Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwasonkhezeredwa Kukhala Monga Yesu?

Kodi Mwasonkhezeredwa Kukhala Monga Yesu?

 Kodi Mwasonkhezeredwa Kukhala Monga Yesu?

“[A]naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa.”​—MARKO 6:34.

1. N’chifukwa chiyani zili zomveka kuti anthu ena amasonyeza mikhalidwe yosiririka?

M’MBIRI yonse ya anthu, anthu ambiri asonyeza mikhalidwe yosiririka. Mutha kumvetsa chifukwa chake. Yehova Mulungu ali ndi chikondi, ndi wokoma mtima, wowoloŵa manja, komanso ali ndi mikhalidwe ina imene amaisonyeza ndipo timaithokoza. Anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu. Choncho titha kuona chifukwa chake ambiri amatha kusonyeza mkhalidwe wa chikondi, chifundo, ndi mikhalidwe ina yaumulungu, monga momwe ambiri amasonyezera kuti ali ndi chikumbumtima. (Genesis 1:26; Aroma 2:14, 15) Komano, mungaone kuti ena amasonyeza kwambiri mikhalidwe imeneyi kuposa ena.

2. Kodi ndi ntchito zina zotani zimene anthu angachite, mwinanso akumaona kuti akutsanzira Kristu?

2 Muyenera kuti mumadziŵa amuna ndi akazi amene nthaŵi zambiri amachezera kapena kuthandiza odwala, kusonyeza chifundo kwa anthu opuwala, kapena amene amapatsa osauka mowoloŵa manja. Talingaliraninso za anthu amene chifukwa cha chifundo chawo amadzipereka kukagwira ntchito m’nyumba za anthu akhate kapena m’nyumba zosungiramo ana amasiye, aja amene amachita ntchito yodzifunira m’zipatala kapena kuthandiza anthu odwala matenda osachiritsika, kapenanso anthu amene amayesetsa kuthandiza anthu opanda nyumba kapena othaŵa kwawo chifukwa cha mavuto. Mwachionekere, ena a iwo amaona kuti akutsanzira  Yesu, amene anapatsa Akristu chitsanzo. Timaŵerenga m’Mauthenga Abwino kuti Kristu anachiritsa odwala ndi kudyetsa anjala. (Marko 1:34; 8:1-9; Luka 4:40) Pamene Yesu anasonyeza chikondi ndi chifundo, iye anasonyeza “mtima wa Kristu,” amenenso anali kutsanzira Atate wake wakumwamba.​—1 Akorinto 2:16.

3. Kuti tikhale ndi kaonedwe koyenera ka ntchito zabwino za Yesu, kodi tiyenera kulingalira za chiyani?

3 Koma kodi mwaona kuti ambiri lerolino amene asonkhezeredwa ndi chikondi ndi chifundo cha Yesu amanyalanyaza mbali yofunika kwambiri ya mtima wa Kristu? Tingamvetse zimenezi mwa kupenda Marko chaputala 6 mosamalitsa. Pamenepo timaŵerenga kuti anthu anabwera ndi anthu odwala kwa Yesu kuti awachiritse. Nkhani imeneyo imatisonyezanso kuti ataona kuti anthu zikwi zambiri amene anadza kwa iye anamva njala, Yesu anawadyetsa mozizwitsa. (Marko 6:35-44, 54-56) Kuchiritsa odwala ndi kudyetsa anjala zinali zisonyezero zapadera za chikondi ndi chifundo, koma kodi ndizo zinali njira zofunika kwambiri zimene Yesu anathandizira ena? Ndipo ndi motani mmene tingatsanzirire bwino kwambiri chitsanzo chake changwirocho cha chikondi, kukoma mtima, ndi chifundo, monga momwenso iye anatsanzirira Yehova?

Anasonkhezeredwa Kuthandiza pa Zosoŵa Zauzimu

4. Kodi nkhani ya pa Marko 6:30-34 inachitika motani?

4 Yesu anamvera chisoni anthu om’zinga makamaka chifukwa cha zosoŵa zawo zauzimu. Zosoŵa zimenezo ndizo zinali zofunika koposa, kuposanso zosoŵa zakuthupi. Talingalirani nkhani ya pa Marko 6:30-34. Chochitika chosimbidwa pamenepo chinachitikira pagombe la Nyanja ya Galileya, kutangotsala pang’ono kuti Paskha achitike mu 32 C.E. Atumwi anali osangalala, ndipotu pachifukwa chabwino. Popeza anali atangomaliza kumene kuchezera madera ambiri, anadza kwa Yesu, mosakayikira akufunitsitsa kum’simbira zimene akumana nazo. Komabe, khamu lalikulu la anthu linasonkhana. Linali lalikulu zedi moti Yesu ndi atumwi ake sanadye kapena kupumula. Yesu anauza atumwiwo kuti: “Idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi.” (Marko 6:31) Atakwera ngalaŵa, mwina chapafupi ndi Kapernao, anapita kutsidya lina la Nyanja ya Galileya kumalo achete. Koma khamulo linathamanga m’mbali mwa gombelo ndi kufika kumeneko ngalaŵayo isanafike. Kodi Yesu anatani? Kodi anakhumudwa kuti akum’sokoneza panthaŵi yake yopuma? Kutalitali!

5. Kodi Yesu anamva bwanji poona makamu amene anadza kwa iye, ndipo anachitanji powathandiza?

5 Mtima wa Yesu unakhudzidwa poona khamu la anthu zikwi zambiri, kuphatikizapo odwala, amene anali kum’dikira mwachidwi. (Mateyu 14:14; Marko 6:44) Polongosola zimene zinapangitsa Yesu kumva chifundo ndi zimene Iye anachita, Marko analemba kuti: “[A]naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Marko 6:34) Yesu anaona zambiri m’khwimbi la anthulo. Anaona anthu osoŵa mwauzimu. Iwo anali monga nkhosa zotayika zopanda wozithandiza, zopanda mbusa woti azitsogolere kumabusa obiriŵira kapena kuziteteza. Yesu anadziŵa kuti atsogoleri achipembedzo ouma mtimawo, amene anafunikira kukhala abusa osamala, anali kunyansidwa ndi anthu wambawo m’malo mwake ndipo ananyalanyaza zosoŵa zawo zauzimu. (Ezekieli 34:2-4; Yohane 7:47-49) Yesu anafuna kuwatenga m’njira yosiyana, kuwachitira zabwino zonse zomwe angathe. Anayamba kuwaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu.

6, 7. (a) Kodi n’chiyani chimene Mauthenga Abwino amasonyeza kuti chinali chofunika kwambiri pa zimene Yesu anachitira anthu pa zosoŵa zawo? (b) Kodi n’chiyani chinasonkhezera Yesu kulalikira ndi kuphunzitsa?

6 Onani ndondomeko yake ndiponso chimene chikuoneka kukhala chofunika koposa chomwe chikuonekera m’nkhani inanso yofanana ndi imeneyo. Imeneyi inalembedwa ndi Luka, amene anali dokotala komanso wosamala kwambiri za thanzi la ena. ‘Unyinji wa anthu . . . anam’tsata [Yesu]; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nawo za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasoŵa kuchiritsidwa.’ (Luka 9:11; Akolose 4:14) Ngakhale kuti sizili motero ndi nkhani iliyonse yonena za chozizwitsa, panopa, kodi n’chiyani chimene nkhani youziridwa ya Luka inatchula kaye? Inali mfundo yakuti Yesu anaphunzitsa anthu.

7 Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yaikulu imene tikupeza pa Marko 6:34. Vesi limenelo limasonyeza bwino lomwe chinthu chachikulu chimene chinasonkhezera Yesu kuti amve chisoni.  Anaphunzitsa anthuwo, kuwathandiza pa zosoŵa zawo zauzimu. Kuchiyambi kwa utumiki wake, Yesu anali atanena kuti: “Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku midzi inanso.” (Luka 4:43) Komanso, tingakhale tikulakwitsa kuganiza kuti Yesu analengeza uthenga wa Ufumu chabe chifukwa chakuti anapatsidwa ntchitoyo, ngati kuti anali kulalikira chabe chifukwa chakuti anauzidwa kutero. Ayi, chikondi chake ndi chifundo chake pa anthu ndicho chinali chisonkhezero chachikulu chogaŵanira nawo uthenga wabwino. Chinthu chabwino koposa chimene Yesu akanachita, ngakhale kwa odwala, ogwidwa ndi ziŵanda, osauka, kapena anjala, chinali kuwathandiza kudziŵa, kulandira, ndi kukonda choonadi chonena za Ufumu wa Mulungu. Choonadi chimenecho chinali chofunika koposa chifukwa cha zimene Ufumu udzachita pokweza uchifumu wa Yehova ndi kupereka madalitso osatha kwa anthu.

8. Kodi Yesu anali kuiona motani ntchito yake yolalikira ndi yophunzitsa?

8 Kulalikira za Ufumu mokangalika kumene Yesu anachita ndiko kunali chimodzi mwa zifukwa zazikulu zimene anadzera padziko lapansi. Chakumapeto kwa utumiki wake wapadziko lapansi, Yesu anauza Pilato kuti: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mawu anga.” (Yohane 18:37) M’nkhani ziŵiri zoyambazo, taona kuti Yesu anali munthu wachifundo, wosamala kwambiri za ena, anali wofikirika, woganizira ena, wokhulupirira ena, komanso chachikulu pa zonse, wachikondi. Tiyenera kudziŵa mbali zimenezo za umunthu wake ngati tikufuna kumvetsadi mtima wa Yesu. Momwemonso n’kofunika kudziŵa kuti mtima wa Kristu ukuphatikizapo kutsogoza ntchito yake ya kulalikira ndi kuphunzitsa imene anachita.

Analimbikitsa Ena Kuchitira Umboni

9. Kodi ndani anayenera kuika patsogolo ntchito ya kulalikira ndi kuphunzitsa?

9 Kuika ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa patsogolo, monga njira yosonyezera chikondi ndi chifundo, sikunali kwa Yesu yekha. Iye analimbikitsa otsatira ake kuti atsanzire zolinga zake, zinthu zimene anaziika patsogolo, ndi zochita zake. Mwachitsanzo, Yesu atasankha atumwi ake 12, kodi iwo anayenera kuchitanji? Marko 3:14, 15 amatiuza kuti: ‘Anaika khumi ndi aŵiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira, ndi kuti akhale nawo ulamuliro wakutulutsa ziŵanda.’ Kodi mukuona kuti atumwi anayenera kutsogoza chiyani pamenepa?

10, 11. (a) Potumiza atumwi, kodi Yesu anawauza kuchitanji? (b) Ponena za kutumiza atumwi, kodi cholinga chachikulu chinali chiyani?

10 M’kupita kwa nthaŵi, Yesu anapatsa mphamvu anthu 12 amenewo kuti azichiritsa ena ndi kutulutsa ziŵanda. (Mateyu 10:1; Luka 9:1) Kenako anawatumiza kuti akayendere “nkhosa zosokera za banja la Israyeli.” Kukatani? Yesu anawalangiza kuti: “Pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira. Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziŵanda.” (Mateyu 10:5-8; Luka 9:2) Kodi n’chiyanidi chimene anachita? “Ndipo anatuluka [1] nalalikira kuti anthu atembenuke mitima. Ndipo [2] anatulutsa mizimu yoipa yambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala nawachiritsa.”​—Marko 6:12, 13.

11 Popeza kuti si pena paliponse pamene kuphunzitsa kukutchulidwa choyamba, kodi kulingalira zapamwambazo ndiko kukokomeza nkhani yokhudza zinthu zofunika kuziika patsogolo choyamba kapena zolinga zomwe tingakhale nazo? (Luka 10:1-9) Tisanyalanyazetu kuchuluka kwa nthaŵi zimene kuphunzitsa kukutchulidwa kaye asanatchule kuchiritsa. Pankhani yapamwambayo, tapendani zochitika zonse. Kutangotsala pang’ono kuti atumize atumwi ake 12, Yesu anali atamva chisoni ndi mkhalidwe wa makamuwo. Timaŵerenga kuti: “Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse. Koma iye, poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa. Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.”​—Mateyu 9:35-38.

12. Kodi zozizwitsa za Yesu ndi atumwi zinagwiranso ntchito ina yotani?

12 Pokhala ndi iye, atumwi anaphunzirako mbali zina za mtima wa Kristu. Iwo anatha kuona kuti  kukhala kwawo achikondi chenicheni ndi achifundo kwa anthu kunaphatikizapo kulalikira ndi kuphunzitsa za Ufumu, imeneyo ndiyo inayenera kukhala mbali yaikulu ya ntchito zawo zabwino. Mogwirizana ndi zimenezo, ntchito zabwino zakuthupi, monga kuchiritsa odwala, sizinangothandiza osoŵawo. Monga momwe mungaonere, anthu ena akanakopeka ndi machiritso ndiponso chakudya choperekedwa mozizwitsa. (Mateyu 4:24, 25; 8:16; 9:32, 33; 14:35, 36; Yohane 6:26) Koma koposa kungokhala thandizo lakuthupi, ntchito zimenezo zinasonkhezeranso anthu oziona zikuchitikawo kuzindikira kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu komanso “mneneri” amene Mose anam’losera.​—Yohane 6:14; Deuteronomo 18:15.

13. Kodi ulosi wa pa Deuteronomo 18:18 unagogomeza ntchito iti ya “mneneri” yemwe anali kudzayo?

13 N’chifukwa chiyani mfundo yonena kuti Yesu ndiye anali “mneneri” ameneyo inali yofunika? Eya, kodi ntchito yaikulu imene ameneyo analoseredwa kuti adzaichita inali yotani? Kodi “mneneri” ameneyo anali kudzatchuka ndi machiritso ozizwitsa kapena kupangira anjala chakudya mwachifundo? Deuteronomo 18:18 analosera kuti: “Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale awo, wonga iwe [Mose]; ndipo ndidzam’patsa mawu anga m’kamwa mwake, ndipo adzanena nawo zonse ndimuuzazi.” Chotero pamene kuli kwakuti atumwi anaphunzira kukhala ndi chifundo ndi chikondi komanso kuzisonyeza, iwo anazindikira kuti mtima wa Kristu unayenera kusonyezedwanso mwa ntchito yawo ya kulalikira ndi kuphunzitsa. Zimenezo ndizo zinali zinthu zabwino kwabasi zimene akanachitira anthu. Mwakutero, odwala ndi osauka anali kudzapeza mapindu osatha, osati ongopindulitsa moyo waufupi wa munthu kapena ongopeza chakudya nthaŵi zingapo zokha iyayi.​—Yohane 6:26-30.

Khalani ndi Mtima wa Kristu Lerolino

14. Kodi kukhala ndi mtima wa Kristu kumaloŵamo motani m’kulalikira kwathu?

14 Palibe aliyense wa ife amene ayenera kuona mtima wa Kristu kukhala chinthu cha m’zaka za zana loyamba lokha, cha Yesu ndi ophunzira oyambirira okha amene mtumwi Paulo analemba kuti: “Ife tili nawo mtima wa Kristu.” (1 Akorinto 2:16) Ndipo tingavomereze ndi mtima wonse kuti tikulamulidwa kulalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Komano ndi bwino kupenda zolinga zathu zochitira ntchitoyo. Sitiyenera kuichita kungoti popeza ndi ntchito imene tinapatsidwa. Kukonda Mulungu ndicho chifukwa chachikulu chimene timachitira nawo utumiki, ndipo kukhaladi monga Yesu kumaphatikizapo kusonkhezeredwa ndi chifundo kuti tilalikire ndi kuphunzitsa.​—Mateyu 22:37-39.

15. N’chifukwa chiyani chifundo chili mbali yofunika ya utumiki wathu wapoyera?

15 Inde, nthaŵi zina zimavuta kumvera chifundo anthu amene sakhulupirira zimene timakhulupirira, makamaka ngati ndi amphwayi, amatikana, kapena ndi otsutsa. Komabe, kutaya chikondi ndi chifundo chathu pa anthu kungakhale kutaya chinthu chofunika kwambiri chotisonkhezera kutengamo mbali mu utumiki wachikristu. Chotero, kodi chifundo tingachikulitse motani? Tingayese kuona anthu monga momwe Yesu ankawaonera, monga “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Kodi si mmene anthu ambiri alili lerolino? Atsogoleri onyenga achipembedzo awanyalanyaza ndi kuwachititsa  khungu. Ndiye chifukwa chake, iwo sakudziŵa kuti m’Baibulo muli chitsogozo chabwino kapenanso sakudziŵa za Paradaiso amene Ufumu wa Mulungu adzadzetsa padziko lapansi posachedwapa. Tsiku ndi tsiku amakumana ndi mavuto a m’moyo, kuphatikizapo umphaŵi, kusagwirizana kwa pabanja, matenda, ndi imfa, popanda kukhala ndi chiyembekezo cha Ufumu. Ifeyo tili ndi chimene akuchifunacho: uthenga wabwino wopulumutsa moyo wonena za Ufumu wa Mulungu umene tsopano uli wokhazikitsidwa kumwamba!

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kufuna kugaŵirako ena uthenga wabwino?

16 Choncho mukaganizira za zosoŵa zauzimu za anthu okuzingani, kodi mtima wanu sukukusonkhezerani kufuna kuti muchite zonse zomwe mungathe kuti muwauze za chifuno chachikondi cha Mulungu? Inde, ntchito yathu ndi ntchito ya chifundo. Tikamachitira anthu chifundo monga momwe Yesu anachitira, zimenezo zidzaonekeratu mwa kamvekedwe ka mawu athu, kaonekedwe ka nkhope yathu, ndi kaphunzitsidwe kathu. Zonsezo zidzapangitsa uthenga wathu kukhala wosangalatsa kwambiri kwa awo “ofuna moyo wosatha.”​—Machitidwe 13:48, NW.

17. (a) Kodi chikondi ndi chifundo chathu tingachisonyeze m’njira zina ziti kwa ena? (b) N’chifukwa chiyani si nkhani yongosankhapo kuchita ntchito zabwino kapena kuchita nawo utumiki wapoyera?

17 Komano chikondi ndi chifundo chathu ziyenera kuonekeradi m’njira yathu yonse ya moyo. Zimenezi zimaphatikizapo kukhala okoma mtima kwa anthu ovutika, odwala, ndi osauka​—kuchita zomwe tingathe kuti tiwathandize pamavuto awo. Zimafuna kuyesetsa kwathu kwa mawu apakamwa ndi zochita zathu kuti titonthoze awo amene atayikidwa okondedwa awo mu imfa. (Luka 7:11-15; Yohane 11:33-35) Koma kusonyeza chikondi, kukoma mtima, ndi chifundo m’njira imeneyo sikuyenera kukhala chimake cha ntchito zathu zabwino, monga momwe zilili ndi anthu ena othandiza anthu ovutika. Zoyesayesa zopereka thandizo lokhalitsa zosonkhezeredwanso ndi mikhalidwe yaumulungu imodzimodziyo zimasonyezedwa mwa kuchita nawo ntchito yachikristu yolalikira ndi kuphunzitsa. Kumbukirani mawu a Yesu ponena za atsogoleri achipembedzo achiyuda akuti: “Mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.” (Mateyu 23:23) Yesu sanasankhe kungochitapo chinthu chimodzi chokha, kaya kungothandiza anthu pazosoŵa zawo zakuthupi kapena kuwaphunzitsa zinthu zauzimu zopereka moyo, iyayi. Yesu anachita zonse ziŵiri. Ngakhale zinali motero, n’zoonekeratu kuti ntchito yake yophunzitsa ndiyo inali yofunika koposa chifukwa chakuti zinthu zabwino zimene anakwaniritsa mwantchitoyo zinali kudzakhala zothandiza kosatha.​—Yohane 20:16.

18. Kodi kuphunzira za mtima wa Kristu kuyenera kutisokhezera kuchitanji?

18 Ndife othokoza zedi kuti Yehova wativumbulira mtima wa Kristu! Mwa Mauthenga Abwino, tingadziŵe bwino lomwe maganizo, za mumtima, mikhalidwe, zochita, ndi zinthu zimene munthu wamkulu woposa onse amene anakhalapo anaziika patsogolo. Zili ndi ife kuŵerenga, kusinkhasinkha, ndi kutsatira zimene Baibulo limavumbula ponena za Yesu. Kumbukirani kuti ngati tikufuna kuchitadi zinthu monga Yesu, choyamba tiyenera kuphunzira kalingaliridwe, kamvedwe ka mumtima, ndi kupenda zinthu monga ankachitira iyeyo, pamlingo wokwanira womwe tingathe monga anthu opanda ungwiro. Chotero tiyeni tikhale otsimikizira mumtima kuti tidzakulitsa ndi kusonyeza mtima wa Kristu. Palibe njira inanso yabwino kuposa imeneyi yokhalira ndi moyo, palibe njira inanso yabwino kuposa imeneyi yokhalira ndi anthu, ndipo palibe njira inanso yabwino kuposa imeneyi yoyandikirira kwa uyo amene Yesuyo anam’tsanzira mwangwiro, Mulungu wathu wachikondi ndi wachifundo, Yehova.​—2 Akorinto 1:3; Ahebri 1:3.

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi Baibulo limatiphunzitsa chiyani ponena za mmene Yesu anathandizira anthu osoŵa?

• Kodi Yesu anagogomezanji polangiza otsatira ake?

• Kodi “mtima wa Kristu” tingausonyeze motani pazochita zathu?

[Mafunso]

 [Chithunzi chachikulu patsamba 23]

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi chinthu chabwino kwambiri chimene Akristu angachitire ena n’chiyani?