Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimbitsa Chikhulupiro mwa Kuphunzira Baibulo ku India

Kulimbitsa Chikhulupiro mwa Kuphunzira Baibulo ku India

 Ndife a Iwo Omwe Ali Ndi Chikhulupiriro

Kulimbitsa Chikhulupiro mwa Kuphunzira Baibulo ku India

KUCHOKERA kumpoto ku mapiri aatali a Himalaya ophimbidwa ndi chipale chofeŵa mpaka kumwera ku gombe la nthunzi la nyanja ya Indian Ocean, India ndi dziko lokhala ndi malo, nyengo, ndi zipembedzo zosiyanasiyana kwambiri. Lili ndi chiŵerengero cha anthu chopitirira biliyoni imodzi, ndipo pafupifupi 83 peresenti ndi Ahindu, 11 peresenti ndi Asilamu, ndipo chigawo chotsalacho ndi chophatikizika Akristu, Asiki, Abuda ndi Ajaini. Onse ali ndi ufulu wakulambira. “Chipembedzo n’chofunikira pachikhalidwe cha ku India,” imatero The World Book Encyclopedia.

Kukhala mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo Chachikristu kumasiyanitsa Mboni za Yehova, zimene zili m’chiŵerengero chopitirira 21,200 ku India. Mofanana ndi Akristu anzawo m’mbali zina za dziko lapansili, Mboni ku India zimaona kukhala mwayi waukulu kuthandiza anansi awo kuti akulitse chikhulupiriro m’Mawu a Mulungu, Baibulo Loyera. (2 Timoteo 3:16, 17) Taonani mwachitsanzo mmene banja lina ku Chennai kumwera kwa India linadziŵira choonadi cha Baibulo.

Banjali lisanakumane ndi Mboni za Yehova, linali lokangalika m’gulu lochita zozizwitsa la Katolika, lodzinenera kukhala loona masomphenya, kulankhula malilime ndi kuchiritsa odwala. Linali lotchuka mu tchalitchi ndi kwa anthu onse, moti anthu ankatchula ena a m’banjali kuti “swami,” kutanthauza “mbuye.” Kenako tsiku lina wa Mboni anawachezera ndi kuŵasonyeza m’Baibulo kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, osati Mulungu Wamphamvuyonse, ngati mmene anthu ambiri amakhulupirira. Mboniyo inaŵaonetsanso kuti dzina la Mulungu ndi Yehova ndi kuti chifuno chake ponena za dziko lapansili n’chakuti likhale paradaiso.​—Salmo 83:18; Luka 23:43; Yohane 3:16.

Chifukwa chakuti amalemekeza Mawu a Mulungu ndiponso amakonda zimene amamva, a m’banjali anavomera phunziro lokhazikika la Baibulo ndi Mboni za Yehova. Izi zinabweretsa chitonzo kuchokera kwa anzawo akutchalitchi. Ngakhale zinali choncho, banjali linakhalabe lofunitsitsa kupitiriza kuphunzira Baibulo. Pamene chidziŵitso ndi chikhulupiriro chawo chimakula ndi kulimba, anasiya zikhulupiriro zawo zonyenga. Tsopano, anthu atatu a m’banjali ndi okangalika komanso Mboni zobatizidwa ndipo mayi wabanjali amachita upainiya wothandiza pa mpata uliwonse.

Chikhulupiro Chingathandize Olemala

Sunder Lal, wachinyamata wokhala ku mudzi wa ku Punjab, anafunikira chikhulupiriro ndi chilimbikitso kuti ayambe kugaŵana ndi ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Choyamba, Sunder Lal anasiya kukhulupirira kuti kuli milungu yambiri imene a m’banja ndi akumudzi wakwawo anali kukhulupirira, n’kuyamba kulambira Mulungu woona, Yehova. Chifukwa chinanso n’chakuti, Sunder Lal alibe miyendo.

Mpaka chaka cha 1992, moyo wa Sunder Lal unali wabwinobwino. Ankagwira ntchito yothandizira dokotala komabe anali akupitiriza kulambira pamodzi ndi banja lake milungu yosiyanasiyana motsogozedwa ndi mphunzitsi wawo. Koma tsiku lina usiku, anagwa powoloka njanji. Ndiyetu sitima inam’ponda n’kuduliratu miyendo yonse m’nchafu. Ngakhale sanafe, iye anaona kuti moyo wake wawonongeka kotheratu. M’pomveka  kuti Sunder Lal anakhala wopsinjika maganizo ngakhalenso kuganiza zodzipha kumene. Ngakhale kuti abale ake anali othandiza kwambiri, iye anatairatu mtima ponena za m’tsogolo.

Kenako wa Mboni za Yehova anacheza naye Sunder Lal ndi kumuonetsa m’Baibulo kuti Mulungu analonjeza kusandutsa dziko lapansili kukhala paradaiso wokongola ndi kupereka moyo wathanzi kwa onse amene amam’konda ndi kumuopa. Sunder Lal anavomera phunziro la Baibulo, ndipo anaphunzira mwakhama kwa chaka chathunthu. Anamuitanira ku misonkhano yachikristu, kumene pomalizira pake anapita panjinga ndi bwenzi lake. Ngakhale kuti unali ulendo wopweteka, mphotho yake inali yaikulu. Anatsimikizira zimene anali ataphunzira pa phunziro laumwini kukhala zoona atakumana ndi ena amene amakhulupiriradi malonjezo a Mawu a Mulungu ndi kukhala mogwirizana ndi ziphunzitso za Baibulo.

Sunder Lal anayamba kugaŵana uthenga wabwino ndi anansi ake, ndipo mu 1995 anabatizidwa. Poyamba, njira yopitira muulaliki wa kukhomo ndi khomo kwa iye inali kudzikhwekhwereza. Koma tsopano analandira mphatso kwa abale ake auzimu​—njinga ya olemala ya mawiro atatu yotchova ndi manja. Ndi njinga imeneyi tsopano amatha kuyenda yekha mtunda wa makilomita 12 kupita kumisokhano ya mpingo. Nthaŵi zina amatchova mu mvula ya mkuntho ndipo nthaŵi zina kutatentha kwambiri mpaka 43 digiri Celsius.

Kuphatikiza pa kupita kumisonkhano, Sunder Lal amachititsa maphunziro ambiri a Baibulo ndi ena amene amafuna chithandizo kuti alimbitse chikhulupiriro chawo mwa Mulungu woona Yehova. Panopa 7 mwa ophunzira ake ndi obatizidwa, komanso ena atatu amene anawalalikira koma anaphunzitsidwa Baibulo ndi Mboni zina.

Malinga ndi kunena kwa Baibulo, “si onse ali nacho chikhulupiriro.” (2 Atesalonika 3:2) Koma kwa “onse amene anaikidwiratu ku moyo wosatha.” Phunziro lokhazikika la Mawu a Mulungu lingalimbitse chikhulupiriro chawo. (Machitidwe 13:48) Phunziro lotero limapangitsa maso kuwala ndi chiyembekezo chodabwitsa cha m’tsogolo​—chimene anthu ambiri a ku India akuchikhulupirira.

[Mapu patsamba 30]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AFGANISTAN

PAKISTAN

NEPAL

BHUTAN

CHINA

BANGLADESH

MYANMAR

LAOS

THAILAND

VIETNAM

CAMBODIA

SRI LANKA

INDIA

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom. Inc.