Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo Wosalira Zambiri Ndi Wosangalatsa

Moyo Wosalira Zambiri Ndi Wosangalatsa

DANIEL NDI MIRIAM anakwatirana mu September 2000 ndipo ankakhala mumzinda wa Barcelona ku Spain. Daniel anati: “Moyo wathu unali wabwino kwambiri. Tonse tinali pa ntchito ndipo tinkapita kukadya m’malesitilanti abwino, kupita m’mayiko osiyanasiyana komanso tinkavala zovala zapamwamba. Tinkalowanso mu utumiki mlungu uliwonse.” Koma kenako zinthu zinasintha.

Pamsonkhano wachigawo wa mu 2006, Daniel anakhudzidwa kwambiri atamva nkhani ina imene inali ndi funso lakuti: “Kodi tikuchita zonse zimene tingathe kuti tithandize anthu ‘amene akudzandira popita ku imfa’ kuti ayambe kuyenda pamsewu wopita ku moyo wosatha?” (Miy. 24:11) Nkhaniyi inatsindika kufunika kolalikira uthenga wa m’Baibulo umene ungapulumutse anthu. (Mac. 20:26, 27) Daniel ananena kuti: “Ndinangomva ngati Yehova akulankhula ndi ineyo.” Nkhaniyo inasonyeza kuti munthu akawonjezera zimene amachita mu utumiki amasangalala kwambiri. Daniel ankadziwa kuti zimenezi ndi zoona chifukwa chakuti Miriam anali atayamba kale upainiya ndipo ankasangalala.

Daniel anati: “Apa ndinazindikira kuti ndiyenera kusinthiratu.” Iye anasinthadi. Anachepetsa maola amene ankagwira ntchito n’kuyamba upainiya. Ankaganiziranso kwambiri mmene angasangalalire ndi mkazi wake ngati atasamukira kumene kukufunika ofalitsa ambiri.

SIZINALI ZOPHWEKA KOMA ANADALITSIDWA KWAMBIRI

Mu 2007, Daniel ndi Miriam anasiya ntchito zawo ndipo anasamukira ku Panama, kumene anali atafikako kale. Iwo ankalalikira kuzilumba zambiri za m’nyanja ya Caribbean kumene kumakhala anthu a mtundu wa Guaymi. Daniel ndi Miriam ankaona kuti ali ndi ndalama zokwanira kuti akhale ku Panama kwa miyezi 8.

Iwo ankayenda pa boti komanso pa njinga polalikira kuzilumbazi. Ulendo wawo woyamba wokalalikira kuchilumba chinachake anayenda pa njinga makilomita pafupifupi 32. Anadutsa m’mapiri ndipo dzuwa linkatentha kwambiri moti Daniel anatsala pang’ono kukomoka. Komabe pa ulendowo anthu ankawalandira bwino kwambiri makamaka pamene Daniel ndi Mariam anaphunzira mawu ena achilankhulo cha Chigwaimi. Pasanathe nthawi yaitali, iwo anapeza maphunziro a Baibulo okwana 23.

Koma ndalama zawo zitatha, iwo anadandaula kwambiri. Daniel ananena kuti: “Tinkafuna kulira tikaganizira zobwerera ku Spain. Sitinkafuna kusiya anthu amene tinkaphunzira nawo Baibulo.” Koma patangopita mwezi umodzi, iwo analandira uthenga wosangalatsa. Miriam anati: “Tinapemphedwa kuti tikhale apainiya apadera. Tinasangalala kwambiri titadziwa kuti tikhalabe ku Panama.”

CHIMENE CHIMAWASANGALATSA KWAMBIRI

Mu 2015, zinthu zitasintha m’gulu la Yehova, Daniel ndi Miriam anapemphedwa kuti akhalenso apainiya okhazikika. Kodi iwo anatani? Anadalira kwambiri lonjezo la pa Salimo 37:5 lakuti: “Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako, umudalire ndipo iye adzachitapo kanthu.” Iwo anapeza ntchito kuti iziwathandiza kupeza kangachepe uku akuchita upainiyawo. Panopa akutumikira mumpingo wa ku Veraguas ku Panama komweko.

Daniel ananena kuti: “Tisanachoke ku Spain tinkakayikira ngati tingakwanitse kukhala moyo wosalira zambiri. Koma panopa n’zimene tikuchita ndipo sitisowa zinthu zofunika pa moyo.” Kodi n’chiyani chimene chimawasangalatsa kwambiri? Iwo anati: “Kuthandiza anthu ofatsa kuti adziwe Yehova n’kumene kumatisangalatsa kwambiri.”