Mfundo Zothandiza Pophunzira

Mfundo Zothandiza Pophunzira

Muziloweza “Nyimbo Zauzimu”

Lorraine wa ku U.S.A. ananena kuti, “Ndikayamba kudziona ngati wachabechabe, Yehova amandilimbikitsa pogwiritsa ntchito nyimbo za pa JW Broadcasting®.”

Akhristu akhala akugwiritsa ntchito “nyimbo zauzimu” polambira. (Akol. 3:16) Ngati mutaphunzira komanso kuloweza nyimbozi zingakuthandizeni ngakhale pamene mulibe buku kapena chipangizo chamakono. Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kuti muzitha kuloweza nyimbozi.

  • Muziwerenga mawu ake mosamala kuti mumvetse tanthauzo lake. Munthu amatha kukumbukira mawu ngati wamvetsa tanthauzo lake. Pa jw.org pamapezeka mawu a nyimbo zathu kuphatikizapo za Broadcasting komanso za ana. Pitani pamene alemba kuti Laibulale, kenako Nyimbo.

  • Muzilemba mawu a nyimboyo pamanja. Mukamachita zimenezo m’pamene mawu a nyimboyo amakhazikika m’maganizo mwanu.—Deut. 17:18.

  • Muziyeserera motulutsa mawu. Muziwerenga komanso kuimba mawu a nyimboyo mobwerezabwereza.

  • Dziyeseni kuti muone ngati mwaloweza. Muziyesa kukumbukira mawu a nyimboyo popanda kuonera, kenako muziona ngati mwawaloweza.