Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchereza Alendo Ndi Kofunika Kwambiri

Kuchereza Alendo Ndi Kofunika Kwambiri

“Muzicherezana popanda kudandaula.”—1 PET. 4:9.

NYIMBO: 100, 87

1. Kodi Akhristu a munthawi ya atumwi anakumana ndi zotani?

PAKATI pa chaka cha 62 ndi 64 C.E., mtumwi Petulo analembera ‘alendo osakhalitsa, amene anali omwazikana ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asia ndi ku Bituniya.’ (1 Pet. 1:1) M’mipingo imeneyi munali anthu a mitundu yosiyanasiyana ndipo anthuwo ankafunika kulimbikitsidwa komanso kupatsidwa malangizo. Iwo ankavutika chifukwa chotsutsidwa ndi anthu ena, kunyozedwa komanso ankakumana ndi mayesero oopsa ngati “moto.” Ankakhalanso pa nthawi yovuta kwambiri. N’chifukwa chake Petulo analemba kuti: “Mapeto a zinthu zonse ayandikira.” Mapeto oopsa anabwera pamene Yerusalemu anawonongedwa pasanapite ndi zaka 10 zomwe. Kodi n’chiyani chimene chikanathandiza Akhristu onse kuti apirire mavutowa?​—1 Pet. 4:4, 7, 12.

2, 3. N’chifukwa chiyani Petulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti azicherezana? (Onani chithunzi choyambirira.)

2 Malangizo ena amene Petulo anapereka kwa abale akewo anali akuti: “Muzicherezana.” (1 Pet. 4:9) Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti ‘kucherezana’ amatanthauza ‘kukonda kapena kukomera mtima anthu achilendo.’ Koma Petulo anauza Akhristu anzake kuti  ‘azichereza’ anthu amene ankadziwana nawo. Ndiye kodi kucherezana kukanawathandiza bwanji?

3 Kukanawathandiza kuti azigwirizana kwambiri. Taganizirani zimene zinakuchitikirani inuyo. Kodi munaitanidwapo kuti mukacheze kunyumba ya munthu wina? Muyenera kuti mukukumbukirabe mmene munasangalalira. Kapena mwina munaitana anthu ena amumpingo kuti adzacheze nanu ndipo zinathandiza kuti muzigwirizana kwambiri. Tikaitanira abale ndi alongo athu kunyumba m’pamene timadziwana nawo bwino kwambiri. Akhristu a mu nthawi ya Petulo ankafunika kugwirizana kwambiri kuti athe kupirira mavuto awo. Ifenso timafunika kugwirizana kwambiri chifukwa tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’​—2 Tim. 3:1.

4. Kodi tikambirana mafunso ati munkhaniyi?

4 Kodi tingakhale ochereza m’njira ziti? Nanga tingatani kuti tisamalephere kukhala ochereza? Kodi tiyenera kuchita chiyani anthu akatiitana?

ZIMENE TINGACHITE KUTI TIKHALE OCHEREZA

5. Kodi tingakhale bwanji ochereza pamisonkhano?

5 Pamisonkhano: Munthu aliyense yemwe wafika pamisonkhano amabwera kuti adzalandire chakudya chauzimu. Choncho tonse timakhala ngati alendo amene aitanidwa ndi Yehova komanso gulu lake. (Aroma 15:7) Koma anthu atsopano akafika, amakhalanso ngati alendo athu. Ndiye tiyenera kuwalandira bwino mosaganizira za mmene akuonekera kapena mmene avalira. (Yak. 2:1-4) Ngati munthu wina wangobwera popanda winawake amene wamuitana, ndi bwino kumupempha kuti tikhale naye pamodzi. Mwina tingamuthandize kuti azitsatira bwinobwino nkhani zimene zikukambidwa komanso kuti aziona nawo Malemba. Tikatero tidzakhala tikutsatira malangizo akuti: “Khalani ochereza.”​—Aroma 12:13.

6. Kodi tiyenera kuyamba ndi kuitana anthu ati kunyumba kwathu?

6 Kuwaitanira chakudya: Kale anthu ankasonyeza mtima wochereza poitanira anthu kunyumba kwawo kuti adzadye chakudya. (Gen. 18:1-8; Ower. 13:15; Luka 24:28-30) Munthu akachita zimenezi ankasonyeza kuti akufuna kuti amene wamuitanayo akhale mnzake komanso akhale naye pamtendere. Koma kodi tiyenera kuyamba ndi kuitana anthu ati? Tiyenera kuyamba ndi abale ndi alongo amumpingo wathu. Tikutero chifukwa tikadzakumana ndi mavuto aakulu tidzafunika kudalirana. Choncho tingachite bwino kuti tizikhala nawo mwamtendere komanso kugwirizana kwambiri. N’zochititsa chidwi kuti mu 2011, Bungwe Lolamulira linasintha nthawi imene banja la Beteli ku United States linkachitira Phunziro la Nsanja ya Olonda. Poyamba phunziroli linkayamba 6:45 madzulo koma panopa limayamba 6:15 madzulo. N’chifukwa chiyani anasintha? Analengeza kuti izi zingapereke mpata woti abale ndi alongo aziitana anzawo a pa Beteli kuti adzacheze nawo. Maofesi a nthambi osiyanasiyana anachitanso zomwezi. Zimenezi zathandiza kuti abale ndi alongo a pa Beteli azigwirizana kwambiri.

7, 8. Kodi tingachereze bwanji anthu ena m’gulu la Yehova?

7 Timakhalanso ndi mwayi wochereza alendo pa nthawi imene abale ochokera m’mipingo ina abwera kudzakamba nkhani, kukabwera oyang’anira madera kapena abale ochokera ku ofesi ya nthambi. (Werengani 3 Yohane 5-8.) Mwachitsanzo, tikhoza kuwaitanira zakudya kapena zakumwa. Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuchereza?

8 Mlongo wina wa ku United States anati: “Ine ndi mwamuna wanga takhala tikuitana kunyumba kwathu abale amene ankabwera kudzakamba nkhani. Nthawi zonse tikamacheza nawo limodzi ndi akazi awo timasangalala kwambiri ndipo zimatilimbikitsa mwauzimu. Sitinong’oneza bondo ngakhale pang’ono.”

9, 10. (a) Kodi ndi anthu ati amene tingawaitane kuti adzagone kwathu? (b) Kodi anthu amene alibe nyumba zabwino angaitane anthu kuti adzagone kwawo? Perekani chitsanzo.

9 Kulola kuti afikire kwathu: Kale anthu  ankalola kuti alendo osakayikitsa agone kunyumba kwawo. (Yobu 31:32; Filim. 22) Masiku anonso timafunika kulandira anthu kuti agone kunyumba kwathu. Mwachitsanzo, oyang’anira madera amafunika malo ogona akafika pampingo. Abale ndi alongo amene amapita kusukulu zophunzitsa Baibulo kapena kukathandiza ntchito zomangamanga amafunikanso malo ogona. Komanso pakachitika ngozi zadzidzidzi, mabanja ena amafunika malo ogona mpaka pamene nyumba zawo zakonzedwa. Sikuti anthu opeza bwino okhaokha ndi amene ayenera kuchereza alendo. Tikutero chifukwa chakuti mwina iwo achita zimenezi maulendo ambirimbiri. Choncho ngakhale titapanda kukhala ndi nyumba yabwino, tikhozabe kuitana anthu kuti afikire kwathu.

10 M’bale wina wa ku South Korea amakumbukira zimene zinachitika pa nthawi imene ophunzira ku sukulu yophunzitsa Baibulo anafikira kwawo. Iye analemba kuti: “Poyamba tinkakayikira chifukwa tinali titangokwatirana kumene ndipo nyumba yathu inali yaing’ono. Koma tinasangalala kwambiri kukhala ndi ophunzirawa. Zinatithandiza kuona kuti anthu okwatirana amasangalala kwambiri akamatumikira Yehova limodzi n’kumayesetsa kukwaniritsa zolinga zauzimu.”

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchereza anthu amene asamukira mumpingo wathu?

11 Kuthandiza anthu atsopano mumpingo: Masiku ano anthu ena akhoza kusamukira m’dera lathu. Ena angabwere chifukwa choti kudera lathulo kukufunika ofalitsa ambiri. Mwachitsanzo, apainiya angatumizidwe kuti adzathandize mumpingo mwathu. Pa nthawiyi, onsewa amakhala kuti ali m’dera lachilendo, mumpingo watsopano ndiponso mwina ayenera kuphunzira chilankhulo kapena chikhalidwe chatsopano. Choncho kuwaitanira chakudya, zakumwa kapena kuwatenga kuti tikacheze nawo kumalo enaake kungawathandize kuti asachedwe kuzolowera mpingo wawo watsopano.

12. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kuchereza alendo sikufuna zambiri.

12 Kuchereza alendo sikumafuna zambiri. (Werengani Luka 10:41, 42.) M’bale wina anafotokoza zimene zinamuchitikira atangoyamba kumene umishonale. Iye anati: “Tinali achinyamata, sitinkadziwa zambiri ndipo tinkalakalaka kwathu. Tsiku lina mkazi wanga ankavutika kwambiri chifukwa chosowana ndi anthu akwathu ndipo ndinayesetsa kumukhazika mtima m’malo koma sizinathandize. Ndiye cha m’ma 7:30 madzulo tinangomva kugogoda pakhomo. Mayi wina amene ankaphunzira Baibulo anatibweretsera malalanje atatu. Anabwera kudzatilandira poti tinali amishonale atsopano. Tinamuuza kuti alowe ndipo tinamupatsa madzi akumwa. Kenako tinamukonzera zakumwa zina. Ife sitinkadziwa Chiswahili ndipo iyenso sankadziwa Chingelezi. Koma zimene anachitazi zinatithandiza kuti tiyambe kupeza anzathu m’dzikolo.”

ZIMENE ZINGATILEPHERETSE KUKHALA OCHEREZA

13. Kodi kuchereza alendo kungatithandize bwanji?

13 Kodi munakayikirapo kuitana anthu pa zifukwa zina? Ngati zili choncho, mwinatu munaphonya mwayi wocheza ndi anthu ena komanso kupeza anzanu abwino kwambiri. Kuchereza alendo ndi kumene kungathandize munthu kuti asamasowe ocheza nawo. Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani munthu angakayikire kuitana anthu?’ Pangakhale zifukwa zingapo.

14. Kodi tingatani ngati tikulephera kucheza ndi anthu chifukwa chosowa nthawi kapena kutopa?

14 Kusowa nthawi komanso kutopa: Atumiki a Yehova amakhala ndi zochita zambiri. Choncho ena amaona kuti alibe nthawi komanso atopa moti sangachereze alendo. Ngati ndi mmene zilili ndi inuyo, mwina mungachite bwino kuonanso zimene mumachita tsiku lililonse. Kodi mungasinthe zinthu zina n’cholinga choti mukhale ndi nthawi yoitanira anthu kapena yopita kukacheza  ndi anthu ena? Malemba amalimbikitsa Akhristu kuti azikhala ochereza. (Aheb. 13:2) Si kulakwa kupeza nthawi yochitira zimenezi, ndipotu ndi zimene tiyenera kuchita. Koma muyenera kukhala okonzeka kusintha zinthu zina zimene mumachita.

15. Kodi anthu ena amakayikira kuitana anthu chifukwa chiyani?

15 Kudzikayikira: Kodi munafunapo kuitana anthu koma n’kulephera chifukwa chodzikayikira? Ena ndi amanyazi ndipo amaopa kuti adzasowa nkhani zoti azidzacheza ndi anthuwo kapena amaganiza kuti alendowo sangasangalale. Ena si opeza bwino ndipo amaganiza kuti sangakwanitse kupatsa anthu zimene anthu ena mumpingo angawapatse. Koma tizikumbukira kuti chofunika si nyumba yapamwamba koma mtima wochereza komanso nyumba yaukhondo.

16, 17. N’chiyani chingatithandize kuti tisamaope kuitana alendo kunyumba kwathu?

16 Ngati mumakayikira zoitana anthu, dziwani kuti si inu nokha. M’bale wina wa ku Britain, yemwe ndi mkulu, anati: “Ukaitana alendo sulephera kuda nkhawa. Koma mofanana ndi zinthu zina zonse zimene timachita potumikira Yehova, ubwino wake umakhala waukulu kuposa nkhawa zimene tinali nazo. Nthawi zina ndimangoitana anthu kuti timwe khofi ndipo timasangalala.” Tizikumbukira kuti nthawi zonse kusonyeza chidwi kwa alendo n’kothandiza kwambiri. (Afil. 2:4) Pafupifupi aliyense amafuna kufotokoza zimene zachitika pa moyo wake. Ndiye pocheza ndi anthu m’pamene timakhala ndi mwayi wofotokoza zimene zachitika pa moyo wathu. Mkulu winanso analemba kuti: “Ndikaitana anthu amumpingo kunyumba kwathu ndimayamba kuwadziwa bwino komanso ndimadziwa mmene anayambira choonadi.” Kusonyeza chidwi kwa anthu ena kumathandiza kuti musangalale pocheza nawo.

17 Mlongo wina amene akuchita upainiya ankalola kuti ophunzira mu sukulu zophunzitsa Baibulo zosiyanasiyana azifikira kwawo ndipo anati: “Poyamba ndinkakayikira chifukwa choti nyumba yanga si yabwino kwenikweni komanso mipando yanga ndi yakale. Koma zimene mkazi wa mlangizi wina wa pa sukuluzo ananena zinandilimbikitsa kwambiri. Ananena kuti iye ndi mwamuna wake akamachezera mipingo, amasangalala kwambiri akafikira kunyumba ya munthu wokonda zauzimu ngakhale kuti si wopeza bwino. Amaona kuti zolinga zawo zimakhala zofanana pa nkhani yotumikira Yehova ndi kukhala moyo wosalira zambiri. Izi zinandikumbutsa zimene mayi athu ankakonda kutiuza tili ana. Ankanena kuti: ‘Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi.’” (Miy. 15:17) Choncho ngati timaitana anthu chifukwa cha chikondi, sitiyenera kudera nkhawa chilichonse.

18, 19. Kodi kukhala ochereza kungatithandize bwanji kuti tiyambe kugwirizana ndi anthu?

18 Mmene mumaonera anthu ena: Kodi mumpingo wanu muli munthu wina amene zochita zake sizikusangalatsani? Zimakhala zovuta kuti muzikonda munthu wotereyu ndipo ngati simuchitapo kanthu, maganizo amenewa sangakuthereni. Zingakuvuteni kuitana kunyumba kwanu anthu amene simugwirizana nawo. Komanso ngati wina anakukhumudwitsani, zingavute kuiwala nkhaniyo.

19 Koma Baibulo limanena kuti kuchereza anthu, ngakhale adani athu, kumathandiza kuti tizigwirizana nawo. (Werengani Miyambo 25:21, 22.) Kuchereza munthu kungathandize kuti tiyambe kugwirizana naye. Zikhoza kuthandiza kuti tiyambe kuona makhalidwe ake abwino amene anachititsa kuti Yehova amukokere m’gulu lake. (Yoh. 6:44) Chikondi chikakulimbikitsani kuitana munthu amene simunkagwirizana naye poyamba zingathandize kuti muyambe kugwirizana. Ndiye kodi mungadziwe bwanji kuti mukuitana munthu chifukwa cha chikondi? Chinthu china chimene chingatithandize ndi kutsatira malangizo a pa Afilipi 2:3. Lembali limati:  ‘Mukhale odzichepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.’ Tikamaganizira zinthu zimene ena amachita bwino kuposa ifeyo, tingayambe kuwakonda kwambiri komanso kufuna kuwachereza. Anthuwa angatipose pa nkhani yokhala ndi chikhulupiriro, kupirira, kulimba mtima kapena makhalidwe ena.

ZIMENE TIYENERA KUCHITA TIKAITANIDWA

Nthawi zambiri munthu akaitana alendo amakonzekera bwino (Onani ndime 20)

20. Kodi tingasonyeze bwanji ulemu ngati munthu wina watiitana, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezo?

20 Davide anafunsa Yehova kuti: “Inu Yehova, ndani amene angakhale mlendo m’chihema chanu?” (Sal. 15:1) Pambuyo pofunsa funso limeneli, anafotokoza makhalidwe amene Yehova amafuna kuti alendo ake akhale nawo. Khalidwe lina ndi kunena zoona. Baibulo limati munthu amene amanena zoona amati, “akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.” (Sal. 15:4) Anthu ena akatiitana ife n’kuvomera, si bwino kungosintha popanda zifukwa zomveka. N’kutheka kuti woitanayo anachita zambiri pokonzekera ndiye zonse zimene wachita zingakhale zopanda ntchito. (Mat. 5:37) Ena amavomera akaitanidwa ndi munthu koma n’kusintha chifukwa choti aitanidwanso ndi anthu ena amene akuganiza kuti akhoza kusangalala nawo kwambiri. Kodi zimenezi zingasonyeze kuti ndife achikondi komanso aulemu? Ndiyetu tikaitanidwa n’kuvomera tiyenera kuyamikira zilizonse zimene oitanawo angatipatse. (Luka 10:7) Koma ngati pali zifukwa zomveka zimene zingatilepheretse, tiyenera kudziwitsa wotiitanayo mwamsanga.

21. Kodi kulemekeza chikhalidwe cha anthu amene atiitana n’kothandiza bwanji?

21 Chinthu china chofunika ndi kulemekeza chikhalidwe cha amene atiitana. M’madera ena, munthu akhoza kungofika pakhomo kudzacheza koma m’madera ena pamafunika kuneneratu tisanapite kwa munthu. M’madera enanso munthu akaitana alendo, alendowo ndi amene amayamba kudya zabwino kwambiri pomwe m’madera ena alendo ndi eni khomo amadya mofanana. Kwina munthu akaitanidwa amatenga kenakake kuti akawonjezere pa zimene woitanayo wakonza koma kwina woitana sayembekezera kuti alendo abweretse zinthu. M’madera ena, mlendo amafunika kukana kamodzi kapena kawiri akaitanidwa kenako amavomera pomwe kwina ukangokana, ngakhale kamodzi, zimaoneka kuti sukufuna. Ndiye chofunika n’kuyesetsa kuti tisakhumudwitse anthu amene atiitana.

22. N’chifukwa chiyani kucherezana n’kofunika kwambiri?

22 Chinthu chofunika kwambiri kuchikumbukira n’chakuti “mapeto a zinthu zonse ayandikira.” (1 Pet. 4:7) Posachedwapa tikumana ndi chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo padzikoli. Choncho mavuto akamawonjezereka, tidzafunika kusonyezana chikondi kwambiri ndi abale ndi alongo athu. Panopa m’pamene tiyenera kutsatira kwambiri malangizo a Petulo akuti “muzicherezana” ndipo zimenezi n’zimene tizidzachita mpaka kalekale.​—1 Pet. 4:9.