Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Msonkhano wa Pachaka pa October 7, 2000

Msonkhano wa Pachaka pa October 7, 2000

 Msonkhano wa Pachaka pa October 7, 2000

MSONKHANO WA PACHAKA wa mamembala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitika pa October 7, 2000, pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova, pa 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, ku New Jersey. Kukumana koyambirira kwa mamembala okhaokha kudzakhalako pa 9:15 a.m., motsatiridwa ndi msonkhano wa onse wa pachaka pa 10:00 a.m.

Mamembala a bungweli ayenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano lino za kusintha kulikonse kwa makeyala awo a makalata m’kati mwa chaka chapita kotero kuti iwo adzathe kulandira makalata owadziŵitsa anthaŵi zonse ndi mapepala opangira voti m’July.

Mapepala opangira voti, amene adzatumizidwa kwa mamembalawo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wa pachaka, ziyenera kubwezedwa kotero kuti zidzafike ku Ofesi ya Mlembi wa Sosaite pasanafike pa August 1. Membala aliyense ayenera kudzaza ndi kutumiza pepala lake lopangira voti mofulumira, akumafotokoza kuti kaya adzapezeka pamsonkhanowo kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pa pepala lopangira voti lililonse chiyenera kukhala chotsimikizirika pamfundoyi, popeza kuti chidzakhala chodziŵira amene adzapezekapo.

Pulogalamu yonse, kuphatikizapo msonkhano wa kayendetsedwe ka zinthu ndi malipoti, zikuyembekezeka kudzatha pa 1:00 p.m. kapena kupitirira pang’ono pamenepo. Sipadzakhala pulogalamu yamasana. Chifukwa cha kuchepa kwa malo, okhala ndi matikiti okha ndiwo amene adzaloledwa kuloŵa. Sipadzakhala makonzedwe akugwirizanitsa matelefoni ndi nyumba zina zosonkhanira pamsonkhano wa pachakawu.