Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chiyani chinathandiza Sitefano kuti akhalebe wodekha pamene ankazunzidwa?

SITEFANO anali pakati pa gulu la anthu okwiya kwambiri mu Khoti Lalikulu la Ayuda. Khotili linali ndi oweruza 71 ndipo anthu amenewa anali amphamvu kwambiri mu Isiraeli. Apa n’kuti patangopita miyezi yochepa kuchokera pamene mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa ankatsogolera zinthu pa nthawi imene Yesu anaweruzidwa kuti aphedwe. (Mat. 26:57, 59; Mac. 6:8-12) Ndiye Kayafa yemweyu anasonkhanitsanso oweruza n’kumaitana mboni zonama kuti zimuneneze. Koma onse anadabwa kuti nkhope ya Sitefano inkaoneka “ngati nkhope ya mngelo.”​—Mac. 6:13-15.

Kodi n’chiyani chinathandiza Sitefano kuti asaope koma akhalebe wodekha? Iye asanapititsidwe kukhotili ankagwira ntchito ya Mulungu mwakhama ndipo mzimu woyera unkamuthandiza kwambiri. (Mac. 6:3-7) Ndiye akuzengedwa mlandu, mzimu womwewo unkamulimbikitsa komanso kumuthandiza kukumbukira malemba. (Yoh. 14:16) Mfundo zimene Sitefano ananena pofotokoza mbali yake pamlanduwu, zikupezeka m’chaputala 7 cha Machitidwe ndipo mzimu woyera unamuthandiza kukumbukira mavesi oposa 20 a m’Malemba Achiheberi. (Yoh. 14:26) Koma chikhulupiriro cha Sitefano chinalimba kwambiri ataona masomphenya a Yesu ali kudzanja lamanja la Mulungu.​—Mac. 7:54-56, 59, 60.

Mwina nafenso tsiku lina tidzakhala pakati pa anthu olusa. (Yoh. 15:20) Tikakhala ndi chizolowezi chophunzira Mawu a Mulungu komanso kulalikira, timalola mzimu wa Yehova kuti uzitithandiza. Ndipo mzimuwo ukhoza kutithandiza kuti tidzakhale ndi mtendere wamumtima pa nthawi imene anthu ena akutizunza.​—1 Pet. 4:12-14.