Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Oganiza Bwino pa Zoyembekeza Zathu?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Oganiza Bwino pa Zoyembekeza Zathu?

 N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Oganiza Bwino pa Zoyembekeza Zathu?

ZOYEMBEKEZA zathu zikakwaniritsidwa ndipo zofuna zathu zikachitika zimatipangitsa kukhala okhutira. Komabe, n’zoona, kuti maloto athu ambiri ndi zoyembekeza zathu sizichitika mmene timafunira. Kuchitikanso kwa zinthu zogwiritsa mwala m’moyo kungatipangitse kudzikwiyira tokha ngakhalenso kukwiyira anthu ena. Munthu wanzeru ananena moyenerera kuti: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.”​—Miyambo 13:12.

Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zingatichititse kumva kukhala ogwiritsidwa mwala? Kodi tingachite bwanji kuti tikhale oganiza bwino pa zoyembekeza zathu? Ndiponso, n’chifukwa chiyani kuteroko kuli kotipindulitsa?

Zoyembekeza ndi Zogwiritsa Mwala

Malinga n’kuthamanga kwa moyo masiku ano, pamene tikufuna kupita patsogolo, m’pamene timaona kuti tikutsalira m’mbuyo. Zofuna nthaŵi ndi nyonga yathu zingachuluke kwambiri, ndipo pamene tilephera kuchita zomwe timafuna kuchita, timakonda kudziimba tokha mlandu. Tingathenso ngakhale kuyamba kumva ngati tikugwiritsa ena mwala. Cynthia, mkazi wokwatiwa ndiponso mayi amene akudziŵa zovuta za kulera ana, anati: “Kulephera kuchita khama pa kuwongolera ana anga komanso kudzimva ngati ndikulephera kuwaphunzitsa mokwanira kumandipsetsa mtima.” Mtsikana wina wotchedwa Stephanie, ponena za maphunziro ake anati: “Ndilibe nthaŵi yokwanira yochita zonse zimene ndikufuna kuchita, ndipo zimenezi zimandipangitsa kukhala wosaleza mtima.”

Zoyembekeza zonkitsa zingapangitse munthu kumangofuna zabwino koposa zokhazokha, ndipo zimenezi zingakhale zokhumudwitsa kwambiri. Ben, mwamuna wachinyamata wokwatira, anavomereza kuti: “N’kapenda zochita zanga, zoganiza zanga, kapena mmene ndimamvera, nthaŵi zonse ndimaona mmene zikanakhalira bwinopo. Nthaŵi zonse ndimafuna kuti zinthu zichitike mwangwiro, ndipo zimenezi zimandipangitsa kusaleza mtima, kukhumudwa, ndipo kugwiritsidwa mwala.” Gail, mkazi wokwatiwa wachikristu, anati: “Maganizo ofuna zangwiro salola kulephera kulikonse. Timafuna kukhala anakubala opambana ndi akazi okwatiwa opambana kwambiri. Tiyenera kugwira ntchito kuti tisangalale, choncho kuyesetsa kosaphula kanthu kumatikwiyitsa.”

Komanso chinthu china chimene chingagwiritse mwala aliyense payekha ndiko kufooka kwa thanzi ndi ukalamba. Kulephera kuyenda kwambiri ndi kuchepa kwa nyonga zimaonetsa kwambiri zolephera zathu ndipo zimawonjezera kukhumudwa. “Ndinkavutika mtima kwambiri polephera kuchita zinthu zimene ndinkachita mosavuta ndi mwachibadwa ndisanayambe kudwala,” anatero Elizabeth.

Zonenedwa pamwambazi zangokhala zitsanzo za zinthu zimene zingasonkhezere malingaliro a kugwiritsidwa mwala. Kupanda kudziletsa, malingaliro oterowo angatichititse kukhulupirira kuti ena satiyamikira. Choncho, tingatani kuti tisagwiritsidwe mwala ndi kuti tikhale ndi zoyembekeza zosankitsa?

Njira Zokulitsira Kuganiza Bwino pa Zoyembekeza Zathu

Choyamba, kumbukirani kuti Yehova n’ngwoganiza bwino ndipo amamvetsa. Salmo 103:14 limatikumbutsa kuti: “Adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” Podziŵa zimene tingathe kuchita ndi zolephera zathu, Yehova amayembekeza kwa ife chabe zimene tingathe kupereka. Ndipo chinthu chimodzi chimene iye  amafuna kwa ife ndicho “kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu [wathu].”​—Mika 6:8.

Yehova amatilimbikitsanso kutembenukira kwa iye m’pemphero. (Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:17) Koma kodi ndi motani mmene zimenezo zimatithandizira? Pemphero limakhazikitsa kuganiza kwathu kuti kukhale koyenera. Pemphero lochokera pansi pa mtima ndi chivomerezo chakuti timafuna thandizo​—ndi chizindikiro cha kudekha ndi kudzichepetsa. Yehova ali wofunitsitsa kuyankha mapemphero athu mwa kutipatsa mzimu wake woyera, umene zipatso zake zimaphatikizapo chikondi, chifundo, ubwino, ndi kudziletsa. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23) Pemphero limachepetsanso nkhaŵa ndi kukhumudwa. Kupyolera m’pemphero, “mumapeza chitonthozo chosapezeka kwina kulikonse,” anatero Elizabeth. Kevin anavomereza kuti: “Ndimapempherera mtima wodekha ndi malingaliro abwino kotero kuti ndithe kugonjetsa vuto. Yehova sandigwiritsa mwala konse.” Mtumwi Paulo anadziŵa phindu lapadera la pemphero. N’chifukwa chake anavomereza kuti: “Komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Inde, kulankhula ndi Yehova kumatithandizadi kukulitsa kuganiza bwino pa zoyembekeza zathu ndi za ena.

Komabe, nthaŵi ndi nthaŵi, timafunika chilimbikitso cha panthaŵi yomweyo. Mawu a panthaŵi yake n’ngabwino. Kukambirana zakukhosi ndi mnzathu wachikulire amene timam’khulupirira kungatithandize kukhala ndi malingaliro atsopano a zimene zikutigwiritsa mwala kapena kutipangitsa nkhaŵa. (Miyambo 15:23; 17:17; 27:9) Achinyamata amene akuvutika ndi zolefula amaphunzira kuti kufunafuna malangizo ochokera kwa makolo kumawathandiza kupezanso chidaliro. Mtsikana wina wotchedwa Kandi anavomereza moyamikira kuti: “Malangizo achikondi ochokera kwa makolo anga anandipangitsa kukhala woganiza bwino kwambiri ndi wokhutira ndiponso kuti ena adzikonda kucheza nane.” Inde, mawu okumbutsa a pa Miyambo 1:8, 9 n’nga panthaŵi yake: “Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako; Pakuti izi ndi korona wa chisomo pamtu pako, ndi mkanda pakhosi pako.”

Pamene munthu afuna zangwiro zokhazokha, zotsatira zake zinafotokozedwa bwino ndi mwambi wachingelezi wakuti: “Kuyembekeza kuti moyo utsate zofuna zathuzathu ndiko kupempha kugwiritsidwa mwala.” Kuti tipewe maganizo oterowo, n’kofunika kuwongolera kuganiza kwathu. Kudzichepetsa ndi kudekha​—kuzindikira ndi kuvomereza zolephera zathu​—kudzatithandiza kukhala ndi zoyembekeza zoyenera. Moyenerera, Aroma 12:3 amatichenjeza kuti munthu aliyense “asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa.” Kuwonjezera pamenepo, Afilipi 2:3 amatilimbikitsa kukhala ndi mtima wodzichepetsa ndi kuona ena monga otiposa.

Elizabeth, amene tam’tchula poyamba paja, anali wotekeseka chifukwa cha kudwala kwake. Iye anafunikira nthaŵi yakuti adziŵe mmene Yehova amaonera zinthu, ndi kuti atonthozedwe podziŵa kuti Yehova saiŵala utumiki wathu. Colin satha kuyenda chifukwa cha matenda opuwalitsa. Poyambirira, anaona ngati kuti utumiki wake tsopano unali wopanda pake poyerekeza ndi mmene an’kachitira pamene anali bwino. Posinkhasinkha malemba onga ngati 2 Akorinto 8:12, iye anatha kuchotsa malingaliro amenewo. Lembali limati: “Ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chim’soŵa.” “Ngakhale ndili ndi zochepa zopereka,” akutero Colin, “ndingathe kuperekabe, ndipo n’zolandirika kwa Yehova.” Pa Ahebri 6:10, tikukumbutsidwa kuti: “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera ku dzina lake.”

Komabe, ndi motani mmene tingadziŵire ngati zoyembekeza zathu n’zoyenera? Dzifunseni nokha kuti, ‘Kodi zoyembekeza zanga zimagwirizana ndi zoyembekeza za Mulungu?’ Agalatiya 6:4 amati: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.” Kumbukirani, Yesu ananena kuti: “Goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” Inde, monga Akristu, tili ndi goli loyenera kusenza, koma ndi “lofewa” ndi “lopepuka,” ndipo Yesu analonjeza kuti lidzakhala lotipumulitsa tikaphunzira kulinyamula bwino.​—Mateyu 11:28-30.

 Zoyembekeza Zoyenera Zimabweretsa Mphoto

Mphoto zamwamsanga ndi zokhalitsa zimabwera pomvera ndi kuchita zimene uphungu wa Mawu a Mulungu umanena pamene tikuyesetsa kukhala ndi zoyembekeza zoyenera. Ndiponso, kumvera mawu a Mulungu kuli ndi phindu kwa ife mwa kuthupi. Jennifer, amene wapindula ndi zikumbutso za Yehova, anavomereza kuti: “Ndili ndi nyonga ndi mphamvu zowonjezereka za moyo.” Moyenerera, Miyambo 4:21, 22 amatilimbikitsa kumvera mawu a Yehova mosamalitsa ndi maso athu ndi mitima yathu, “pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lawo lonse.”

Mphoto ina ndiyo kulingalira ndi kuganiza bwino. “Ndikaika malingaliro ndi mtima wanga ku Mawu a Mulungu, ndimapeza kuti ndimakhala munthu wokondwa koposa,” anatero Theresa. Zoonadi, tidzapitirizabe kukumana ndi zogwiritsa mwala m’moyo. Komabe tidzatha kuzipirira mosavuta kwambiri. “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu,” amatilimbikitsa choncho Yakobo 4:8. Yehova amalonjezanso kutilimbitsa pokumana ndi zovuta za moyo ndi kutidalitsa ndi mtendere.​—Salmo 29:11.

Kukhala ndi zoyembekeza zoyenera kumatichititsa kukhalabe okhazikika mwauzimu. Ndi dalitsonso limeneli. Tingathe kuika kwambiri maganizo athu pa zinthu zofunika kwenikweni m’moyo. (Afilipi 1:10) Choncho zolinga zathu zimakhala zotsimikizika ndi zotheka, ndipo zimabweretsa chimwemwe chochuluka kwabasi ndi chikhutiro. Tidzakhala ofunitsitsa kudziikiza tokha kwa Yehova, podziŵa kuti iye adzapangitsa zinthu kutiyendera bwino kwambiri. “Potero dzichepetseni pansi pa dzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni,” akutero Petro. (1 Petro 5:6) Kodi pangakhalenso chinthu china chobweretsa mphoto kuposa kulemekezedwa ndi Yehova?

[Zithunzi patsamba 31]

Kukhala ndi zoyembekeza zoyenera kungatithandize kuthana ndi zokhumudwitsa ndi zogwiritsa mwala