Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pezani Chitonthozo M’nyonga ya Yehova

Pezani Chitonthozo M’nyonga ya Yehova

 Pezani Chitonthozo M’nyonga ya Yehova

“Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.”​—SALMO 94:19.

KWA onse amene akufunitsitsadi chitonthozo, Baibulo lili nawo mawu otonthoza. Tsonotu n’zosadabwitsa kuti buku lotchedwa The World Book Encyclopedia limanena kuti “anthu osaŵerengeka atembenukira ku Baibulo kuti apeze chitonthozo, chiyembekezo, ndi chilangizo m’nthaŵi ya mavuto ndi ya kuthedwa nzeru.” Chifukwa chiyani?

Chifukwa chakuti Baibulo n’louziridwa ndi Mlengi wathu wachikondi, “Mulungu wa chitonthozo chonse,” Yemwe ali “wotitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Iye ali “Mulungu . . . wachitonthozo.” (Aroma 15:5) Yehova wapereka chitsanzo potipatsa tonsefe njira yopezera mpumulo. Iye anatumiza Mwana wake wobadwa yekha, Kristu Yesu, kudziko lapansi kudzatipatsa chiyembekezo ndi chitonthozo. Yesu anaphunzitsa kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Baibulo limam’longosola Yehova kukhala yemwe “tsiku ndi tsiku atisenzera katundu, Ndiye Mulungu wa chipulumutso chathu.” (Salmo 68:19) Anthu oopa Mulungu anganene motsimikiza mtima kuti: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthaŵi zonse: Popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.”​—Salmo 16:8.

Ndime za m’Baibulo zoterozo zimasonyeza chikondi chakuya chomwe Yehova Mulungu ali nacho kwa ife anthu. N’zoonekeratu kuti iye n’ngwofunitsitsa kuchokera pansi pa mtima, komanso n’ngwokhoza, kupereka chitonthozo chochuluka ndi kuthetsa zoŵaŵa zathu m’nthaŵi za mavuto. “Iye alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.” (Yesaya 40:29) Tsono tingapeze motani chitonthozo m’nyonga ya Yehova?

Kutonthoza Mtima kwa Chisamaliro cha Yehova

Wamasalmo analemba kuti: “Um’senze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Inde, Yehova Mulungu amasamala kwambiri za mtundu wa anthu. Mtumwi Petro anatsimikizira Akristu a m’zaka za zana loyamba kuti: “Iye [Mulungu] asamalira inu.” (1 Petro 5:7) Yesu Kristu anagogomeza mmene Mulungu amawaonera anthu kukhala amtengo wapatali mwa kunena kuti: “Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiŵiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiŵalika pamaso pa Mulungu; komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu aŵerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.” (Luka 12:6, 7) Ndife ofunika kwambiri kwa Mulungu kotero kuti amaonetsetsa kanthu kalikonse pa ife ngakhale kakang’ono kwambiri. Akudziŵa zinthu zomwe enife sitidziŵa chifukwa chakuti amasamala kwambiri za aliyense wa ife.

Kuzindikira chidwi chenicheni cha Yehova chimenechi kunali kotonthoza kwambiri kwa Svetlana, msungwana wachiwerewere amene watchulidwa m’nkhani yapitayo. Msungwanayu anangotsala pang’ono kuti adziphe pamene anakumana ndi Mboni za Yehova. Nthaŵi yomweyo anavomera kuphunzira Baibulo, lomwe linam’thandiza kum’dziŵa bwino Yehova monga munthu weniweni amene amasamaladi za moyo wake. Zimenezi zinam’khudza mtima, zinam’sonkhezera kusintha njira zake za moyo ndi kudzipatulira kwa Mulungu. Zinam’panganso Svetlana kudzimva monga wofunika kotero kuti mosasamala kanthu za mavuto ake, analimbikira ndi kukhala ndi kaonedwe koyenera ka moyo. “Ndili wotsimikiza” iye akutero tsopano, “kuti Yehova sadzandisiya konse. Ndaona kuti zomwe zalembedwa pa 1 Petro 5:7 n’zoona. Lembalo limati: ‘Tayani pa [Yehova] nkhaŵa zanu zonse pakuti Iye asamalira inu.’”

Chiyembekezo Chozikidwa pa Baibulo N’chotonthoza

Njira yapadera yomwe Mulungu akuperekera chitonthozo ndiyo kupyolera m’Mawu ake olembedwa, omwe ali ndi chiyembekezo cham’tsogolo chosangalatsa kwambiri. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha Malemba, tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Paulo anamveketsa bwino kugwirizana kwa chiyembekezo chenicheni ndi chitonthozo pamene iye analemba kuti: “Ndipo . . . Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso [“chitonthozo,” NW] chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo, asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mawu onse abwino.” (2 Atesalonika 2:16, 17) “Chiyembekezo chokoma” chimenechi chikuphatikizapo chiyembekezo cha moyo wangwiro, wachimwemwe, ndi wosatha wa padziko lapansi la Paradaiso.​—2 Petro 3:13.

Chiyembekezo chotsimikizirika ndi chabwino choterocho n’chomwe chinalimbikitsanso Laimonis, chidakwa chopuŵala  chotchulidwa m’nkhani yoyamba ija. Mwa kuŵerenga mabuku ozikidwa pa Baibulo a Mboni za Yehova, iye anali wachimwemwe kuphunzira za dziko latsopano mu Ufumu wa Mulungu, momwe thanzi lake lidzabwezeretsedwa kotheratu. M’Baibulo iye anaŵerenga lonjezo labwino zedi la kuchiritsa mozizwitsa lakuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba.” (Yesaya 35:5, 6) Kuti ayenerere moyo wa m’Paradaiso ameneyo, Laimonis anasintha kotheratu. Analeka kumwa moŵa, ndipo kusintha kwakeku kunali koonekeratu kwa anansi ndi mabwenzi ake. Tsopano amachititsa maphunziro a Baibulo ambiri, amagaŵana ndi ena chitonthozo chomwe chiyembekezo chozikidwa pa Baibulo chimapereka.

Ntchito ya Pemphero

Pamene tikumva kupweteka mumtima kaamba ka zifukwa zina, tingapeze chitonthozo mwa kupemphera kwa Yehova. Kuchita zimenezi kungatipepuze nkhaŵa zathu. Pamene tikupemphera, tingatonthozedwe pokumbukira zinthu zonenedwa m’Mawu a Mulungu. Salmo lalitali loposa onse m’Baibulo lili ngati pemphero lokoma. Wopeka wake anaimba kuti: “Ndinakumbukira maweruzo anu kuyambira kale, Yehova, ndipo ndinadzitonthoza.” (Salmo 119:52) M’mikhalidwe yovuta kwenikweni, makamaka yomwe imakhudza mavuto a umoyo, kaŵirikaŵiri sipakhala yankho limodzi lokha lothetsera mavuto onsewo. M’nyonga yathuyathu, sitingadziŵe kwenikweni komwe tiyenera kutembenukira. Ambiri aona kuti pamene zonse zimene munthu akanatha kuchita zalephera, kutembenukira kwa Mulungu m’pemphero kumadzetsa chitonthozo chachikulu ndipo nthaŵi zina, njira za mwadzidzidzi zothetsera mavutowo.​—1 Akorinto 10:13.

Pat, yemwe anathamangira naye ku chipinda cha matenda akayakaya, analandira chitonthozo cha pemphero choterechi. Atachira, mkaziyu anati: “Ndinapemphera kwa Yehova ndipo ndinadziŵadi kuti ndinayenera kusiya moyo wanga m’manja mwake, kum’khulupirira iye kuchita chilichonse chomwe chinali chifuno chake. M’nthaŵi yonseyi, maganizo anga anali atadekha; ndinali pa mtendere wa Mulungu wotchulidwa pa Afilipi 4:6, 7.” Mavesi ameneŵa angakhale otonthoza kwambiri kwa tonsefe! Pamenepo Paulo akutilangiza kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”

Mzimu Woyera Monga Wotonthoza

Usiku uja imfa yake isanachitike, Yesu anauza atumwi ake momveka bwino lomwe kuti posakhalitsa adzawasiya. Zimenezi zinawavutitsa ndi kuwamvetsa chisoni. (Yohane 13:33, 36; 14:27-31) Pozindikira kufunikira kwawo chitonthozo chowonjezereka, Yesu analonjeza kuti: “Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe ina [kapena kuti wotonthoza], kuti akhale ndi inu ku nthaŵi yonse.” (Yohane 14:16; NW mawu a m’munsi) Pano Yesu anali kunena za mzimu woyera wa Mulungu. Mwa zina, mzimu wa Mulungu unatonthoza atumwiwo m’nthaŵi ya mayesero awo, ndipo unawalimbitsa kuti apitirizebe kuchita chifuno cha Mulungu.​—Machitidwe 4:31.

Angie, yemwe mwamuna wake anangotsala pang’ono kumwalira atachita ngozi yoopsa, anali wokhoza kupirira mavuto onse ndi zoŵaŵa za mkhalidwe wakewo. N’chiyani chinam’thandiza? Iye akuti: “Popanda kuchirikizidwa ndi mzimu woyera wa Yehova, sitikanatha kupyola zomwe takumana nazozi ndikukhalabe wolimba. Ndithudi nyonga ya Yehova yaonekera mwa zofooka zathu, ndipo wasonyezadi kukhala linga m’nthaŵi yathu ya mavuto.”

Ubale Wotonthoza

M’mkhalidwe uliwonse umene munthu angakhale m’moyo, kaya ndi mkhalidwe wopweteka chotani womwe ungabuke, iye angathe kupeza chitonthozo mu ubale womwe ulipo mumpingo wa Yehova. Ubale umenewu umapereka chichirikizo chauzimu ndi chithandizo kwa onse ogwirizana nawo. Mu ubale umenewu, aliyense angapeze gulu la mabwenzi achikondi, osamalira za ena, ndiponso otonthoza, omwe ali okonzeka ndi ofunitsitsa kuthandiza ndi kutonthoza ena m’nthaŵi ya mavuto.​—2 Akorinto 7:5-7.

 Amene ali ziwalo za mpingo wachikristu amaphunzitsidwa ‘kuchitira onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja [lawo] la chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Maphunziro ozikidwa pa Baibulo omwe amalandira amawasonkhezera kusonyeza chikondi cha pa abale ndi kukondana wina ndi mnzake ndi chikondi chenicheni. (Aroma 12:10; 1 Petro 3:8) Abale ndi alongo auzimu mumpingo, amasonkhezereka kukhala okoma mtima, otonthoza, komanso amtima wachifundo.​—Aefeso 4:32.

Joe ndi Rebecca, omwe mwatsoka anatayikidwa mwana wawo wamwamuna mu imfa, anapeza chichirikizo chotonthoza chimenecho kuchokera kwa anthu a mumpingo wachikristu. Iwo akuti: “Yehova ndi mpingo wake wachikondiwu watithandiza kupyola nthaŵi yathu yovuta. Tinalandira makadi, makalata ndi matelefoni ambirimbiri. Zimenezi zatichititsa kuzindikira mmene ubale wathuwu ulili wamtengo wapatali. Pamene tinali pachisoni chachikulu kaamba ka tsokalo, mipingo yambiri ya kwathuko inatithandiza, kutipatsa chakudya ndi kutiyeretsera m’nyumba.”

Pezani Chitonthozo!

Pamene mkuntho wamphamvu wa masoka uyamba kuwomba, ndiponso pomwe mvula ya matalala a mavuto yosalekeza ipitirizabe kuvumbwa, Mulungu amakhala wokonzeka kupereka chitetezo chotonthoza. Limodzi la masalmo likum’longosola monga malo othaŵiramo motere: “Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathaŵira kunsi kwa mapiko ake; Choonadi chake ndicho chikopa chochinjiriza.” (Salmo 91:4) Pano tingafanizire ndi chiwombankhanga. Chithunzi chili pano ndi cha mbalame imene yazindikira ngozi ndiyeno pofuna kuteteza anapiye ake itambasula mapiko ake ndi kuphimba nawo anapiye akewo. Kwakukulukulu, Yehova ndiye Mtetezi weniweni kwa onse othaŵira kwa iye.​—Salmo 7:1.

Ngati mukufuna kuphunzira zambiri ponena za Mulungu, umunthu wake, zolinga zake, ndiponso mphamvu zake zokhoza kupereka chitonthozo, phunzirani Mawu ake. Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukuthandizani pambali imeneyi. Inde, nanunso mungapeze chitonthozo m’nyonga ya Yehova!

[Zithunzi patsamba 7]

Chiyembekezo cha m’tsogolo chozikidwa pa Baibulo chingapereke chitonthozo