Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

 Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Atatu mwa Mauthenga Abwino akusimba za kudandaula chifukwa chakuti Yesu anadzozedwa mafuta amtengo wapatali. Kodi odandaulawo anali atumwi ambiri, kapena anali Yudasi yekhayo?

Chochitika chimenechi tikuchipeza m’Mauthenga Abwino a Mateyu, Marko, ndi Yohane. Zikuonetsa kuti Yudasi ndi yemwe anatsogolera kung’ung’udza kumeneku, kenako atumwi ena angapo anavomerezana naye. Chochitikachi chikusonyeza chifukwa chake tingakhalire othokoza pokhala ndi Mauthenga Abwino anayi ameneŵa. Zomwe mlembi aliyense analemba zinali zolondola, koma si onse omwe analemba nkhani zofanana. Mwa kuyerekeza nkhani zofananazo, timamva zambiri za zochitikazo mwatsatanetsatane.

Nkhani ya pa Mateyu 26:6-13 imatchula malo​—nyumba ya Simoni wakhate, ku Betaniya​—koma siimatchula dzina la mkazi yemwe anatsanulira mafuta onunkhira bwino pamutu pa Yesu. Mateyu akuti: ‘Koma mmene ophunzira anaona, anada mtima’ nadandaula kuti mafutawo akanatha kugulitsidwa ndi kupatsa ndalamazo anthu aumphaŵi.

Nkhani ya Marko ikuphatikiza mfundo zambiri mwa zimenezo. Koma akuwonjezera kuti mkaziyo anaswa nsupayo. M’nsupamo munali mafuta omwe anali “nardo weniweni,” kukhala ngati anachita kuitanitsidwa kuchokera ku Indiya. Ponena za kung’ung’udzako, Marko anati ‘anakhalako ena anavutika mtima,’ ndipo “anadandaulira mkaziyo.” (Marko 14:3-9) Choncho nkhani ziŵirizi zikusonyeza kuti si mtumwi mmodzi yekha amene anadandaula. Komabe kodi zimenezo zinayamba motani?

Yohane, yemwe anaona zimenezi zikuchitika, anawonjezera mfundo zogwira mtima. Iye anatchula dzina la mkaziyo kuti anali Mariya, mchemwali wake wa Marita ndi Lazaro. Yohane anaperekanso mfundoyi, yomwe tingaitenge ngati umboni wowonjezera osati wotsutsa nkhaniyi. Iye anati: ‘Anadzoza mapazi a Yesu, napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake.’ Titagwirizanitsa nkhanizi, tingaone kuti Mariya ayenera kuti anam’dzozadi Yesu m’mutu ndi mapazi, mafuta omwe Yohane anatsimikizira kuti anali a “nardo a mtengo wake wapatali.” Yohane anali bwenzi lapamtima la Yesu ndipo anali kukwiya msanga ngati wina achitira Yesu ngakhale chipongwe chochepa chabe. Timaŵerenga kuti: “Yudase Isikariote, mmodzi wa akuphunzira ake, amene [“anali” Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono] kudzam’pereka Iye, ananena: Nanga mafuta onunkhira awa sanagulitsidwa chifukwa ninji ndi malupiya atheka mazana atatu, ndi kupatsidwa kwa osauka?”​—Yohane 12:2-8.

N’zoona kuti Yudasi anali “mmodzi wa akuphunzira ake,” koma mungaone mmene Yohane analili wokwiya kuti winawake mwa iwo anakonza zopereka Yesu. Wotembenuza wina Dr. C. Howard Matheny ananenapo za Yohane 12:4 kuti: “Mawu onse aŵiri awa akuti ‘anali kudza . . . ,’ ndi akuti “anali kudzam’pereka” akufotokoza za chochitika chopitiriza kapena chimene chikuchitikabe. Zimenezi zikusonyeza kuti kuperekedwa kwa Yesu ndi Yudasi sichinali chinthu chongochitika mwadzidzidzi panthaŵi yomweyo chifukwa chakuti anaganizira ndi kukonzekera masiku ambirimbiri za mmene adzam’perekere.” Yohane anawonjezera mfundo yakuti Yudasi anang’ung’udza ‘osati chifukwa chodera nkhaŵa osaukawo, koma chifukwa anali mbala ndipo ankasunga thumba la ndalama, amaba zoikidwamo.’

Chotero n’zoonekeratu kuti mbalayo Yudasi ndiye amene anayambitsa kung’ung’udzako chifukwa chakuti akanakhala ndi zochuluka zoti abe ngati mafuta amtengo wake wapataliwo akanagulitsidwa ndi kuika ndalamazo m’thumba lomwe Yudasiyo ankasunga. Yudasi atadandaula choncho, atumwi enawo ayenera kuti anang’ung’udzanso akumavomereza yomwe inaoneka ngati mfundo yoyenera. Komabe Yudasi, ndiye anatsogolera kung’ung’udzako.