Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Manja Anu ‘Asalefuke’

Manja Anu ‘Asalefuke’

“Usalefuke.”—ZEF. 3:16.

NYIMBO: 81, 32

1, 2. (a) Kodi anthu ambiri masiku ano akukumana ndi mavuto otani, nanga zotsatira zake zimakhala zotani? (b) Kodi Mulungu wapereka lonjezo liti pa Yesaya 41:10, 13?

MLONGO wina akuchita upainiya ndipo mwamuna wake ndi mkulu koma ananena kuti: “Ngakhale kuti timayesetsa kuchita zinthu zonse zokhudza kulambira, ndakhala ndikuvutika ndi nkhawa kwa zaka zambiri. Izi zimapangitsa kuti ndizisowa tulo, ndizidwaladwala komanso ndizilephera kucheza bwino ndi anzanga. Nthawi zina ndimalakalaka nditangosanduka nyerere n’kulowa pansi.”

2 Kodi inuyo munamvapo ngati mmene mlongoyu amamvera? M’dziko la Satanali, timapanikizika ndi zinthu zambiri ndipo timakhala ndi nkhawa. Timakhala ngati boti limene amangirirapo nangula moti silingayendenso. (Miy. 12:25) Koma kodi ndi zinthu ziti zimene zimatichititsa kukhala ndi nkhawa? Ndi zinthu monga imfa ya mnzathu kapena m’bale wathu, matenda, mavuto azachuma komanso kutsutsidwa. Zinthu zoterezi zingachititsenso kuti tizingokhala okhumudwa komanso tilefuke. Komabe tisamaiwale kuti Mulungu ndi wokonzeka kutithandiza.—Werengani Yesaya 41:10, 13.

3, 4. (a) Kodi Baibulo limagwiritsa ntchito bwanji mawu akuti “manja”? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingachititse kuti tifooke?

3 Baibulo limagwiritsa ntchito mbali zosiyanasiyana za thupi lathu pofotokoza zinthu zosiyanasiyananso. Mwachitsanzo  limagwiritsa ntchito dzanja m’njira zambirimbiri. Kulimbitsa manja a munthu kumatanthauza kumulimbikitsa, ngati mmene Yonatani analimbikitsira Davide. Kumatanthauzanso kuthandiza munthu kupezanso mphamvu. (1 Sam. 23:16; Ezara 1:6, Mawu am’munsi.) Kungatanthauzenso kukhala ndi chiyembekezo choti zinthu zikhala bwino m’tsogolo.

4 Nthawi zina, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti manja a lende potanthauza munthu amene wafooka, wataya mtima kapena akuganiza kuti zinthu sizidzakhalanso bwino. (2 Mbiri 15:7; Aheb. 12:12) Munthu wotereyu sachedwa kukhumudwa kapena kugwa ulesi. Kodi mungatani ngati zinthu zina zikukudetsani nkhawa kwambiri moti mwafooka ndipo nthawi zina simufuna kuchita zinthu zokhudza kulambira? Nanga mungatani kuti mupezenso mphamvu, mupirire komanso muzisangalala?

“DZANJA LA YEHOVA SILINAFUPIKE MOTI N’KULEPHERA KUPULUMUTSA”

5. (a) Tikakumana ndi mavuto, kodi tingatani? (b) Koma kodi tiyenera kukumbukira chiyani? (c) Kodi m’nkhaniyi tikambirana chiyani?

5 Werengani Zefaniya 3:16, 17. Tikakumana ndi mavuto tingachite mantha kapena kulefuka. Koma tiyenera ‘kumutulira nkhawa zathu zonse’ Yehova, yemwe ndi Atate wathu wachikondi. (1 Pet. 5:7) Paja iye anauza Aisiraeli kuti ‘dzanja lake silalifupi moti n’kulephera kupulumutsa’ atumiki ake okhulupirika. (Yes. 59:1) Tiyeni tikambirane zitsanzo zitatu za m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti Yehova amathandiza anthu ake, ngakhale mavuto awo ataoneka ngati aakulu. Ndiyeno muziganizira mmene zitsanzozi zingakuthandizireni.

6, 7. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitika kuti Aisiraeli agonjetse Aamaleki?

6 Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo, Aamaleki anabwera kudzamenyana nawo. Yoswa anatsatira malangizo a Mose ndipo anatsogolera asilikali achiisiraeli ku nkhondo. Koma Mose anatenga Aroni ndi Hura n’kupita paphiri ndipo ankatha kuona malo amene nkhondoyo inkachitikira. Kodi amuna atatuwa anachita izi pothawa kupita kunkhondoko? Ayi.

7 Mose anachita zinthu zimene zinathandiza Aisiraeli kuti apambane. Iye ananyamula ndodo ya Mulungu woona. Mose akakweza m’mwamba ndodoyo, Yehova ankawathandiza Aisiraeli kuti azigonjetsa Aamaleki. Koma manja ake akatopa n’kuyamba kugwa pansi, Aamaleki ankayamba kupambana. Aroni ndi Hura ataona zimenezi, nthawi yomweyo “anatenga mwala ndi kumuikira, ndipo anakhalapo.” Iwo “anachirikiza manja ake, wina mbali ina winanso mbali ina, moti manja ake anakhalabe choncho mpaka dzuwa kulowa.” Choncho Aisiraeli anapambana nkhondoyo chifukwa Mulungu anawathandiza ndi dzanja lake lamphamvu.—Eks. 17:8-13.

8. (a) Kodi Asa anatani Aitiyopiya ataopseza Ayuda? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Asa pa nkhani yodalira Mulungu?

8 M’nthawi ya Mfumu Asa, Yehova anasonyezanso kuti dzanja lake si lalifupi. Baibulo limatchula nkhondo zambiri zimene zinachitika kalelo. Koma limasonyeza kuti gulu la nkhondo limene linali ndi asilikali ambiri linali la Zera yemwe anali Mwitiyopiya. Iye anali ndi asilikali odziwa bwino kumenya nkhondo okwana 1 miliyoni. Chiwerengerochi chinali pafupifupi kuwirikiza kawiri chiwerengero cha asilikali achiisiraeli. Kungoona asilikaliwo, munthu akanaganiza kuti n’zosatheka kugonjetsa Aitiyopiya. Ndipo Asa akanatha kuda nkhawa, kuchita mantha komanso kuyamba kuganiza kuti basi chawo palibe. Koma iye anapempha Yehova kuti amuthandize. Paja “zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.” (Mat. 19:26) Yehova anasonyeza mphamvu zake ndipo  “anagonjetsa Aitiyopiyawo pamaso pa Asa” chifukwa choti ankamutumikira ndi “mtima wathunthu masiku ake onse.”—2 Mbiri 14:8-13; 1 Maf. 15:14.

9. (a) Kodi n’chiyani chinathandiza Nehemiya kuti amangenso makoma a Yerusalemu? (b) Kodi Mulungu anayankha bwanji pemphero la Nehemiya?

9 Nayenso Nehemiya atapita ku Yerusalemu anapeza zinthu zitasokonekera. Chitetezo cha mzindawo sichinali bwino ndipo Ayuda ena anali atagwa ulesi. Iwo ataopsezedwa ndi anthu a mitundu ina, anasiya kugwira ntchito yomanga mpanda wa Yerusalemu. Kodi izi zinafooketsanso Nehemiya? Ayi. Iye anachita zinthu mofanana ndi Mose, Asa komanso atumiki ena okhulupirika. Izi zinatheka chifukwa chakuti iye anali ndi chizolowezi chodalira Yehova ndipo n’zimenenso anachita pa nthawiyi. Nehemiya anapemphera kwa Yehova ndipo anawathandiza kuthana ndi vuto limene linkaoneka ngati losatheka. Mulungu anagwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu komanso ‘dzanja lake lamphamvu’ polimbitsa manja a Ayuda amene anafooka. (Werengani Nehemiya 1:10; 2:17-20; 6:9.) Kodi inuyo mumakhulupirira kuti Yehova amagwiritsa ntchito ‘mphamvu zake zazikulu’ komanso ‘dzanja lake lamphamvu’ polimbikitsa atumiki ake masiku ano?

YEHOVA ADZALIMBITSA MANJA ANU

10, 11. (a) Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira ziti pofuna kutilepheretsa kutumikira Mulungu? (b) Kodi Yehova amagwiritsa ntchito chiyani kuti atilimbikitse komanso kutipatsa mphamvu? (c) Kodi zimene timaphunzira zakuthandizani bwanji inuyo?

10 Tikudziwa kuti Mdyerekezi akuyesetsa kuchita zonse zimene angathe kuti atilepheretse kutumikira Mulungu. Iye amagwiritsa ntchito maboma, anthu ampatuko ndiponso atsogoleri azipembedzo kuti afalitse mabodza komanso kutiopseza. Iye amachita zonsezi pofuna kutigwetsa ulesi kuti tisamagwire mwakhama ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Koma Yehova amatithandiza pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera. (1 Mbiri 29:12) Choncho m’pofunika kuti tizipempha mzimuwu chifukwa ndi umene ungatithandize kulimbana ndi mavuto osiyanasiyana omwe Satana angatibweretsere. (Sal. 18:39; 1 Akor. 10:13) Tilinso ndi mwayi chifukwa tili ndi Mawu a Mulungu omwe anthu analemba mothandizidwa ndi mzimu woyera. Taganiziraninso za chakudya chauzimu chochokera m’Baibulo chimene timalandira mwezi uliwonse. Mawu a pa Zekariya 8:9, 13 (werengani) analankhulidwa pa nthawi imene kachisi wa ku Yerusalemu ankamangidwanso ndipo ndi othandizanso masiku ano.

11 Mulungu amatipatsanso mphamvu pogwiritsa ntchito zimene timaphunzira pa misonkhano yampingo, yadera, yachigawo komanso masukulu osiyanasiyana. Zimene timaphunzirazi zimatithandiza kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Mulungu. Zimatithandizanso kukhala ndi zolinga zauzimu komanso kuti tizitha kukwaniritsa maudindo athu. (Sal. 119:32) Kodi nanunso mumayesetsa kuti muzipeza mphamvu kuchokera pa zimene timaphunzira?

12. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale olimba mwauzimu?

12 Yehova anathandiza Aisiraeli kugonjetsa Aamaleki ndi Aitiyopiya komanso anapatsa mphamvu Nehemiya ndi anzake kuti amalize ntchito yawo. Iye angatithandizenso ifeyo kuti tizilalikirabe m’gawo lovuta ndiponso tisamafooke tikamatsutsidwa kapena tikakhala ndi nkhawa. (1 Pet. 5:10) Sitiyembekezera kuti Yehova azitichitira zozizwitsa. M’malomwake tiyenera kuchita khama pa zinthu monga kuwerenga Baibulo  tsiku ndi tsiku komanso kukonzekera ndi kupezeka pamisonkhano mlungu uliwonse. Tiziphunziranso Baibulo patokha, kuchita kulambira kwa pabanja ndiponso kupemphera nthawi zonse. Tisamalole chilichonse kutilepheretsa kuchita zinthu zimene Yehova amagwiritsa ntchito potilimbikitsa komanso kutipatsa mphamvu. Ngati mukuona kuti simukuchita bwino pambali zina zimene tatchulazi, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Mukatero, mzimu wa Mulungu ‘udzalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.’ (Afil. 2:13) Koma kodi tingatani kuti nafenso tizilimbitsa manja a Akhristu anzathu?

TIZILIMBITSA MANJA A AKHRISTU ANZATHU

13, 14. (a) Kodi m’bale wina analimbikitsidwa bwanji mkazi wake atamwalira? (b) Kodi ifeyo tingalimbikitse bwanji anthu ena?

13 Yehova watipatsa abale padziko lonse amene angatilimbikitse. Paja mtumwi Paulo analemba kuti: “Limbitsani manja amene ali lende ndi mawondo olobodoka, ndipo pitirizani kuwongola njira zimene mapazi anu akuyendamo.” (Aheb. 12:12, 13) M’nthawi ya atumwi, Akhristu ambiri ankalimbikitsidwa ndi anzawo. N’chimodzimodzinso masiku ano. Mwachitsanzo, mkazi wa m’bale wina atamwalira, m’baleyo anakumananso ndi mavuto ena. Koma iye anati: “Ndazindikira kuti sitingasankhe mayesero oti tikumane nawo, nthawi yoti afike komanso kuti afike kangati. Nthawi zambiri ndimamva ngati ndili m’madzi koma kupemphera ndi kuphunzira Baibulo pandekha kumandithandiza kuti ndisamire. Komanso abale ndi alongo amandithandiza ndiponso kundilimbikitsa kwambiri. Ndazindikiranso kuti tiyenera kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova mavuto aakulu asanatigwere.”

Aliyense mumpingo angathe kulimbikitsa ena (Onani ndime 14)

14 Pa nthawi imene Aisiraeli ankamenyana ndi Aamaleki, Aroni ndi Hura anathandiza Mose kuti manja ake asagwe. Nafenso tiyenera kuyesetsa kuthandiza Akhristu amene akuvutika. Mwachitsanzo, tingathandize okalamba ndi odwala. Tingathandizenso amene akutsutsidwa ndi abale awo, akusowa ocheza nawo komanso omwe aferedwa. Ndi bwinonso kulimbikitsa achinyamata amene amakakamizidwa kuti achite zoipa, apeze chuma chambiri kapena aphunzire kwambiri n’cholinga choti adzapeze ntchito yapamwamba. (1 Ates. 3:1-3; 5:11, 14) Tiziyesetsanso kulimbikitsa anthu nthawi zonse kaya ndi ku Nyumba ya Ufumu, mu utumiki, tikamadya nawo kapena tikamacheza nawo pafoni.

15. Kodi mawu athu angalimbikitse bwanji Akhristu anzathu?

15 Asa atapambana pa nkhondo, mneneri Azariya anapita kukamulimbikitsa iyeyo limodzi ndi anthu ake. Ananena kuti: “Koma inuyo khalani olimba mtima ndipo musagwe ulesi, [kapena kuti manja anu asalefuke] pakuti mudzapeza mphoto chifukwa cha ntchito yanu.” (2 Mbiri 15:7) Izi zinalimbikitsa Asa kusintha zinthu zambiri n’cholinga choti anthu ayambirenso kulambira Yehova. Nafenso mawu athu akhoza kulimbikitsa anthu ena kuti azichita zambiri potumikira Yehova. (Miy. 15:23) Tisaiwalenso kuti tikapereka ndemanga zabwino pamisonkhano timalimbikitsa kwambiri anthu ena.

16. (a) Kodi akulu angatsanzire bwanji Nehemiya polimbitsa manja a Akhristu mumpingo? (b) Kodi Akhristu ena anakuthandizani bwanji inuyo?

16 Yehova anathandiza Nehemiya ndi anzake kuti alimbitse manja awo n’kumaliza ntchito yomanga mpanda wa Yerusalemu. Ntchitoyi inatha patangodutsa masiku 52 okha. (Neh. 2:18; 6:15, 16) Sikuti Nehemiya ankangoyang’anira ntchitoyi koma nayenso  ankagwira nawo. (Neh. 5:16) Masiku anonso, akulu ambiri amatsanzira Nehemiya pogwira nawo ntchito zomanga kapena kuyeretsa Nyumba za Ufumu. Iwo amalimbitsanso manja a anthu ofooka poyenda nawo mu utumiki komanso kuchita maulendo aubusa.—Werengani Yesaya 35:3, 4.

MANJA ANU ‘ASALEFUKE’

17, 18. Tikakhala ndi nkhawa kapena tikakumana ndi mavuto, kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?

17 Tikamatumikira limodzi ndi abale ndi alongo athu, timakhala ogwirizana. Zimathandizanso kuti tizikondana kwambiri komanso kuti tiziyembekezera madalitso amene tidzapeze mu Ufumu wa Mulungu. Tikamayesetsa kulimbitsa manja awo, timawathandiza kuti asafooke komanso kuti azikhulupirira zoti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Izi zimathandiza kuti nafenso tizikonda zinthu zauzimu komanso tizikhulupirira kwambiri kuti Mulungu adzakwaniritsa malonjezo ake. Choncho tingati ifenso manja athu amalimba.

18 M’nkhaniyi takambirana kuti Yehova anathandiza atumiki ake okhulupirika atakumana ndi mavuto. Kuganizira zimenezi kungatithandize kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti tizimudalira kwambiri. Choncho mukakumana ndi mavuto, muzipemphera kwa Yehova ndipo musamalole kuti manja anu ‘alefuke.’ Komanso musamakayikire kuti iye adzakuthandizani ndi dzanja lake lamphamvu kuti mupirire n’kudzalandira madalitso mu Ufumu wake.—Sal. 73:23, 24.