Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 48

“Malizitsani” Zimene Munayamba Kuchita

“Malizitsani” Zimene Munayamba Kuchita

“Malizitsani kupatsa kumeneku.”​—2 AKOR. 8:11.

NYIMBO NA. 35 “Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”

ZIMENE TIPHUNZIRE *

1. Kodi Yehova amatipatsa ufulu wotani?

YEHOVA amatipatsa ufulu wosankha zochita pa moyo wathu ndipo iye amatiphunzitsa kuti tizisankha bwino zochitazo. Komanso tikasankha zinthu zomusangalatsa, amatithandiza kuti tizikwaniritse. (Sal. 119:173) Tikamatsatira kwambiri nzeru zochokera m’Mawu a Mulungu m’pamene timatha kusankha bwino zochita.​—Aheb. 5:14.

2. Kodi tingavutike kuchita chiyani pambuyo posankha zochita?

2 Koma ngakhale titasankha mwanzeru, tikhoza kuvutika kuti timalizitse zimene tinayamba kuchita. Taganizirani zitsanzo izi. M’bale wachinyamata waganiza zoti awerenge Baibulo lonse. Ndiye wayamba kuwerenga kwa milungu ingapo kenako n’kusiya pa zifukwa zina. Mlongo wina akufuna kuyamba upainiya koma akungozengereza. Akulu ena agwirizana kuti azichita kwambiri maulendo aubusa koma miyezi ingapo yadutsa asanayambe. Zitsanzozi ndi zosiyana koma zikufanana pa mfundo imodzi. Onse anasankha zochita koma sanazichite. Akhristu a ku Korinto analinso ndi vuto lomweli. Tiyeni tikambirane zimene tingaphunzire kwa Akhristuwo.

3. Kodi Akhristu a ku Korinto anasankha kuchita chiyani, koma chinachitika n’chiyani?

3 Cha m’ma 55 C.E., Akhristu a ku Korinto anasankha kuchita zinthu zofunika kwambiri. Iwo anamva kuti abale awo a ku Yerusalemu ndi ku Yudeya akuzunzidwa komanso akusowa zinthu zofunika ndipo mipingo ina ikusonkha ndalama zowathandizira. Chifukwa cha chifundo komanso mtima wopatsa, Akhristu a ku Korinto anasankha kuti athandize nawo ndipo anafunsa mtumwi Paulo zimene angachite. Iye anapereka malangizo ku mpingowo ndipo anasankha Tito kuti awathandize kusonkhanitsa ndalamazo. (1 Akor. 16:1; 2 Akor. 8:6) Koma patapita miyezi ingapo, Paulo anamva kuti Akhristuwo sanachite zomwe anasankhazo. Izi zikanachititsa kuti mphatso zawo zisatumizidwe ku Yerusalemu pamodzi ndi zimene mipingo ina inapereka.​—2 Akor. 9:4, 5.

4. Malinga ndi 2 Akorinto 8:7, 10, 11, kodi Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Korinto kuchita chiyani?

4 Akhristu a ku Korinto anasankha kuchita zinthu zabwino ndipo Paulo anawayamikira chifukwa cha chikhulupiriro chawo komanso mtima wawo wopatsa. Koma iye ankafunikanso kuwalimbikitsa kuti amalize zimene anayamba kuchitazo. (Werengani 2 Akorinto 8:7, 10, 11.) Zimene zinawachitikirazi zikutiphunzitsa kuti ngakhale Akhristu okhulupirika angavutike kukwaniritsa zinthu zabwino zimene anasankha.

5. Kodi tiyankha mafunso ati?

5 Mofanana ndi Akhristuwo, ifenso tingavutike kukwaniritsa zomwe tinasankha. Izi zingachitike chifukwa si ife angwiro ndipo nthawi zina timazengereza kuchita zinthu. Mwinanso pangachitike zinthu zina zosayembekezereka zomwe zingatilepheretse kukwaniritsa zomwe tinasankha kuchita. (Mlal. 9:11; Aroma 7:18) Kodi tingatani ngati tikufunika kuganiziranso zimene tinasankha kuti tione ngati m’pofunika kusintha? Nanga kodi tingatani kuti tizimaliza zimene tinayamba kuchita?

MUSANASANKHE ZOCHITA

6. N’chifukwa chiyani tingafunike kusintha zimene tinasankha?

6 Pali zinthu zina zofunika zimene timasankha zomwe sitiyenera kusintha. Mwachitsanzo, sitiyenera kusintha zimene tinasankha zoti tizitumikira Yehova komanso kukhala wokhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wathu. (Mat. 16:24; 19:6) Koma pali zinthu zina zimene tinasankha zomwe tingafunike kusintha. Zili choncho chifukwa choti zinthu zingasinthe pa moyo wathu. Kodi n’chiyani chingatithandize kusankha zochita mwanzeru?

7. Kodi tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?

7 Muzipempha Mulungu kuti akupatseni nzeru. Yehova anauzira Yakobo kuti alembe kuti: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse.” (Yak. 1:5) Tonsefe ‘timasowa nzeru’ nthawi zina. Choncho tiyenera kudalira Yehova posankha zochita komanso ngati tikufunika kuganiziranso zimene tinasankha. Tikatero Yehova adzatithandiza kusankha zinthu mwanzeru.

8. Kodi tiyenera kuchita chiyani tisanasankhe zochita?

8 Muzifufuza mokwanira. Muzifufuza m’Mawu a Mulungu, m’mabuku athu komanso muzikambirana ndi anthu odalirika. (Miy. 20:18) Zimenezi n’zofunika kuti musankhe mwanzeru pa zinthu monga kusintha ntchito, kusamuka kapena maphunziro amene angakuthandizeni kupeza zofunika uku mukutumikira Yehova.

9. Kodi kudziwa zifukwa zimene tasankhira zinazake kungatithandize bwanji?

9 Muziganizira zifukwa zake. Yehova amafuna kuti tizichita zinthu pa zifukwa zoyenera. (Miy. 16:2) Iye amafunanso kuti tizichita zinthu zonse moona mtima. Choncho tiyenera kudzifufuza moona mtima kuti tidziwe zifukwa zimene tikufunira kuchita zinthu zina. Sitiyeneranso kubisira anthu ena zifukwazo. Ngati tasankha zinthu popanda kuzindikira zifukwa zake, tingamavutike kuchita zimene tasankhazo. Mwachitsanzo, m’bale wachinyamata angasankhe kuyamba upainiya wokhazikika. Koma patapita nthawi, angayambe kuvutika kuti akwanitse maola ake ndipo angasiye kusangalala ndi utumikiwu. Mwina ankaganiza kuti akufuna kuyamba upainiya n’cholinga choti azisangalatsa Yehova. Koma kwenikweni ankangofuna kusangalatsa makolo ake kapena munthu wina amene amamulemekeza.

10. Kodi n’chiyani chingatithandize kusintha zinthu pa moyo wathu?

10 Taganizirani chitsanzo china. Tiyerekeze kuti munthu wina amene akuphunzira Baibulo wasankha kuti asiye kusuta. Kwa mlungu umodzi kapena iwiri wayesetsa kwambiri kuti asasute koma kenako walephera kudziletsa ndipo wasutanso. Ndiye patapita nthawi, wakwanitsa kusiyiratu. Iye wakwanitsa chifukwa choti amakonda kwambiri Yehova komanso akufunitsitsa kumusangalatsa.​—Akol. 1:10; 3:23.

11. N’chifukwa chiyani tiyenera kudziwa bwinobwino zimene tikufuna kuchita?

11 Muzidziwa bwinobwino zimene mukufuna kuchita. Mukhoza kumaliza zimene mwayamba ngati mukudziwa bwinobwino zimene mukufuna kuchita. Mwachitsanzo, mwina mwasankha kuti muziwerenga Baibulo pafupipafupi. Koma ngati simunasankhe nthawi imene mukufuna kuti muziliwerenga, mwina simungakwaniritse cholinga chanucho. * Akulunso angasankhe kuti azichita maulendo aubusa pafupipafupi. Koma patapita nthawi, angapezeke kuti sakuchita zimene anasankhazo. Kuti akwaniritse zimene anasankha, angachite bwino kudzifunsa mafunso awa: “Kodi ndi abale ndi alongo ati amene akufunikira kulimbikitsidwa kwambiri? Nanga tasankha nthawi yeniyeni yoti tiwayendere?”

12. Kodi nthawi zina tingafunike kuchita chiyani? Perekani chifukwa.

12 Muzidziwa zimene mungakwanitse. Palibe munthu amene ali ndi nthawi, zinthu kapena mphamvu zokwanira zoti azichitira chilichonse chimene akufuna. Choncho muyenera kudziwa zimene mungakwanitse kuchita. Ndipo nthawi zina mungafunike kusintha zimene munasankha chifukwa choti simungakwanitse kuzichita. (Mlal. 3:6) Koma tiyerekeze kuti mwaonanso zimene munasankha n’kusintha zinthu zina ndipo panopa mukuona kuti mungazikwaniritse. Kodi mungatani? Tiyeni tsopano tikambirane zinthu 5 zimene zingakuthandizeni kuti mumalize zimene munayamba kuchita.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUKWANIRITSE ZIMENE MWASANKHA

13. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukwaniritsa zimene munasankha?

13 Muzipempha Yehova kuti akupatseni mphamvu. Mulungu angakuthandizeni kuti mukwanitse kuchita zimene mwasankha. (Afil. 2:13) Choncho muzimupempha kuti akupatseni mphamvu ya mzimu woyera. Muzipitiriza kupemphera ngakhale pamene zikuoneka kuti pemphero lanu silikuyankhidwa. Paja Yesu ananena kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.”​—Luka 11:9, 13.

14. Kodi mfundo ya pa Miyambo 21:5 ingakuthandizeni bwanji kukwaniritsa zimene munasankha?

14 Muzikhala ndi pulani. (Werengani Miyambo 21:5.) Mumafunika kukhala ndi pulani komanso kuitsatira bwino kuti mumalizitse zimene mukufuna. Choncho mukasankha zochita, muzilemba zimene muyenera kuchita kuti mukwaniritse zimene mwasankhazo. Ngati zinthu zina zimene muyenera kuchita ndi zovuta, mungachite bwino kugawa zinthuzo m’magawo ang’onoang’ono. Ndiye mukakwanitsa kumaliza gawo lililonse mudzaona kuti n’zotheka kukwaniritsa cholingacho. Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Korinto kuti aziika kenakake pambali “tsiku lililonse loyamba la mlungu” m’malo modikira kuti adzatolere ndalama zonse Pauloyo akadzafika. (1 Akor. 16:2) Kugawa zinthu zikuluzikulu m’magawo ang’onoang’ono kungakuthandizeni kuti musamaone kuti simungakwaniritse zimene mwasankha.

15. Kodi muyenera kuchita chiyani pambuyo pokhala ndi pulani?

15 Kulemba pulani yanu yochitira zinthu kungakuthandizeni kuti mukwaniritse zimene munasankha. (1 Akor. 14:40) Mwachitsanzo, mabungwe a akulu amalimbikitsidwa kuti azisankha mkulu woti azilemba zimene bungwelo lasankha kuchita, amene asankhidwa kuti azichite komanso nthawi imene ayenera kumaliza zinthuzo. Akulu amene amatsatira malangizowa amakwaniritsa zimene asankha mosavuta. (1 Akor. 9:26) Zimenezi zingakuthandizeninso kukwaniritsa zomwe munasankha. Mwachitsanzo, mukhoza kulemba zinthu zimene mukufunika kuchita tsiku lililonse n’kusonyeza zimene muziyambira kuchita ndi zimene muzimalizira. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mumalize zimene munayamba kuchita komanso kuti muchite zinthu zambiri pa nthawi yochepa.

16. Kodi pamafunika chiyani kuti muzichita zimene munasankha, nanga lemba la Aroma 12:11 limagwirizana bwanji ndi zimenezi?

16 Muzichita khama. Pamafunika khama kuti mutsatire pulani yanu komanso mumalize zimene munayamba. (Werengani Aroma 12:11.) Paulo anauza Timoteyo kuti ‘apitirize kukhala wodzipereka’ n’kumayesetsa kukhala mphunzitsi wabwino. Malangizowa angatithandizenso kuti tizikwaniritsa zolinga zina zauzimu.​—1 Tim. 4:13, 16.

17. Kodi malangizo a pa Aefeso 5:15, 16 angatithandize bwanji kukwaniritsa zimene tinasankha?

17 Muzigwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru. (Werengani Aefeso 5:15, 16.) Sankhani nthawi imene mudzachitire zimene munasankha ndipo musasinthe nthawiyo. Musamadikire nthawi yabwino yoti muchite zinthuzo chifukwa mwina singapezeke. (Mlal. 11:4) Musamalole kuti zinthu zosafunika zizikusokonezani moti n’kusowa nthawi ndi mphamvu zochitira zinthu zofunika kwambiri. (Afil. 1:10) Ngati zingatheke, muzisankha nthawi imene anthu ena sangakusokonezeni. Mungauzenso anthu kuti akupatseni mpata ndipo mungachite bwino kuthimitsa foni komanso kupewa kuona maimelo kapena mameseji. *

18-19. N’chiyani chingakuthandizeni kuti mukwaniritse zimene munasankha ngakhale mutakumana ndi mavuto?

18 Muziganizira zotsatira zake. Tingayerekezere kukwaniritsa zimene munasankha ndi kukafika kumalo amene mukupita. Ngati mukufunadi kukafika kumaloko, mumapitirizabe ulendo ndipo ngakhale njira itatsekedwa, mumasintha n’kudzera njira ina. Mofanana ndi zimenezi, tikakhala ndi cholinga chokwaniritsa zimene tinasankha, timayesetsabe kuzikwaniritsa ngakhale titakumana ndi mavuto.​—Agal. 6:9.

19 Zimakhala zovuta kuti tisankhe zinthu mwanzeru komanso kukwaniritsa zimene tasankhazo. Koma Yehova angakupatseni nzeru ndi mphamvu zoti mumalizitse zimene munayamba kuchita.

NYIMBO NA. 65 Pita Patsogolo

^ ndime 5 Kodi pali zinthu zina zimene mumaona kuti simunasankhe bwino? Kapena kodi mumavutika kusankha bwino zochita komanso kukwaniritsa zimene munasankha? Nkhaniyi ikuthandizani kuthana ndi mavuto amenewa n’kumamalizitsa bwinobwino zimene munayamba kuchita.

^ ndime 11 Kuti mukwaniritse cholinga chanu chowerenga Baibulo, mungagwiritse ntchito “Ndandanda Yowerengera Baibulo” imene ikupezeka pa jw.org®.

^ ndime 17 Kuti mudziwe zinthu zina zimene zingakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu, onani nkhani yakuti “Mfundo 20 Zothandiza Kuti Muzikhala ndi Nthawi Yokwanira” mu Galamukani! ya April 2010.