Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Likusinthabe Moyo Wanu?

Kodi Baibulo Likusinthabe Moyo Wanu?

“Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.”—AROMA 12:2.

NYIMBO: 61, 52

1-3. (a) Kodi ndi makhalidwe ati amene tingavutike kusintha ngakhale kuti tinabatizidwa? (b) Nanga ndi mafunso ati amene tingamadzifunse tikamavutika kusintha? (Onani chithunzi pamwambapa.)

POYAMBA munthu wina dzina lake Kevin [1] ankakonda kutchova juga, kusuta, kuledzera komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza ubongo. Koma ataphunzira Baibulo ankafuna kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Kuti zimenezi zitheke anafunika kusiya makhalidwe oipawo. Kevin anadalira Yehova komanso Mawu ake kuti amuthandize ndipo anasinthadi.—Aheb. 4:12.

2 Kevin atabatizidwa ankafunika kupitirizabe kusintha zinthu zina kuti akhale Mkhristu wabwino. (Aef. 4:31, 32) Mwachitsanzo, ankafunika kusintha khalidwe lake losachedwa kupsa mtima ndipo kuchita zimenezi sikunali kophweka. Kevin anati: “Ndinavutika kwambiri kuti ndiyambe kuugwira mtima, kusiyana  ndi mmene ndinavutikira kusiya makhalidwe anga oipa aja.” Kevin ankaphunzira Baibulo mwakhama komanso kupemphera ndipo izi zinamuthandiza kuti asinthe.

3 Ambirife tinasinthanso zinthu zambiri tisanabatizidwe. Tinachita zimenezi kuti moyo wathu uzigwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Komabe n’kutheka kuti pali zinthu zina zing’onozing’ono zomwe tiyenera kusintha kuti tizitha kutsanzira kwambiri Mulungu ndi Yesu. (Aef. 5:1, 2; 1 Pet. 2:21) Mwachitsanzo, mwina ndife ovuta, timaopa anthu komanso mwina timachita miseche. Kodi mukuona kuti zikukuvutani kwambiri kusintha makhalidwe ngati amenewa? Ngati ndi choncho, mwina mumadzifunsa kuti, ‘Ine ndinasintha zinthu zikuluzikulu ndiye ititi tikundivuta bwanji? Nanga ndingatani kuti Baibulo lizisinthabe moyo wanga?’

N’ZOTHEKA KUKONDWERETSA MULUNGU

4. N’chifukwa chiyani nthawi zina timalephera kuchita zinthu zokondweretsa Yehova?

4 Akhristufe timakonda Yehova ndipo timafunitsitsa kuchita zomusangalatsa. Koma popeza ndife ochimwa, nthawi zina timalephera kuchita zimenezi. Tingamamve ngati mmene mtumwi Paulo ankamvera. Iye anati: “Ndimafuna kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita.”—Aroma 7:18; Yak. 3:2.

5. Kodi tiyenera kuti tinasiya zinthu ziti tisanabatizidwe, koma tingamavutikebe ndi zinthu ngati ziti?

5 Tiyenera kuti tinasiya machimo akuluakulu omwe akanatilepheretsa kukhala mumpingo wachikhristu. (1 Akor. 6:9, 10) Komabe si ife angwiro. Choncho nthawi ndi nthawi tikhoza kumalakalaka zinthu zoipa kapena kuvutika kudziletsa khalidwe linalake. Tingapitirizebe kulimbana ndi mavuto ngati amenewa kwa zaka zambiri.—Akol. 3:9, 10.

6, 7. (a) Kodi n’chiyani chimatithandiza kuti tikhale pa ubwenzi ndi Yehova ngakhale kuti si ife angwiro? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kupempha Yehova kuti azitikhululukira?

6 Ngakhale kuti si ife angwiro,tingathe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova komanso kum’tumikira. Taganizirani izi: Pamene Yehova ankatikoka kuti tikhale naye pa ubwenzi, ankadziwa kuti tizilakwitsa zinthu zina. (Yoh. 6:44) Popeza Mulungu amatidziwa bwino komanso amadziwa zimene zili mumtima mwathu, ayeneranso kuti ankadziwa zinthu zimene zidzativute kusintha. Ankadziwanso kuti nthawi zina tingachite tchimo. Komabe zimenezi sizinamulepheretse kuti atikoke kukhala anzake.

7 Mulungu amatikonda kwambiri ndipo anatipatsa mphatso yamtengo wapatali. Iye anatumiza Mwana wake padziko lapansi kuti adzapereke moyo wake ngati nsembe ya dipo. (Yoh. 3:16) Tikalakwa n’kupempha kuti Yehova atikhululukire, amagwiritsa ntchito nsembe imeneyi ndipo tingathe kukhalabe naye pa ubwenzi. (Aroma 7:24, 25; 1 Yoh. 2:1, 2) Sitiyenera kukayikira mphamvu ya nsembeyi n’kumadzionabe ngati ochimwa kwambiri moti Mulungu sangatikhululukire. Kuchita zimenezi kungakhale ngati kukana madzi osamba m’manja chonsecho m’manja mwathu ndi mwakuda. Tisaiwale kuti nsembe ya dipo inaperekedwa kuti izithandiza anthu ochimwa amene alapa. Choncho timayamikira kwambiri Yehova pa zimene anachitazi chifukwa zimatithandiza kuti tikhale naye pa ubwenzi ngakhale kuti timalakwitsa zinthu zina.—Werengani 1 Timoteyo 1:15.

8. N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza zolakwa zathu?

8 Komabe, sitiyenera kunyalanyaza zolakwa zathu kapena kumangodzikhululukira. Kuti  tipitirize kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, tiyenera kukhala ndi makhalidwe amene iye amafuna. (Sal. 15:1-5) Tiyeneranso kuyesetsa kuti tizimutsanzira kwambiri ndiponso kutsanzira Khristu. Tifunikanso kusintha makhalidwe olakwika amene tingakhale nawo. Kaya tabatizidwa kumene kapena tinabatizidwa kalekale, tiyenera ‘kupitirizabe kusintha maganizo athu.’—2 Akor. 13:11.

9. Kodi tikudziwa bwanji kuti kuvala umunthu watsopano kuyenera kuchitika mopitirizabe?

9 Pamafunika khama kuti munthu ‘asinthe maganizo’ ndi “kuvala umunthu watsopano.” Paulo anakumbutsa Akhristu anzake kuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale, umenenso ukuipitsidwa malinga ndi zilakolako zonyenga za umunthuwo. Ndipo munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.” (Aef. 4:22-24) Mawu akuti “mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu,” akusonyeza kuti kuvala umunthu watsopano kuyenera kuchitika mopitirizabe. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri chifukwa zikusonyeza kuti kaya takhala tikutumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tingathe kumasinthabe n’kumavala umunthu watsopano. Baibulo lingatithandize kuti tipitirize kusintha n’kumatsanzira kwambiri Mulungu.

N’CHIFUKWA CHIYANI ZIMATIVUTA KUSINTHA?

10. Kodi timafunika kuchita chiyani kuti Baibulo lipitirizebe kutisintha, nanga tingamadzifunse mafunso ati?

10 Tiyenera kuchita khama kuti Mawu a Mulungu apitirize kusintha moyo wathu. Komano n’chifukwa chiyani zimativuta kusintha? Nanga n’chifukwa chiyani Yehova sanachititse kuti tisamavutike kuchita zimenezi? Kodi sizingatheke kuti Yehova angosintha mmene timaganizira kuti tisamavutike kuchita zimene amafuna?

11-13. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizichita khama kusintha makhalidwe oipa?

11 Zinthu zimene zili m’chilengedwechi zimasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire. Mwachitsanzo, analenga dzuwa lomwe ndi lamphamvu kwambiri. Pasekondi iliyonse dzuwa limatulutsa kuwala kwambiri ndi kutentha kosaneneka. Komabe kuti padzikoli pakhale zamoyo pamangofunika kuwala ndi kutentha kochepa chabe. (Sal. 74:16; Yes. 40:26) Yehova amaperekanso mphamvu kwa atumiki ake. (Yes. 40:29) Izi zikusonyeza kuti iye akanatha kumatipatsa mphamvu kuti tisamavutike kusintha makhalidwe oipa komanso kuti tisamachite kumva nkhwangwa ili m’mutu. Koma n’chifukwa chiyani sachita zimenezi?

12 Yehova anatilenga ndi ufulu woti tizisankha tokha zochita. Choncho tikasankha kutumikira Yehova n’kumayesetsa kuchita zimene amafuna, timasonyeza kuti timamukonda kwambiri ndipo timafunitsitsa kumusangalatsa. Timasonyezanso kuti timafuna kuti azitilamulira. Satana anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira. Choncho Yehova amayamikira kwambiri tikamamumvera mwa kufuna kwathu chifukwa timasonyeza kuti tili kumbali yake. (Yobu 2:3-5; Miy. 27:11) Koma akanapanda kulola kuti tizichita khama posintha makhalidwe oipa, sizikanadziwika kuti timasankha tokha kukhala kumbali yake.

13 Yehova amatiuza kuti ‘tiziyesetsa mwakhama’  kutsanzira makhalidwe ake. (Werengani 2 Petulo 1:5-7; Akol. 3:12) Amafunanso kuti tizichita khama kulamulira maganizo ndi mtima wathu. (Aroma 8:5; 12:9) Tikakwanitsa kuchita zimenezi timasangalala kwambiri chifukwa timadziwa kuti Baibulo likusinthabe moyo wathu.

MAWU A MULUNGU APITIRIZE KUKUSINTHANI

14, 15. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale ndi makhalidwe abwino? (Onani bokosi lakuti, “ Kuphunzira Baibulo Komanso Pemphero Zinawathandiza Kusintha.”)

14 Kodi tingatani kuti tikhale ndi makhalidwe abwino komanso kuti tizisangalatsa Yehova? Nkhani si yongochita khama kusintha zinthu zimene timalakwitsa. Tiyenera kuyesetsa kutsatira malangizo a Yehova. Paja lemba la Aroma 12:2 limati: “Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” Yehova amagwiritsa ntchito Mawu ake komanso mzimu wake potithandiza kudziwa zimene amafuna ndiponso kusintha moyo wathu n’kumachita zimene amafunazo. Choncho tiziwerenga Baibulo tsiku lililonse, kuganizira kwambiri zimene tawerengazo komanso kupempha mzimu woyera. (Luka 11:13; Agal. 5:22, 23) Tikamatsogoleredwa ndi mzimu woyera komanso kuyesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionera, zoganiza zathu, mawu athu komanso zochita zathu zimakhala zabwino. Koma ngakhale titafika pamenepa, tiyenera kusamalabe kuti tisayambirenso kuchita makhalidwe olakwika amene tinasiya.—Miy. 4:23.

Ena amatolera malemba ndiponso nkhani za m’magazini zogwirizana ndi vuto lawo n’kumaziwerenga pafupipafupi (Onani ndime 15)

15 Chinthu china chofunikanso n’kuwerenga mabuku athu. Akhristu ena amaona kuti zimawathandiza akatolera malemba ndiponso nkhani za m’magazini zokhudza vuto lawo n’kumaziwerenga pafupipafupi kuti akhale ndi makhalidwe abwino komanso athetse vuto lawolo.

16. N’chifukwa chiyani sitiyenera kutaya mtima ngati tikuona kuti zikutivuta kusintha?

16 Ngati tikuona kuti zikutivuta kusintha, tisataye mtima chifukwa zimatenga nthawi ndithu. Paja nkhani yovala umunthu watsopano siitha. Tiyenera kukhala oleza mtima n’kumalola kuti Baibulo lizitithandiza kusintha. Mwina poyamba zingamativute kwambiri kuti tizichita zimene Baibulo limanena. Koma pang’ono ndi pang’ono tingayambe kuganiza komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu amafuna.—Sal. 37:31; Miy. 23:12; Agal. 5:16, 17.

 MUZIGANIZIRA MMENE ZINTHU ZIDZAKHALIRE M’TSOGOLO

17. Tikakhala okhulupirika kwa Yehova, kodi tingayembekezere zotani?

17 Anthu a Yehova okhulupirika adzakhala angwiro n’kumamutumikira mpaka kalekale. Pa nthawi imeneyo, zidzakhala zosavuta kusonyeza makhalidwe abwino. Panopa timayamikira kwambiri kuti Yehova anapereka dipo la Yesu ndipo izi zimatithandiza kuti tizitha kumutumikira. Ngakhale kuti si ife angwiro, tikhoza kusangalatsa Mulungu tikamalola kuti Mawu ake atisinthe.

18, 19. Kodi tingatsimikize bwanji kuti Baibulo lili ndi mphamvu yotha kusintha munthu?

18 Kevin yemwe tam’tchula poyambirira uja, anayesetsa kuti asinthe khalidwe lake lopsa mtima msanga. Iye ankaganizira ndiponso kutsatira mfundo za m’Baibulo komanso malangizo ochokera kwa Akhristu anzake. Patadutsa zaka zingapo, Kevin anasintha kwambiri. Kenako anakhala mtumiki wothandiza ndipo tsopano wakhala akutumikira monga mkulu kwa zaka 20. Ngakhale zili choncho, iye amayesetsa kuti vuto lake lija lisayambirenso.

19 Zimene zinachitikira Kevin, zikusonyeza kuti Baibulo limathandiza anthu kusintha moyo wawo. Choncho, tiyeni tizilola kuti Mawu a Mulungu apitirize kutisintha komanso kutithandiza kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. (Sal. 25:14) Yehova adzatidalitsa tikamayesetsa kusintha makhalidwe olakwika. Zikatere, timaona umboni woti Baibulo limathandizadi anthu kusintha moyo wawo.—Sal. 34:8.

^ [1] (ndime 1) Dzinali lasinthidwa.