Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Danieli Lifotokozedwa!

Buku la Danieli Lifotokozedwa!

 Buku la Danieli Lifotokozedwa!

OPEZEKA pa msonkhanowo anali ofunitsitsa kupeza kope lawolawo la buku longotulutsidwa kumene lamasamba 320 lakuti, Pay Attention to Daniel’s Prophecy! Kodi iwo anamva bwanji ponena za bukulo? Tamverani zomwe ena ananena.

“Monga achinyamata ambiri, ndimavutika kuphunzira nkhani za m’mbiri yamakedzana. Choncho pamene ndinalandira kope langalanga la buku latsopanoli, Pay Attention to Daniel’s Prophecy!, ndinalibe chidwi chenicheni choliŵerenga, koma ndinayesera kuliŵerenga. Kunena zoona, ndimaganiza molakwika kwambiri! Limeneli ndi limodzi mwa mabuku abwino kwambiri omwe ndaŵerengapo. Ndi buku lochititsa chidwi kwambiri! Sindiganizanso kuti ndikuŵerenga nkhani imene inachitika zaka zikwi zambiri zapitazo. Kwanthaŵi yoyamba, nditha kumvetsa mmene zinthu zinalili kwa Danieli. Ndithudi ndikutha kuyerekeza mmene zinthu zingakhalire utachotsedwa ku banja lanu, kutumizidwa ku dziko lachilendo, ndipo chikhulupiriro chako n’kumayesedwa mobwerezabwereza. Zikomo kwambiri chifukwa cha buku limeneli.”​—Anya.

“Chomwe chimandithandiza kwambiri ndicho uthenga womveka bwino wakuti Yehova ali ndi mphamvu kotheratu pa nkhani zimene zimakhudza anthu ake. Kudzera m’masomphenya ndiponso m’maloto a Danieli komanso a anthu ena amene iye anamasulira, n’zoonekeratu kuti nthaŵi zonse Mulungu wathu adzachita zinthu mogwirizana ndi chifuno chake. Zimenezi zikulimbikitsa chiyembekezo chomwe tili nacho pa maulosi ovumbulidwa m’Baibulo okhudza dziko latsopano limene adzadzetsa.”​—Chester.

“Ndinasangalala ndi mmene munachititsira kuti Danieli akhale ngati tikumuona ali wamoyo. Ndinam’dziŵa bwino kwambiri chifukwa cha njira imene munasonyezera kuvutika mtima kwake ndiponso nkhaŵa yake. Ndikutha kumvetsa chifukwa chake Yehova anamuona kukhala munthu wokondedwa. M’mayesero ake onse ndiponso m’zizunzo zonse, samaganiza za iye mwini. Nkhaŵa yake yaikulu inali pa Yehova ndi dzina Lake labwino. Zikomo kwambiri chifukwa chomveketsa bwino lomwe mfundo zimenezi.”​—Joy.

“Zimenezi ndi zimene takhala tikudikira! Zinali zisanasonyezedwepo mmene buku la Danieli limakhudzira aliyense wa ife. Nditaŵerenga mbali yaikulu ya buku latsopanoli usiku tsiku limene ndinalilandira, ndinasiya kuŵerenga n’kuthokoza Yehova m’pemphero.”​—Mark.

“Sitinadziŵe kuti liwakhudza bwanji ana athu. Wina ali ndi zaka zisanu ndipo winayo ali ndi zaka zitatu zakubadwa. . . . Pamene kuli kwakuti nkhani za Danieli, Hananiya, Misaeli, ndi Azariya zakhala zina mwa nkhani zowasangalatsa kwambiri m’Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kafotokozedwe kake m’buku la Daniel’s Prophecy kawakhudza mtima m’njira yomwe sitinailingalirepo. Ngakhale pausinkhu wawo waung’ono, iwo akuoneka kuti akutha kuzindikira kuti sasiyana ndi anyamata olungama ameneŵa. Iwo ndi zitsanzo zabwino kwambiri kwa ana athu! Mwatipatsa chida chapamwamba kwambiri! Zikomo kwambiri!”​—Bethel.

“Ndinaona ngati kuti ndinali pamodzi ndi anyamata achihebri ameneŵa panthaŵi yomwe chikhulupiriro chawo chimayesedwa; ndipo zimenezi zinandilimbikitsa kupenda chikhulupiriro changa. Bokosi la kubwereramo lakuti “Kodi Mwazindikira Chiyani?” limakhomereza mu mtima mfundo za m’mutu uliwonse. Kachiŵirinso, zikomo kwambiri chifukwa cha buku linanso laukatswiri.”​—Lydia.