NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) September 2017

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira October 23 mpaka November 26, 2017.

Tiziyesetsa Kukhala Odziletsa

Kodi zitsanzo za m’Baibulo zingatithandize bwanji kukhala odziletsa? N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kuyesetsa kukhala odziletsa?

Tizitsanzira Yehova pa Nkhani ya Chifundo

Pa nthawi ina, Yehova anauza Mose dzina lake komanso makhalidwe ake. Khalidwe lina limene anatchula ndi la chifundo. Kodi munthu wachifundo amatani nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira za khalidweli?

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndakhala ndi Mwayi Wotumikira Limodzi ndi Abale Okhulupirika

David Sinclair amasangalala akaganizira mwayi umene wakhala nawo wotumikira limodzi ndi abale ndi alongo okhulupirika kwa zaka 61 ku Beteli.

“Mawu a Mulungu Wathu Adzakhala Mpaka Kalekale”

Baibulo likupezekabe ngakhale kuti padutsa zaka zambiri kuchokera pamene linalembedwa. Izi zachitika ngakhale kuti pakhala kusintha kwa zilankhulo ndi olamulira komanso anthu ena ankaletsa kulimasulira.

‘Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu’

Anthu ambiri asintha moyo wawo chifukwa chophunzira Mawu a Mulungu. Kodi tingatani kuti Mawu a Mulungu azitithandiza?

‘Limba Mtima Ndipo Ugwire Ntchitoyi’

N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala olimba mtima ndipo n’chiyani chingatithandize pa nkhaniyi?