Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Aulosi a Mulungu Amapatsa Chiyembekezo cha M’tsogolo

Mawu Aulosi a Mulungu Amapatsa Chiyembekezo cha M’tsogolo

 Mawu Aulosi a Mulungu Amapatsa Chiyembekezo cha M’tsogolo

MOTHANDIZIDWA ndi Mawu a Mulungu, Baibulo Lopatulika, Akristu oona amaona za m’tsogolo mwachikhulupiriro, komanso mwachiyembekezo. Pokhala otetezeka mu unansi wawo ndi Yehova Mulungu, iwo amayembekeza za m’tsogolo. Kwa zaka zambiri, Mboni za Yehova zakhala ophunzira akhama a maulosi a Baibulo monga momwe inafotokozera nkhani yoyambirira pa Misonkhano Yachigawo yakuti “Mawu Aulosi a Mulungu.” Choncho, kodi n’chiyani chimene Yehova anasungira anthu ake pamisonkhano imeneyi? Ali ndi mabaibulo m’manja mwawo, anthu onse amene anasonkhana anali okonzeka kuti afufuze. Mutu wa tsiku lililonse la msonkhanowo walembedwa monga kamutu kapadera.

TSIKU LOYAMBA: Kuyenda M’kuunika kwa Mawu a Mulungu

Nkhani yakuti “Tikutsogozedwa ndi Mawu a Mulungu” inafotokoza kuti anthu a Yehova ali ngati munthu wonyamuka ulendo mu mdima wa usiku. Pamene dzuŵa likutuluka, iye amangoona mwachimbuzimbuzi, koma pamene dzuŵa lafika pamutu, amaona bwinobwino. Monga momwe kunanenedweratu pa Miyambo 4:18, anthu a Yehova afikira pa kuona njira yawo bwinobwino n’kuunika kwa dzuŵa la choonadi chochokera m’mawu aulosi a Mulungu. Iwo sanasiyidwe kuti aziphunthwa mu mdima wauzimu.

Nkhani yaikulu yakuti, “Labadirani Mawu Aulosi a Mulungu,” inakumbutsa omvetsera kuti anthu amene amadalira Yehova sakhumudwitsidwa monga zimakhalira kwa anthu omwe amatsatira amesiya onyenga ndiponso aneneri onyenga. Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, ziyeneretso za Mesiya woona, Yesu Kristu, n’zogwira mtima! Mwachitsanzo, kusandulika kozizwitsa kwa Yesu kunachitira chithunzi za iye monga Mfumu yoikidwa ya Ufumu wa Mulungu. Chikhalire m’mphamvu ya Ufumu mu 1914, Yesu ndiyenso “nthanda” yotchulidwa pa 2 Petro 1:19. “Monga Nthanda Yaumesiya, akulengeza tsiku latsopano, kapena kuti nyengo, limene likuyamba kwa anthu onse omvera,” anatero mlankhuliyo.

Pologalamu yamasana inayamba ndi nkhani yakuti,  “Kuŵala Monga Zounikira” imene inafotokoza mwatsatanetsatane Aefeso 5:8, pamene mtumwi Paulo akutilangiza kuti “yendani monga ana a kuunika.” Akristu ali zounikira, osati mwa kungogaŵana Mawu a Mulungu ndi anthu ena komanso mwa kugwiritsa ntchito Baibulo m’moyo wawo motsanzira Yesu.

Kuti tikhale chounikira cha mtundu umenewu, tiyenera ‘Kusangalala ndi Kuŵerenga Mawu a Mulungu.’ Nkhani imeneyi inakambidwa m’zigawo zitatu mosiyirana. Pambuyo pogwira mawu a Abraham Lincoln, amene anati Baibulo ndi “mphatso yabwino koposa imene Mulungu anapatsapo anthu,” mlankhuli woyamba anafunsa omvetsera zimene chizoloŵezi chawo cha kuŵerenga chimavumbula ponena za kukula kwa chiyamikiro chawo pa Mawu a Yehova. Omvetsera analimbikitsidwa kuŵerenga Baibulo mosamala kwambiri, kukhala ndi nthaŵi yomayerekeza nkhani za m’Malemba m’maganizo mwawo ndiponso kugwirizanitsa mfundo zatsopano ndi zinthu zomwe akuzidziŵa kale.

Mbali yotsatira ya nkhani yosiyiranayi inagogomezera kufunika kwa kuphunzira, osati kungoŵerenga mwachisawawa, ngati titi tigaye “chakudya chotafuna.” (Ahebri 5:13, 14) Kuphunzira kumalimbikitsa kwambiri makamaka ngati ‘tiikiratu [“tikonzekeretsa,” NW] mitima yathu’ pasanakhale, monga momwe anachitira wansembe wachiisrayeli Ezara, anatero mlankhuliyo. (Ezara 7:10) Koma kodi n’chifukwa chiyani kuphunzira kuli kofunika motere? Chifukwa chakuti kumakhudza mwachindunji ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho, phunziro la Baibulo lifunika kukhala lamtengo wapatali, losangalatsa, komanso lotsitsimula, ngakhale kuti zimenezi zimafuna kuganiza kwambiri ndiponso khama. Kodi timapeza motani nthaŵi yokhala ndi phunziro lopindulitsa kwambiri? Mwa ‘kuchita machawi, [“kuombola nthaŵi,” NW]’ ku zinthu zosafunika kwenikweni, anatero mlankhuli womaliza wa nkhani yosiyiranayi. (Aefeso 5:16) Inde, njira yomwe tingapezere nthaŵi ndiyo kugwiritsa ntchito moyenera nthaŵi yomwe tilinayo.

Nkhani yakuti “Mulungu Amapereka Mphamvu kwa Otopa” inasonyeza kuti lerolino anthu ambiri ndi otopa. Chotero, kuti tikhale ndi “mphamvu yoposa yachibadwa” kaamba ka utumiki wachikristu, tikufunika kudalira Yehova, amene “alimbitsa olefuka.” (2 Akorinto 4:7, NW; Yesaya 40:29) Zinthu zolimbikitsa zimaphatikizapo Mawu a Mulungu, pemphero, mpingo wachikristu, kuchita nawo utumiki mokhazikika, oyang’anira achikristu, ndi zitsanzo za anthu okhulupirika. Mutu wakuti “Khalani Aphunzitsi Chifukwa cha Nyengoyi” unagogomeza kufunika kwakuti Akristu akhale aphunzitsi komanso alaliki ndi kuchita khama pa kukulitsa “luso la kuphunzitsa.”​—2 Timoteo 4:2, NW.

Nkhani yomaliza ya tsikuli yamutu wakuti, “Olimbana ndi Mulungu Sadzapambana,” inanena za zoyesayesa zamakono zosokeretsa zimene anthu akuchita m’mayiko ena zofuna kuti Mboni za Yehova zizioneka monga kagulu koopsa ka chipembedzo. Koma sitikufunikira kuchita mantha, popeza Yesaya 54:17 amati: “‘Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi choloŵa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chawo chimene chifuma kwa Ine,’ ati Yehova.”

 TSIKU LACHIŴIRI: Zinthu Zodziŵikitsidwa mwa Malemba Aulosi

Pambuyo pa kukambirana lemba la m’Baibulo la tsikulo, anthu amene anasonkhana anasangalala ndi nkhani yosiyirana yachiŵiri pamsonkhanowo, yamutu wakuti “Kulemekeza Yehova Monga Oŵalitsa Kuunika.” Nkhani yoyamba inasonyeza kuti cholinga cha Mkristu ndicho kulemekeza Yehova mwa kulalikira paliponse. Mbali yotsatira inanena za kufunika kwa kutsogolera anthu omvetsera ku gulu la Mulungu. Motani? Mwa kuthera mphindi zisanu kapena khumi tisanayambe phunziro la Baibulo lapanyumba kapena titangomaliza zowasonyeza mmene gulu la Mulungu limayendera. Nkhani yachitatu m’nkhani yosiyiranayi inagogomeza kufunika kwa kulemekeza Mulungu ndi ntchito zabwino.

Nkhani yakuti “Kondani Zikumbutso za Yehova Kwambiri” inalongosola mavesi osankhidwa mu Salmo 119. Ndithudi, timafunikira zikumbutso, popeza kuti tonsefe timaiŵala. Choncho, n’kofunika kwambiri kuti tikulitse chikondi pa zikumbutso za Yehova, monga momwe wamasalmo anachitira!

Kenako zinthu zinafika pachimake ndi nkhani ya ubatizo yamutu wakuti “Kumvera Mawu Aulosi Kumatsogolera ku Ubatizo.” Anthu opita ku ubatizo anakumbutsidwa kuti azitsanzira Kristu osati kokha mwa kubatizidwa komanso mwa kutsatira mapazi ake mosamalitsa. (1 Petro 2:21) Achatsopano ameneŵa ali ndi mwayi waukulu kwambiri wa kutenga nawo mbali m’kukwaniritsidwa kwa Yohane 10:16, pamene Yesu analosera kuti iye adzasonkhanitsa “nkhosa zina” kuti zitumikire pamodzi ndi ophunzira ake odzozedwa ndi mzimu!

Poyamba pologalamu yamasana, nkhani yakuti “Imvani Chimene Mzimu Unena” inafotokoza kuti mzimu wa Yehova umalankhula nafe kudzera m’Baibulo, mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndiponso m’chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo. (Mateyu 24:45) Choncho, Akristu safunikira kuchita kumva mawu enieni ochokera kumwamba kuti adziŵe mmene angakondweretsere Mulungu. Makambirano otsatira, “Kuchirikiza Molimba Chiphunzitso Chogwirizana ndi Kudzipereka Kwaumulungu,” analangiza Akristu kuti asatsate malingaliro ofalitsidwa ndi dziko ili amene amawononga makhalidwe abwino. Ndithudi, chidwi chosaletseka chingatiike pangozi ya kulandira chidziŵitso chovulaza chofalitsidwa ndi ampatuko ndiponso atumiki a Satana. N’kwabwino kwambiri kumaŵerenga Baibulo mokhazikika kuphatikizanso nkhani zonse za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Ndi mutu wakuti “Gwiranibe Chitsanzo cha Mawu a Moyo,” nkhani yotsatira inagogomezera kufunika kwa kudziŵa bwino “chitsanzo” cha m’Malemba, kapena kuti mpangidwe, wa choonadi. (2 Timoteo 1:13) Kumvetsa chitsanzo chimenechi ndiyo njira yokhalira wodzipereka kwa Mulungu komanso yodziŵira zinthu zomwe sizigwirizana ndi choonadi.

Talingalirani kuti Yehova akukuonani kukhala wofunika. Ungakhale ulemu waukulu kwabasi! Nkhani yozikidwa pa ulosi wa Hagai, yakuti “Zinthu “Zofunika” Zikudzaza Nyumba ya Yehova” inali yolimbikitsa kwambiri chifukwa chakuti inatsimikizira omvetsera kuti munthu aliyense wa “khamu lalikulu” ndi wofunika kwambiri kwa Yehova. (Chivumbulutso 7:9) Choncho, Yehova sadzawawononga pa ‘kugwedeza’ kwake amitundu komaliza pa ‘chisautso chachikulu’ m’tsogolomu. (Hagai 2:7, 21, 22; Mateyu 24:21) Komabe pakali pano, anthu a Yehova ayenera kukhala ogalamuka mwauzimu, monga inalongosolera nkhani yakuti “Malemba a Maulosi Amatigalamutsa.” Mlankhuli anagwira mawu a Yesu akuti: “Dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.” (Mateyu 24:42) Kodi timakhala motani atcheru mwauzimu? Mwa kukangalika pa utumiki wa Yehova, kupemphera mosaleka, ndi kuyembekezera tsiku lalikulu la Yehova.

Nkhani yomaliza ya tsikuli inali ndi mutu wakuti “Mawu Aulosi m’Nthaŵi ya Chimaliziro.” Imeneyi izikumbukiridwa kwa zaka zambiri. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mlankhuli analengeza za kutulutsidwa kwa buku latsopano​—Pay Attention to Daniel’s Prophecy! “Buku lazithunzithunzi zokongola limeneli la masamba 320 likukhudza mbali iliyonse ya m’buku la Danieli,” anatero mlankhuliyo. Ndi umboni wolimbikitsa chikhulupiriro kwambiri wakuti Yehova akuunika Mawu ake aulosi!

TSIKU LACHITATU: Mawu Aulosi a Mulungu Salephera Konse

Tsiku lomaliza la msonkhanowo linayamba ndi nkhani yosiyirana yakuti, “Mawu Aulosi a  Panthaŵi Yoikika.” Mbali zitatuzo zinafotokoza zilengezo zitatu za mneneri Habakuku zonena za ziŵeruzo za Yehova. Chilengezo choyamba chinali kwa mtundu wopulupudza wa Yuda ndipo chachiŵiri kwa Babulo wopondereza. Chomaliza, chomwe chikwaniritsidwe posachedwapa, chikukhudza chiwonongeko cha anthu oipa. Ponenapo za Armagedo, mbale womaliza pa nkhani yosiyiranayi anasonkhezera omvetsera kukhala ndi mantha oyenera aumulungu pamene ananena kuti: “Ndithudi, zidzakhala zochititsa mantha pamene Yehova adzamasula mphamvu zake zonse zazikulu.”

“Kuyamikira Choloŵa Chathu Chauzimu” ndiwo unali mutu wa seŵero la Baibulo losangalatsa kwambiri. Nkhani yokhudza mtima imeneyi inasiyanitsa maganizo a Yakobo ndi a Esau pa zinthu zauzimu. Esau ananyoza choloŵa chake chauzimu, chotero chinaperekedwa kwa Yakobo, amene anachiyamikira kwambiri. “Kodi [choloŵa chauzimu] n’chiyani chimene Yehova watipatsa?” anafunsidwa motero osonkhanawo. “Choonadi cha Mawu ake, Baibulo; chiyembekezo cha moyo wosatha; komanso mwayi womuimira monga alengezi a uthenga wabwino,” anayankha motero mlankhuliyo.

Mbali yotsatira inali ndi mutu wakuti “Kodi Choloŵa Chathu Chamtengo Wapatali Chimatanthauzanji kwa Inu?” Timasonyeza maganizo abwino pa choloŵa chathu chauzimu mwa kuika utumiki wa Yehova ndiponso zinthu zauzimu patsogolo pa zinthu zaumwini kapena zakuthupi. Mwanjira imeneyi timasumika moyo wathu pa ubwenzi wathu ndi Yehova, mosiyana kwambiri ndi Adamu, Esau, ndi Aisrayeli osakhulupirika.

Nkhani yapoyera, “Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano​—Monga Kunanenedweratu,” inaphatikiza pamodzi maulosi akuluakulu anayi okhudza “miyamba yatsopano” ndi “dziko latsopano.” (Yesaya 65:17-25; 66:22-24; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:1, 3-5) Ndithudi, Yehova anali kuganiza za kukwaniritsidwa kwina kwakukulu kwa maulosi ameneŵa kuwonjezera pa kukwaniritsidwa kwake pa anthu ake obwezeretsedwa mu 537 B.C.E. Inde, anali kuganiza za boma lake la Ufumu (“miyamba yatsopano”) ndi nzika zake za padziko lapansi (“dziko latsopano”), zomwe zingadzakhale padziko lonse lapansi m’paradaiso waulemerero.

Nkhani yakuti “Ziyembekezo Zathu Pamene Mawu a Mulungu Akutitsogolera” ndiyo imene inafikitsa msonkhanowu pamapeto osangalatsa ndiponso olimbikitsa. Inakumbutsa onse kuti “yafupika nthaŵi” yomalizira ntchito yolalikira za Ufumu. (1 Akorinto 7:29) Inde, tili pafupi penipeni pa kukwaniritsidwa kwa lamulo la Yehova la kuwononga Satana limodzi ndi dongosolo lake lonse loipa. Tiyeni tikhale ndi malingaliro a wamasalmo amene anaimba kuti: “Moyo wathu walindira Yehova. Iye ndiye thandizo lathu ndi chikopa chathu.” (Salmo 33:20) Ndi chiyembekezo chaulemerero waukulu kwambiri chimene chili m’tsogolo mwa anthu amene ziyembekezo zawo zimadalira mawu aulosi a Mulungu!

[Chithunzi patsamba 7]

Seŵero logwira mtima linakulitsa kuyamikira choloŵa chauzimu cha atumiki a Yehova

[Chithunzi patsamba 7]

Anthu ambiri amene anamvera mawu aulosi a Mulungu anabatizidwa