Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwamuna Wachitsanzo Chabwino Amene Anavomera Kum’langiza

Mwamuna Wachitsanzo Chabwino Amene Anavomera Kum’langiza

Mwamuna Wachitsanzo Chabwino Amene Anavomera Kum’langiza

“KU Zambia, Ng’ona Zimadya Anthu 30 Pamwezi.” Inatero nyuzipepala ina ya mu Afirika zaka zingapo zapitazo. Malinga ndi kunena kwa wophunzira za nyama amene anazigwira kuti aziphunzire, “panafunikira amuna 12 kuti agwire ng’ona imodzi.” Ng’ona ndi nyama yoopsa chifukwa cha mchira wake wamphamvu ndi kamwa lake lamphamvu.

Mwachionekere potchula ng’ona kukhala “liviyathanu,” (NW) Mlengi anagwiritsira ntchito “mfumu ya zodzitama zonse” imeneyi kuti aphunzitse mtumiki wake Yobu phunziro lofunika. (Yobu 41:1, 34) Izi zinachitika zaka pafupifupi 3,500 zapitazo kudziko la Uzi, chakumpoto kwa Arabia. Pamene amafotokoza za nyama imeneyi, Mulungu anauza Yobu kuti: “Palibe wolimba mtima kuti adzaiputa. Ndipo ndaniyo adzaima pamaso pa Ine?” (Yobu 41:10) Zoonadi zimenezo! Ngati timaopa ng’ona, ndiye tiyenera kuopa kwambiri kutsutsana ndi Uyo amene anailenga! Yobu anasonyeza kuyamikira phunziro limeneli pamene anavomereza tchimo lake.​—Yobu 42:1-6.

Pamene Yobu watchulidwa, tingakumbukire chitsanzo chake cha kukhulupirika popirira mazunzo. (Yakobo 5:11) Kwenikweni, Yehova anakondwera ndi Yobu ngakhale pamene chikhulupiriro chake chinali chisanayesedwe modetsa nkhaŵa. Malinga ndi kuona kwa Mulungu, panthaŵi imeneyo ‘panalibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.’ (Yobu 1:8) Zimenezi ziyenera kutisonkhezera kuphunzira zambiri za Yobu, pakuti potero zidzatithandiza kudziŵa mmene ifenso tingakondweretsere Mulungu.

Anaika Patsogolo Unansi Wake ndi Mulungu

Yobu anali munthu wolemera. Kupatulapo golidi, anali ndi nkhosa 7,000, ngamila 3,000, abulu aakazi 500, ng’ombe 1000, komanso antchito ake anali ambiri. (Yobu 1:3) Koma Yobu anadalira Yehova, osati chuma chake. Analingalira kuti: “Ngati ndayesa golidi chiyembekezo changa, ndi kunena ndi golidi woyengetsa, Ndiwe chikhazikitso changa; ngati ndinakondwera popeza chuma changa n’chachikulu, ndi dzanja langa lapeza zochuluka . . . , ichinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wake; pakuti ndikadakana Mulungu ali m’mwamba.” (Yobu 31:24-28) Mofanana ndi Yobu, tiyenera kuona unansi wathu wolimba ndi Yehova kukhala woposeratu zinthu zakuthupi.

Anachita Chilungamo kwa Anthu Anzake

Kodi Yobu anachita nawo motani atumiki ake? Mawu a Yobu akuti “ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga, kapena wa mdzakazi wanga, potsutsana nane iwo, ndidzatani ponyamuka Mulungu? Ndipo pondizonda Iye ndidzam’yankha chiyani?” Amasonyeza kuti atumiki akewo anam’yesa munthu wopanda tsankhu komanso wosavuta. (Yobu 31:13, 14) Yobu anachimvetsa chifundo cha Yehova n’chifukwa chake anawachitiranso chifundo akapolo ake. Ati chitsanzo chake kukoma ati, makamaka kwa awo amene ali ndi maudindo oyang’anira mu mpingo wachikristu! Nawonso ayenera kukhala osakondera komanso osavuta kuwafikira.

Yobu anasamaliranso amene sanali a pabanja lake. Kusonyeza kuganizira kwake ena, anati: “Ngati ndakaniza aumphaŵi chifuniro chawo, kapena kutopetsa maso a amasiye, . . . ngati ndinasamulira ana amasiye dzanja langa, popeza ndinaona thandizo langa kuchipata; libanthuke phewa langa paphalo, ndi dzanja langa liduke pagwangwa.” (Yobu 31:16-22) Tiyenitu tsono tiwaganizire ovutika amene timawadziŵa mu mpingo wathu.

Chifukwa chosamala za ena mopanda dyera, Yobu anachereza alendo. N’chifukwa chake anati: “Mlendo sakagona pakhwalala, koma ndinatsegulira wam’njira pakhomo panga.” (Yobu 31:32) Ndi chitsanzo chabwinotu kwa atumiki a Mulungu lerolino! Pamene anthu atsopano ochita chidwi ndi choonadi cha Baibulo afika pa Nyumba ya Ufumu, kuwalandira kwathu mwachikondi kungawathandize kukula mwauzimu. Zoonadi, woyang’anira woyendayenda komanso Akristu ena timafunika kuwachereza mwachikondi.​—1 Petro 4:9; 3 Yohane 5-8.

Yobu analinso ndi maganizo abwino ngakhale pa adani ake. Sanakondwere ndi tsoka lomwe linagwera wina wodana naye. (Yobu 31:29, 30) M’malo mwake, anali wofunitsitsa kuwachitira zabwino anthu otero, malinga ndi momwe tikuonera changu chake popempherera anthu atatu aja om’tonthoza monyenga.​—Yobu 16:2; 42:8, 9; yerekezani ndi Mateyu 5:43-48.

Anali Wosadetsedwa ndi Chigololo

Yobu anali wokhulupirika kwa mkazi wake, ndipo sanalole mtima wake kukopeka ndi mkazi wina. Yobu anati: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali? Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi, ngati ndalalira pakhomo la mnzanga, mkazi wanga aperere wina; wina namuike kumbuyo [“ndipo amuna ena am’weramire,” NW]. Pakuti icho ndi choipitsitsa, ndicho mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wake.”​—Yobu 31:1, 9-11.

Yobu sanalole chilakolako choipa kuwononga mtima wake. M’malo mwake, analondola njira yoongoka. M’posadabwitsa kuti Yehova Mulungu anasangalala naye mwamuna wokhulupirika ameneyu amene analimbana ndi chilakolako choipa!​—Mateyu 5:27-30.

Anadera Nkhaŵa Mkhalidwe Wauzimu wa Banja Lake

Nthaŵi zina, ana aamuna a Yobu anakonza mapwando kumene ana ake onse aamuna ndi aakazi anapezekapo. Atapita masiku a mapwando ameneŵa, Yobu anada nkhaŵa kwambiri kuti mwina ana ake anachimwira Yehova m’njira inayake. Choncho Yobu anachitapo kanthu, chifukwa nkhani ya m’Malembayo imati: “Atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mawu, nawapatula, nauka mamaŵa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuŵerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m’mtima mwawo.” (Yobu 1:4, 5) Izi ziyenera kuti zinawathandizadi a pabanja la Yobu kuzindikira kuti chimene iye amafuna kwakukulu n’chakuti iwo akhale ndi mantha aulemu kwa Yehova ndi kuyenda m’njira Yake!

Lero, amuna achikristu amene ali mitu ya mabanja ayenera kuphunzitsa mabanja awo Mawu a Mulungu, Baibulo. (1 Timoteo 5:8) Ndipotu ayenera kupempherera mabanja awo.​—Aroma 12:12.

Anapirira Mokhulupirika Mayesero

Anthu ambiri amene amaŵerenga Baibulo amadziŵa bwino mayesero ovuta amene anagwera Yobu. Satana Mdyerekezi anatsutsa kuti atakumana ndi mayesero, Yobu akananyoza Mulungu. Yehova analola chinenezo chimenechi, ndipo mosachedwa Satana anabweretsa tsoka pa Yobu. Anatayikidwa ziŵeto zake zonse. Choipitsitsanso, anataya ana ake onse mu imfa. Pasanapite nthaŵi, Satana anam’kantha Yobu ndi zilonda zoŵaŵa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pa mutu wake.​—Yobu, chaputala 1, 2.

Kodi zotsatira zake zinali zotani? Pamene mkazi wake anamuumiriza kuti atukwane Mulungu, Yobu anati: “Ulankhula monga amalankhula akazi opusa. Ha! tidzalandira zokoma kwa Mulungu kodi, osalandiranso zoipa?” Nkhani ya m’Baibulo ikupitiriza kuti: “Pa ichi chonse Yobu sanachimwa ndi milomo yake.” (Yobu 2:10) Inde, Yobu anapirira mokhulupirika ndipo anasonyezadi kuti Mdyerekezi anali wonama. Nafenso tipirire mayesero ndi kusonyeza kuti chimene chimatisonkhezera kutumikira Yehova ndi kumkonda kwathu basi osatinso zina.​—Mateyu 22:36-38.

Modzichepetsa Anavomera Kum’langiza

Ngakhale Yobu anali chitsanzo chabwino m’njira zambiri, sanali munthu wangwiro. Iye mwini ananena kuti: “Adzatulutsa choyera m’chinthu chodetsa ndani? Nnena mmodzi yense.” (Yobu 14:4; Aroma 5:12) Ndiyetu pamene Mulungu anati Yobu anali wangwiro, zinali zoona m’lingaliro lakuti anachita zonse zimene Mulungu anafuna kwa mmodzi wa atumiki ake opanda ungwiro ndi ochimwa. Zimenezo n’zolimbikitsa kwabasi!

Yobu anapirira chiyeso chake, koma chinavumbula chofooka chake. Atamva za masoka onse amene anam’gwera, anthu atatu ochita ngati om’tonthoza anadzam’chezera. (Yobu 2:11-13) Iwo anati Yehova anali kulanga Yobu chifukwa chochita machimo akulu. Mwachibadwa, Yobu zinam’pweteka chifukwa chom’namizira, ndipo mwamphamvu anaganiza zodziteteza. Koma ananyanyira pofuna kudzilungamitsa. Inde, Yobu anafika popereka chithunzi chakuti anali wolungama kuposa Mulungu!​—Yobu 35:2, 3.

Chifukwa chakuti Mulungu anakonda Yobu, anagwiritsa ntchito mnyamata wina kuti avumbule kulakwa kwa Yobu. Nkhaniyo imati: “Adapsa mtima Elihu . . . adapsa mtima pa Yobu; pakuti anadziyesera yekha wolungama, wosati Mulungu.” Elihu anati: “Yobu wanena, Ine ndine wolungama, ndipo Mulungu wandichotsera choyenera ine.” (Yobu 32:2; 34:5) Koma Elihu sanagwirizane ndi “otonthoza” atatu aja pamaganizo awo olakwika akuti Mulungu anali kulanga Yobu chifukwa cha machimo ake. M’malo mwake, Elihu sanakayikire kukhulupirika kwa Yobu ndipo anam’langiza kuti: ‘Mlanduwo uli pamaso pake [Yehova], ndipo mum’lindire.’ Zoonadi, Yobu akanayembekezera Yehova m’malo mofulumira kulankhula pofuna kudziteteza. Elihu anatsimikizira Yobu kuti: “Mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka [Mulungu] samasautsa.”​—Yobu 35:14; 37:23.

Kaganizidwe ka Yobu kanafunikira kukawongola. N’chifukwa chake, Yehova anam’phunzitsa za kuchepa kwa munthu poyerekeza ndi ukulu wa Mulungu. Yehova ananena za dziko lapansi, nyanja, nyenyezi zakumwamba, nyama, ndi zinthu zina zambiri zodabwitsa m’chilengedwe. Pomalizira pake, Mulungu anatchula za Liviyathanu​—ng’ona. Yobu modzichepetsa analangika, ndipo chifukwa cha ichi akuperekanso chitsanzo china.

Ngakhale pamene tingamachite bwino potumikira Yehova, tidzalakwabe. Ngati talakwa kwambiri, Yehova adzatilanga mwanjira ina yake. (Miyambo 3:11, 12) Tingakumbukire lemba limene lingakhudze chikumbumtima chathu. Mwinamwake Nsanja ya Olonda kapena chofalitsa china chilichonse cha Watch Tower Society chinganene kenakake kamene kangavumbule kulakwa kwathu. Kapenanso Mkristu mnzathu mwachifundo angatiuze kuti talephera kugwiritsa ntchito mfundo ina ya m’Baibulo. Kodi tidzachita motani ndi kulanga koteroko? Yobu anasonyeza mzimu wolapa, nati: “Ndekha ndidzinyansa, ndi kulapa m’fumbi ndi mapulusa.”​—Yobu 42:6.

Yehova Anam’fupa

Yehova anafupa Yobu, inde kum’lola mtumiki wake kukhalabe ndi moyo zaka zina 140. Nthaŵi imeneyo, analandira zoposa zomwe anataya. Ndipo ngakhale kuti Yobu anamwalira pomalizira pake, adzaukadi m’dziko latsopano la Mulungu.​—Yobu 42:12-17; Ezekieli 14:14; Yohane 5:28, 29; 2 Petro 3:13.

Nafenso Mulungu angatiyanje ndi kutidalitsa ngati tim’tumikira mokhulupirika ndi kuvomereza malangizo onse a m’Baibulo amene timalandira. Tikatero, tidzakhala ndi chiyembekezo chodalirika chokhala ndi moyo m’dongosolo la zinthu latsopano la Mulungu. Chofunika kwambiri, tidzalemekeza Mulungu. Tidzafupidwa chifukwa cha kukhulupirika kwathu ndipo kukhulupirika kumeneko kudzawonjeza umboni wakuti anthu ake amam’tumikira chifukwa cha chikondi chochokera pansi pa mtima osati chifukwa cha dyera. Ati chimwayi chake kukula chomwe tili nacho chokondweretsa mtima wa Yehova, monga anachitira Yobu wokhulupirika, amene modzichepetsa anavomera kum’langiza!​—Miyambo 27:11.

[Zithunzi patsamba 26]

Yobu anasamalira ana amasiye, akazi amasiye, ndi ena chifukwa chowakonda

[Zithunzi patsamba 28]

Yobu anafupidwa kwambiri chifukwa modzichepetsa, anavomera kum’langiza