NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) June 2018

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa August 6 mpaka pa September 2, 2018.

“Ufumu Wanga Suli Mbali ya Dziko Lino”

Kodi zimene Yesu ankachita popewa kukhala kumbali inayake pa nkhani zandale zingatithandize bwanji masiku ano?

Tonsefe Tikhale Ogwirizana Ngati Yehova ndi Yesu

Kodi tingalimbikitse bwanji mgwirizano m’gulu la Mulungu?

Akanatha Kusangalatsa Mulungu

Chitsanzo cha Mfumu Rehobowamu chingatithandize kudziwa zimene Mulungu amafuna kuti tizichita.

Muziphunzitsa Chikumbumtima Chanu ndi Malamulo Komanso Mfundo za Mulungu

Yehova anatipatsa chikumbumtima koma kuti tiyenera kuchiphunzitsa kuti chizititsogolera bwino.

“Onetsani Kuwala Kwanu” Kuti Yehova Alemekezeke

Pamafunika kuchita zambiri osati kungolalikira uthenga wabwino basi.

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndakhala Ndikulimbikitsidwa pa Mavuto Anga Onse

Edward Bazely anakumana ndi mavuto a m’banja, okhudza kulambira, anakhumudwapo komanso anadwala matenda amaganizo.

Kupatsana Moni N’kothandiza Kwambiri

Ngakhale moni wachidule angathandize kwambiri.

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mungayankhe mafunso awa amene akuchokera m’magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda?