Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Uphungu Wanzeru wa Mayi

Uphungu Wanzeru wa Mayi

 Uphungu Wanzeru wa Mayi

“Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amako.”​—Miyambo 1:8.

MAKOLO athu​—abambo ndi amayi athu​—angakhale opereka chilimbikitso ndi chichirikizo chabwino kwambiri, ndiponso uphungu wabwino. Buku la Baibulo la Miyambo limatiuza za mfumu inayake yachinyamata, yotchedwa Lemueli, imene inalandira “uthenga” wa ‘chiphunzitso’ kuchokera kwa amayi wake. Mawu ameneŵa analembedwa mu Miyambo chaputala 31, ndipo nafenso tingapindule ndi uphungu wanzeru wa mayi umenewu.​—Miyambo 31:1.

Uphungu Woyenerera Mfumu

Amayi a Lemueli akuyamba ndi mafunso angapo omwe akudzutsa chidwi chathu: “Chiyani mwananga, chiyani mwana wa mimba yanga? Chiyani mwana wa zoŵinda zanga?” Kuchonderera kwawo kobwerezedwa katatuko kukusonyeza kufunitsitsa kwawo kwakukulu kuti mwana wawoyo alabadire mawu awo. (Miyambo 31:2) Nkhaŵa yawo pa umoyo wauzimu wa mwana wawo ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo achikristu lerolino.

Ponena za umoyo wa mwana, kodi n’chiyani chingadetse nkhaŵa mayi koposa michezo ndi kuipa kwa vinyo, akazi, ndi nyimbo, zinthu zotchukazo? Amayi a Lemueli akufotokoza mfundoyo mwachindunji: “Musapereke mphamvu yako kwa akazi.” Iwo akunena moyo wachiwerewere kukhala “njira yowononga mafumu.”​—Miyambo 31:3.

Kumwa mowa mwauchidakwa sikufunikira kuonedwa mopepuka. “Mafumu, Lemueli, mafumu sayenera kumwa vinyo,” iwo akuchenjeza motero. Kodi mfumu ingaweruze bwanji mwanzeru ndi molondola ndiponso ‘osaiwala malamulo kapena kuweruza mokhota anthu onse osautsidwa’ ngati imakhala yoledzera nthaŵi zonse?​—Miyambo 31:4-7.

Mosiyana ndi zimenezo, mwa kusachita nawo zinthu zoipa ngati zimenezo, mfumu ingathe ‘kuweruza molungama ndi kunenera osauka ndi aumphaŵi.’​—Miyambo 31:8, 9.

Ngakhale kuti achinyamata achikristu sangakhale “mafumu” lerolino, uphungu wanzeru wa amayi a Lemueli ndi wapanthaŵi yake, mwina kwambirinso. Kumwa moŵa mwauchidakwa, kusuta fodya, ndiponso chisembwere n’zofala pakati pa achinyamata lerolino, ndipo n’kofunika kuti anyamata achikristu azimvetsera pamene makolo awo akuwapatsa ‘mauthenga.’

Mkazi Waluso

Amayi amadera nkhaŵa kwambiri za ziyembekezo zaukwati wa anyamata awo amene akuyandikira uchikulire. Kenako amayi a Lemueli akulunjikitsa malingaliro awo pa mikhalidwe ya mkazi woyenerera. Mosakayikira, wachinyamata angapindule kwambiri mwa  kulingalira za mmene mkazi akuionera nkhani imeneyi.

M’vesi 10 (NW), “mkazi waluso” akuyerekezeredwa ndi ngale za mtengo wapatali ndiponso zosapezekapezeka, zomwe m’nthaŵi za Baibulo zimapezeka kokha mwa kuyesayesa kokulirapo. Mofananamo, kupeza mkazi waluso kumafunikira kuyesetsa. M’malo molakalaka kuthamangira muukwati, mnyamata angachite bwino kudekha kuti akhale ndi nthaŵi yokwanira yosankha. Atatero, m’pamene angaone mkazi amene wapezayo kukhala wamtengo wapatali.

Ponena za mkazi waluso, Lemueli akuuzidwa kuti: “Mtima wa mwamuna wake um’khulupirira.” (Vesi 11) M’mawu ena tinganene kuti, sayenera kunena kuti mkazi wake azimupempha chilolezo m’zinthu zilizonse. Inde, okwatirana ayenera kumakambirana asanasankhe chochita chachikulu, monga ngati nkhani zokhudza kugula katundu wapamwamba kapena za kaleredwe ka ana. Kuyankhulana pankhani ngati zimenezi kumathandiza kuti okwatirana akhale okondana kwambiri.

Inde, mkazi waluso amakhala ndi zinthu zambiri zoti achite. M’mavesi 13 mpaka 27 mwandandalikidwa uphungu komanso mfundo zachikhalidwe zomwe zingagwiritsidwe ntchito ndi akazi a mbadwo uliwonse kuti apindulire mabanja awo. Mwachitsanzo, malinga ndi kukwera kwa mitengo ya zovala ndi ziŵiya za m’nyumba, mkazi waluso amaphunzira kukhala wotakataka kwambiri ndiponso wosasakaza zinthu kotero kuti banja lake limakhala ndi zovala zokwanira komanso zooneka bwino. (Mavesi 13, 192122) Kuti achepetseko ndalama zogwiritsidwa ntchito pa chakudya, iye amalima mbewu zomwe angathe kulima ndiponso amagula zakudya mosamala kwambiri.​—Mavesi 1416.

Mwachidziŵikire mkazi ameneyu “sadya zakudya za ulesi.” Amagwira ntchito molimbikira, ndiponso amagwira ntchito za panyumba pake bwino lomwe. (Vesi 27) ‘Amamanga m’chuuno mwake ndi mphamvu,’ zimene zimatanthauza kuti amakonzekera kugwira ntchito zolemetsa. (Vesi 17) Amadzuka m’mawa kuti ayambe kugwira ntchito zake za tsikulo, ndipo amagwira ntchito mwakhama mpaka usiku. Kuli monga ngati kuti nyali zounikira ntchito yake zinali zosazima.​—Vesi 1518.

Koposa zonse, mkazi waluso ameneyu ndi munthu wauzimu. Amaopa Mulungu ndipo amam’lambira mwaulemu ndiponso mwamantha aulemu. (Vesi 30) Mofananamo amathandizanso mwamuna wake kuphunzitsa ana awo kuti azichita zinthu zofananazo. Vesi 26 limanena kuti, amalangiza ana ake, “ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake.”

Mwamuna Waluso

Kuti akope mkazi waluso, Lemueli anafunikira kukwaniritsa ntchito za mwamuna waluso. Amayi a Lemueli akumukumbutsa zingapo mwa ntchito zimenezi.

Mwamuna waluso amalandira mbiri yabwino kuchokera kwa “akulu a dziko.” (Miyambo 31:23) Zimenezo zikutanthauza kuti ayenera kukhala wokhoza kuchita zinthu, woona mtima, wodalirika, ndi woopa Mulungu. (Eksodo 18:21; Deuteronomo 16:18-20) Motero, amakhala ‘wodziŵika’ “kubwalo,” kumene amuna akuluakulu amasonkhana kukakambirana nkhani zochitika mu mzinda. Kuti ‘adziŵike’ kukhala woopa Mulungu, iye ayenera kukhala wanzeru ndi kugwira ntchito mogwirizana ndi akulu a “dziko,” mwinamwake kutanthauza bomalo kapena chigawo.

Mosakayikira, chifukwa cha zokumana nazo zaumwini, amayi a Lemueli akukumbutsa mwana wawo za kufunika kwa kuyamikira mkazi wake wam’tsogolo. Palibe wina padziko lapansi amene angakhale wokondedwa kwambiri kwa iye kusiyapo mkazi wakeyo. Tsono talingalirani kukhudzidwa mtima kwa mwamunayu m’mawu ake pamene akunena pamaso pa onse kuti: “Ana akazi ambiri anachita mwangwiro [“mwaluso,” NW] koma iwe uposa onsewo.”​—Miyambo 31:29.

Mwachionekere, Lemueli anayamikira uphungu wanzeru wa amayi wake. Mwachitsanzo, timadziŵa kuti m’vesi 1, akutchula mawu a amayi wake ngati akeake. Choncho, anaika “uthenga” wa amayi wake mu mtima ndipo anapindula ndi malangizo awo. Nafenso tipindule ndi “uthenga” umenewu mwa kugwiritsa ntchito mfundo zake za chikhalidwe m’moyo wathu.

[Zithunzi patsamba 31]

Mkazi waluso “sadya zakudya za ulesi”