Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Limba Mtima Ndipo Ugwire Ntchitoyi’

‘Limba Mtima Ndipo Ugwire Ntchitoyi’

“Limba mtima, ugwire ntchitoyi mwamphamvu. Usaope kapena kuchita mantha chifukwa Yehova . . . ali ndi iwe.”​—1 MBIRI 28:20.

NYIMBO: 60, 29

1, 2. (a) Kodi Solomo anapatsidwa ntchito yofunika iti? (b) N’chifukwa chiyani Davide ankadera nkhawa kuti Solomo sangakwanitse ntchitoyi?

SOLOMO anauzidwa kuti ayang’anire ntchito yaikulu kwambiri yomanga kachisi ku Yerusalemu. Iye anauzidwa kuti nyumbayo iyenera kudzakhala “yokongola, yaulemerero wosaneneka ndiponso yotchuka ndi yotamandika kumayiko onse.” Koma chofunika kwambiri chinali chakuti kachisiyo anali “nyumba ya Yehova Mulungu woona.” Yehova ndi amene anasankha Solomo kuti ayang’anire ntchitoyi.​—1 Mbiri 22:1, 5, 9-11.

2 Davide ankadziwa kuti Mulungu adzathandiza pa ntchitoyi koma ankaona kuti Solomo anali wamng’ono komanso wosadziwa zambiri. Kodi Solomo akanatha kulimba mtima kuti agwire ntchitoyi? Kapena kodi akanalephera kuigwira chifukwa choti anali wamng’ono? Kuti zinthu ziyende bwino, Solomo anafunika kulimba mtima n’kugwira ntchitoyo.

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Solomo anaphunzira zambiri kwa bambo ake pa nkhani yolimba mtima?

3 Solomo ayenera kuti anaphunzira zambiri kwa bambo ake pa nkhani yolimba mtima. Paja Davide ali mwana analimbana ndi zilombo  zolusa n’kupulumutsa nkhosa za bambo ake. (1 Sam. 17:34, 35) Anasonyezanso kulimba mtima pokamenyana ndi Goliati yemwe anali chimphona chodziwa nkhondo. Mulungu anathandiza Davide moti anapha Goliati pogwiritsa ntchito mwala umodzi wokha.​—1 Sam. 17:45, 49, 50.

4. N’chifukwa chiyani Solomo anafunika kulimba mtima?

4 M’pomveka kuti Davide anauza Solomo kuti alimbe mtima n’kumanga kachisi. (Werengani 1 Mbiri 28:20.) Solomo anafunikadi kulimba mtima chifukwa kupanda kutero akanachita mantha ndipo sakanayamba kugwira ntchitoyi. Zimenezi zikanakhala zoipa kwambiri kusiyana ndi kuyamba ntchitoyo n’kuilephera.

5. N’chifukwa chiyani nafenso tiyenera kukhala olimba mtima?

5 Ifenso timafunika kuthandizidwa ndi Yehova kuti tilimbe mtima n’kumaliza ntchito yathu. Tiyeni tsopano tione zimene tingaphunzire kwa anthu ena amene anali olimba mtima. Kenako tiona mmene tingasonyezere kulimba mtima n’kumaliza ntchito yathu.

ZITSANZO ZA ANTHU AMENE ANALIMBA MTIMA

6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yosefe anali wolimba mtima?

6 Chitsanzo choyamba ndi cha Yosefe. Iye anasonyeza kulimba mtima pamene mkazi wa Potifara ankamunyengerera kuti agone naye. Yosefe ayenera kuti ankadziwa kuti akakana zinthu sizingamuyendere bwino. Ngakhale zinali choncho, iye analimba mtima ndipo anakana.​—Gen. 39:10, 12.

7. Kodi Rahabi anasonyeza bwanji kulimba mtima? (Onani chithunzi choyambirira.)

7 Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi Rahabi. Iye sanachite mantha pamene Aisiraeli ena anabwera kudzazonda mzinda wa Yeriko. Chifukwa chakuti Rahabi anadalira Yehova, iye analimba mtima n’kubisa Aisiraeliwo m’nyumba yake ndipo kenako anawathandiza kuti athawe. (Yos. 2:4, 5, 9, 12-16) Rahabi ankakhulupirira kuti Yehova ndi Mulungu woona ndipo ankadziwa kuti iye adzapereka dzikolo kwa Aisiraeli. Iye sanalole kuti kuopa anthu, ngakhale mfumu ya Yeriko ndi asilikali ake, kumulepheretse kuchita zinthu zoyenera. M’malomwake, anachita zinthu molimba mtima ndipo zimenezi zinathandiza kuti iyeyo komanso banja lake apulumuke.​—Yos. 6:22, 23.

8. Kodi chitsanzo cha Yesu chinathandiza bwanji atumwi?

8 Nawonso atumwi okhulupirika a Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iwo ankaona zimene Yesu ankachita posonyeza kulimba mtima. (Mat. 8:28-32; Yoh. 2:13-17; 18:3-5) Zimenezi zinawathandiza kuti nawonso akhale olimba mtima. Mwachitsanzo, pamene Asaduki ankawatsutsa, atumwiwo sanasiye kuphunzitsa za Yesu.​—Mac. 5:17, 18, 27-29.

9. Kodi lemba la 2 Timoteyo 1:7 limasonyeza kuti ndi ndani amene angatithandize kukhala olimba mtima?

9 Kulimba mtima kunathandiza Yosefe, Rahabi, Yesu ndiponso atumwi kuti achite zinthu zoyenera. Sikuti ankalimba mtima chifukwa chodzidalira koma chifukwa chodalira Yehova. Nafenso timafunika kulimba mtima pa nkhani zosiyanasiyana. Koma m’malo modzidalira, tiyenera kudalira Yehova. (Werengani 2 Timoteyo 1:7.) Tiyeni tsopano tikambirane mmene tingasonyezere kulimba mtima m’banja lathu komanso mumpingo.

KODI TIYENERA KUKHALA OLIMBA MTIMA PA NKHANI ZITI?

10. N’chifukwa chiyani achinyamata ayenera kukhala olimba mtima?

10 Achinyamata amafunika kulimba mtima pa nkhani zosiyanasiyana kuti azitumikira Yehova. Iwo akhoza kuphunzira zambiri pa nkhani ya Solomo. Paja iye analimba mtima n’kusankha zochita mwanzeru ndipo anamaliza ntchito yomanga kachisi. N’zoona kuti makolo ayenera kutsogolera achinyamata, koma achinyamatawo nawonso amafunika kusankha zochita.  (Miy. 27:11) Iwo amafunika kulimba mtima kuti asankhe bwino pa nkhani monga anthu ocheza nawo, zosangalatsa, kupewa makhalidwe oipa komanso kuti abatizidwe. Tikutero chifukwa choti Satana, yemwe amatonza Mulungu, safuna kuti achinyamata asankhe bwino pa nkhani zimenezi.

11, 12. (a) Kodi Mose anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima? (b) Kodi achinyamata angatsanzire bwanji Mose?

11 Achinyamata amafunika kusankha zoti achite pa moyo wawo ndipo nkhani imeneyi ndi yofunika kwambiri. M’mayiko ena, achinyamata amalimbikitsidwa kuti aphunzire kwambiri kuti adzapeze ntchito yapamwamba. Ndipo m’mayiko ena, mavuto azachuma amachititsa achinyamata kuona kuti ayenera kuyesetsa kupeza ndalama zothandizira achibale awo. Ngati ndinu wachinyamata ndipo mwakumana ndi zimenezi, muyenera kuganizira za Mose. Popeza analeredwa ndi mwana wa Farao, Mose akanatha kukhala ndi mtima wofuna kutchuka kapena kulemera. N’kuthekanso kuti anthu a m’banja lachifumu, aphunzitsi ake komanso alangizi ake ankamulimbikitsa kuchita zimenezi. Koma iye sanalole zimenezo ndipo analimba mtima n’kusankha kutumikira Yehova. Mose atachoka ku Iguputo, ankadalira Yehova. (Aheb. 11:24-26) Zimenezi zinachititsa kuti Yehova amudalitse ndipo adzamudalitsanso kwambiri m’tsogolomu.

12 Nawonso achinyamata amene amalimba mtima n’kusankha kuti aziika kutumikira Yehova pamalo oyamba adzadalitsidwa kwambiri. Iye adzawathandiza kupeza zofunika pa moyo wawo komanso wa achibale awo. Munthawi ya atumwi, wachinyamata wina dzina lake Timoteyo anasankha kuchita zimenezi ndipo umenewu ndi umboni wakuti nanunso mukhoza kukwanitsa. *​—Werengani Afilipi 2:19-22.

Kodi inuyo mumachita zinthu molimba mtima pa moyo wanu? (Onani ndime 13-17)

13. Kodi kulimba mtima kunathandiza bwanji mlongo wina kuti akwaniritse zolinga zake?

13 Mlongo wina wa ku Alabama m’dziko la United States anafunikanso kulimba mtima kuti akwaniritse zolinga zake. Iye analemba kuti: “Ndili mwana ndinali wamanyazi kwambiri. Zinkandivuta kulankhula ndi anthu ku Nyumba ya Ufumu ndipo sindinkayerekeza kugogoda pakhomo la anthu osawadziwa kuti ndiwalalikire.” Koma makolo ake komanso anthu ena mumpingo anamuthandiza kuti akwaniritse cholinga chake chokhala mpainiya wokhazikika. Mlongoyu anati: “Dziko la Satanali limatilimbikitsa kukhala ndi mtima wofuna kuphunzira kwambiri, kutchuka komanso kupeza chuma. Koma nthawi zambiri anthu amene amayesetsa kuti apeze zinthu zimenezi sazipeza ndipo sakhala osangalala. Koma kutumikira Yehova kwandithandiza kuti ndikhale wosangalala komanso ndiziona kuti ndikuchita zanzeru.”

14. Kodi makolo achikhristu amafunika kulimba mtima kuti achite zinthu ziti?

14 Makolo achikhristu amafunikanso kulimba mtima. Mwachitsanzo, abwana awo akhoza kuwapempha kuti azigwira ntchito nthawi imene iwo amakalalikira, kusonkhana kapena kuchita kulambira kwa pabanja. Makolowo amafunika kulimba mtima kuti akane zimenezi n’kupereka chitsanzo chabwino kwa ana awo. Nthawi zinanso, makolo ena mumpingo amalola ana awo kuchita zinthu zimene inuyo simungalole kuti ana anu achite. Mwina makolowo akhoza kufunsa chifukwa chimene ana anuwo sachitira zinthuzo. Zoterezi zikachitika, pamafunika kulimba mtima n’kuwafotokozera mwaulemu zifukwa zake.

15. Kodi lemba la Salimo 37:25 ndi Aheberi 13:5 lingathandize bwanji makolo kukhala olimba mtima?

15 Pamafunika kulimba mtima kuti tithandize ana athu kuti asankhe kuchita zambiri potumikira Yehova. Mwachitsanzo, makolo ena amaopa kulimbikitsa ana awo kuti ayambe upainiya, apite kukatumikira kumene kukufunika ofalitsa ambiri, akatumikire ku Beteli kapena akagwire  nawo ntchito zomanga Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano. Mwina amaona kuti anawo akachita zimenezi sadzakwanitsa kuwasamalira akadzakalamba. Koma makolo anzeru amakhala olimba mtima n’kumakhulupirira zimene Yehova walonjeza. (Werengani Salimo 37:25; Aheberi 13:5.) Makolo amene amalimba mtima n’kumadalira Yehova amathandiza ana awo kuti azichitanso zomwezo.​—1 Sam. 1:27, 28; 2 Tim. 3:14, 15.

16. Kodi makolo ena athandiza bwanji ana awo kukhala ndi zolinga zabwino, nanga zimenezi zathandiza bwanji anawo?

16 Banja lina la ku United States linathandiza ana awo kuti akhale ndi cholinga chotumikira Yehova. Bambo a m’banjali anati: “Ana athu asanayambe n’komwe kuyenda ndi kulankhula, tinayamba kuwauza ubwino wochita upainiya komanso kutumikira mumpingo. Panopa ana athu akufunitsitsa kuchita zimenezi. Zolinga za ana athuwa zawathandiza kuti asakopeke ndi zinthu za m’dziko la Satanali koma aziganizira kwambiri zimene angachite potumikira Yehova.” M’bale wina amene ali ndi ana awiri anati: “Makolo ambiri amachita khama komanso amawononga ndalama zambiri pothandiza ana awo kuti azichita bwino pa masewera enaake kapena pa maphunziro. Koma chofunika kwambiri n’kuyesetsa kuthandiza ana athu kuti akhale ndi zolinga zimene zingawathandize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Timasangalala kwambiri kutumikira Yehova limodzi ndi ana athu komanso kuwaona akukwaniritsa zolinga zawo zabwino.” Dziwani kuti Yehova adzadalitsa makolo amene amathandiza ana awo kukhala ndi mtima wofuna kuchita zambiri pomutumikira.

TIZILIMBA MTIMA POCHITA ZINTHU MUMPINGO

17. Kodi tingafunike kulimba mtima kuti tichite zinthu ziti mumpingo?

17 Timafunikanso kusonyeza kulimba mtima mumpingo. Mwachitsanzo, akulu ayenera kulimba mtima kuti athandize anthu amene achita machimo akuluakulu komanso amene akudwala. Akulu ena amapita kundende kuti akaphunzire ndi anthu kapena kuchititsa misonkhano. Alongo osakwatiwa amafunikanso kulimba mtima kuti achite zambiri potumikira Yehova. Mwachitsanzo akhoza kuchita upainiya, kusamukira kudera limene kukufunika ofalitsa ambiri, kuthandiza nawo pa zomangamanga kapena kulowa  Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Alongo enanso amakhala ndi mwayi wopita ku Sukulu ya Giliyadi.

18. Kodi alongo achikulire angasonyeze bwanji kulimba mtima?

18 Alongo achikulire amathandizanso mumpingo ndipo timawakonda kwambiri. Mwina ena sangachite zambiri potumikira Mulungu ngati mmene ankachitira kale, koma akhoza kulimbabe mtima n’kumagwira nawo ntchito zina. (Werengani Tito 2:3-5.) Mwachitsanzo, mlongo angafunike kulimba mtima ngati wapemphedwa kuti alangize mlongo wachitsikana pa nkhani ya kavalidwe. Mlongoyu sayenera kudzudzula mlongo wachitsikanayo koma ayenera kumulimbikitsa kuti aziganizira mmene kavalidwe kake kangakhudzire anthu ena. (1 Tim. 2:9, 10) Alongo achikulire akamalimbikitsa ena mwachikondi amathandiza kwambiri mpingo.

19. (a) Kodi abale obatizidwa angasonyeze bwanji kulimba mtima? (b) Kodi lemba la Afilipi 2:13 ndi 4:13 lingathandize bwanji abale kuti akhale olimba mtima?

19 Nawonso abale obatizidwa amafunika kulimba mtima n’kumagwira nawo ntchito zapampingo. Abale amene amalimba mtima n’kumayesetsa kuti akhale atumiki othandiza kapena akulu, amathandiza kwambiri mpingo. (1 Tim. 3:1) Koma abale ena safuna kuchita zimenezi. Mwachitsanzo, m’bale amene anachita zinthu zolakwika m’mbuyomu akhoza kuganiza kuti si woyenerera kukhala mtumiki wothandiza kapena mkulu. Pomwe m’bale wina angaone kuti udindowu ndi waukulu kwambiri moti sangaukwanitse. Koma ngati muli ndi maganizo amenewa, Yehova angakuthandizeni kukhala olimba mtima. (Werengani Afilipi 2:13; 4:13.) Kumbukirani kuti Mose nayenso ankaona kuti sangakwanitse ntchito imene Yehova anamupatsa. (Eks. 3:11) Koma Yehova anamuthandiza ndipo Mose analimba mtima n’kugwira bwinobwino ntchitoyo. Kuti m’bale wobatizidwa akhale wolimba mtima ayenera kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku komanso kumapempha Mulungu kuti amuthandize. Kuganizira nkhani za anthu amene anasonyeza kulimba mtima kungamuthandizenso. Akhozanso kupempha akulu kuti azimuphunzitsa ntchito zosiyanasiyana mumpingo ndipo ayenera kukhala wokonzeka kuchita chilichonse chimene angamupemphe. Tikulimbikitsa abale obatizidwa onse kuti akhale olimba mtima n’kumagwira ntchito mwakhama kuti azithandiza mumpingo.

‘YEHOVA ALI NDI IWE’

20, 21. (a) Kodi Davide anauza Solomo chiyani? (b) Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?

20 Davide anauza Solomo kuti Yehova akhala naye mpaka ntchito yonse yomanga kachisiyo itatha. (1 Mbiri 28:20) Solomo ayenera kuti ankaganizira kwambiri mawu amenewa ndipo anamuthandiza kuti asamadziderere chifukwa choti anali wamng’ono komanso wosadziwa zambiri. Iye analimba mtima n’kuyamba ntchitoyo ndipo Yehova anamuthandiza kuti amalize kumanga kachisi wokongolayo m’zaka 7 ndi hafu zokha.

21 Yehova angatithandizenso kuti tizichita zinthu molimba mtima n’kukwaniritsa ntchito yathu m’banja komanso mumpingo. (Yes. 41:10, 13) Tisamakayikire kuti tikakhala olimba mtima polambira Yehova, iye adzatidalitsa panopa komanso m’tsogolo. Choncho tiyeni tonsefe ‘tikhale olimba mtima n’kumagwira ntchito’ zabwino.

^ ndime 12 Mfundo zina zothandiza kuti musankhe bwino zochita, mungazipeze mu nkhani yakuti “Khalani ndi Zolinga Zauzimu Kuti Mulemekeze Nazo Mlengi Wanu,” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2004.