NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA) November 2016

M’magaziniyi muli nkhani zophunzira kuyambira mlungu wa December 26, 2016 mpaka January 29, 2017.

Mawu Olimbikitsa Kwambiri

Kodi Yesu anagwiritsa ntchito mawu ati omwe amasonyeza ulemu komanso kukoma mtima?

Tipitirize Kulimbikitsana Tsiku ndi Tsiku

Kodi kulimbikitsana n’kofunika bwanji? Kodi tikuphunzira chiyani kwa Yehova, Yesu ndi Paulo pa nkhani yolimbikitsa ena?

Mawu a Mulungu Amatithandiza Kuti Tizichita Zinthu Mwadongosolo

Yehova ndi Mulungu wadongosolo. Kodi si zomveka kuti atumiki ake ayeneranso kuchita zinthu mwagongosolo?

Kodi Mumaona Kuti Baibulo Ndi Buku Lapadera?

Zinthu zimawayendera bwino anthu a Mulungu akamayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo komanso akamathandiza gulu lake.

“Ntchitoyi Ndi Yaikulu”

Muli ndi mwayi woti mungathe kuthandiza pa ntchitoyi.

Anthu a Mulungu Anaitanidwa Kuchoka mu Mdima

Kodi zinatani kuti anthu a Mulungu alowe mu ukapolo wa Babulo Wamkulu atumwi atamwalira? Nanga ndi liti pamene kuwala kunayamba kuoneka, ndipo chinachitika n’chiyani?

Anatuluka mu Babulo Wamkulu

Kodi anthu a Mulungu anatuluka liti mu ukapolo wa Babulo Wamkulu?

“Ofalitsa a ku Britain Galamukani!”

Kwa zaka 10, utumiki sunkayenda bwino ku Britain. Kodi n’chiyani chinathandiza kuti ziyambenso kuyenda bwino?