NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) February 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira April 3 mpaka 30, 2017.

Cholinga cha Yehova Chidzakwaniritsidwa

Kodi cholinga cha Mulungu chokhudza anthu ndi dzikoli chinali chotani? N’chiyani chinalakwika? Nanga n’chifukwa chiyani tingati dipo la Yesu limathandiza kuti cholingacho chidzakwaniritsidwe?

Dipo ndi ‘Mphatso Yangwiro’ Yochokera kwa Atate

Dipo lidzathandiza kuti anthu adzapeze madalitso ambiri koma linathandizanso pa nkhani zokhudza chilengedwe chonse.

MBIRI YA MOYO WANGA

Mulungu Anatisonyeza Kukoma Mtima Kwakukulu M’njira Zambiri

A Douglas Guest ndi akazi amaona kuti Mulungu anawasonyeza kukoma mtima kwakukulu pamene anali apainiya ku Canada komanso amishonale ku Brazil ndi ku Portugal.

Yehova Amatsogolera Anthu Ake

Kale Mulungu agwiritsa ntchito anthu potsogolera anthu ake. N’chiyani chikusonyeza kuti iye ankatsogolera anthu ake pogwiritsa ntchito anthuwo?

Kodi Ndi Ndani Akutsogolera Anthu a Mulungu Masiku Ano?

Yesu analonjeza kuti adzakhala ndi Akhristu mpaka mapeto. Kodi iye akutsogolera bwanji anthu ake masiku ano?

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mtumwi Paulo analemba kuti Mulungu “sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire.” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti amaganizira kaye zimene tingapirire n’kusankha mayesero oti tikumane nawo?

KALE LATHU

‘Kungatalike Bwanji Ndipo Msewu Ungaipe Bwanji Ankafikako’

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1920 ndi kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1930, apainiya akhama anayesetsa kulalikira kumadera akumidzi a ku Australia.