NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) March 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa April 30 mpaka June 3, 2018.

Munthu Ayenera Kubatizidwa Kuti Akhale Mkhristu

Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani zokhudza ubatizo? Munthu ayenera kuchita zinthu ziti asanabatizidwe? Nanga n’chifukwa chiyani munthu ayenera kukumbukira kufunika kobatizidwa pophunzitsa ana ake kapena anthu ena Baibulo?

Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kuti Ayenerere Kubatizidwa?

Kodi makolo ayenera kutsimikizira za chiyani ana awo asanabatizidwe?

MAFUNSO OCHOKERA KWA OWERENGA

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

N’chifukwa chiyani mabuku a Mboni za Yehova amasonyeza kuti mtumwi Paulo anali wadazi?

Kuchereza Alendo Ndi Kofunika Kwambiri

N’chifukwa chiyani Malemba amalimbikitsa Akhristu kuti azicherezana? Kodi tingakhale ochereza m’njira ziti? Kodi tingatani kuti zinthu zina zisatilepheretse kukhala ochereza?

MBIRI YA MOYO WANGA

Yehova Sanandigwiritsepo Mwala

Erika Nöhrer Bright watumikirapo monga mpainiya wokhazikika, mpainiya wapadera komanso mmishonale. Akufotokoza zimene Mulungu wachita pomusamalira, kumulimbikitsa komanso kumuthandiza pa zaka zonse za utumiki wake.

Mulungu Amatilangiza Chifukwa Chotikonda

Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu amene anapatsidwa malangizo ndi Mulungu? Kodi tingatsanzire bwanji Yehova popereka malangizo?

“Mverani Malangizo Kuti Mukhale Anzeru”

Kodi Yehova amatiphunzitsa bwanji kuti tikhale odziletsa? Kodi tingatani kuti tipindule ndi malangizo amene timalandira mumpingo wachikhristu?