Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pangani Ubwenzi Wathithithi ndi Yehova

Pangani Ubwenzi Wathithithi ndi Yehova

 Pangani Ubwenzi Wathithithi ndi Yehova

WOPHUNZIRA Yakobo analemba kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Ndipo wamasalmo Davide anaimba kuti: “Ubwenzi ndi Yehova n’ngwa iwo akuopa iye” (Salmo 25:14, NW.) Ndithudi, Yehova Mulungu amafuna kuti tikhale naye paubwenzi wathithithi. Komabe, si onse amene amalambira Mulungu ndi kumvera malamulo ake amene ali oyandikana naye.

Bwanji nanga inuyo? Kodi muli paubwenzi wathithithi ndi Mulungu? Mosapeneka, mukufuna kuyandikira kwa iye. Ndi motani mmene tingapangire ubwenzi wathithithi ndi Mulungu? Kodi zimenezi zidzatanthauzanji kwa ife? Chaputala chachitatu cha buku la Baibulo la Miyambo chimapereka mayankho.

Sonyezani Kukoma Mtima Kwachikondi ndi Choonadi

Mfumu Solomo ya mu Israyeli wakale ikuyamba chaputala chachitatu cha Miyambo ndi mawu akuti: “Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; pakuti adzakuwonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.” (Miyambo 3:1, 2) Popeza Solomo analemba mouziridwa ndi Mulungu, malangizo a atate ameneŵa ndithu akuchokera kwa Yehova Mulungu ndipo akuperekedwa kwa ife. Pano tikulangizidwa kumvera zikumbutso za Mulungu, lamulo lake, ngakhalenso ziphunzitso zake, ndiponso malamulo ake olembedwa m’Baibulo. Ngati tichita zimenezi, ‘adzatiwonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.’ Inde, ngakhale pakalipano tingasangalale ndi moyo wamtendere ndipo tingapewe kuchita zinthu zomwe zingatiike pangozi zochititsa kufa msanga zimene kaŵirikaŵiri zimachitikira anthu ochita zoipa. Ndiponso, tingakhale ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’dziko latsopano la mtendere.​—Miyambo 1:24-31; 2:21, 22.

Popitiriza, Solomo akunena kuti: “Chifundo [“kukoma mtima kwachikondi,” NW] ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako; motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.”​Miyambo 3:3, 4.

Liwu loyambirira la “kukoma mtima kwachikondi” limatembenuzidwanso kuti “chikondi chokhulupirika” ndipo limatanthauza kudzipereka, kugwirizana, ndi kukhulupirika. Kodi tatsimikiza mtima kuti ngakhale pakhale zovuta zamtundu wanji tidzamamatira Yehova? Kodi timasonyeza kukoma mtima kwachikondi m’maunansi athu ndi okhulupirira anzathu? Kodi timayesetsa kuti tikhale nawobe paunansi wabwino? Pochita nawo m’moyo wa tsiku ndi tsiku, kodi timasunga ‘lamulo la kukoma mtima kwachikondi pa lilime lathu’ ngakhale m’mikhalidwe yovuta?​—Miyambo 31:26.

Popeza Yehova ndi wodzala kukoma mtima kwachikondi, iye “ndi wokhululukira.” (Salmo 86:5) Ngati tinalapa machimo athu akale ndipo tsopano tikuwongola njira za mapazi athu, ndiye kuti tatsimikiza mtima kuti “nyengo zakutsitsimutsa” zidzachokera kwa Yehova. (Machitidwe 3:19) Kodi sitingatsanzire Mulungu wathu mwa kukhululukira ena zolakwa zawo?​—Mateyu 6:14, 15.

 Yehova ndi “Mulungu wa choonadi,” ndipo amafuna kuti onse ofuna ubwenzi wathithithi ndi iye akhale a “choonadi.” (Salmo 31:5) Kodi tingayembekezere Yehova kukhala Bwenzi lathu ngati tili ndi moyo wapaŵiri? Wina pamene tili ndi anzathu achikristu ndi wina pamene tili patokha kukhala ngati “anthu osadziŵa choonadi” amene amabisa mtundu waumunthu wawo? (Salmo 26:4) Kumeneku kungakhale kupusa zedi, popeza “zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake” pa Yehova!​—Ahebri 4:13.

Tiyenera kukuona kukoma mtima kwachikondi ndi choonadi monga mkanda wa mtengo wapatali ‘womangidwa pakhosi pathu,’ popeza kumatithandiza ‘kupeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.’ Sitiyenera kuonetsa mikhalidwe imeneyi kunja kokha komanso ‘kulembedwa pamtima pathu,’ kuipanga kukhala mbali yofunika ya moyo wathu.

Kukhulupirira Yehova ndi Mtima Wonse

Mfumu yanzeru ikupitiriza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze [“um’zindikire,” NW] m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.”​Miyambo 3:5, 6.

Yehova ndi woyenereradi kumukhulupirira ndi mtima wonse. Monga Mlengi, ndi “wolimba mphamvu” ndipo ndi Gwero la ‘mphamvu zazikulu.’ (Yesaya 40:26, 29) Ndi wokhoza kuchita zonse zimene akufuna. Ndithudi, dzina lake lokhalo kwenikweni limatanthauza “Amachititsa Kukhalako,” ndipo limalimbitsa chidaliro chathu kuti akhoza kukwaniritsa zomwe walonjeza! Chifukwa chokhacho chakuti “Mulungu sakhoza kunama” chimam’pangitsa kukhala chitsanzo chapadera cha choonadi. (Ahebri 6:18) Mkhalidwe wake waukulu ndi chikondi. (1 Yohane 4:8) Iye ndi “wolungama m’njira zake zonse, ndi wachifundo m’ntchito zake zonse.” (Salmo 145:17) Ngati sitikhulupirira Mulungu, tingakhulupirire ndani? Zoona, kuti tim’khulupirire, tiyenera ‘kulawa, ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino’ mwakugwiritsira ntchito zimene timaphunzira m’Baibulo ndiponso mwa kusonyeza zinthu zabwino zomwe kuchita zimenezi kumabweretsa m’moyo wathu.​—Salmo 34:8.

Kodi ‘tingam’zindikire Yehova m’njira zathu zonse’ motani? Wamasalmo wouziridwayo akuti: “Ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.” (Salmo 77:12) Popeza Mulungu saoneka, kuti tipange unansi wathithithi ndi iye, n’kofunika kusinkhasinkha pa zochita zake zazikulu ndi mmene amachitira ndi anthu ake.

Pemphero ndi njiranso yofunika pakuzindikira Yehova. Mfumu Davide anaitanira pa Yehova “tsiku lonse.” (Salmo 86:3) Nthaŵi zambiri Davide anali kupemphera usiku wonse, monga pamene anathaŵira m’chipululu. (Salmo 63:6, 7) “Mupemphere nthaŵi yonse mwa Mzimu,” analangiza motero mtumwi Paulo. (Aefeso 6:18) Kodi timapemphera kangati? Kodi timasangalala kulankhulana moona mtima ndi Mulungu? Pamene tili m’mikhalidwe yovuta, kodi timapemphera kuti atithandize? Kodi mwapemphero timafuna chitsogozo chake tisanasankhe zofunika? Mapemphero athu a mtima wonse kwa Yehova adzapangitsa iye kutikonda. Ndipo tili ndi chidaliro kuti adzamva mapemphero athu ndipo ‘adzaongola mayendedwe athu.’

N’kupusa ‘kuchirikizika pa luntha lathu’ kapena pa luntha la anthu otchuka m’dziko pamene tikudziŵa kuti tikhoza kudalira kwambiri Yehova! “Usadziyese wekha wanzeru;” akutero Solomo. Komano, akulimbikitsa kuti: “Opa Yehova, nupatuke pazoipa; mitsempha yako idzalandirapo moyo, ndi mafupa ako uwisi.” (Miyambo 3:7, 8) Mantha oyenera oopa kusakondweretsa Mulungu ayenera kulamulira zochita zathu, maganizo athu, ndi mitima yathu. Kuopa kwaulemu kumeneku kumatipeŵetsa kuchita choipa ndipo n’kochiritsa ndi kotsitsimula mwauzimu.

M’patseni Yehova Zinthu Zabwino Kwambiri

Kodi tingayandikire kwa Mulungu m’njira zina ziti? “Lemekeza Yehova ndi chuma chako,  ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha;” ikulangiza motero mfumu. (Miyambo 3:9) Kulemekeza Yehova kumatanthauza kum’patsa ulemu kwambiri ndi kum’kweza mwa kuchita nawo ndiponso kuchirikiza kulengeza dzina lake. Chuma chomwe tingalemekeze nacho Yehova ndicho nthaŵi yathu, maluso athu, mphamvu zathu, ndi chuma chathu chakuthupi. Izi ziyenera kukhala zoyambirira kucha zabwino kwambiri zomwe tili nazo. Kodi mmene timagwiritsira ntchito chuma chathu sikuyenera kusonyeza kutsimikiza mtima kwathu kupitirizabe ‘kufuna choyamba Ufumu ndi chilungamo cha Mulungu’?​—Mateyu 6:33.

Kulemekeza Yehova ndi chuma chathu n’kopindulitsa. “Motero nkhokwe zako zidzangoti the,” akutsimikiza motero Solomo, “Mbiya zako zidzasefuka vinyo.” (Miyambo 3:10) Ngakhale kuti kulemera mwauzimu pakokha sikulemeretsa mwakuthupi, kugwiritsa ntchito zinthu zathu moolowa manja kulemekezera Yehova kumadzetsa madalitso ochuluka. Kwa Yesu, kuchita chifuniro cha Mulungu chinali “chakudya” chom’limbitsa. (Yohane 4:34) Mofananamo, kutenga nawo mbali mu ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira yomwe imalemekeza Yehova kumatilimbitsa. Ngati tipitiriza m’ntchito imeneyi, nkhokwe zathu zauzimu zidzadzala. Chimwemwe chathu chophiphiritsidwa ndi vinyo watsopano chidzasefukira.

Kodi ifenso sitiyang’ana kwa Yehova ndi kupempha chakudya chakuthupi chokwanira cha tsiku lililonse? (Mateyu 6:11) Kunena zoona, chilichonse chimene tili nacho chimachokera kwa Atate wathu wachikondi wakumwamba. Yehova adzatitsanulira madalitso molingana ndi mmene timagwiritsira ntchito chuma chathu pom’tamanda.​—1 Akorinto 4:7.

Landirani Chilango cha Yehova

Poona kufunika kwa chilango popanga unansi wathithithi ndi Yehova, mfumu ya Israyeli ikutilangiza kuti: “Mwananga, usapeputse mwambo wa [“chilango cha,”] Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.”​Miyambo 3:11, 12.

Komabe, sikukhala kwapafupi kulandira chilango. “Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu choŵaŵa,”  analemba motero mtumwi Paulo “koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” (Ahebri 12:11) Chidzudzulo ndi chilango ndi mbali zofunika za maphunziro omwe amatiyandikiza kwa Mulungu. Chilango chochokera kwa Yehova, kaya tichilandire kuchokera kwa makolo, kudzera mwa mpingo wachikristu, kapena mwa kusinkhasinkha Malemba pochita phunziro lathu laumwini, zimasonyeza chikondi chake pa ife. Tidzachita bwino kuchilandira.

Sunganibe Nzeru ndi Kuzindikira

Kenako, Solomo akugogomezera kufunika kwa nzeru ndi kuzindikira popanga unansi wathithithi ndi Mulungu. Akuti: “Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha [“wozindikira,” NW]; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka. . . . Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira n’ngwodala.”​Miyambo 3:13-18.

Potikumbutsa mmene Yehova anasonyezera nzeru ndi kuzindikira mu ntchito yodabwitsa pachilengedwe, mfumu inati: “Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zam’mwamba ndi luntha [“kuzindikira,” NW]. . . . Mwananga, zisachokere ku maso ako; sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo.”​Miyambo 3:19-22.

Nzeru ndi kuzindikira ndi mikhalidwe ya Mulungu. Sitiyenera kungokhala ndi mikhalidwe imeneyi komanso kuikulitsa mwa kusatopa kuphunzira kwathu Malemba mwakhama ndi kugwiritsa ntchito zimene tikuphunzira. Solomo akupitiriza kuti, “pompo udzayenda m’njira yako osaopa, osapunthwa phazi lako.” Ndipo akuwonjezera kuti: “Ukagona, sudzachita mantha; udzagona tulo tokondweretsa.”​Miyambo 3:23, 24.

Inde, tingayende motetezeka ndi kugona mu mtendere wamaganizo pamene tikudikira tsiku lobwera ngati mbala la “chiwonongeko [chamwadzidzidzi, NW]” chimene chidzagwere dziko la Satana loipali. (1 Atesalonika 5:2, 3; 1 Yohane 5:19) Ngakhale pa chisautso chachikulu chimene chili pafupichi, tingakhale ndi chidaliro ichi: “Usaope zoopsa zodzidzimutsa, ngakhale zikadza zopasula oipa; pakuti Yehova adzalimbitsa mtima wako, nadzasunga phazi lako lingakodwe.”​Miyambo 3:25, 26; Mateyu 24:21.

Chitani Zabwino

Solomo akutilangiza kuti: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino.” (Miyambo 3:27) Kuchitira ena zabwino kumaphatikizapo kugwiritsa ntchito zinthu zathu mmalo mwa iwo, ndipo kuli ndi mbali zambiri. Kodi kuthandiza ena kupanga unansi wathithithi ndi Mulungu woona, sichinthu chabwino kwambiri chimene tingawachitire mu “nthaŵi yachimaliziro” ino? (Danieli 12:4) Ano tsopano ndiwo masiku ofunika kusonyeza changu mu ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira.​—Mateyu 28:19, 20.

Mfumu yanzeruyi ikutchulanso zina mwa zinthu zoti tipewe, ikuti: “Usanene kwa mnzako, ukabwerenso, ndipo maŵa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu. Usapangire mnzako chiwembu; popeza akhala nawe pafupi osatekeseka. Usakangane ndi munthu chabe, ngati sanakuchitira choipa. Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse.”​Miyambo 3:28-31.

Pofotokoza mwachidule chifukwa choperekera uphungu wakewo, Solomo akuti: “Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili [“ubwenzi wake uli,” NW] ndi oongoka. Mulungu atemberera za m’nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama. Anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo. Anzeru adzalandira ulemu choloŵa chawo; koma opusa adzakweza manyazi.”​Miyambo 3:32-35.

Ngati tikufuna kukhala paubwenzi wathithithi ndi Yehova, sitiyenera kuganiza zachinyengo ndi zachiwembu. (Miyambo 6:16-19) Kokha ngati tichita zoyenera m’maso mwa Mulungu tidzapeza chiyanjo ndi madalitso ake. Tingalandirenso ulemu wochuluka pamene ena aona kuti timachita mogwirizana ndi nzeru ya Mulungu. Chotero tiyeni tikane njira zachinyengo za dziko loipa ndi lachiwawali. Ndithudi, tiyeni titsate njira yowongoka ndi kupanga ubwenzi wathithithi ndi Yehova!

[Zithunzi patsamba 25]

“Lemekeza Yehova ndi chuma chako”