Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?

Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?

“Chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.”—1 AKOR. 10:31.

NYIMBO: 34, 61

1, 2. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amayesetsa kuvala moyenera? (Onani chithunzi pamwambapa.)

MTOLANKHANI wa nyuzipepala ina anafotokoza mmene anthu anavalira pamsonkhano wina wa atsogoleri azipembedzo. Anati: “Ambiri anavala motayirira chifukwa kunkatentha.” Koma ponena za a Mboni, iye anati: “Pamsonkhano wa Mboni za Yehova. . . . Amuna amavala majekete ndi mataye pamene akazi amavala masiketi aatali bwino . . . komanso okongola.” A Mboni za Yehova nthawi zonse amayamikiridwa kuti ‘amadzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu ndi mwanzeru . . . mogwirizana ndi mmene akazi amene amati amalemekeza Mulungu amayenera kudzikongoletsera.’ (1 Tim. 2:9, 10) Palembali Paulo ankanena za akazi koma mfundo zake zikugwiranso ntchito kwa amuna.

2 Akhristufe timaona kuti kuvala zoyenera n’kofunika chifukwa ndi zimene Yehova Mulungu amene timamulambira amafuna. (Gen. 3:21) Zimene Malemba amanena pa nkhaniyi, zimasonyeza kuti Yehova amafuna kuti atumiki ake azivala mosiyana ndi anthu a m’dzikoli. Choncho pa nkhani ya zovala tisamangoganizira zimene zikutisangalatsa ifeyo. Tiziganiziranso zimene zingasangalatse Ambuye Wamkulu Koposa.

3. Kodi tingaphunzire chiyani pa Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli?

 3 Mwachitsanzo, m’Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli munali malamulo amene ankawateteza kuti asatengere makhalidwe oipa a anthu a mitundu ina. Chilamulo chinkasonyeza kuti Yehova sasangalala ndi zovala zimene anthu akavala, pamakhala povuta kusiyanitsa ngati munthuyo ndi wamkazi kapena wamwamuna. (Werengani Deuteronomo 22:5.) Malangizo amene Mulungu anapereka okhudza kavalidwe amasonyeza kuti iye sasangalalanso ndi masitayilo a zovala amene amapangitsa kuti amuna azioneka ngati akazi, akazi azioneka ngati amuna, kapena anthu asamathe kusiyanitsa pakati pa amuna ndi akazi.

4. Kodi n’chiyani chingathandize Akhristu kuti azisankha bwino pa nkhani ya zovala?

4 M’Baibulo muli mfundo zimene zingathandize Akhristu kuti azisankha bwino pa nkhani ya zovala. Mfundozi zimagwira ntchito mosatengera kumene munthu amakhala, chikhalidwe chake kapena nyengo ya kwawoko. Sitifunika mndandanda wa malamulo onena za zovala zoyenera ndi zosayenera. M’malomwake timatsatira mfundo za m’Malemba ndipo Mkhristu aliyense amasankha zimene angakonde, koma mogwirizana ndi mfundozo. Tiyeni tikambirane mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuzindikira “chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro” posankha zovala.—Aroma 12:1, 2.

‘TIZISONYEZA KUTI NDIFE ATUMIKI A MULUNGU’

5, 6. Kodi chingachitike n’chiyani tikamavala bwino?

5 Mtumwi Paulo anauziridwa kuti atsindike kufunika kwa mfundo ya pa 2 Akorinto 6:4. (Werengani.) Tizikumbukira kuti zovala zathu zimauza anthu kuti ndife otani. Anthu amatha kutiganizira zinthu zosiyanasiyana chifukwa cha mmene tikuonekera. (1  Sam. 16:7) Popeza timatumikira Mulungu, sitimangovala chilichonse chimene chatisangalatsa. Mfundo zimene timaphunzira m’Baibulo zimatithandiza kuti tizipewa kuvala zothina, zoonekera mkati kapena zochititsa anthu kuganiza zachiwerewere. Komanso si bwino kuvala zovala zimene zingaonetse kapena kudinda malo obisika. Zovala zathu zisamachititse anthu kuyang’ana kumbali.

6 Tikadzikongoletsa moyenera komanso kuvala zovala zaukhondo ndi zaulemu, anthu ambiri amazindikira kuti ndife atumiki a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Izi zingachititse kuti nawonso ayambe kulambira Mulungu. Komanso tikamavala bwino anthu amalankhula zabwino zokhudza gulu lathu. Zimenezi zingapangitsenso kuti anthu azimvetsera uthenga wathu.

7, 8. Ndi nthawi iti makamaka imene timayenera kuvala bwino?

7 Timalemekeza Mulungu wathu woyera, Akhristu anzathu komanso anthu amene timawalalikira. Choncho timayesetsa kuvala zovala zimene zingachititse kuti anthu alemekeze Yehova komanso zogwirizana ndi uthenga wathu. (Aroma 13:8-10) Timachita zimenezi makamaka tikamapita kukalalikira kapena kukasonkhana. Tiyenera kuvala ‘mogwirizana ndi mmene anthu amene amati amalemekeza Mulungu ayenera kuvalira.’ (1 Tim. 2:10) Komabe tikudziwa kuti zovala zimene zingakhale zoyenera pamalo ena, zingakhale zosayenera pamalo ena. Ndi bwinonso kuganizira chikhalidwe cha komwe tikukhala n’cholinga choti tisakhumudwitse ena.

Kodi Zovala zanu zimachititsa kuti anthu alemekeze Mulungu? (Onani ndime 7ndi 8)

 8 Werengani 1 Akorinto 10:31. Tikamapita kumsonkhano wadera kapena wachigawo, tiyenera kuvala zovala zabwino osati zotengera masitayilo oipa a m’dzikoli. Komanso ngati tikugonera komweko, tikamacheza madzulo kapena m’mawa nthawi ya msonkhano isanakwane, tiyenera kuvala bwino osati motayirira. N’chimodzimodzinso ngati tikugonera kuhotelo. Tikatero sitichita manyazi kuuza anthu kuti ndife a Mboni komanso timatha kulalikira mpata ukapezeka.

9, 10. Kodi mfundo ya palemba la Afilipi 2:4 ingatithandize bwanji posankha zovala?

9 Werengani Afilipi 2:4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mmene zovala zathu zingakhudzire Akhristu anzathu? Chifukwa chimodzi n’chakuti anthu a Mulungufe timayenera kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: ‘Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa ndi chilakolako cha kugonana.’ (Akol. 3:2, 5) Sitikufuna kuti Akhristu anzathu azivutika kutsatira malangizo amenewa chifukwa cha zimene timavala. Pali abale ndi alongo amene anasiya khalidwe lachiwerewere koma nthawi zina amalimbanabe ndi maganizo olakwika. (1 Akor. 6:9, 10) Choncho tiyenera kusamala kuti mavalidwe athu asapangitse kuti anthuwa azivutika kwambiri ndi maganizo olakwikawo.

10 Zovala zimene timavala, kaya ndi kumisonkhano, pocheza kapena pochita zinthu zina ndi Akhristu anzathu, zizikhala zoti zingathandize kuti mpingo ukhalebe woyera. N’zoona kuti aliyense ali ndi ufulu wosankha zovala zimene amakonda. Komabe  ndi udindo wathu kuvala zovala zimene zingathandize ena kuti aziganiza zoyenera, kulankhula zoyenera komanso kukhala ndi makhalidwe oyera. (1 Pet. 1:15, 16) Paja chikondi ‘sichichita zosayenera komanso sichisamala zofuna zake zokha.’—1 Akor. 13:4, 5.

TIZIVALA ZOVALA ZOGWIRIZANA NDI MALO AMENE TILI

11, 12. Kodi ndi zinthu ziti zimene timaganizira tikamasankha zovala?

11 Akhristu akamasankha zovala amakumbukira mfundo yakuti pali “nthawi yochitira chinthu chilichonse ndiponso yokhudza ntchito iliyonse.” (Mlal. 3:1, 17) N’zoona kuti pa nkhani ya zovalayi timaganiziranso nyengo ya komwe tili. Nthawi zinanso anthu amavala mosiyana ndi anzawo chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wawo komanso mmene nyengo yasinthira. Komabe tizikumbukira kuti mfundo za Yehova sizisintha chifukwa cha nyengo.—Mal. 3:6.

12 M’madera otentha, zimakhala zovuta kuti anthu asankhe mwanzeru zovala zimene zingapereke ulemu. Komabe abale ndi alongo athu amayamikira tikamayesetsa kupewa zovala zothina komanso zoonetsa mkati. (Yobu 31:1) Komanso zovala zimene timavala kunyanja kapena malo ena osambirira ziyenera kukhala zoyenera. (Miy. 11:2, 20) Ngakhale kuti anthu ambiri a m’dzikoli akakhala kunyanja savala bwino, Akhristufe timaona kuti tiyenera kuvala moyenera kuti tikondweretse Mulungu wathu woyera amene timamukonda.

13. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira malangizo a pa 1 Akorinto 10:32, 33?

13 Palinso chinthu china chimene chingatithandize kuti tizivala moyenera. Tiyenera kuganizira chikumbumtima cha Akhristu anzathu komanso cha anthu ena. (Werengani 1 Akorinto 10:32, 33.) Choncho tiziona kuti ndi udindo wathu kupewa zovala zimene zingakhumudwitse ena. Paulo anati: “Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa. Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha.” (Aroma 15:2, 3) Yesu ankaona kuti kuthandiza ena n’kofunika kwambiri kuposa zofuna zake. Ankaonanso kuti sangachite chifuniro cha Mulungu popanda kuthandiza ena. Ifenso tingasankhe kuti tisavale zovala zinazake zimene tingakonde, ngati tikuona kuti zingalepheretse ena kumvetsera uthenga wathu.

14. Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kuti azilemekeza Mulungu pa nkhani ya zovala?

14 Makolo achikhristu ali ndi udindo wophunzitsa ana awo kuti azitsatira mfundo za m’Baibulo. Ayenera kuonetsetsa kuti iwowo komanso ana awo akusangalatsa mtima wa Yehova pa nkhani ya zovala ndi kudzikongoletsa. (Miy. 22:6; 27:11) Makolo angaphunzitse ana awo kuti azilemekeza Mulungu powapatsa chitsanzo chabwino komanso powalangiza mwachikondi. Angachitenso bwino kuphunzitsa ana awo kuti adziwe zovala zoyenera komanso kumene angazipeze. Ayenera kuwaphunzitsa kuti zovala zabwino si zimene anawo amakonda basi, koma ndi zimenenso zingawathandize kuti azidziwika kuti ndi atumiki a Mulungu.

MUZIGWIRITSA NTCHITO BWINO UFULU WANU WOSANKHA ZOCHITA

15. Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisankha bwino pa nkhani ya zovala?

15 M’Baibulo muli malangizo amene angatithandize tonsefe kuti tizisankha zovala zimene zingalemekeze Mulungu. Komabe sikuti  tonse timavala zofanana. Zili choncho chifukwa chakuti anthufe timasiyana zokonda komanso kapezedwe ka ndalama. Komabe tonse timafunika kuvala zovala zoyenera komanso zaukhondo. Zovalazo ziyeneranso kukhala zogwirizana ndi malo amene tili komanso chikhalidwe cha kuderalo.

16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuvala bwino?

16 N’zoona kuti si zapafupi kusankha zovala zabwino moganizira mfundo zonse zimene takambiranazi. Masiku ano, m’masitolo ambiri mumangopezeka zovala zamafashoni amakono ndipo munthu amafunika kuchita khama kuti apeze siketi, diresi, bulauzi, suti kapena thalauza yoyenera komanso yosathina. Koma tikamayesetsa kusankha zovala zoyenera, Akhristu anzathu amaona ndiponso amayamikira. Ifenso timasangalala podziwa kuti zovala zathu zikulemekeza Atate wathu wakumwamba ndipo sitidandaula ndi zimene anthu ena angatinene.

17. Kodi m’bale ayenera kuganizira mfundo ziti asanasankhe kusunga ndevu?

17 Nanga kodi abale ayenera kusunga ndevu? Chilamulo cha Mose chinkanena kuti amuna azisunga ndevu. Koma Akhristu satsatira Chilamulo. (Lev. 19:27; 21:5; Agal. 3:24, 25) M’madera ena si vuto kukhala ndi ndevu zoduliridwa bwino ndipo sizingalepheretse anthu kumvetsera uthenga wathu. Ndipotu pali abale ena audindo amene amasunga ndevu. Komabe abale ena amasankha kuti asamasunge ndevu. (1 Akor. 8:9, 13; 10:32) M’mayiko ena mulibe chikhalidwe chimenechi ndipo anthu amaona kuti n’zosayenera kuti atumiki a Mulungu azisunga ndevu. M’bale akakhala ndi ndevu zazitali m’madera oterewa, anthu omuona sangalemekeze Mulungu.—Aroma 15:1-3; 1 Tim. 3:2, 7.

18, 19. Kodi lemba la Mika 6:8 lingatithandize bwanji kuti mavalidwe athu azisangalatsa Mulungu?

18 Timayamikira kwambiri kuti Yehova sanatipatse malamulo ambirimbiri okhudza zovala ndi kudzikongoletsa. M’malomwake amafuna kuti tiziphunzira mfundo za m’Malemba n’kumagwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha. Choncho pa nkhani imeneyinso, tili ndi mwayi wosonyeza kuti timafuna ‘kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wathu.’—Mika 6:8.

19 Tiyenera kudzifufuza kuti tione ngati zimene timasankha pa nkhani ya zovala zimagwirizana ndi mfundo za Yehova. Tikatero timasonyeza kuti ndife odzichepetsa komanso tikufuna kuti Yehova azititsogolera. Munthu wodzichepetsa amaganiziranso ena komanso amapewa kuwaweruza. Choncho tiyeni tipitirize kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wathu potsatira mfundo zake zapamwamba komanso kulemekeza maganizo a anthu ena.

20. Kodi chingachitike n’chiyani tikamavala komanso kudzikongoletsa moyenera?

20 Tiyeni tiziyesetsa kuvala zovala zimene zingathandize anthu kudziwa kuti ndife anthu a Mulungu. Akhristu anzathu komanso anthu ena azitha kuona kuti tikuimiradi Yehova Mulungu wathu. Tikamayesetsa kutsatira mfundo zake zapamwamba timasangalala kwambiri. Tikuyamikira kwambiri abale ndi alongo amene kavalidwe ndi khalidwe lawo labwino, zathandiza kuti anthu a maganizo abwino amvetsere uthenga wa Baibulo. Izi zimalemekezanso Yehova ndipo zimasangalatsa mtima wake. Choncho tiyeni tipitirize kusankha bwino pa nkhani ya zovala kuti tizitamandabe Mulungu wathu amene ‘amadziveka ulemu ndi ulemerero.’—Sal. 104:1, 2.