Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungadziŵe za M’tsogolo!

Mungadziŵe za M’tsogolo!

 Mungadziŵe za M’tsogolo!

Anthu ambiri amalingalira kwambiri za m’tsogolo. Amafuna kukonzekera, kusunga ndalama mwanzeru n’cholinga choti zidzawapindulire, ndiponso kudzimva kukhala otetezeka. Koma kodi pali njira ina iliyonse yotsimikizira za zinthu zomwe zili m’tsogolo?

POFUNA kufufuza zinthu zomwe zili m’tsogolo, anthu ayesa zinthu za mitundu yonse. Asayansi ya chikhalidwe cha anthu otchedwa kuti anthu ofufuza zinthu zodzachitika m’tsogolo amapenda zochitika za masiku ano ndi kulosera malinga ndi zochitika zimenezi. Nawonso akatswiri a zachuma amachita zofananazo kumbali yawo. Okhulupirira nyenyezi komanso alauli amadalira choloserera cha nyenyezi, mipira ya magalasi, ndi kupenduza, ndipo ali ndi anthu ambiri owatsatira. Mwachitsanzo, wokhulupirira nyenyezi wachifalansa Nostradamus akupitirizabe kukhala wotchuka, ngakhale kuti anamwalira zaka mazana ambiri zapitazo.

Anthu onse odziyesa aneneri ameneŵa akhala osadalirika m’pang’ono pomwe ndiponso ogwiritsa mwala kwambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti amanyalanyaza Yehova Mulungu pamodzi ndi Mawu ake, Baibulo. Pachifukwa chimenechi iwo amalephera kuyankha mafunso ofunika monga aŵa: ‘Ndingatsimikize bwanji kuti zinthu zoloseredwa m’Baibulo zidzachitika? Zimagwirizana motani ndi cholinga cha Mulungu pa anthu? Kodi ndi motani mmene ine ndi banja langa tingapindulire ndi maulosi ameneŵa?’ Baibulo limayankha mafunso ameneŵa.

Komanso ulosi wa Baibulo ndi wapamwamba m’njira zina zambiri. Mosiyana ndi maulosi a okhulupirira nyenyezi, ulosi umenewu umapereka ufulu wa kudzisankhira. Choncho, palibe munthu yemwe ali kapolo wa chikonzero cha Mulungu. (Deuteronomo 30:19) Zolemba monga ngati za Nostradamus n’zosathandiza pachikhalidwe, m’malo mwake zangodzala zinsinsi komanso zimangotenga mtima. Koma ulosi wa Baibulo uli ndi maziko olimba pachikhalidwe. Umafotokoza chifukwa chimene Mulungu adzachitire zinthu monga mmene anafunira. (2 Mbiri 36:15) Ndipo maulosi a Yehova salephera, chifukwa ‘Mulungu . . . sanama.’ (Tito 1:2) Choncho, anthu amene akutsogozedwa ndi Mawu a Mulungu amakhala ndi moyo wounikidwa, watanthauzo, komanso wachimwemwe popanda kuwonongera nthaŵi yawo yamtengo wapatali ndiponso chuma chawo pazinthu zopanda pake.​—Salmo 25:12, 13.

Mfundo zimenezi komanso zina zambiri zinalongosoledwa pa Misonkhano Yachigawo ya Mboni za Yehova ya 1999/2000 ya “Mawu Aulosi a Mulungu” imene inachitika kuzungulira dziko lonse. Nkhani, kufunsa, zitsanzo, komanso seŵero la Baibulo zakopera chidwi cha omvetsera ku choloŵa chauzimu chimene anthu omwe akuŵerenga ndi kugwiritsa ntchito mawu aulosi a Mulungu akusangalala nacho. Nkhani yotsatira idzafotokoza mfundo zina zikuluzikulu za msonkhanowo.