NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) November 2019

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira pa December 30, 2019–February 2, 2020.

Pezani Anzanu Apamtima Mapeto Asanafike

Tingaphunzire zambiri pa nkhani ya Yeremiya, yemwe anzake anamuthandiza kupulumuka Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa.

Kodi Mzimu Woyera Umatithandiza Bwanji?

Mzimu woyera wa Mulungu ungatithandize kupirira. Koma kuti uzitithandiza mokwanira, pali zinthu 4 zimene tiyenera kuchita.

Kodi Mukusamalira ‘Chishango Chanu Chachikulu Chachikhulupiriro’?

Chikhulupiriro chathu chimakhala ngati chishango chotiteteza. Kodi tingatani kuti tizisamalira bwino chishango chathu chachikhulupiriro?

Zimene Tingaphunzire M’buku la Levitiko

M’buku la Levitiko muli malamulo amene Yehova anapatsa Aisiraeli. Akhristufe sitiyendera malamulo amenewo koma mfundo zake zikhoza kutithandiza.

“Malizitsani” Zimene Munayamba Kuchita

Tikasankha bwino zochita, nthawi zina timavutika kumalizitsa zimene tinasankhazo. Onani mfundo zimene zingakuthandizeni kumalizitsa zimene munayamba kuchita.

Kodi Mukudziwa?

Kodi ntchito za mtumiki woyang’anira nyumba zinali zotani?