Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Olimbikitsa Kwambiri

Mawu Olimbikitsa Kwambiri

NTHAWI zina Yesu ankagwiritsa ntchito mawu akuti, “mayi” akamalankhula ndi akazi ndipo mawuwa anali osonyeza ulemu. Mwachitsanzo, pamene ankachiritsa mzimayi wina yemwe anadwala matenda opindika msana kwa zaka 18, anati: “Mayi, mwamasuka ku matenda anu.” (Luka 13:10-13) Yesu ankagwiritsiranso ntchito mawuwa polankhula ndi amayi ake. (Yoh. 19:26; 20:13) Koma panalinso mawu ena osonyeza ulemu akuti “mwana wanga.” Munthu ankagwiritsa ntchito mawu amenewa posonyeza kukoma mtima komanso chikondi.

Mawuwa ankagwiritsidwanso ntchito polankhula ndi akazi. Mwachitsanzo, Yesu anagwiritsa ntchito mawu amenewa pomwe ankalankhula ndi mzimayi amene anadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12. Zimene mzimayiyu anachita kuti akafike pamene panali Yesu, zinali zosemphana ndi Chilamulo. Munthu wodwala matenda amenewa anali wodetsedwa ndipo sankafunika kupita kugulu la anthu. (Lev. 15:19-27) Koma chifukwa chothedwa nzeru, mzimayiyu anapitabe. Ndipotu Baibulo limati “madokotala ambiri anam’chititsa kumva zopweteka zambiri. Iye anawononga chuma chake chonse koma osapindula kanthu, m’malomwake matendawo ankangokulirakulira.”—Maliko 5:25, 26.

Mzimayiyu anadutsa kumbuyo kwa Yesu ndipo anayenda mwakachetechete n’kukagwira m’mphepete mwa malaya ake akunja. Nthawi yomweyo anachira. Iye ankaganiza kuti aliyense sanadziwe zimene anachitazi. Koma Yesu anafunsa kuti: “Ndani wandigwira?” (Luka 8:45-47) Apa mayiyu anachita mantha kwambiri n’kuyamba kunjenjemera. Ndiyeno anagwada pamaso pa Yesu “ndi kumuuza zoona zonse.”—Maliko 5:33.

Koma Yesu anamulankhula mokoma mtima kuti: “Mwanawe, limba mtima.” (Mat. 9:22) Malinga ndi zimene akatswiri a Baibulo amanena, mawu achiheberi ndi achigiriki amene anawamasulira kuti “mwana” angagwiritsidwe ntchito posonyeza “kukoma mtima komanso chikondi.” Kenako Yesu anauza mzimayiyo mawu olimbikitsa akuti: “Chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.”—Maliko 5:34.

Nayenso Boazi amene anali munthu wolemera wa ku Isiraeli anagwiritsa ntchito mawu akuti “mwana wanga” polankhula ndi Rute wa ku Mowabu. Rute anali ndi mantha chifukwa ankakunkha balere m’munda mwa munthu wosamudziwa. Koma Boazi anamuuza kuti: “Tamvera mwana wanga.” Kenako anamulangiza kuti azikunkhabe m’munda mwakemo. Rute atamva zimenezi, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi ndipo anati: “Zatheka bwanji kuti mundiganizire ndi kundikomera mtima chotere, ine wokhala mlendo?” Boazi anayankha pomuuza mawu olimbikitsa akuti: “Ndamva zonse zimene wachitira apongozi ako [a Naomi] . . . Yehova akudalitse chifukwa cha zimene wachita.”—Rute 2:1-12.

Zimene Yesu ndi Boazi anachita ndi chitsanzo chabwino kwa akulu. Nthawi zina akulu awiri angapite kwa mlongo amene akufunika kumuthandiza ndi mfundo za m’Malemba komanso kumulimbikitsa. Akuluwo ayenera kupemphera komanso kumvetsera pamene mlongoyo akulankhula. Akatero angathe kumuuza mawu olimbikitsa pogwiritsa ntchito Baibulo.—Aroma 15:4.