Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitonthozo Chikufunikatu Kwambiri!

Chitonthozo Chikufunikatu Kwambiri!

 Chitonthozo Chikufunikatu Kwambiri!

“Taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwoŵa analibe wakuwatonthoza.”​—MLALIKI 4:1.

KODI mukufuna kutonthozedwa? Kodi mukulakalaka mutatonthozedwa pang’ono chabe kuti mumasuke ku nkhaŵa yaikulu imene muli nayo? Kodi mukukhumba kutonthozedwa ngakhale ndi mawu ochepa chabe kuti muyese kupeputsa mavuto owawitsa ndi zochitika zosakondweretsa m’moyo uno?

Panthaŵi inayake, tonsefe timafuna kwambiri chitonthozo ndi chilimbikitso. Izi zili choncho chifukwa chakuti muli zinthu zambirimbiri m’moyo zomwe zimadzetsa chisoni. Tonsefe timafuna kutetezedwa, kusangalatsidwa, kukumbatiridwa. Enafe ndife okalamba ndipo ukalambawo sitikondwera nawo. Ena ndi okhumudwa kwambiri chifukwa chakuti sanakhale moyo umene amayembekezera. Komano ena ataya mtima pakumva zotsatira kuchokera ku chipinda chopimira matenda.

Komanso, n’ngoŵerengeka chabe omwe angatsutse kuti zochitika m’nthaŵi yathu ino zachititsa kufunika kwakukulu kwa chitonthozo ndi chiyembekezo. M’zaka 100 zokha zapitazi, anthu oposa 100,000,000 aphedwa m’nkhondo. * Pafupifupi onsewo anasiya banja lili lachisoni​—amayi ndi abambo, achemwali ndi achimwene, akazi amasiye ndi ana amasiye​—ali ofunikira kutonthozedwa. Lerolino, anthu oposa biliyoni imodzi ali pa umphaŵi wadzaoneni. Theka la anthu padziko lonse akusoŵa njira zopezera chithandizo cha mankhwala nthaŵi zonse komanso mankhwala oyenerera. Mamiliyoni a ana onyalanyazidwa akungoyendayenda m’misewu ya m’mizinda ikuluikulu, ambiri mwa iwo amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi kuchita uhule. Miyandamiyanda ya othaŵa kwawo akuvutika kwambiri m’misasa yoipa.

Komabe ziŵerengerozi, ngakhale kuti n’zazikulu chonchi, sizikusonyeza ululu wa munthu aliyense payekha ndi mavuto amene ena akukumana nawo m’moyo wawo. Mwachitsanzo, talingalirani za Svetlana, msungwana wa ku Balkans yemwe anabadwira mu umphaŵi wadzaoneni. * “Kuti tipeze ndalama,” akutero msungwanayu, “makolo anga  ankandituma kukapemphetsa kapena kukaba. Moyo m’banjamo unaipiratu mwakuti ine ndinayamba kugonedwa ndi achibale. Ndinapeza ntchito yoperekera zakumwa m’bala, ndipo mayi anga, omwe ankalandira ndalama zomwe ankandilipirazo, ananena kuti ngati ndidzasiya ntchitoyo, iwo adzadzipha. Zonsezi zinandipangitsa kuyamba moyo wa uhule. Ndinali ndi zaka 13 zokha. M’kupita kwa nthaŵi, ndinatenga mimba ndipo ndinaichotsa. Pamsinkhu wa zaka 15, ndinkaoneka ngati munthu wa zaka 30.”

Laimonis, mnyamata wa ku Latvia, akusimba mmene anafunikira chitonthozo ndi zochitika zimene zinam’dzetsera chisoni chachikulu. Ali ndi zaka 29, anachita ngozi yagalimoto yomwe inam’puwalitsa kuyambira m’chiunomu mpaka kumapazi. Iye anatayiratu mtima moti anaganiza zongoloŵerera uchidakwa. Pambuyo pa zaka zisanu iye anali atatheratu, anali chidakwa chotha ntchito chopanda tsogolo lililonse. N’kuti kumene akanapeza chitonthozo?

Kapena lingalirani za Angie. Mwamuna wake anam’chita opaleshoni ya ubongo katatu konse yomwe poyamba inali itam’chititsa kukhala wozerezeka pang’ono. Kenako, patapita zaka zisanu chichitire opaleshoni yotsiriza, anachita ngozi yoopsa kwambiri, ngozi yomwe ikanamupha. Mkazi wake ataloŵa m’chipinda cha matenda akayakaya ndi kuona mwamuna wake ali chikomokere atavulala m’mutu modetsa nkhaŵa, anadziŵa kuti tsoka linali lomwelo. Tsogolo lake ndi labanja lake linali kudzakhala lovuta. Akanapeza motani thandizo ndi chilimbikitso?

Kwa Pat, tsiku lina m’dzinja zaka zingapo zapitazo linaoneka ngati layamba monga mwa masiku onse. Komano sanadziŵe n’komwe zomwe zinachitika masiku ena atatu otsatira. Pambuyo pake mwamuna wake anamuuza kuti m’chifuŵa mwake mutayamba kupweteka kwambiri, mtima wake unalekeratu kugunda. Mtima wake unayamba kugunda mothamanga kwambiri komanso mwa apa ndi apo, kenako unangosiiratu osagundanso. Analeka kupuma. “Kwenikweni achipatala ankangoti ndafa kale,” akutero Pat. Koma mosayembekezereka anakhalabe moyo. Ponena za kukhala kwake m’chipatala nthaŵi yaitali iye akuti: “Ndinkaopa kwambiri kundipima kochuluka kumene anachita, makamaka pamene amayesa mtima wanga mwa kuupangitsa kugunda mofulumira kwambiri mwa apa ndi apo ndiyeno n’kusiya, monga momwe unachitira poyambapo.” N’chiyani chomwe chikanam’patsa chitonthozo chofunikiracho ndi mpumulo m’nthaŵi yovutayi?

Joe ndi Rebecca anatayikidwa mwana wawo wamwamuna wazaka 19 pangozi ya galimoto. “Tinali tisanakumanepo ndi china chilichonse chosakaza motero,” iwo akutero. “Ngakhale kuti ife, m’mbuyomu, timalira nawo maliro anthu ena pamene anafedwa, sitinali kumva ululu waukulu wa mumtima monga momwe tikumvera tsopano lino.” N’chiyani kwenikweni chomwe chingatonthoze “ululu waukulu wa mumtima” kapena kuti chisoni chosaneneka cha kutaya winawake yemwe mumam’konda kwambiri?

Ndithudi anthu onseŵa, ndi enanso miyandamiyanda, apeza gwero lapamwamba zedi la chitonthozo ndi chisangalalo. Kuti muone mmene inunso mungapindulire kuchokera pa gwero limenelo, chonde pitirizanibe kuŵerenga.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Chiŵerengero chenicheni cha asilikali ndi anthu wamba omwe afa sichikudziŵika. Mwachitsanzo, buku la 1998 lakuti Facts About the American Wars (Zoona Zake za Nkhondo za America) linanenapo za nkhondo yachiŵiri yokha yadziko lonse kuti: “Mabuku ambiri amapereka chiwonkhetso cha omwe anafa pa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse (asilikali ndi anthu wamba) kukhala 50 miliyoni koma ambiri omwe afufuza mosamalitsa nkhaniyi akukhulupirira kuti chiŵerengero cholondola n’chokwera kwambiri, ngakhale kuŵirikiza kaŵiri nambala imeneyo.”

^ ndime 6 Tasintha dzina lake.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

UNITED NATIONS/​CHITHUNZI CHOJAMBULIDWA NDI J. K. ISAAC

CHITHUNZI CHA UN 146150 CHOJAMBULIDWA NDI O. MONSEN