Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Musaiwale Kuchereza Alendo”

“Musaiwale Kuchereza Alendo”

“Musaiwale kuchereza alendo.”—AHEB. 13:2.

NYIMBO: 124, 79

1, 2. (a) Kodi anthu amakumana ndi mavuto ati akasamukira kudera lina? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) Kodi mtumwi Paulo anapereka malangizo ati, nanga tikambirana mafunso ati?

ZAKA 30 zapitazo, mnyamata wina dzina lake Osei [1] anasamuka ku Ghana n’kupita ku Europe. Pa nthawiyo iye sanali Mboni ndipo anati: “Pasanapite nthawi yaitali, ndinazindikira kuti anthu a kumeneku analibe nane ntchito. Nyengo yake inalinso yozizira koopsa moti nditangofika ndinayamba kulira.” Osei sankadziwanso chilankhulo cha kumeneko moti anakhala chaka chathunthu asanapeze ntchito yabwino. Popeza anali kutali ndi kwawo, ankawasowa achibale ake komanso anzake.

2 Kodi mukanakhala inuyo mukanafuna kuti anthu akuchitireni zotani? Mwina mukanasangalala atakulandirani bwino ku Nyumba ya Ufumu mosaganizira kumene mukuchokera kapena mtundu wanu. Paja Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti: “Musaiwale kuchereza alendo.” (Aheb. 13:2) Pa nthawi ino, tiyeni tikambirane mafunso awa: Kodi Yehova amaona bwanji anthu a mitundu ina? N’chifukwa chiyani tiyenera kusintha mmene timaonera  anthu a mitundu ina? Nanga tingathandize bwanji kuti alendo azimasuka mumpingo wathu?

MMENE YEHOVA AMAONERA ANTHU A MITUNDU INA

3, 4. Malinga ndi Ekisodo 23:9, kodi Aisiraeli ankayenera kuchita bwanji ndi anthu a mitundu ina ndipo n’chifukwa chiyani?

3 Yehova atapulumutsa anthu ake kuchoka ku Iguputo, anawapatsa malamulo ndipo ena mwa malamulowo ankawalimbikitsa kukomera mtima anthu amene sanali Aisiraeli. (Eks. 12:38, 49; 22:21) Popeza nthawi zambiri anthu a mitundu ina ankavutika, Yehova anapereka malamulo othandiza anthu amenewa. Limodzi mwa malamulowo linali lowalola kuti azikunkha zotsala m’minda.—Lev. 19:9, 10.

4 M’malo mongouza Aisiraeli kuti azilemekeza anthu a mitundu ina, Yehova anawauza kuti aziganizira mmene anthuwo akumvera. (Werengani Ekisodo 23:9.) Aisiraeli ankadziwa ‘mmene zimakhalira munthu akakhala mlendo.’ Ngakhale pa nthawi imene sanali akapolo, Aiguputo ankawasalabe chifukwa chosiyana mitundu komanso chipembedzo. (Gen. 43:32; 46:34; Eks. 1:11-14) Aisiraeli anavutika kwambiri pamene anali alendo komabe Yehova ankafuna kuti iwo aziona anthu a mitundu ina okhala pakati pawo “ngati mbadwa” za m’dzikolo.—Lev. 19:33, 34.

5. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tiziganizira anthu ochokera m’mayiko ena ngati mmene Yehova amachitira?

5 Masiku anonso Yehova amaganizira anthu a mitundu ina amene timasonkhana nawo m’mipingo yathu. (Deut. 10:17-19; Mal. 3:5, 6) Tikamaganizira mavuto amene akukumana nawo, monga kusalidwa komanso kusadziwa chinenero, tingapeze njira zowathandizira.—1 Pet. 3:8.

TIYENERA KUSINTHA MMENE TIMAONERA ANTHU A MITUNDU INA

6, 7. N’chiyani chikusonyeza kuti nthawi ya atumwi, Akhristu anasintha maganizo a tsankho?

6 M’nthawi ya atumwi, Ayuda anayesetsa kusintha mtima wa tsankho umene anali nawo. Mwachitsanzo, pa Pentekosite mu 33 C.E., Akhristu a ku Yerusalemu analandira Akhristu atsopano ochokera m’mayiko osiyanasiyana. (Mac. 2:5, 44-47) Zimene anachitazi zinasonyeza kuti ankamvetsa tanthauzo la mawu oti “kuchereza” omwe amatanthauza kulandira alendo mokoma mtima.

7 Mpingo wachikhristu utayamba kukula, panabuka nkhani ina yokhudza tsankho. Ayuda olankhula Chigiriki ankadandaula kuti akazi amasiye achigiriki akunyalanyazidwa pogawa chakudya. (Mac. 6:1) Pofuna kuthetsa nkhaniyi, atumwi anasankha amuna 7 kuti athandize pogawa chakudyacho mosakondera. Amuna 7 onsewo anali ndi mayina achigiriki ndipo izi zikusonyeza kuti atumwiwo ankafuna kuthetseratu nkhani yoti Akhristu a mtundu wina akusalidwa.—Mac. 6:2-6.

8, 9. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasonyeze kuti tili ndi tsankho? (b) Malinga ndi 1 Petulo 1:22, kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

8 Anthufe nthawi zonse timatengera chikhalidwe cha kumene takulira. (Aroma 12:2) Ndipo timamva anzathu kunyumba, kuntchito kapena kusukulu akunyoza anthu a mtundu wina. Kodi inuyo mumamva bwanji anthu akamanena zimenezi? Nanga mumamva bwanji munthu wina akamanyoza mtundu wanu kapena chikhalidwe chanu?

 9 Poyamba, mtumwi Petulo sankakonda anthu a mitundu ina koma kenako anasintha n’kuchotseratu maganizo amenewa mumtima mwake. (Mac. 10:28, 34, 35; Agal. 2:11-14) Ifenso tikazindikira kuti tili ndi kamtima ka tsankho kapena konyadira mtundu wathu, tiyenera kuyesetsa kukachotsa. (Werengani 1 Petulo 1:22.) Kaya ndife a mtundu uti, tizikumbukira kuti tonsefe ndi ochimwa ndipo tinali osayenera kupulumuka. (Aroma 3:9, 10, 21-24) Ndiye ngati zili choncho, kodi pali chifukwa choganizira kuti timaposa anzathu? (1 Akor. 4:7) Tiyenera kukhala ndi maganizo amene mtumwi Paulo anali nawo. Paja iye anauza anzake odzozedwa kuti iwo sanalinso ‘anthu osadziwika kapena alendo m’dziko la eni, koma a m’banja la Mulungu.’ (Aef. 2:19) Tikamayesetsa kuthetsa maganizo a tsankho, tidzatha kuvala umunthu watsopano.—Akol. 3:10, 11.

KODI TINGASONYEZE BWANJI KUKOMA MTIMA?

10, 11. Kodi Boazi anatsanzira bwanji Yehova pochita zinthu ndi Rute?

10 Boazi ankatsanzira Yehova pochita zinthu ndi anthu a mitundu ina. Mwachitsanzo, atapita kumunda kukayendera antchito ake okolola, anaona mkazi wa ku Mowabu dzina lake Rute akukunkha m’mundamo. Kenako anamva kuti iye anachita kupempha kuti azikunkha nawo ngakhale kuti anali ndi ufulu wochita zimenezo. Boazi anamulola kuti azikunkha komanso azitengako mitolo ina ya balere.—Werengani Rute 2:5-7, 15, 16.

11 Zimene Boazi anauza Rute zikusonyeza kuti ankaganizira mavuto amene ankakumana nawo chifukwa chokhala m’dziko lachilendo. Iye anamuuza kuti azikhala limodzi ndi atsikana ake antchito n’cholinga choti asavutitsidwe ndi aliyense. Anamuuzanso kuti azidya nawo chakudya komanso kumwa madzi. Iye ankamulankhula mwaulemu komanso anamulimbikitsa.—Rute 2:8-10, 13, 14.

12. Kodi chingachitike n’chiyani tikamakomera mtima anthu a mitundu ina?

12 Boazi anachita chidwi atadziwa kuti Rute anakomera mtima Naomi komanso anayamba kulambira Yehova. Apa zinali ngati Rute wathawira ‘m’mapiko a Yehova’ ndipo Yehovayo anagwiritsa ntchito Boazi pofuna kuti amuthandize. (Rute 2:12, 20; Miy. 19:17) Nafenso tikamakomera mtima anthu a mtundu uliwonse timawathandiza kuzindikira kuti Yehova amawakonda.—1 Tim. 2:3, 4.

Tizipereka moni mwansangala kwa alendo pa Nyumba ya Ufumu (Onani ndime 13 ndi 14)

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kupereka moni kwa alendo ku Nyumba ya Ufumu? (b) Kodi mungatani ngati mumachita manyazi kulankhula ndi anthu a mitundu ina?

13 Ifenso tingasonyeze kukoma mtima tikamayesetsa kupereka moni kwa alendo ku Nyumba ya Ufumu. Inunso mukudziwa kuti nthawi zina alendo amachita manyazi ndipo amangokhala paokha. Zinthu zimene anthu ena amakumana nazo zimawachititsa kuganiza kuti mtundu wawo ndi wosanunkha kanthu poyerekezera ndi mitundu ina. Choncho tiyenera kuyesetsa kuwalandira mwansangala komanso mokoma mtima. Ngati n’zotheka, mungwiritse ntchito pulogalamu ya JW Chinenero kuti muphunzire moni wa zinenero zosiyanasiyana.—Werengani Afilipi 2:3, 4.

14 Mwina inuyo mumachita manyazi kulankhula ndi anthu a mitundu ina. Ngati ndi choncho, poyambira pabwino n’kungowafotokozera zinthu zina zokhudza inuyo. Mudzadabwa  kuona kuti mukufanana nawo pa zinthu zambiri ndipo mudzazindikira kuti chikhalidwe chilichonse chili ndi ubwino komanso kuipa kwake.

MUZIWATHANDIZA KUTI AZIMASUKA

15. N’chiyani chingatithandize kuti tiziwamvetsa anthu amene akuyesetsa kusintha kuti azolowere moyo wa m’dziko lina?

15 Kuti tithandize alendo kukhala omasuka, tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikanakhala m’dziko lachilendo, ndikanafuna kuti anthu andichitire zotani?’ (Mat. 7:12) Muzikhala oleza mtima ndi anthu amene akuvutikabe kuzolowera moyo watsopano. Poyamba tingamavutike kumvetsa maganizo ndiponso zochita za anthu achilendowo. M’malo moyembekezera kuti iwo asinthe tiyenera kungololera kuti azichita zinthu mogwirizana ndi chikhalidwe chawo.—Werengani Aroma 15:7.

16, 17. (a) Kodi tingatani kuti tiwadziwe bwino anthu ochokera m’mayiko ena? (b) Kodi tingathandize bwanji alendo amene afika mumpingo wathu?

16 Tikadziwa zinthu zina zokhudza chikhalidwe cha alendowo komanso kumene anachokera, tikhoza kupeza zolankhula pocheza nawo. Mwina pa nthawi ya kulambira kwa pabanja tingafufuze za anthu achilendo mumpingo wathu kapena m’gawo lathu. Kuwaitana kuti adzadye nafe chakudya kumathandizanso kuti tizigwirizana nawo. Popeza Yehova “anatsegulira anthu a mitundu ina khomo lolowera m’chikhulupiriro,” nafenso tiyenera kuitanira kunyumba kwathu “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro.”—Mac. 14:27; Agal. 6:10; Yobu 31:32.

Kodi timakomera mtima anthu ochokera m’mayiko ena? (Onani ndime 16 ndi 17)

17 Kupeza mpata wocheza ndi anthu achilendo kungatithandize kudziwa zinthu zambiri zimene asintha kuti azolowere moyo watsopano. Tikhoza kuzindikiranso kuti akufunika  kuwathandiza kuphunzira chinenero chathu. Tingawathandizenso kukumana ndi anthu amene angawapezere nyumba yabwino kapena ntchito. Akhristu achilendo angayamikire kwambiri ngati mutawachitira zinthu ngati zimenezi.—Miy. 3:27.

18. Kodi anthu ochokera kumayiko ena angatsanzire bwanji Rute?

18 Koma nawonso alendowo ayenera kuyesetsa kusintha zinthu zina kuti azolowere chikhalidwe chatsopano. Rute anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Choyamba, iye anasonyeza kuti ankalemekeza chikhalidwe cha anthu a kumene anasamukira popempha kuti akunkhe nawo. (Rute 2:7) Sanaganize kuti anthu ayenera kumulola kukunkha chifukwa choti ndi ufulu wake. Chachiwiri, iye anayamikira chifundo chimene anasonyezedwa. (Rute 2:13) Anthu achilendo akamachita zimenezi amalemekezedwa kwambiri ndi Akhristu anzawo komanso anthu ena.

19. N’chifukwa chiyani tiyenera kulandira bwino alendo?

19 Yehova ndi wokoma mtima kwambiri ndipo walola anthu a mitundu yosiyanasiyana kuti amve uthenga wabwino. Ena mwa anthuwa akanakhalabe m’dziko lawo sakanaphunzira Baibulo kapena kupezeka pa misonkhano yathu. Choncho akafika pa misonkhano tiyenera kuyesetsa kuwathandiza kuti azimasuka. Tikamawasonyeza kukoma mtima, ngakhale kuti tilibe zinthu zambiri, tidzawathandiza kudziwa kuti Yehova amawakonda. Tiyeni tipitirize ‘kutsanzira Mulungu’ ndipo tizilandira bwino alendo.—Aef. 5:1, 2.

^ [1] (ndime 1) Dzina lasinthidwa.