Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’kugonjetseranji Malingaliro Osafuna Kulakwitsa Kanthu?

N’kugonjetseranji Malingaliro Osafuna Kulakwitsa Kanthu?

 N’kugonjetseranji Malingaliro Osafuna Kulakwitsa Kanthu?

Kodi nthaŵi zonse mukuyesetsa zolimba kuchita zinthu bwino monga momwe mungathere? Ndithudi, kuchita zimenezo kungakupindulitseni m’njira zambiri limodzinso ndi awo amene ali pafupi nanu. Kumbali ina, ena achita zinthu mopambanitsa kotero kuti afikira pakukhala anthu ofuna kuchita zinthu bwino popanda kulakwitsa kanthu. Kodi zimenezo zikutanthauzanji?

CHABWINO, tanthauzo limodzi la mawu akuti “kusafuna kulakwitsa kanthu” ndilo “kulingalira nthaŵi zonse kuti chilichonse chomwe sichili changwiro n’chosaloleka.” Mwachionekere, mwakumanapo ndi anthu olingalira choncho. Mungaone kuti zinthu zonkitsa zimene amafuna kuti ena awachitire zingadzetse mavuto ambiri, zingachititse munthu kukhala wosakhutira ndi wofooketsedwa. Anthu ambiri olingalira bwino amazindikira kuti kufuna zinthu zangwiro zokhazokha mwa kulamula mopambanitsa ndi mopanda nzeru pa zochitika zonse m’moyo ndithudi n’kosakondweretsa. Kuyeneradi kuthetsedwa. Komabe, vuto n’lakuti kunena za malingaliro a enife kapena mkhalidwe wathu, kungakhale kovuta kuzindikira chizoloŵezi chimenechi chofuna zangwiro zokhazokha, choncho n’kovuta kuchithetsa.

Nelson ali ndi udindo waukulu ndi mavuto ambiri oti athetse. Iye nthaŵi zonse amaŵerengera masamu, ndipo amalingalira kuti kupeza phindu ndiko chinthu chofunika kwambiri. Kufuna kuchita zinthu mosalakwitsa m’pang’ono pomwe nthaŵi zambiri kumaoneka ngati kofunika kuti upambane pampikisano wofuna kupeza ndi kusungabe ntchito yako. Ngakhale kuti ena angakhumbire kuchita bwino kwa Nelson, kufuna kwake kuchita zinthu mosalakwitsa m’pang’ono pomwe kumam’dzetsera mavuto akuthupi, monga kupweteka kwa mutu ndi kupsinjika maganizo. Kodi zochita za Nelson ndi zanu n’zofanana?

Achinyamata nawonso amafuna atachita zinthu popanda kulakwitsa m’pang’ono pomwe. Akali mwana, Rita, wa ku Rio de Janeiro, ankakonda kwambiri kupita kusukulu. Ankayesetsa kuti asaoneke ngati akufuna kutchuka, komabe anali kukhumudwa kwambiri ngati alephera kupeza malikisi apamwamba. Rita akuti: “Kuyambira ubwana wanga, ndinali kudziyerekeza ndi anthu ena omwe anali ndi nthaŵi yochuluka, pomwe ine nthaŵi zonse ndinali wopsinjika maganizo ndi wochita zinthu mwaphuma. Sindikukumbukira n’komwe zakuti ndinali ndi nthaŵi yopuma chifukwa  chakuti nthaŵi zonse ndinali ndi zinthu zoti ndichite.”

Monga msungwana, Maria ankalira mokhumudwa pamene, monga ena onse, anali kulephera kujambula. Komanso, poyesayesa kuti akhale katswiri woimba wochita bwino zinthu kopambana, kaŵirikaŵiri amakhala wopsinjika maganizo ndi wodandaula m’malo mosangalala ndi kuimbako. Msungwana wina wa ku Brazil, Tânia, yemwe amayesa kukhala wanzeru ndi kupeŵa mpikisano, anavomereza kuti anali kudziikirabe miyezo yapamwamba kwambiri, kusukulu ndi kunyumba komwe. Msungwanayu ankalingalira kuti anthu sadzam’konda kwambiri pokhapokha ngati ntchito yake itakhala yangwiro. Kuwonjeza pamenepo, Tânia nthaŵi zina ankayembekezera zopambanitsa kwa ena. Zimenezi zinam’khumudwitsa ndi kum’mvetsa chisoni.

Ngakhale kuti kuchita zinthu bwino, khama, ndi mtima wokhutira zili zofunika, malingaliro oipa, monga kuopa kulephera, angadze chifukwa chopanga zolinga zomwe sizingatheke. Makolo kapena anthu ena angaikire achinyamata miyezo yakuti achite zinthu bwino popanda kulakwitsa kusukulu kapena pa maseŵera zomwe achinyamatawo zingawavute kukwaniritsa. Mwachitsanzo, mayi ake a Ricardo ankayembekezera zopambanitsa kuchokera kwa iye. Ankafuna kuti adzakhale dokotala, woimba piyano, ndikuti azidzalankhula zinenero zambirimbiri. Kodi mukuona kuti ngati zimenezi zitachitidwa mopambanitsa zingadzetse mavuto kapena kukhumudwitsa?

N’kupeŵeranji Kusafuna Kulakwitsa Kanthu?

Ntchito yochitidwa mwaluso kwambiri, kukwaniritsa miyezo yapamwamba zedi yolinganizika ndi ulemerero zikufunika kwambiri. Chotero anthu ayenera kupikisana kuti apeze ntchito. Chinthu china chomwe chikuchititsa anthu ambiri kuyesetsa zolimba ndicho kuopa kutaya njira zawo zopezera zofuna zawo. Antchito ena akukhala ngati katswiri wa maseŵera olimbitsa thupi amene akudzipereka monyanyira kuti atchuke kwambiri. Kenako pamene akumana ndi akatswiri anzake ovuta, angalingalire kuti n’koyenera kuti akakonzekere mowonjezereka, mwinamwake akumagwiritsa ntchito mankhwala okuza thupi kuti mwina zingasinthe ndi kuyembekezera kudzapambana. M’malo mopeza ulemerero mwaubwino, kusafuna kulakwitsa pochita zinthu kumachititsa anthu kukhala “osonkhezereka ndi mantha” kapena “kufunitsitsa kukhala wopambana onse.”​—The Feeling Good Handbook.

Kunena zoona, ena amalingalira kuti zomwe angachite paluso linalake kapena pa maseŵera nthaŵi zonse zingawongoleredwe. Komabe, malinga n’kunena kwa Dr. Robert S. Eliot, “kusafuna kulakwitsa kanthu ndiko chiyembekezo cha zinthu zosatheka.” Iye anawonjezera kuti: “Iko kumaphatikizapo kudzimva wamlandu, wosatetezeka, ndi kuopa kunyozedwa.” Chotero, mawu a Mfumu yanzeruyo Solomo n’ngoonatu zedi. Iye anati: “Ndinapenyera mavuto onse ndi ntchito zonse zom’pindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ake achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.”​—Mlaliki 4:4.

Kodi mungachitenji ngati mutaona kuti mwayamba kungofuna zangwiro zokhazokha? Kodi n’zoona kuti mukamayesetsa zolimba, m’pamenenso mumakhumudwa kwambiri? Kodi mungakonde kukhala wosafuna zambiri ndi womasuka kwambiri? Kodi kukhala wangwiro kumatanthauzanji? Kodi simukufunitsitsa kugwiritsa ntchito luso lanu monga momwe mungathere panthaŵi imodzimodziyo mukumapeŵa malingaliro ongofuna zangwiro zokhazokha? Ngati anthu opanda ungwiro angagwiritse ntchito maluso awo omwe Mulungu anaŵapatsa kuvumbula zinthu zopindulitsa ena, talingalirani zomwe mtundu wa anthu udzakwaniritsa m’mikhalidwe yangwiro ndi m’chitsogozo chaumulungu!

[Chithunzi patsamba 4]

Makolo kapena anthu ena angafune kuti achinyamata azichita zinthu popanda kulakwitsa chilichonse, zomwe achinyamatawo sangazikwanitse