Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mtendere​—Kodi Mungaupeze Bwanji?

Mtendere​—Kodi Mungaupeze Bwanji?

POPEZA m’dzikoli muli mavuto ambiri, timafunika kuchita khama kuti tipeze mtendere. Ndipo ngakhale titaupeza, zingavute kuti tiusungebe. Kodi Mawu a Mulungu amati n’chiyani chimene chingatithandize kupeza mtendere weniweni komanso wosatha? Nanga tingathandize bwanji anthu ena kuti apezenso mtendere?

KODI MUNTHU ANGAPEZE BWANJI MTENDERE WENIWENI?

Kuti tikhale ndi mtendere weniweni tiyenera kukhala otetezeka komanso opanda nkhawa. Tiyeneranso kuyesetsa kuti tizigwirizana ndi anthu. Koma chofunika kwambiri ndi kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Kodi tingachite bwanji zimenezi?

Anthu ambiri sakhala pa mtendere chifukwa choda nkhawa

Tikamamvera malamulo komanso mfundo zachilungamo za Yehova, timasonyeza kuti timamukhulupirira komanso tikufuna kukhala naye pa ubwenzi wolimba. (Yer. 17:7, 8; Yak. 2:22, 23) Tikatero, iyenso amatiyandikira ndipo amatipatsa mtendere wamumtima. Lemba la Yesaya 32:17 limati: “Ntchito ya chilungamo chenicheni idzakhala mtendere, ndipo zochita za chilungamo chenicheni zidzakhala bata ndi mtendere mpaka kalekale.” Kunena zoona, tikhoza kupeza mtendere weniweni tikamamvera Yehova ndi mtima wonse.​—Yes. 48:18, 19.

Mzimu woyera umene Mulungu amapereka ungatithandizenso kupeza mtendere wosatha.​—Mac. 9:31.

MZIMU WA MULUNGU UMATITHANDIZA KUKHALA NDI MTENDERE

Mtendere ndi khalidwe lachitatu limene Paulo anatchula pofotokoza “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” (Agal. 5:22, 23) Popeza mzimu wa Mulungu ndi umene umathandiza kuti munthu apeze mtendere weniweni, tiyenera kulola mzimuwo kuti uzititsogolera. Kodi mzimu wa Mulungu ungatithandize kupeza mtendere m’njira ziwiri ziti?

Yoyamba, timapeza mtendere tikamawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse. (Sal. 1:2, 3)  Tikamasinkhasinkha zimene tawerenga m’Baibulo, mzimu wa Mulungu umatithandiza kuzindikira maganizo a Yehova pa nkhani zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, timatha kuona zimene amachita kuti azikhalabe wamtendere komanso chifukwa chake mtendere ndi wofunika kwambiri kwa iye. Ndiyeno tikamayesetsa kutsatira zimene taphunzira m’Mawu a Mulungu, timakhalanso ndi mtendere.​—Miy. 3:1, 2.

Yachiwiri, tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake. (Luka 11:13) Yehova walonjeza kuti ngati titamupempha kuti atithandize, “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima [yathu] ndi maganizo [athu] mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Tikamapemphera kwa Mulungu komanso kudalira mzimu wake, iye amatipatsa mtendere wamumtima umene umapezeka ndi anthu amene ali naye pa ubwenzi.​—Aroma 15:13.

Kodi anthu ena anatsatira bwanji malangizo amenewa n’kusintha? Nanga zawathandiza bwanji kuti akhale ndi mtendere mumtima komanso akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso anzawo?

ZIMENE ANACHITA KUTI APEZE MTENDERE

Masiku ano pali anthu ena mumpingo amene poyamba anali ‘okonda kukwiya’ koma panopa amaganizira ena, ndi okoma mtima, oleza mtima komanso amakhala mwamtendere ndi anthu ena. * (Miy. 29:22) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale David ndi Mlongo Rachel amene anathandizidwa kuti asiye kukhala okwiya n’kuyamba kugwirizana ndi anthu ena.

Tikhoza kupeza mtendere tikamatsatira mfundo za m’Baibulo komanso kupempha mzimu wa Mulungu

Poyamba khalidwe la David silinali labwino ndipo zinkachititsa kuti asamalankhule bwino. Iye asanadzipereke kwa Mulungu, ankakonda kunena zoipa zokhudza anthu ena ndipo ankalankhula anthu a m’banja lake mwamwano. Koma kenako David anaona kuti ayenera kusintha n’kumachita zinthu mwamtendere. Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti ayambe kuchita zinthu mwamtendere? Iye anati: “Ndinayamba kutsatira mfundo za m’Baibulo ndipo zinathandiza kuti tizilemekezana m’banja lathu.”

 Nayenso Rachel anali ndi khalidwe loipa chifukwa cha banja limene anakulira. Iye ananena kuti: “Ndimalimbanabe ndi khalidwe lokwiya msanga chifukwa ndi mmene anthu a m’banja lathu ankachitira.” Kodi n’chiyani chamuthandiza kuti ayambe kuchita zinthu mwamtendere? Iye anati: “Ndinayamba kupemphera kwa Yehova nthawi zonse komanso kumudalira.”

Nkhani ya David ndi Rachel ikusonyeza kuti tikamatsatira mfundo za m’Malemba ndiponso kudalira mzimu wa Mulungu tikhoza kumakhala mwamtendere. Choncho ngakhale kuti tikukhala m’dziko loipa tikhoza kukhala ndi mtendere wamumtima n’kumagwirizana ndi anthu a m’banja lathu komanso Akhristu anzathu. Koma Yehova amatiuza kuti tiyenera kukhala “mwamtendere ndi anthu onse.” (Aroma 12:18) Kodi zimenezi n’zotheka? Nanga kuyesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu onse n’kothandiza bwanji?

TIZIYESETSA KUKHALA MWAMTENDERE NDI ANTHU

Tikamalalikira timathandiza anthu kuti amve uthenga wathu wamtendere wonena za Ufumu wa Mulungu. (Yes. 9:6, 7; Mat. 24:14) Chosangalatsa n’chakuti anthu ambiri amamvetsera uthengawu ndipo amasiya kudandaula ndi zinthu zoipa zimene zikuchitika m’dzikoli. M’malomwake amayembekezera zinthu zabwino m’tsogolo ndipo amayesetsa ‘kufunafuna mtendere ndi kuusunga.’​—Sal. 34:14.

Koma si anthu onse amene amamvetsera uthenga wathu. (Yoh. 3:19) Ngakhale zili choncho, mzimu wa Mulungu umatithandiza kuwalalikira mwamtendere komanso mwaulemu. Tikamachita zimenezi, timatsatira malangizo a Yesu a pa Mateyu 10:11-13 akuti: “Pamene mukulowa m’nyumba, perekani moni kwa a m’banja limenelo. Ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere umene mukuifunira ukhale panyumbayo, koma ngati si yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.” Kutsatira malangizowa kumathandiza kuti tichoke kunyumba ya munthu amene sanamvetsere tidakali pamtendere. Kungathandizenso kuti nthawi ina munthuyo adzamvetsere.

Kulankhula mwaulemu ndi akuluakulu a boma, ngakhale amene amatitsutsa, kumathandizanso kuti tizikhala mwamtendere. Mwachitsanzo, boma la dziko lina la ku Africa linkakana kuti tizimanga Nyumba za Ufumu. Pofuna kuthetsa vutoli mwamtendere, m’bale wina yemwe anakhala mmishonale m’dziko limeneli anapemphedwa kuti akalankhule ndi kazembe wa dzikoli ku England. Iye anapemphedwa kuti akauze kazembeyo za ntchito zimene a Mboni za Yehova amagwira mwamtendere m’dziko lake. Kodi zimenezi zinathandiza bwanji?

M’baleyu ananena kuti: “Nditafika ku ofesi ya kazembeyo, ndinazindikira kuti mzimayi amene ankalandira alendo ndi wa mtundu winawake chifukwa cha mmene anavalira. Ndipo ine ndinali nditaphunzira chilankhulo cha mtunduwo. Choncho ndinamulonjera m’chilankhulo chake. Iye anadabwa n’kundifunsa kuti, ‘Tikuthandizeni?’ Ndinamuuza mwaulemu kuti ndabwera kudzaonana ndi kazembe. Mzimayiyu anaimbira foni kazembeyo ndipo iye anatuluka mu ofesi yake n’kundipatsa moni m’chilankhulo chake. Kenako anamvetsera mosamala kwambiri pamene ndinkamufotokozera za ntchito zimene a Mboni amagwira mwamtendere.”

Ulemu umene m’baleyu anasonyeza, unathandiza kuti kazembeyo asakhalenso ndi maganizo olakwika okhudza ntchito yathu. Patapita nthawi, boma la dzikolo linalola kuti tizimanga Nyumba za Ufumu. Abale anasangalala kwambiri ndi zimenezi. Apa zikuonekeratu kuti kuchita zinthu mwaulemu ndi anthu ena n’kothandiza kwambiri ndipo kumabweretsa mtendere.

MUKHOZA KUKHALA NDI MTENDERE MPAKA KALEKALE

Masiku ano anthu a Yehova amakhala mwamtendere m’paradaiso wauzimu. Inunso mungalimbikitse mtendere m’gulu lathu mukamayesetsa kukhala ndi khalidwe limene mzimu woyera umatulutsali. Koma chofunika kwambiri n’chakuti mukamachita zimenezi mudzasangalatsa Yehova komanso mudzapeza mtendere wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.​—2 Pet. 3:13, 14.

^ ndime 13 Tidzakambirana khalidwe la kukoma mtima munkhani yam’tsogolo yofotokoza makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.