Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chokani M’dera Langozi!

Chokani M’dera Langozi!

 Chokani M’dera Langozi!

NDI udindo wa akatswiri odziŵa za kuphulika kwa mapiri kufufuza ndi kupenda umboni ndiyeno n’kuchenjeza za kuphulika kwa volokano komwe kudzachitika. (Phiri la Fugen litaphulika, apolisi anali ndi ntchito yochotsa anthu m’dera langozi.) Mofananamo, ophunzira Baibulo aona chizindikiro cha “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano” ndipo akuchenjeza ena za ngozi imene yayandikirayo.​—Mateyu 24:3.

M’chaputala chomwecho cha Baibulo chomwe chimachenjeza za tsoka la dziko lonse lomwe layandikiralo, tingaŵerenge kulongosola uku kwa zochitika zoyambirira: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akuti akuti. . . . Aneneri onama ambiri adzauka, nadzasokeretsa anthu ambiri. Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala. . . . Ndipo uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”​—Mateyu 24:7-14.

Sitifunikira kukhala openda nkhani kuti tizindikire kukwaniritsidwa kwamakono kwa ulosi umenewu. Makamaka chiyambire 1914, taona kukwaniritsidwa kwake. M’zaka za zana lino mwachitika nkhondo ziŵiri padziko lonse, nkhondo zochuluka zapachiŵeniŵeni, nkhondo za m’mafuko ndi nkhondo za pakati pa mitundu ndi zipembedzo. Kuwonjezera pa kusoŵa zofunika m’moyo kochititsidwa ndi masoka achilengedwe, mtundu wa anthu wakhala ukusoŵanso chakudya chifukwa cha nkhondo zoterozo. Zivomezi nazo zadula miyoyo ya anthu ambiri. Kwabuka mipatuko yomwe atsogoleri ake n’ngwokayikitsa ndipo otsatira awo n’ngwotengeka maganizo. “Kuchuluka kwa kusayeruzika” kwapangitsa anthu kuleka kusonyezana chikondi, ndipo kuona aliyense monga mnansi sikulinso monga mfundo yamakhalidwe yochitira ena zabwino.

Ntchito yolalikira yapadziko lonse, yomwe ili mbali inanso ya chizindikiro, ikukwaniritsidwadi. Tangotembenukirani ku chikuto cha magazini ino, ndipo muona mawu omwe ali mbali ya dzina onena kuti “Yolengeza Ufumu wa Yehova.” Nsanja  ya Olonda, ikusindikizidwa m’zinenero 132 ndipo makope oposa 22 miliyoni akufalitsidwa. Iyo ili chida champhamvu cha awo amene akulengeza “uthenga uwu wabwino wa Ufumu” padziko lonse lapansi. Uthenga wabwino umenewo ukuphatikizapo uthenga wakuti Yehova Mulungu, Mlengi wa chilengedwe chonse, wakhazikitsa Ufumu kumwamba womwe udzawononga dongosolo la zinthu loipali ndi kudzetsa paradaiso padziko lapansi. Ndithudi, chizindikiro chakuti posachedwapa Mulungu achitapo kanthu n’choonekeratu tsopano lino, kusonyezeratu kuti miyoyo ya anthu m’dongosolo lino la zinthu ili pangozi.​—Yerekezani ndi 2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:3, 4; Chivumbulutso 6:1-8.

Tsiku Loopsa la Yehova

Kodi n’chiyani chomwe chidzachitika pamene nthaŵi yakuti Yehova apereke chiweruzo chake ifika? Tamverani mafotokozedwe akeake amphamvu a zomwe zidzachitika panthaŵiyo: “Ndidzaonetsa zodabwitsa kuthambo ndi pa dziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo. Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu loopsa.”​—Yoweli 2:30, 31.

Tsiku limenelo, loopsa kwambiri ndi losakaza kuposa kuphulika kwina kulikonse kwa phiri kapena kugwedeza kwa chivomezi, layandikira. Mneneri Zefaniya akuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza . . . , dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m’dziko.” Ngakhale kuli kwakuti “siliva wawo, ngakhale golidi wawo sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova,” pali njira yopulumukira tsiku loopsa limenelo.​—Zefaniya 1:14-18.

Posonyeza njirayo, Zefaniya akuti: “Usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko . . . , funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Zefaniya 2:2, 3) Tingabisike mwa ‘kufuna Yehova, kufuna chilungamo, ndi kufuna chifatso.’ Kodi ndani lerolino amene akufuna Yehova?

Mosakayikira inuyo mumagwirizanitsa liwulo lakuti “Yehova” ndi Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito yawo yolalikira. Mwina munalandirapo magazini ino kuchokera kwa mmodzi wa iwo. Amadziŵika monga nzika zamakhalidwe abwino zomwe miyoyo yawo ndi yolungama. Amayesetsa kuvala “umunthu watsopano” umene umaphatikiza kukulitsa chifatso. (Akolose 3:8-10, NW) Iwo amavomereza kuti, zimenezi zimatheka chifukwa chakuti amaphunzitsidwa ndi gulu looneka la Yehova, loimiridwa padziko lonse ndi mipingo ya Mboni za Yehova. Inde, mungabisale limodzi ndi ‘gulu lonse la abale’ a Mboni za Yehova padziko lonse.​—1 Petro 5:9.

Bisalani Tsopano Lino

Kuti tibisale mwa kufunafuna Yehova, tiyenera kukhala abwenzi ake. Kodi zimenezo zimaphatikizapo chiyani? Baibulo likuyankha kuti: “Kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) Kuti tikhale abwenzi a Mulungu, tiyenera kuchotsa malingaliro alionse odzigwirizanitsa ndi dziko lamakono loipali, lodzala ndi maganizo oukira Mulungu.

Baibulo likutichenjeza kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.” (1 Yohane 2:15-17) Anthu ambiri lerolino amasonkhezereka ndi zilakolako zathupi, monga kugonana kosalamulirika, kufunafuna ndalama mwadyera, ndi kugwiritsa ntchito mphamvu molakwika. Koma kuti munthu akhale kumbali ya Yehova, ayenera kugonjetsa zilakolako zoterozo.​—Akolose 3:5-8.

Mwinamwake inuyo mumaŵerenga magazini ino nthaŵi ndi nthaŵi, ndipo mungavomereze kugwiritsa ntchito kwake ulosi wa Baibulo. Komano, mwina mungazengereze kupita patsogolo mwa kuyamba kugwirizana ndi Mboni za Yehova. Komabe, ngati tayang’anizana ndi tsoka, kodi kungomva chenjezo kuli kokwanira? Monga momwe tikuonera pa zomwe zinachitika pamene Phiri la Fugen linaphulika, tiyenera kuchitapo  kanthu pamene tachenjezedwa. Kumbukirani kuti atolankhani ndi ojambula zithunzi ngati 15 anataya miyoyo yawo chifukwa chofunitsitsa kupeza nkhani zochititsa chidwi zoti akalembe. Ndithudi, wojambula zithunzi wina anafa chala chake chili pa batani la kamera yakeyo lomwe amasindikiza akamatola chithunzi. Katswiri wina wodziŵa za kuphulika kwa mapiri, yemwenso anali atanena kuti, “ngati tsiku lina ndidzafa, ndikufuna kuti ndidzafere m’munsi mwa phiri lophulika,” anatayadi moyo wake m’njira yomwe anafuna. Onseŵa anadzipatula ku ntchito yawo ndi zochita zawo. Koma, analipira ndi miyoyo yawo. Umenewo ndiwo mtengo wa kunyalanyaza chenjezo.

Ambiri lerolino akumva uthenga wokhudza cholinga cha Mulungu cha kuwononga dongosolo loipali la zinthu ndi kuzindikira, pamlingo winawake, kuti chenjezolo n’loonadi. ‘M’kupita kwa nthaŵi chidzafika, koma osati lero’ iwo angalingalire choncho. Iwo pomwepo amakankhira tsiku la Yehova patsogolo ndi cholinga chakuti asapatutsidwe pa zomwe zikuoneka kukhala zofunika kwambiri m’maso mwawo panthaŵiyo.

Baruki analinso ndi vuto limeneli. Pokhala mlembi wa mneneri Yeremiya wakaleyo, Baruki ankachenjeza Aisrayeli molimba mtima za chiweruzo cha Yerusalemu chomwe chinali kuyandikira. Komano, iye nthaŵi ina anatopa ndi ntchito yakeyo. Pamenepo, Yehova anamuwongolera akumati: “Udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune.” Baruki sanayenera ‘kudzifunira yekha zinthu zazikulu’ kaya chikhale chuma, kutchuka, kapena kudzikundikira katundu. Anafunikira kukonda chinthu chimodzi, kuchita chifuno cha Mulungu pothandiza anthu kuima kumbali Yake. Chotsatira chake, akanalandira ‘moyo wake ngati chofunkha.’ (Yeremiya 45:1-5) Mofananamo, m’malo ‘modzifunira tokha zinthu zazikulu,’ tiyenera kufuna Yehova, chomwe chingatsogolere ku kupulumutsidwa kwa miyoyo yathu.

Pa Phiri la Fugen, apolisi ndi ozimitsa moto odzifunira oposa khumi ndi aŵiri anali pantchito pamene thope lotentha kwambiri la m’phiri lophulikalo linaŵatentha. Ankayesa kuthandiza ndi kuteteza anthu omwe anali pangoziwo. Anali ngati amuna ndi akazi amaganizo abwino omwe atanganidwa m’kukonza dziko lino kuti likhale labwinopo. Ngakhale kuti ali ndi zolinga zabwino, koma “chokhotakhota sichingawongokenso.” (Mlaliki 1:15) Dongosolo la zinthu lokhotakhotali silingawongokenso. Kodi n’chinthu chanzeru kudzipanga kukhala “bwenzi la dziko lapansi” mwa kuyesa kupulumutsa dongosolo ladziko lonse lomwe Mulungu watsimikiza mtima kulithetsa?

Mukangothaŵa, Mukhale Kutali

Kuthaŵa m’dongosolo lomwe lili pangozi lino n’chinthu chimodzi, koma kukhalabe m’chisamaliro chotetezera cha “gulu lonse la abale” ndi chinthu chinanso chapadera. (1 Petro 2:17, NW) Tisaiwale za alimi omwe, pambuyo posamutsidwa, anabwereranso kukayendera minda yawo pafupi ndi Phiri la Fugen. Ayenera kuti ankangofuna atabwerera ku moyo wawo “wamasiku onse” monga momwe amakhalira m’mbuyomu. Koma mwazindikira kuti malingaliro awo ofuna kubwerera anali opanda nzeru. Mwinamwake kumeneku sikunali kuyamba kuloŵa m’dera langozilo. Mwinamwake analoŵa m’dera langozilo kwa kanthaŵi kochepa ndipo palibe china chilichonse chomwe chinachitika. Panthaŵi ina, mwina anakhala kwa nthaŵi yotalikirapo, ndipo palibenso chomwe chinachitika. Mwachionekere, posapita nthaŵi chinangokhala chizoloŵezi chawo chomalumpha malire otetezerawo ndipo ankalimba mtima ndi kunyalanyaza kuchoka m’dera lokhala pangozilo.

Yesu Kristu ananenanso za mkhalidwe wofananawo womwe udzachitika panthaŵi ya “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” Iye anati: “Monga m’masiku aja, chisanafike chigumula, anthu analinkudya ndi kumwa, analikukwatira ndi kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analoŵa m’chingalaŵa, ndipo iwo sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu.”​—Mateyu 24:3, 38, 39.

Onani kuti Yesu anatchula kudya, kumwa, kukwatira, ndi kukwatiwa. Palibe chilichonse cholakwika ndi zinthu zimenezi mwa izo zokha pamaso pa Yehova. N’chiyani nanga chomwe chinalakwika? Anthu a m’tsiku la Nowa “sanadziŵa kanthu,” anali otanganidwa ndi zochitika m’moyo wawo wamasiku onse. M’nthaŵi yangozi, palibe amene angakhale monga “mwamasiku onse.” Pamene mwathaŵa, kapena kudzipatula, kuchoka m’dziko lamakono lokhala pangozili, muyenera  kulimbana ndi chisonkhezero chilichonse chakuti mubwerere kukagwiritsa ntchito china chilichonse chimene chingafunkhidwe m’dzikomo. (1 Akorinto 7:31) Mungakhoze kumayendayenda kunja kuchoka m’dera lotetezereka mwauzimu, ndiyeno n’kubwereranso osakalika n’komwe mwinanso popanda aliyense kudziŵa. Komabe, zimenezo mwachionekere zidzakulimbitsani mtima ndi kukupangitsani kubwereranso ku dziko, mukumazengereza kuchokamo kwa nthaŵi yaitali. Posapita nthaŵi mungayambe kuganiza kuti: “Mapeto safika lero.”

Lingaliraninso za madalaivala atatu omwe anataya miyoyo yawo chifukwa chodikira atolankhani ndi ojambula zithunzi pamene thope la m’phiri lophulikalo linatsikira m’munsi mwa phirilo. Ena lerolino angakhale m’gulu la anthu ena omwe alimba mtima kubwerera kudziko. Kaya pakhale chifukwa chotani, n’chachionekere kuti kunyengedwa ndi ena kuti mubwererenso ku dera loopsa n’kosayenererana ndi ngozi yake.

Onse amene anaphedwa ndi kuphulika kwa Phiri la Fugen analumpha malire otetezera ndi kukaloŵa m’dera langozi. Ngakhale kuti anali kuyembekezera kuti tsiku lina phirilo lidzaphulika, palibe amene analingalira kuti lingaphulike tsiku limenelo. Poona chizindikiro cha mapeto a dongosolo lino la zinthu, ambiri akuyembekezera kufika kwa tsiku la Yehova koma mwachionekere osati posachedwa. Ena amafika polingalira kuti tsikulo silingakhale “lero.” Ndithudi malingaliro oterowo n’ngovulaza zedi.

Mtumwi Petro anachenjeza kuti: “Tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala.” Tifunikira kukhala atcheru, “akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu,” kuchita ‘changu kuti tipezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanga chilema.’ (2 Petro 3:10-14) Dongosolo lazinthu loipa lilipoli likadzawonongedwa, tidzayembekezera dziko lapansi la paradaiso mu Ufumu wa Mulungu. Tisanyengedwetu kuloŵa m’dera langozi ngakhale tikhale ndi zifukwa zotani m’malingaliro athu, popeza kuti tsiku lomwe tidzalumpha malire n’kubwerera kudziko lingadzakhale tsiku la Yehova.

Bisalani limodzi ndi anthu a Yehova ndipo khalani nawobe.

[Zithunzi patsamba 7]

Bisalani limodzi ndi anthu a Yehova ndipo khalani nawobe

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Iwasa/​Sipa Press