Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzifufuza Chuma Chamtengo Wapatali Kuposa Golide

Muzifufuza Chuma Chamtengo Wapatali Kuposa Golide

Kodi inuyo munatolapo mwala wa golide? M’dzikoli si anthu ambiri amene anachita mwayi umenewu. Koma pali anthu ambiri amene anapeza chuma chamtengo wapatali kuposa golide. Chuma chake ndi nzeru zochokera kwa Mulungu ndipo “golide woyenga bwino sangaperekedwe mosinthana nazo.”—Yobu 28:12, 15.

ANTHU amene akuphunzira Baibulo tingawayerekezere ndi anthu amene akufufuza golide. Iwo amafunika kuphunzira Malemba mwakhama kuti apeze nzeru zochokera kwa Mulungu. Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene anthu amapezera golide kenako tione zimene tikuphunzirapo.

MUNTHU AMAYAMBA NDI KUPEZA KACHIDUTSWA

Tiyerekeze kuti mukuyenda m’mbali mwa mtsinje ndipo mwaona kenakake kakunyezimira. Ndiye mutawerama n’kutola mukupeza kuti ndi kamwala ka golide. Kamwalako n’kakang’ono ngati mutu wa machesi koma kosowa kuposa dayamondi. Kodi inuyo munganyamuke n’kumapita, kapena mungafufuze kuti muone ngati pali miyala ina?

Mwina umu ndi mmene zinalili munthu wa Mboni za Yehova atabwera kudzakuuzani uthenga wa m’Baibulo. N’kutheka kuti mutadziwa dzina la Mulungu kapena mfundo ina munamva ngati mwapeza kachidutswa ka golide. (Sal. 83:18) Nanga munamva bwanji mutazindikira kuti Yehova akhoza kukhala mnzanu? (Yak. 2:23) Mwina munaoneratu kuti mwapeza chuma chamtengo wapatali kuposa golide ndipo munkafunitsitsa kudziwa zambiri.

KENAKO AMAPEZANSO GOLIDE WINA

Nthawi zambiri tizidutswa ta golide timapezeka tambiri m’makhwawa ndi m’mitsinje. Munthu akachita khama amatha kupeza golide wambirimbiri m’malo ngati amenewa.

N’kutheka kuti mutayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni munkamva ngati mwayamba kupeza golide. Mwina kuganizira malemba amene mwaphunzira kunakuthandizani kuti mudziwe zambiri komanso kuti muzikonda zinthu zauzimu. Kuganizira mfundo zomwe mwaphunzira m’Baibulo kunakuthandizani kudziwa zimene mungachite kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova. Munadziwanso zoyenera kuchita kuti iye azikukondani komanso kuti mudzapeze moyo wosatha.—Yak. 4:8; Yuda 20, 21.

Kodi mumachita khama kuphunzira Baibulo ngati mmene anthu amachitira pofufuza golide?

Mofanana ndi zimene anthu amachita kuti apeze golide wambiri, muyenera kuti munachita  khama kuti mudziwe mfundo zambiri za m’Malemba. Mutaphunzira zambiri, munadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa.—Mat. 28:19, 20.

PITIRIZANI KUFUNAFUNA

Nthawi zina munthu amaona kuti tizidutswa ta golide tili m’kati mwa miyala. Mwina poyamba tizidutswati sitingaoneke bwinobwino chifukwa timakhala tating’onoting’ono. Koma munthuyo amalolera kuswa mwala n’cholinga choti apeze golideyo ngakhale mwalawo utakhala waukulu.

Munthu akadziwa “chiphunzitso choyambirira cha Khristu” amafunika kuchitabe khama. Izi zimathandiza kuti adziwe zambiri komanso aone mmene angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wake. (Aheb. 6:1, 2) Ndiye kodi mungatani kuti muzipindulabe ndi kuphunzira Baibulo ngakhale kuti mwaliphunzira kwa zaka zambiri?

Muzikhala ndi cholinga chophunzira mfundo zatsopano. Kuti izi zitheke, muzifufuza mfundo zina zokhudza nkhaniyo. Mukapitiriza kuphunzira mwakhama, mudzapeza malangizo komanso nzeru zochokera kwa Mulungu. (Aroma 11:33) Komanso muzigwiritsa ntchito zinthu zofufuzira zimene zikupezeka m’chilankhulo chanu. Muzifufuza moleza mtima mayankho a mafunso amene muli nawo komanso mfundo zimene zingakuthandizeni. Mukhozanso kufunsa Akhristu anzanu malemba ndi nkhani zimene akuona kuti n’zothandiza. Mungachitenso bwino kumauza ena mfundo zosangalatsa zimene mwaphunzira m’Mawu a Mulungu.

Komabe cholinga chanu chisakhale kungofuna kudziwa zambiri. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti “kudziwa zinthu kumachititsa munthu kudzitukumula.” (1 Akor. 8:1) Choncho muziyesetsa kukhalabe odzichepetsa komanso kulimbitsa chikhulupiriro chanu. Kulambira kwa pabanja komanso kuphunzira Baibulo panokha kungakuthandizeni kuti muzitsatira mfundo za Yehova ndiponso kuti muzithandiza ena. Chofunika kwambiri n’chakuti mudzasangalala chifukwa chodziwa kuti mwapeza chuma chamtengo wapatali kuposa golide.—Miy. 3:13, 14.