambana mutawonjezerapo madalitso aakulu a Yehova pa kudzipereka ngati kumeneko?

 [Chithunzi patsamba 9]

Katundu womangira nyumba

[Zithunzi patsamba 9]

Antchito pamalo ena omanga

[Zithunzi patsamba 10]

Pamene ntchito yomanga nyumbazo inali kumalizidwa, tinasangalala kuona zimene mzimu wa Mulungu unachita