Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ofunika Kwambiri kwa Yehova Ndi Amene Amam’konda

Anthu Ofunika Kwambiri kwa Yehova Ndi Amene Amam’konda

Olengeza Ufumu Akusimba

Anthu Ofunika Kwambiri kwa Yehova Ndi Amene Amam’konda

LEBANO wakhala wodziŵika chifukwa cha zinthu zake zachilengedwe kuyambira nthaŵi za m’Baibulo. (Salmo 72:16; Yesaya 60:13) Chochititsa chidwi kwambiri chinali mitengo yake ikuluikulu yamikungudza imene inkafunika kwambiri monga yomangira, chifukwa cha kukongola kwake, kununkhira kwake, ndiponso kulimba kwake. M’zaka za zana loyamba, chinachake chofunika kwambiri chinaoneka ku Lebano. Uthenga Wabwino wa Marko umanena kuti kuchokera ku Turo ndi Sidoni, gawo lakale mu Lebano, “khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo [Yesu] anazichita, linadza kwa Iye.”​—Marko 3:8.

Lerolinonso, Lebano akupitirizabe kubala zipatso zimene zili zofunika kwambiri kwa Yehova. Zochitika zotsatirazi zikusonyeza zimenezi.

• Mboni ina yachinyamata yotchedwa Wissam inapemphedwa kukamba nkhani m’kalasi yake kusukulu kwa mphindi 30. Wissam anaganiza kuti udzakhala mwayi wabwino wochitira umboni. Choncho anakonzekera nkhani ya zachilengedwe ndipo anagwiritsira ntchito buku lakuti Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Koma aphunzitsi a Wissam ataona kaye nkhaniyo, ananena kuti popeza kuti inali nkhani yabwino, Wissam angathe kuwonjezera nkhani yakeyo kufika pamphindi 45.

Pamene Wissam anayamba nkhaniyo, aphunzitsi akewo anamuimitsa n’kutuma wina kukaitana woyang’anira pasukulupo. Mosakhalitsa woyang’anirayo anafika, ndipo Wissam anayambiranso. Pamene woyang’anirayo anamva mafunso amene Wissam anafunsa kuchiyambi cha nkhani yake, anasangalala ndipo ananena kuti ophunzira onse ayenera kulandira kope la nkhaniyo.

Patangopita kanthaŵi pang’ono mphunzitsi wina, amene anali kudutsa, anaona chisangalalo chimene chinali m’kalasimo ndipo anafuna kudziŵa zimene zinali kuchitika. Atadziŵitsidwa, anafunsa ngati Wissam ankayesa kuvomereza chilengedwe kapena chisinthiko. “Chilengedwe,” linatero yankho. Atazindikira kuti Wissam anali wa Mboni za Yehova, mphunzitsiyo anauza ophunzirawo kuti: “Mudzaona kuti ndi nkhani yakeyi sayansi imachirikiza chilengedwe, osati chisinthiko.”

Zinadziŵika kuti mphunzitsi ameneyu anali ndi buku la Creation ndipo wakhala akuligwiritsa ntchito pophunzitsa pa yunivesite! Asanachoke, iye anafunsa ngati akanatha kubwera tsiku lotsatira pamodzi ndi ophunzira ake kuti Wissam adzakambe kwa ophunzirawo. Zimenezo zinachititsa umboni winanso wabwino kwa Yehova.

• Nina wa zaka 22 anali ndi ludzu la madzi a choonadi. Tsiku lina msuwani wake anam’patsa Baibulo n’kumudziŵikitsa ku Tchalitchi cha Pentecostal. Nina anaŵerenga Baibulo ndi chidwi ndipo anaphunzira m’kuŵerenga kwake kuti Akristu ayenera kulalikira, choncho anayamba kulankhula ndi anzake. Aliyense amene analankhula naye anam’funsa kuti: “Kodi ndiwe wa Mboni za Yehova?” Zimenezi zinam’dabwitsa kwabasi.

Patapita zaka zisanu ndi chimodzi, Mboni za Yehova zinafika panyumba yake ndipo zinamuuza za Ufumu wa Mulungu. Poyamba, anayesa kupeza chifukwa ndi ziphunzitso zawo. Komabe, anaona kuti mayankho awo anali anzeru ndiponso ochokera m’Baibulo.

Zimene Nina anaphunzira pomalizira pake​—dzina la Mulungu lakuti, Yehova; madalitso a Ufumu; ndi zina zotero​—zinam’khutiritsa kuti wapeza choonadi. Anapatulira moyo wake kwa Mulungu ndipo anabatizidwa. Kwazaka zisanu ndi ziŵiri zapitazi, Nina wakhala akutumikira monga mlaliki wanthaŵi zonse. Zoonadi, Yehova amadalitsa onse amene ali ndi chikondi chenicheni kwa iye.​—1 Akorinto 2:9.