Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudziŵa “Mtima wa Kristu”

Kudziŵa “Mtima wa Kristu”

 Kudziŵa “Mtima wa Kristu”

“Wadziŵa ndani mtima wa Ambuye [“wa Yehova,” NW], kuti akam’langize Iye? Koma ife tili nawo mtima wa Kristu.”​—1 AKORINTO 2:16.

1, 2. M’Mawu ake, kodi Yehova anaona kuti chofunika ndicho kuvumbula chiyani ponena za Yesu?

KODI Yesu ankaoneka motani? Kodi maonekedwe a tsitsi lake anali otani? nanga khungu lake? nanga maso ake? Kodi anali wamtali chotani? Kodi anali wonenepa kapena woonda chotani? M’zaka mazana onseŵa, zithunzithunzi za Yesu zajambulidwa mosiyanasiyana. Zina zooneka bwino, zinanso zokokomeza. Ena am’jambula monga mwamuna wamphamvu zake, pamene ena am’jambula monga munthu wofooka ndi wosakondwa.

2 Komano Baibulo silitchula zambiri zokhudza maonekedwe a Yesu. M’malo mwake, Yehova anaona kuti chofunika ndicho kuvumbula chinthu china chofunika kwambiri: mtundu wa munthu umene Yesu anali. Nkhani za m’Mauthenga Abwino sizimangosimba zimene Yesu ananena ndi kuchita komanso zimavumbula zenizeni zimene zinali mumtima mwake ndi m’maganizo mwake kuti anene mawu akewo ndi kuchita zinthu zimene anachita. Nkhani zouziridwa zinayizi zimatithandiza kusuzumira mu umene mtumwi Paulo anautcha kuti “mtima wa Kristu.” (1 Akorinto 2:16) M’pofunika kuti tidziŵe bwino malingaliro a Yesu, za mumtima mwake, ndi umunthu wake. Chifukwa chiyani? Pali zifukwa pafupifupi ziŵiri.

3. Kodi kudziŵa bwino mtima wa Kristu kudzatipangitsa kudziŵa chiyani?

3 Choyamba, mtima wa Kristu umatisonyeza zinazake ponena za mtima wa Yehova Mulungu. Yesu anali paunansi wathithithi ndi Atate wake moti Yesuyo anati: “Palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye.”  (Luka 10:22) Zili ngati kuti Yesuyo anali kunena kuti, ‘Ngati mukufuna kum’dziŵa Yehova kuti ndi wotani, yang’anani kwa ine.’ (Yohane 14:9) Chotero pamene tiphunzira zimene Mauthenga Abwino amavumbula ponena za malingaliro a Yesu ndi mmene ankamvera mumtima, kwenikweni timakhala tikuphunzira mmene Yehova amalingalirira ndi mmene amamvera mumtima. Chidziŵitso chimenechi chimatithandiza kuyandikira kwambiri kwa Mulungu wathu.​—Yakobo 4:8.

4. Ngati tikufuna kuchitadi zinthu monga Kristu, kodi choyamba tiyenera kuphunzira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

4 Chifukwa chachiŵiri n’chakuti kudziŵa mtima wa Kristu kumatithandiza ‘kulondola mapazi ake.’ (1 Petro 2:21) Kulondola Yesu si nkhani yongobwereza mawu ake ndi kuchita zomwe anachita. Popeza kuti zonena ndi zochita zimakhala zotsatira za zimene munthu akulingalira ndi mmene akumvera mumtima, kulondola Kristu kumafuna kuti tikulitse “mtima” womwe iyeyo anali nawo. (Afilipi 2:5) M’mawu ena, ngati tikufuna kuchitadi zinthu monga Kristu, choyamba tiyenera kuphunzira kuganiza ndi kumva monga iye mumtima, komatu, monga momwe tingathere monga anthu opanda ungwiro. Chotero, tiyeni, mothandizidwa ndi olemba Mauthenga Abwino, tisuzumire mumtima wa Kristu. Choyamba tidzakambirana zinthu zimene zinapangitsa Yesu kuti azilingalira ndi kumva m’njira imeneyo mumtima mwake.

Moyo Wake Asanadzakhale Munthu wa Padziko Lapansi

5, 6. (a) Kodi mabwenzi athu angatisonkhezere motani? (b) Kodi ndi unansi wotani umene Mwana woyamba wa Mulungu anali nawo kumwamba asanadze padziko lapansi, ndipo kodi unansiwo unam’khudza motani?

5 Zochita za mabwenzi athu a ponda apa m’pondepo zingatikhudze, m’njira yabwino kapena yoipa, posonkhezera malingaliro athu, mmene timamvera mumtima, ndi zochita zathu. * (Miyambo 13:20) Talingalirani unansi umene Yesu anali nawo kumwamba asanadze padziko lapansi. Uthenga Wabwino wa Yohane umanena za Yesu asanadzakhale munthu wa padziko lapansi kuti anali “Mawu” a Mulungu kapena kuti Wom’lankhulira wake. Yohane amati: “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu. Aŵa anali pachiyambi kwa Mulungu.” (Yohane 1:1, 2) Popeza kuti Yehova analibe chiyambi, kukhala kwa Mawuwo ndi Mulungu kuyambira “pachiyambi” kukunena za chiyambi cha ntchito yolenga ya Mulungu. (Salmo 90:2) Yesu ndiye “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” Chotero, iye anakhalako zolengedwa zina zonse zauzimu ndi chilengedwe chonsechi zisanakhaleko.​—Akolose 1:15; Chivumbulutso 3:14.

6 Malinga n’kunena kwa asayansi ena, thamboli lakhala lilipo kwa zaka zosachepera 12,000,000,000. Ngati zimenezo zingakhaledi zoona, Mwana woyamba wa Mulungu anali paunansi wathithithi ndi Atate wake kwa zaka mabiliyoni osaŵerengeka Adamu asanalengedwe. (Yerekezani ndi Mika 5:2.) Chotero pakati pa aŵiriwo panakhala unansi wachikondi kwambiri ndiponso wozama. Monga nzeru yolankhula ngati munthu, Mwana woyamba ameneyu asanakhale munthu wa padziko lapansi akusonyezedwa kuti akunena kuti: “Ndinakhala munthu amene [Yehova] anasangalala naye kwambiri tsiku ndi tsiku, pokhala wosangalala pamaso pake nthaŵi zonse.” (Miyambo 8:30, NW) Zoonadi, kukhalira pamodzi ndi Gwero la chikondi kwa zaka mabiliyoni osaŵerengeka kunali ndi chisonkhezero chachikulu kwambiri pa Mwana wa Mulungu! (1 Yohane 4:8) Mwana ameneyu anadziŵa malingaliro a Atate wake, kamvedwe kawo ka mumtima, ndi njira zawo ndipo anazisonyeza mosiyana ndi mmene wina aliyense akanachitira.​—Mateyu 11:27.

Moyo Padziko Lapansi ndi Zisonkhezero Zina

7. Kodi chimodzi mwa zolinga zimene Mwana woyamba wa Mulungu anayenera kudzera padziko lapansi n’chotani?

7 Mwana wa Mulunguyo anali ndi zambiri zoti aphunzire, popeza chifuno cha Yehova chinali chakuti akonzekeretse Mwana wakeyo kukhala Mkulu wa Ansembe wachifundo, wokhoza “kumva chifundo ndi zofooka zathu.” (Ahebri 4:15) Kukwaniritsa ziyeneretso za ntchito imeneyi ndiko chimodzi mwa zolinga zimene Mwanayo anadzera padziko lapansi  monga munthu. Padziko pano, monga munthu wokhala ndi thupi lanyama ndi magazi, Yesu anakumana ndi mikhalidwe ndi zisonkhezero zimene poyambapo anali kungoziona zikuchitika iye ali kumwamba. Koma tsopano anali kumva mmene anthu amamvera. Nthaŵi zina ankatopa, kumva ludzu, ndi njala. (Mateyu 4:2; Yohane 4:6, 7) Komanso, anapirira zovuta zamtundu uliwonse. Chotero “anaphunzira kumvera” ndipo anakhala ndi ziyeneretso zonse zofunika pantchito yake monga Mkulu wa Ansembe.​—Ahebri 5:8-10.

8. Kodi tikudziŵapo chiyani ponena za ubwana wa Yesu padziko lapansi?

8 Nanga bwanji za zokumana nazo za Yesu pamene anali mwana padziko lapansi? Mbiri ya ubwana wake n’njaifupi kwambiri. Ndipotu, Mateyu ndi Luka okha ndi amene anasimba zochitika zokhudzana ndi kubadwa kwake. Olemba Mauthenga Abwino anadziŵa kuti Yesu anali kumwamba asanadze padziko lapansi. Kuposa china chilichonse, moyo wakewo asanakhale munthu wa padziko lapansi unafotokoza mtundu wa munthu amene iye anadzakhala. Komabe, Yesu anali munthu weniweni. Ngakhale kuti anali wangwiro, anayenerabe kukula kuchokera paukhanda kukhala mwana wamng’ono kenako kukhala mnyamata mpaka atakhala munthu wamkulu, nthaŵi yonseyi akuphunzira. (Luka 2:51, 52) Baibulo limanena zinthu zina zokhudza ubwana wa Yesu zimene mosakayikira zinam’khudza.

9. (a) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yesu anabadwira m’banja losauka? (b) Kodi Yesu ayenera kuti anakulira m’mikhalidwe yotani?

9 Umboni ukusonyeza kuti Yesu anabadwira m’banja losauka. Zimenezi zikusonyezedwa ndi nsembe imene Yosefe ndi Mariya anabwera nayo ku kachisi masiku ngati 40 pambuyo pa kubadwa kwake. M’malo mobwera ndi mwana wa nkhosa monga nsembe yopsereza ndi mwana wa nkhunda kapena njiwa monga nsembe yauchimo, iwo anadza ndi “njiwa ziŵiri kapena maunda aŵiri.” (Luka 2:24) Malinga ndi Chilamulo cha Mose, nsembe imeneyi inkaperekedwa ndi osauka. (Levitiko 12:6-8) M’kupita kwa nthaŵi, banja lodzichepetsa limeneli linakula. Pambuyo pa kubadwa kozizwitsa kwa Yesu, Yosefe ndi Mariya anakhala ndi ana enanso mwa njira yachibadwa osachepera pa asanu ndi mmodzi. (Mateyu 13:55, 56) Chotero Yesu anakulira m’banja lalikulu, mwachionekere m’mikhalidwe yosauka.

10. N’chiyani chikusonyeza kuti Mariya ndi Yosefe anali anthu oopa Mulungu?

10 Yesu analeredwa ndi makolo oopa Mulungu amene anam’samalira bwino. Amayi wake, Mariya, anali mkazi wamikhalidwe yapadera. Kumbukirani kuti pom’lonjera, mngelo Gabrieli anati: “Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe.” (Luka 1:28) Yosefe anali wopembedza kwambiri nayenso. Mokhulupirika, chaka chilichonse anali kuyenda ulendo wa makilomita 150 kupita ku Yerusalemu kukachita Paskha. Mariyanso anali kupita nawo, ngakhale kuti amuna okha ndiwo analamulidwa kutero. (Eksodo 23:17; Luka 2:41) Paulendo wina wotero, Yosefe ndi Mariya, atafufuza kwadzaoneni, anapeza Yesu wazaka 12 zakubadwayo ali m’kachisi pakatikati pa aphunzitsi. Poyankhula ndi makolo ake ogwidwa ndi nkhaŵawo, Yesu anati: “Simunadziŵa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m’zake za Atate wanga?” (Luka 2:49) “Atate”​—mawu amenewo ayenera kuti anali apamtima ndiponso osangalatsa kwa Yesu wachinyamatayo. Mfundo ndi yakuti, umboni ukusonyeza kuti iye anauzidwa kuti Yehova ndiye Atate wake weniweni. Ndiponso, Yosefe ayenera kuti anali atate wom’lera wabwino kwa Yesu. Ndithudi, Yehova sakanasankha  mwamuna waukali kapena wankhanza kuti alere Mwana Wake wokondedwa!

11. Kodi Yesu anaphunzira ntchito yanji, ndipo m’nthaŵi ya Baibulo, kodi kuchita ntchito imeneyi kunkaphatikizapo chiyani?

11 Pazaka zimene anali ku Nazarete, Yesu anaphunzira ntchito yaukalipentala, mwachionekere kwa atate wake wom’lera, Yosefe. Yesu anakhala katswiri pantchitoyo moti ankatchedwa kuti “mmisiri wa mitengo.” (Marko 6:3) M’nthaŵi za Baibulo, akalipentala ankalembedwa ntchito pomanga nyumba, kupanga mipando (kuphatikizapo matebulo, mipando ing’onoing’ono, ndi mabenchi), ndi kupanga zida zolimira. M’buku lake lakuti Dialogue With Trypho, Justin Martyr, wa m’zaka za zana lachiŵiri C.E., analemba za Yesu kuti: “Pamene anali pakati pa anthu anali kugwira ntchito monga kalipentala, kupanga makasu olimira ndi ng’ombe ndi magoli.” Ntchito imeneyi siinali yofeŵa, popeza kuti kalipentala wakale sanali kuchita kugula matabwa. Zikuoneka kuti anali kuphothyola m’tchire ndi kusankha mtengo, kuudula ndi nkhwangwa, ndi kuunyamula kupita nawo kunyumba. Chotero Yesu ayenera kuti ankadziŵa kuvuta kwa kupeza zofunika panyumba, kuchita malonda ndi makasitomala, ndi kusamalira banja.

12. N’chiyani chikusonyeza kuti Yosefe ayenera kuti anamwalira Yesu asanamwalire, ndipo zimenezi ziyenera kuti zinatanthauzanji kwa Yesu?

12 Pokhala mwana woyamba m’banjamo, Yesu ayenera kuti anali kuthandiza kusamalira banjalo, makamaka popeza zikuoneka kuti Yosefe anamwalira Yesuyo asanamwalire. * Magazini ya Zion’s Watch Tower ya January 1, 1900, inati: “Mbiri ikusonyeza kuti Yosefe anamwalira Yesu adakali wamng’ono, ndikuti Yesuyo anayamba ntchito yaukalipentala nakhala wochirikiza banja lakelo. Umboni wina wa zimenezi ukupezeka m’Malemba mmene Yesu mwiniyo akutchedwa kuti mmisiri wa matabwa, ndipo amayi ake ndi abale ake akutchulidwa, koma Yosefe sakutchulidwa. (Marko 6:3) . . . Ndiyetu n’zoonekeratu kuti nthaŵi yaitaliyo ya zaka 18 za moyo wa Ambuye wathu, kuchokera panthaŵi ya chochitikacho [cholembedwa pa Luka 2:41-49] mpaka panthaŵi ya ubatizo wake, anaithera pa kusamalira maudindo wamba a m’moyo.” Mariya ndi ana ake, kuphatikizapo Yesu, ayenera kuti ankadziŵa chisoni chimene chimakhalapo pamene mwamuna wokondedwa wa m’banja ndiponso atate amwalira.

13. Pamene Yesu anayamba utumiki wake, n’chifukwa chiyani anali ndi chidziŵitso, nzeru, ndi malingaliro akuya zimene munthu wina aliyense sakanakhala nazo?

13 N’zodziŵikiratu kuti Yesu sanakulire m’moyo wa zinthu za mwana alirenji. M’malo mwake, iye anakhala moyo wa anthu wamba. Ndiyeno mu 29 C.E., nthaŵi inafika yoti Yesu achite ntchito ya Mulungu yomwe anayenera kuchita. Chakumapeto kwa chaka chimenecho, iye anabatizidwa m’madzi ndipo anabadwanso monga Mwana wauzimu wa Mulungu. ‘Kunam’tsegukira kuthambo,’ mwachionekere kusonyeza kuti tsopano anatha kukumbukira moyo wake wakumwamba asanadze padziko lapansi, kuphatikizapo malingaliro ndi momwe ankamvera mumtima. (Luka 3:21, 22) Chotero pamene Yesu anayamba utumiki wake, iye anali ndi chidziŵitso, nzeru, ndi malingaliro akuya zimene munthu wina aliyense sakanakhala nazo. Ndiye chifukwa chaketu zambiri zimene olemba Mauthenga Abwino analemba zinali zokhudza zochitika mu utumiki wa Yesu. Ngakhale zinali motero, iwo sanathe kulemba zonse zimene iye ananena ndi kuchita. (Yohane 21:25) Koma zomwe analembazo zimatitheketsa kusuzumira mumtima wa munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako.

 Mmene Yesu Analili Monga Munthu

14. Kodi Mauthenga Abwino amam’sonyeza motani Yesu monga munthu wachikondi ndi wachifundo kwambiri?

14 Umunthu wa Yesu umene ukuonekera m’Mauthenga Abwino umam’sonyeza kukhala munthu wachikondi ndi wachifundo kwambiri. Anasonyeza mmene amamvera mumtima m’njira zosiyanasiyana: anachitira chifundo munthu wakhate (Marko 1:40, 41); anamva chisoni chifukwa cha anthu ouma khosi (Luka 19:41, 42); anasonyeza mkwiyo wolungama kwa osintha ndalama aumbombo (Yohane 2:13-17). Pokhala munthu wachifundo, Yesu ankatha kugwetsa misozi, ndipo sanabise mmene ankamvera mumtima. Bwenzi lake lapamtima Lazaro litamwalira, kungoona Mariya, mlongo wake wa Lazaro, akulira kunam’khudza kwambiri Yesu moti iyeyo anagwetsa misozi, kulira pamaso pa onse.​—Yohane 11:32-36.

15. Kodi chikondi ndi chifundo cha Yesu chinaonekera motani mwa njira imene ankaonera ndi kukhalira ndi ena?

15 Chikondi ndi chifundo cha Yesu chinali kuonekera kwambiri mwa njira imene ankaonera ena ndiponso momwe ankakhalira nawo. Anafikira osauka ndi otsenderezedwa, kuwathandiza ‘kupeza mpumulo wa miyoyo yawo.’ (Mateyu 11:4, 5, 28-30) Sanali wotanganitsidwa kwambiri moti n’kulephera kuthandiza ovutika pamavuto awo, kaya mkazi wamatenda a kukha magazi yemwe anakhudza chovala chake mwakachetechete kapena wopemphapempha wakhungu amene sanalolere kukhala chete. (Mateyu 9:20-22; Marko 10:46-52) Yesu anali kuyang’ana pa ubwino wa ena ndipo anali kuwathokoza; komabe, anali wokonzekanso kupereka uphungu pamene uli wofunikira. (Mateyu 16:23; Yohane 1:47; 8:44) Panthaŵi imene akazi analibe ufulu wochuluka, Yesu anawasonyeza ulemu woyenerera. (Yohane 4:9, 27) Ndiyetu chifukwa chake gulu la akazi linam’tumikira ndi chuma chawo.​—Luka 8:3.

16. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu anali ndi kaonedwe koyenera ka moyo ndi zinthu zakuthupi?

16 Yesu anali ndi kaonedwe koyenera ka moyo. Zinthu zakuthupi sizimene zinali zofunika kwambiri kwa iye. Zikuoneka kuti analibe zinthu zambiri zakuthupi. Iye ananena kuti ‘analibe potsamira mutu wake.’ (Mateyu 8:20) Panthaŵi imodzimodziyo, Yesu anali kuwonjezera chisangalalo cha ena. Pamene anapezeka paphwando laukwati, pamene nthaŵi zambiri pamakhala nyimbo, kuimba, ndi kusangalala, n’zoonekeratu kuti sanapezekepo kuti asokoneze chochitikacho. Ndithudi, Yesu anachita chozizwitsa chake choyamba pachochitikacho. Pamene vinyo anatha, iye anasandutsa madzi kukhala vinyo, chakumwa ‘chokondweretsa mtima wa munthu.’ (Salmo 104:15; Yohane 2:1-11) Chotero phwandolo linapitiriza, ndipo mosakayikira mkwati ndi mkwatibwi sanachititsidwe manyazi. Kaonedwe kake koyenerako kakusonyezedwabe ndi mfundo yakuti pali nthaŵi zambiri zotchulidwa pamene Yesu anagwira ntchito kwa nthaŵi yaitali ndiponso molimbikira mu utumiki wake.​—Yohane 4:34.

17. N’chifukwa chiyani sizodabwitsa kuti Yesu anali Mphunzitsi Wamkulu, ndipo zophunzitsa zake zinasonyeza chiyani?

17 Yesu anali Mphunzitsi Wamkulu. Zambiri zomwe anaphunzitsa zinasonyeza zochitika zenizeni m’moyo wa tsiku ndi tsiku, zomwe ankazidziŵa bwino. (Mateyu 13:33; Luka 15:8) Kaphunzitsidwe kake kanali kapamwamba koposa​—kotsatirika, kosavuta kumva, ndiponso kothandiza. Koma zofunika kwambiri ndi zimene anaphunzitsa. Ziphunzitso zake zinasonyeza chikhumbo chake cha pansi pa mtima cha kupangitsa omvetsera ake kudziŵa bwino malingaliro, mtima, ndi njira za Yehova.​—Yohane 17:6-8.

18, 19. (a) Kodi Yesu anafotokoza Atate wake pogwiritsa ntchito mafanizo omveka otani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

18 Pogwiritsa ntchito zitsanzo nthaŵi zambiri,  Yesu anafotokoza Atate wake mwa mafanizo omveka ndiponso osaiŵalika msanga. Kulankhula za chifundo cha Mulungu mwachisawawa ndi nkhani ina. Koma ndi nkhani inanso kuyerekezera Yehova ndi atate wokhululukira amene akumva chifundo kwambiri poona mwana wake amene wabwerera moti ‘akuthamanga, nam’kupatira pakhosi mwana wakeyo, nam’psompsonetsa.’ (Luka 15:11-24) Pokana mwambo wopanda chifundo wa atsogoleri achipembedzo omwe amanyozera anthu wamba, Yesu anafotokoza kuti Atate wake ndi Mulungu wofikirika amene anasankha kumvetsera mapempho a wamsonkho m’malo mwa pemphero lodzikweza la Mfarisi wodzitukumula. (Luka 18:9-14) Yesu anasonyeza Yehova kukhala Mulungu wosamala amene amadziŵa mpheta yaing’onong’ono ikagwa. “Musamaopa,” Yesu anatsimikizira ophunzira ake, “inu mupambana mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29, 31) Ndiye chifukwa chaketu anthu anazizwa ndi “chiphunzitso” cha Yesu ndipo anayandikira kwa iye. (Mateyu 7:28, 29) Inde, panthaŵitu ina “khamu lalikulu” linakhala pafupi naye kwa masiku atatu, lopandanso chakudya!​—Marko 8:1, 2.

19 Tiyenera kukhala okondwa kuti Yehova wavumbula mtima wa Kristu m’Mawu ake! Motero, kodi tingakulitse motani mtima wa Kristu ndi kuusonyeza pazochita zathu ndi ena? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Mfundo yonena kuti zolengedwa zauzimu zimasonkhezeredwa ndi mayanjano awo imaonekera pa Chivumbulutso 12:3, 4. Pamenepo Satana akusonyezedwa kukhala “chinjoka” chimene chinagwiritsa ntchito chisonkhezero chake kuti chipangitse “nyenyezi” zinanso, kapena kuti ana aamuna auzimu, kugwirizana nacho pachipanduko chake.​—Yerekezani ndi Yobu 38:7.

^ ndime 12 Nthaŵi yomaliza pamene Yosefe akutchulidwa mwachindunji ndiyo pamene Yesu wazaka 12 zakubadwa anapezeka m’kachisi. Sizikutchulidwa kuti Yosefe analipo paphwando laukwati ku Kana, kuchiyambiyambi kwa utumiki wa Yesu. (Yohane 2:1-3) Mu 33 C.E., atapachikidwa, Yesu anapereka Mariya m’manja mwa mtumwi wake wokondedwa Yohane kuti am’samalire. Zikuoneka kuti Yesu sakanachita zimenezo zikanakhala kuti Yosefe anali adakali moyo.​—Yohane 19:26, 27.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani m’pofunika kuti tiudziŵe bwino “mtima wa Kristu”?

• Kodi Yesu anali paunansi wotani asanadzakhale munthu wa padziko lapansi?

• M’moyo wake wa padziko lapansi, kodi ndi mikhalidwe ndi zisonkhezero zotani zimene Yesu anakumana nazo mwachindunji?

• Kodi Mauthenga Abwino amavumbulanji ponena za umunthu wa Yesu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Yesu anakulira m’banja lalikulu, mwinanso m’mikhalidwe yosauka

[Zithunzi patsamba 12]

Aphunzitsi anadabwa ndi nzeru ndi mayankho a Yesu wazaka 12 zakubadwayo