Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zinthu Zonse Zimene Yehova Amatipatsa Zimakuthandizani?

Kodi Zinthu Zonse Zimene Yehova Amatipatsa Zimakuthandizani?

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.”—YES. 48:17.

NYIMBO: 117, 114

1, 2. (a) Kodi a Mboni za Yehovafe timaliona bwanji Baibulo? (b) Kodi inuyo mumakonda mabuku ati a m’Baibulo?

A MBONI ZA YEHOVAFE timakonda kwambiri Baibulo chifukwa timapezamo malangizo othandiza. Komanso Baibulo limatithandiza kukhala ndi chiyembekezo ndiponso limatitonthoza. (Aroma 15:4) Timaona kuti Baibulo si buku la anthu koma ndi “Mawu a Mulungu.”—1 Ates. 2:13.

2 Mkhristu aliyense ayenera kuti ali ndi mabuku a m’Baibulo amene amawakonda kwambiri. Ena amakonda Mauthenga Abwino chifukwa akawerenga zimene Yesu anachita amaphunzira makhalidwe a Yehova. (Yoh. 14:9) Pomwe ena amakonda mabuku a maulosi ngati Chivumbulutso chifukwa amafotokoza “zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.” (Chiv. 1:1) Ndiye palinso ena amene amakonda kwambiri Masalimo ndi Miyambo chifukwa muli malangizo othandiza. Zonsezi zikusonyeza kuti Baibulo ndi buku la anthu onse.

3, 4. (a) Kodi timaona bwanji zinthu zimene gulu limatulutsa? (b) Pa zinthu zimene timalandira, kodi zina amakonzera ndani?

3 Kuwonjezera pa Baibulo timakondanso zinthu zothandiza  kuphunzira Baibulo zimene gulu limatulutsa. Mwachitsanzo timayamikira kwambiri mabuku, timabuku, magazini komanso zinthu zina zimene timalandira. Zinthu zimenezi zimathandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, tikhale maso komanso kuti tikhale ndi ‘chikhulupiriro cholimba.’—Tito 2:2.

4 Pa zinthu zimene timalandirazi, zina amakonzera anthu monga achinyamata kapena makolo. Palinso magazini komanso zinthu zapawebusaiti yathu zimene amakonzera anthu omwe si Mboni. Zonsezi zimasonyeza kuti Yehova akukwaniritsa lonjezo lake lakuti ‘adzakonzera anthu a mitundu yonse phwando la zakudya zabwinozabwino.’—Yes. 25:6.

5. Kodi Yehova amayamikira tikamayesetsa kuchita chiyani?

5 Ambirife timaona kuti sitikhala ndi nthawi yokwanira yoti tiwerenge Baibulo komanso mabuku onse amene timalandira. Koma tiyenera kudziwa kuti Yehova amayamikira kwambiri tikamayesetsa ‘kugwiritsa ntchito bwino nthawi yathu’ powerenga Baibulo nthawi zonse komanso kuphunzira patokha. (Aef. 5:15, 16) N’zoona kuti sizophweka kuwerenga mwatsatanetsatane chilichonse chimene tingalandire. Komabe m’pofunika kusamala kwambiri pa nkhani imeneyi.

6. Kodi n’chiyani chingatilepheretse kuti tizipindula kwambiri ndi zinthu zonse zimene Yehova watipatsa?

6 Tiyenera kusamala kuti tisamalephere kuphunzira zinthu zina poganiza kuti mfundo zake sizikutikhudza. Mwachitsanzo, kodi munaganizapo kuti nkhani inayake ya m’Baibulo sikukukhudzani inuyo? Nanga mumatani mukaona kuti nkhani ina ya m’magazini kapena m’buku alembera gulu linalake la anthu? Kodi mumangoiwerenga patalipatali mwinanso osaiwerenga n’komwe? Ngati timachita zimenezi ndiye kuti sitingapindule. Ndiye kodi tingatani kuti zoterezi zisamatichitikire? M’pofunika kuti tizikumbukira kuti zinthu zimene timalandira ndi zochokera kwa Yehova. Paja Baibulo limati: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino.” (Yes. 48:17) M’nkhaniyi tikambirana mfundo zitatu zimene zingatithandize kuti tizipindula kwambiri tikamawerenga Baibulo komanso mabuku athu.

ZIMENE MUNGACHITE KUTI BAIBULO LIZIKUTHANDIZANI KWAMBIRI

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti nkhani iliyonse m’Baibulo ingatithandize?

7 Muziona kuti nkhani iliyonse ingakuthandizeni. Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti “malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Tim. 3:16) N’zoona kuti nkhani zina za m’Baibulo analembera anthu enaake kapena gulu linalake la anthu. Koma tiyenera kumaona kuti nkhani iliyonse ingatithandize. M’bale wina anati: “Ndikamawerenga Baibulo, ndimakumbukira kuti pali zinthu zambiri zimene ndingaphunzire pa nkhani iliyonse. Zimenezi zimandithandiza kuti ndizitha kupeza mfundo zatsopano.” Tisanayambe kuwerenga Baibulo, tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse nzeru zimene zingatithandize kumvetsa mfundo zomwe iyeyo akufuna kuti tiphunzire.—Ezara 7:10; werengani Yakobo 1:5.

Kodi mumapindula kwambiri ndi zimene mumaphunzira m’Baibulo? (Onani ndime 7)

8, 9. (a) Tikamawerenga Baibulo, kodi tiyenera kumadzifunsa mafunso ati? (b) Kodi mfundo zokhudza zimene akulu ayenera kuchita zikutiphunzitsa chiyani za Yehova?

8 Muzidzifunsa mafunso. Mukamawerenga nkhani inayake m’Baibulo, muzidzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi zimenezi zikundiphunzitsa chiyani za Yehova? Kodi mfundo zimenezi ndingazigwiritse ntchito bwanji pa  moyo wanga? Nanga ndingazigwiritse ntchito bwanji pothandiza ena? Tikamaganizira mafunso amenewa, Baibulo lingatithandize kwambiri. Mwachitsanzo, taganizirani zimene Malemba amanena kuti akulu azichita. (Werengani 1 Timoteyo 3:2-7.) Popeza kuti ambirife siife akulu, mwina tingamaganize kuti mfundo za m’lembali sizikutikhudza kwenikweni. Koma tikawerenga mavesiwa n’kudzifunsa mafunso aja tingaone kuti zikhoza kutithandiza. Tiyeni tiyese kukambirana m’njira imeneyi.

9 Kodi zimenezi zikundiphunzitsa chiyani za Yehova? Popereka malangizo a zimene akulu ayenera kuchita, Yehova akusonyeza kuti amafuna kuti anthu amene wawapatsa udindo azitsatira mfundo zake zapamwamba. Amafunanso kuti iwo azipereka chitsanzo chabwino ndipo adzayankha mlandu pa zimene amachitira mpingo “umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.” (Mac. 20:28) Yehova amafuna kuti anthu ake azisamalidwa bwino ndi abusa aang’ono. (Yes. 32:1, 2) Mfundo zimenezi zikutithandiza kudziwa kuti Yehova amatikonda kwambiri.

10, 11. (a) Tikamawerenga zimene m’bale angachite kuti ayenerere kukhala mkulu, kodi tingatani kuti mfundozo zitithandizenso ifeyo? (b) Nanga tingagwiritse ntchito bwanji mfundozi pothandiza ena?

10 Kodi mfundo zimenezi ndingazigwiritse ntchito bwanji pa moyo wanga? Nthawi zonse akulu ayenera kumadzifufuza kuti aone mbali zimene afunika kusintha mogwirizana ndi zimene Malemba amanena. M’bale amene “akuyesetsa kuti akhale woyang’anira” ayenera kuonetsetsa kuti akutsatira mfundozi pa moyo wake. (1 Tim. 3:1) Komanso Akhristu onse angaphunzirepo kanthu pamavesi amenewa chifukwa zambiri mwa mfundozi ndi zimene Yehova amafuna kuti tonse tizitsatira. Mwachitsanzo, Akhristu onse amafunika kukhala ololera ndiponso oganiza bwino. (Afil. 4:5; 1 Pet. 4:7) Akulu akakhala “zitsanzo kwa gulu la nkhosa,” timaphunzira zambiri kuchokera kwa iwo komanso ‘timatsanzira chikhulupiriro chawo.’—1 Pet. 5:3; Aheb. 13:7.

11 Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji mfundozi pothandiza ena? Tingagwiritse ntchito zimene Yehova amafuna kuti akulu azichita pothandiza anthu amene  timaphunzira nawo. Tingawasonyeze kuti akulu a Mboni za Yehova ndi osiyana kwambiri ndi atsogoleri a zipembedzo zina. Mfundo zimenezi zimatithandizanso kuzindikira ntchito yayikulu imene akulu amagwira mumpingo. Kuganizira zimenezi kumatilimbikitsa kuti ‘tiziwalemekeza.’ (1 Ates. 5:12) Ndiyeno tikamawalemekeza iwo amagwira ntchito yawo mosangalala.—Aheb. 13:17.

12, 13. (a) Pogwiritsa ntchito zinthu zofufuzira zomwe tili nazo, kodi tingafufuze mfundo ziti tikamaphunzira? (b) Kodi kudziwa zinthu zina zokhudza nkhani imene tikuphunzira kungatithandize bwanji? Perekani chitsanzo.

12 Muzifufuza Mfundo Zina. Mungagwiritse ntchito zinthu zofufuzira zomwe tili nazo kuti mupeze mayankho a mafunso awa:

  • Kodi ndani analemba zimenezi?

  • Analemba liti ndipo analembera kuti?

  • Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinkachitika pa nthawi yomwe zimenezi zinalembedwa?

Kudziwa mayankho a mafunsowa kungakuthandizeni kuti muphunzire zambiri pa nkhaniyo.

13 Mwachitsanzo, taganizirani zimene timawerenga pa Ezekieli 14:13, 14. Lembali limati: “Ngati dziko landichimwira pochita zosakhulupirika, ndidzalitambasulira dzanja langa n’kuthyola ndodo zake zimene amakolowekapo mikate yoboola pakati. Komanso ndidzalitumizira njala ndipo ndidzapha anthu ndi ziweto m’dzikolo. ‘Amuna atatu awa: Nowa, Danieli ndi Yobu, akanakhala m’dzikolo, iwo okhawo akanapulumutsa miyoyo yawo chifukwa chokhala olungama,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” Tikafufuza tingapeze kuti lembali linalembedwa m’chaka cha 612 B.C.E. Pa nthawiyo n’kuti patatha zaka mahandiredi angapo kuchokera pamene Nowa ndi Yobu anamwalira koma Yehova ankawakumbukirabe kuti anali okhulupirika. Koma pa nthawiyi n’kuti Danieli adakali moyo ndipo anali ndi zaka za m’ma 20. Komatu Yehova ankamuona kuti anali wokhulupirika mofanana ndi Nowa ndi Yobu. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Yehova amaona kukhulupirika kwa atumiki ake onse, ngakhalenso achinyamata.—Sal. 148:12-14.

MUZIWERENGA MABUKU KOMANSO MAGAZINI ONSE

14. Kodi zinthu zimene amalembera achinyamata zimawathandiza bwanji, nanga zingatithandizenso bwanji tonsefe? (Onani chithunzi patsamba 23.)

14 M’nkhaniyi taona kuti nkhani zonse zimene zili m’Baibulo zingatithandize. N’chimodzimodzi ndi zinthu zonse zimene gulu limatulutsa. Tiyeni tikambirane zitsanzo zochepa. Mabuku kapena nkhani za achinyamata. Posachedwapa, gulu lakhala likutulutsa mabuku kapena nkhani zambiri za achinyamata. [1] Zina zimawathandiza kuthana ndi mavuto amene amakumana nawo akamakula kapena akakhala kusukulu. Kodi nkhani zoterezi zingatithandize bwanji tonsefe? Tikamawerenga nkhani ngati zimenezi timazindikira mavuto amene achinyamata akukumana nawo. Tikatero tingathe kuwathandiza komanso kuwalimbikitsa.

15. N’chifukwa chiyani achikulirenso ayenera kuwerenga nkhani zimene gulu lalembera achinyamata?

15 Mavuto ena amene amafotokozedwa m’nkhani za achinyamata amachitikiranso munthu aliyense. Tonsefe timafunika kufotokoza zimene timakhulupirira, kudziletsa, kusatengera zochita za anzathu komanso kusankha bwino zosangalatsa ndi anthu ocheza nawo. Zinthu zonsezi zimafotokozedwa bwino m’nkhani zimene amalembera achinyamata. Ndiyeno kodi achikulire ayenera kuganiza  kuti akawerenga nkhani za achinyamata anyozeka? Ayi ndithu. N’zoona kuti nkhanizi zimalembedwa m’njira yoti ziwafike pa mtima achinyamata. Koma malangizo ake amachokera m’Baibulo ndipo akhoza kuthandiza munthu aliyense.

16. Kodi mabuku athu amathandiza bwanji achinyamata?

16 Nkhani zimene amalembera achinyamata zimawathandizanso kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Yehova. (Werengani Mlaliki 12:1, 13.) Zimenezi n’zofunikanso kwa anthu akuluakulu. Mwachitsanzo, mu Galamukani! ya April 2009 munali nkhani yakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Ndingatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzindisangalatsa?” Nkhaniyi inapereka mfundo zingapo zothandiza ndipo munali pepala loti tidule n’kusunga m’Baibulo kuti tiziligwiritsa ntchito. Nkhaniyi sinathandize achinyamata okha. Mwachitsanzo, mayi wina anati: “Poyamba ndinkavutika kuti ndiziwerenga Baibulo. Koma nditatsatira malangizo amene ali m’nkhaniyi, ndinayamba kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Ndinadula pepala lomwe linali m’nkhaniyi n’kusunga. Ndimaona kuti mabuku a m’Baibulo ndi ogwirizana ndipo analembedwa mosangalatsa kwambiri. Panopa kuwerenga Baibulo kumandisangalatsa kwabasi.”

17, 18. Kodi zinthu zimene amakonzera anthu omwe si Mboni zimatithandiza bwanji ifeyo? Perekani chitsanzo.

17 Zinthu zimene amakonzera anthu omwe si Mboni. Kuyambira mu 2008 tinayamba kulandira Nsanja ya Olonda yophunzira imene amalembera a Mboni za Yehovafe. Koma tilinso ndi magazini ogawira. Kodi magazini amenewa angatithandizenso ifeyo? Inde. Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti mutafika pamisonkhano, mwaona kuti munthu amene munamuitana wabwera ndipo mukusangalala kwambiri ndi zimenezi. Pamene m’bale akukamba nkhani ya onse mukuganizira mmene mfundo zake zingathandizire mlendo wanuyo. Izi zikukuthandizani kuona kuti nkhaniyo inali yothandiza kwambiri.

18 Zoterezi n’zimene zingachitikenso tikamawerenga zinthu zimene amakonzera anthu omwe si Mboni. Mwachitsanzo, magazini ogawira a Nsanja ya Olonda amafotokoza nkhani m’njira yoti anthu omwe si Mboni azimvetse. N’chimodzimodzinso ndi nkhani zambiri zimene zimapezeka pawebusaiti yathu ya jw.org/ny monga zakuti, “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” ndi zakuti, “Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri.” Nkhani zimenezi zimatithandiza kuti tizikonda choonadi komanso tizimvetsa bwino mfundo za m’Baibulo. Zimatithandizanso kuphunzira njira zatsopano zofotokozera zimene timakhulupirira tikakhala mu utumiki. Nawonso magazini a Galamukani! amatithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri kuti kuli Mulungu. Amatithandizanso kuti tizitha kufotokoza bwino zimene timakhulupirira.—Werengani 1 Petulo 3:15.

19. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zinthu zimene Yehova amatipatsa?

19 M’nkhaniyi taona kuti Yehova watipatsa zinthu zambiri zomwe zingatithandize kupeza ‘zosowa zathu zauzimu.’ (Mat. 5:3) Tiyeni tipitirize kugwiritsa ntchito zinthu zonsezi. Tikamatero timasonyeza kuti timayamikira Yehova amene ‘amatiphunzitsa kuti zinthu zitiyendere bwino.’—Yes. 48:17.

^ [1] (ndime 14) Apa tikunena zinthu monga buku lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa buku loyamba ndi lachiwiri komanso nkhani zakuti, Zimene Achinyamata Amadzifunsa zomwe zimapezeka pa Intaneti.