NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) October 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa 27 November mpaka 24 December, 2017.

MBIRI YA MOYO WANGA

Timadalitsidwa Tikamachita Zimene Yehova Amatiuza

Mu 1952, Olive Matthews ndi mwamuna wake anavomera kukachita upainiya ku Ireland. Kodi Yehova anawadalitsa bwanji?

“Tizisonyezana Chikondi Chenicheni M’zochita Zathu”

Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili ndi chikondi chenicheni osati chachinyengo?

Choonadi sichibweretsa “mtendere koma lupanga”

Kodi “lupanga” limene Yesu ananena kuti abweretsa n’chiyani, nanga lingakukhudzeni bwanji?

Yosefe wa ku Arimateya Analimba Mtima

Kodi Yosefe wa ku Arimateya anali ndani? Nanga ankadziwana bwanji ndi Yesu? Kodi nkhani yake ndi yofunika bwanji kwa inuyo?

Kodi Masomphenya a Zekariya Akukukhudzani Bwanji?

N’chifukwa chiyani Mulungu anaonetsa Zekariya masomphenya a mpukutu ukuuluka, mkazi ali m’chiwiya komanso akazi awiri akuuluka?

Timatetezedwa ndi Magaleta Komanso Chisoti Chachifumu

Kodi masomphenya omaliza amene Zekariya anaona a mapiri amkuwa, magaleta okonzeka kupita kunkhondo ndiponso wansembe amene anapatsidwa ufumu akutsimikizira chiyani anthu a Mulungu masiku ano?

Anamusonyeza Kukoma Mtima

Kodi kusonyeza munthu kukoma mtima kunathandiza bwanji kuti ayambe kuphunzira Baibulo?

Kodi Mukudziwa?

Kodi Ayuda anali ndi chizolowezi chotani chomwe chinachititsa Yesu kuuza anthu kuti asamalumbire?