Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumathetsa Nkhani Mwachikondi Mukasemphana Maganizo?

Kodi Mumathetsa Nkhani Mwachikondi Mukasemphana Maganizo?

“Sungani mtendere pakati panu.”—MALIKO 9:50.

NYIMBO: 39, 77

1, 2. (a) Kodi buku la Genesis limafotokoza za anthu ati amene anasemphana maganizo? (b) N’chifukwa chiyani nkhanizi zinalembedwa m’Baibulo?

BAIBULO limafotokoza za anthu ena amene anasemphana maganizo. Mwachitsanzo, machaputala oyambirira a buku la Genesis amanena za Kaini ndi Abele. (Gen. 4:3-8) Nayenso Lameki anapha munthu amene anamumenya. (Gen. 4:23) Komanso abusa a Abulahamu (Abulamu) ndi a Loti anakangana. (Gen. 13:5-7) Hagara ankanyoza Sara (Sarai) ndipo Sarayo anakwiyira Abulahamu. (Gen. 16:3-6) Baibulo linaneneratunso kuti dzanja la Isimaeli lidzalimbana ndi aliyense ndipo dzanja la aliyense lidzalimbana ndi la Isimaeli.—Gen. 16:12.

2 N’chifukwa chiyani nkhani zimenezi zinalembedwa m’Baibulo? Chifukwa china n’chakuti nkhani zoterezi zimatithandiza kumvetsa ubwino woyesetsa kukhala mwamtendere ndi ena. Timapindula kwambiri tikamaphunzira m’Baibulo za anthu amene analimbana ndi mavuto enaake. Timaona zimene anachita komanso mmene zingatithandizire tikakumana ndi mavuto ofanana ndi amene anakumana nawo. Mwachidule tingati timadziwa  zoyenera kuchita ndi zoyenera kupewa tikasemphana maganizo.—Aroma 15:4.

3. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

3 M’nkhaniyi tikambirana ubwino wothetsa kusamvana komanso mmene tingachitire zimenezo. Tikambirananso mfundo za m’Malemba zimene zingatithandize kuthetsa kusamvana n’cholinga choti tikhale pa mtendere ndi anzathu komanso ndi Yehova Mulungu.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUTHETSA KUSAMVANA?

4. Kodi anthu ambiri ali ndi maganizo ati ndipo zotsatira zake n’zotani?

4 Satana ndi amene amachititsa kuti anthu azisemphana maganizo. M’munda wa Edeni, iye anayambitsa maganizo oti munthu aliyense ayenera kumasankha yekha zochita, kaya zabwino kapena zoipa popanda kutsogoleredwa ndi Mulungu. (Genesis 3:1-5) Maganizo amenewa abweretsa mavuto ambiri. Dziko lapansi ladzaza ndi anthu onyada, odzikuza komanso okonda mpikisano. Anthu oterewa akutsogoleredwa ndi Satana yemwe amafuna kuti tizichita zinthu mosaganizira anthu ena. Zimenezi zimachititsa kuti anthu azidana komanso azikangana. Tizikumbukira zimene Baibulo limanena kuti: “Munthu wokonda kukwiya amayambitsa mkangano, ndipo aliyense wokonda kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.”—Miy. 29:22.

5. Kodi Yesu anapereka malangizo otani othandiza kupewa mikangano?

5 Koma Yesu anaphunzitsa kuti tiziyesetsa kukhala mwamtendere zivute zitani. Pa ulaliki wapaphiri, iye anapereka malangizo abwino kwambiri othandiza kuti tizipewa kukangana. Mwachitsanzo, anauza ophunzira ake kuti ayenera kukhala ofatsa komanso okonda mtendere. Anawauzanso kuti azipewa kupsa mtima, azithetsa mwamsanga kusamvana komanso azikonda adani awo.—Mat. 5:5, 9, 22, 25, 44.

6, 7. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuthetsa mwamsanga kusamvana? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?

6 Ngati sitingakhale mwamtendere ndi anthu ena, zinthu zimene timachita potumikira Yehova monga kupemphera, kusonkhana ndi kulalikira zimakhala zopanda phindu. (Maliko 11:25) Sitingathe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova ngati sitikhululukira anzathu.—Werengani Luka 11:4; Aefeso 4:32.

7 Mkhristu aliyense ayenera kudzifufuza kuti aone ngati amakhululukadi komanso kukhala mwamtendere ndi ena. Kodi ena akakulakwirani mumawakhululukira ndi mtima wonse? Nanga mumayambanso kucheza nawo ngati kale? Yehova amafuna kuti atumiki ake azikhululukira ena. Ngati mukuona kuti pali zimene muyenera kusintha, pemphani Yehova kuti akuthandizeni ndipo iye adzayankha pemphero lanulo.—1 Yoh. 5:14, 15.

KODI NDI NKHANI YOTI MUNGATHE KUNGOINYALANYAZA?

8, 9. Kodi tiyenera kuchita chiyani munthu wina akatilakwira?

8 Popeza tonsefe si angwiro, nthawi zina munthu wina angachite kapena kulankhula zinthu zimene zingatikhumudwitse ndipo izi n’zosapeweka. (Mlal. 7:20; Mat. 18:7) Ndiye kodi mungatani zoterezi zikachitika? Taganizirani chitsanzo ichi: Pamene abale ndi alongo ena anali pakaphwando, mlongo wina anapereka moni kwa abale ena awiri. Kenako m’bale winayo anauza mnzakeyo kuti sanasangalale ndi zimene mlongo uja anachita popereka moniyo. Komabe mnzakeyo anam’kumbutsa zoti mlongoyo wakhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka 40 ndipo ayenera kuti analibe cholinga chomukhumudwitsa.  Atakambirana kwakanthawi, m’baleyu anavomereza kuti mnzakeyo akunenadi zoona. Choncho anaona kuti ndi bwino angoinyalanyaza nkhaniyo.

9 Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo chimenechi? Anthu ena akachita kapena kulankhula zotikhumudwitsa, tingasankhe kungozinyalanyaza. Munthu wachikondi amakhululuka anthu ena akamulakwira. (Werengani Miyambo 10:12; 1 Petulo 4:8.) Yehova amaona kuti munthu amene ‘amanyalanyaza cholakwa’ ndi “wokongola.” (Miy. 19:11; Mlal. 7:9) Choncho munthu akakulakwirani muzidzifunsa kuti, ‘Kodi n’zotheka kungoinyalanyaza nkhaniyi, kapena pakufunika kuti tikambirane?’

10. (a)Kodi mlongo wina anatani anthu ena atamunenera zoipa? (b) Kodi ndi mfundo iti ya m’Malemba imene inamuthandiza?

10 Koma zimakhala zovuta ngati ena alankhula zotinyoza. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira mpainiya wina amene tangomutchula kuti Lucy. Abale ndi alongo ena ankanena zoipa zokhudza utumiki wake komanso zimene amachita. Lucy anakhumudwa kwambiri ndi zimenezi ndipo anapempha malangizo kwa abale olimba mwauzimu. Iye anati: “Malangizo a m’Malemba amene anandipatsa anandithandiza kuti ndisadane ndi anthuwo komanso ndizindikire kuti kukondweretsa Yehova ndiye kofunika.” Lemba limene linamuthandiza kwambiri Lucy ndi la Mateyu 6:1-4. (Werengani.) Lembali linamulimbikitsa kuti aziyesetsa kukondweretsa Yehova. Lucy anati: “Anthu akamanena zoipa zokhudza utumiki wanga, ine ndimakhalabe wosangalala chifukwa ndikudziwa kuti ndikuyesetsa kusangalatsa Yehova.” Pamapeto pake, Lucy anaganiza kuti angoinyalanyaza nkhaniyo.

MUNGATANI NGATI NKHANIYO NDI YAIKULU?

11, 12. (a)Kodi tiyenera kuchita chiyani tikazindikira kuti m’bale wathu ‘ali nafe chifukwa?’ (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Abulahamu anachita? (Onani chithunzi patsamba 3.)

11 Baibulo limanena kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yak. 3:2) Tiyerekeze kuti mwazindikira kuti m’bale wina wakhumudwa chifukwa cha zimene munalankhula kapena kuchita. Kodi mungatani? Yesu anati: “Ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba, ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.” (Mat. 5:23, 24) Malinga ndi zimene Yesu ananenazi, chofunika n’kukambirana ndi munthuyo. Koma kodi cholinga pokambiranapo chizikhala chiyani? Cholinga si kumuchititsa munthuyo kuona kuti nayenso analakwitsa koma kuvomereza zimene mwalakwitsa n’kukhazikitsa mtendere. Chifukwatu chofunika kwambiri n’kukhala pa mtendere ndi Akhristu anzathu.

12 Nkhani ya Abulahamu ndi Loti imene taitchula poyamba ija ingatithandize kuti tizipewa mikangano. Anthu awiriwa anali ndi ziweto ndipo abusa awo ankakanganira malo odyetsera ziwetozo. Pofuna kupewa mkangano, Abulahamu anauza Loti kuti ayambe kusankha malo amene angakonde kukhala ndi banja lake. (Gen. 13:1, 2, 5-9) Apatu Abulahamu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri. Iye sanaganizire zofuna zake koma ankangofuna kukhazikitsa mtendere. Kodi iye anavutika chifukwa chopereka mwayi kwa Loti woti asankhe malowo? Ayi ndithu. Izi zitangochitika, Yehova analonjeza Abulahamu kuti  adzamudalitsa kwambiri. (Gen. 13:14-17) Yehova sangalole kuti mtumiki wake avutike kwambiri chifukwa choti watsatira mfundo za m’Malemba pothetsa kusamvana. [1]

13. Kodi woyang’anira wina anatani atalankhulidwa mawu achipongwe, nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani?

13 Tiyeni tikambiranenso chitsanzo china cha m’nthawi yathu ino. M’bale wina atangoyamba kuyang’anira ntchito zosiyanasiyana zapamsonkhano wachigawo, anapempha m’bale wina ngati angadzipereke kugwira ntchito inayake. Koma m’baleyo anamuyankha mwachipongwe n’kudula foni. Anachita izi chifukwa choti anakwiya ndi zimene woyang’anira msonkhano woyamba anachita. Woyang’anira watsopanoyu sanakwiye naye koma sanangoisiyanso nkhaniyo. Patapita ola limodzi anaimbanso foni n’kumuuza m’baleyo kuti sanakumanepo naye ndipo anamupempha kuti akumane n’kukambirana nkhaniyo. Patangodutsa mlungu umodzi anthuwa anakumana pa Nyumba ya Ufumu. Iwo anayamba ndi pemphero kenako anakambirana kwa ola lathunthu. M’baleyo anafotokoza zonse zimene zinachitika m’mbuyomo. Woyang’anira watsopanoyo anamvetsera mwachifundo ndipo anakambirana ndi m’baleyo mfundo za m’Malemba. Kenako awiriwa anasiyana, aliyense ali wosangalala. M’baleyo anavomera kutumikira pamsonkhanowo ndipo anathokoza kwambiri woyang’anirayo chifukwa chochita zinthu modekha komanso mokoma mtima.

KODI N’ZOYENERA KUUZA AKULU?

14, 15. (a) Kodi ndi zochitika ziti pamene tingatsatire malangizo a pa Mateyu 18:15-17? (b) Kodi Yesu anatchula zinthu zitatu ziti zimene tiyenera kuchita, nanga cholinga chathu chiyenera kukhala chiyani?

14 Nthawi zambiri nkhani zimene Akhristu  amasemphana maganizo zimakhala zoti angazithetse paokha. Koma Yesu ananenanso kuti nkhani zina n’zofunika kuuza mpingo. (Werengani Mateyu 18:15-17.) Komano kodi chingachitike n’chiyani ngati munthu wolakwayo sakuvomereza kuti walakwa pamaso pa m’bale wakeyo, mboni za nkhaniyo komanso mpingo? Malinga ndi lembali, munthuyo ayenera kuonedwa ngati “wochokera mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.” Masiku ano tinganene kuti munthuyo ayenera kuchotsedwa mumpingo. Nkhani yotereyi iyenera kukhala yaikulu osati kungosemphana maganizo ndi munthu wina. Mwina ingakhale yokhudza chinyengo kapena miseche imene inaipitsa mbiri ya munthu wina. Koma ngati nkhaniyo ili yokhudza machimo aakulu monga chigololo, kugonana pakati pa amuna kapena akazi okhaokha, mpatuko komanso kulambira mafano tiyenera kudziwitsa akulu.

Nthawi zina kuti tibweze m’bale wathu pangafunike kukambirana naye kangapo (Onani ndime 15)

15 Cholinga cha malangizo a Yesuwa ndi kuthandiza mwachikondi munthu wolakwayo. (Mat. 18:12-14) Choyamba, muyenera kuyesetsa kuthetsa nkhaniyo pa awiri. Nthawi zina pangafunike kukambirana nkhaniyo kangapo. Ngati zimenezi zalephereka, mungaitane mboni kapena anthu ena amene angathandize kuona ngati munthuyo analakwadi. Munthuyo akavomereza kulakwa kwake, ndiye kuti ‘mwabweza m’bale wanuyo.’ Muyenera kupititsa nkhaniyo kwa akulu pokhapokha ngati mwayesetsa kuchita zonsezi koma sizinathandize.

16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kutsatira malangizo a Yesu pothetsa kusamvana n’kothandiza komanso kumasonyeza chikondi?

16 Si nthawi zambiri pamene nkhani zoterezi zimafika poti munthu n’kuchotsedwa. Nkhani zambiri zimatha anthu atangokambirana pa awiri kapena ndi mboni zina. Nthawi zambiri munthu amazindikira kulakwa kwake n’kusintha. Zikatere wolakwiridwayo amaona kuti palibenso chifukwa choikokera nkhaniyo choncho amangokhululuka. Malinga ndi zimene Yesu ananena, si bwino kufulumira kuuza akulu nkhani yoti simunakambirane. Akulu ayenera kuuzidwa pokhapokha ngati mwatsatira kale mfundo ziwiri zija komanso ngati pali umboni wosonyeza kuti nkhaniyo inachitikadi.

17. Tikamayesetsa kukhala mwamtendere ndi Akhristu anzathu, kodi zotsatira zake zimakhala zotani?

17 N’zodziwikiratu kuti kusemphana maganizo sikungalephere popeza anthufe si angwiro. M’pake kuti Yakobo analemba kuti: “Ngati wina sapunthwa pa mawu, ameneyo ndi munthu wangwiro, ndipo akhoza kulamuliranso thupi lake lonse.” (Yak. 3:2) Pakakhala kusamvana tiyenera ‘kufunafuna mtendere ndi kuusunga.’ (Sal. 34:14) Izi zingathandize kuti tizikhala bwino ndi Akhristu anzathu komanso kuti mumpingo mukhale mgwirizano. (Sal. 133:1-3) Koma chofunika kwambiri n’chakuti tidzakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, yemwe ndi “Mulungu amene amapatsa mtendere.” (Aroma 15:33) Zonsezi zimatheka ngati timayesetsa kuthetsa nkhani mwachikondi.

^ [1] (ndime 12) Anthu ena amene anathetsa kusamvana mwamtendere ndi awa: Yakobo ndi Esau (Gen. 27:41-45; 33:1-11); Yosefe ndi abale ake (Gen. 45:1-15); ndiponso Gidiyoni ndi anthu a ku Efuraimu. (Ower. 8:1-3) Komanso mwina mukudziwa zitsanzo zina za m’Baibulo za nkhani ngati zimenezi.